Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 11/15 tsamba 10-14
  • Chitani Zonse Chifukwa cha Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitani Zonse Chifukwa cha Uthenga Wabwino
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuthandiza Ayuda Odzichepetsa
  • Kufuna Kupindula Akunja
  • Ongolerani Maluso Anu a Kulalikira
  • Chitsanzo kwa Amishonale
  • Akristu ndi Dziko la Anthu
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kukhala Atumiki Opita Patsogolo ndi Otha Kusintha
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mmene Akristu Oyambirira Anachitira ndi Chilamulo cha Mose
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 11/15 tsamba 10-14

Chitani Zonse Chifukwa cha Uthenga Wabwino

“Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.”​—1 AKORINTO 9:23.

1. Kodi ndi chokhoterero chotani chimene chili chofala kwa tonsefe, koma kodi Mulungu wapereka maziko otani?

NGAKHALE kuti timasiyana m’njira zosiyanasiyana, tonsefe tiri ndi chikhoterero chimodzi. Kupyolera mwa choloŵa cha kwa Adamu, tinabadwa ochimwa otalikirana ndi Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova. (Aroma 5:12; Akolose 1:21) Monga mmene mtumwi Wachikristu Paulo analembera kuti: “Onse anachimwa napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Chotero, kuti apeze chipulumutso, anthu a mtundu ndi fuko lirilonse afunikira kugwirizanitsidwa kwa Mulungu. Ndipo tingakhale oyamikira chotani kuti ndi chikondi ndi chifundo chosayerekezeka, Yehova wapereka maziko a kuyanjanitsidwa kwa iye!

2. (a) Kodi ndi utumiki wotani umene unaikiziridwa kwa Akristu odzozedwa? (b) Kodi tingaphunzire kuchokera m’chitsanzo cha yani, ndipo nchifukwa ninji? (1 Akorinto 11:1)

2 Zaka mazana khumi ndi asanu ndi zinayi zapitazo, mboni zodzozedwa za Yehova zinaikiziridwa ndi “utumiki wa chiyanjanitso.” Paulo anatero kuti: “Tiumiriza inu m’malo mwa Kristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.” (2 Akorinto 5:18-20) Kodi mtumwiyo anatenga utumikiwo ndi mkhalidwe wotani? Iye ananena kuti: “Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadziloŵetsa ndekha ukapolo kwa onse kuti ndipindule ochuluka.” (1 Akorinto 9:19) Mosakaikira, Paulo anapanga kuyesayesa kwakhama kupereka uthenga wake m’njira yokhutiritsa, popeza kuti ananenanso kuti: “Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.” (1 Akorinto 9:23) Chotero, kodi tingaphunzirenji m’chitsanzo cha Paulo?

Kuthandiza Ayuda Odzichepetsa

3. Kodi kufunitsitsa kwa Paulo kwa kuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino kunasonyezedwa motani m’chigwirizano ndi Timoteo ndi Ayuda?

3 Chiyambi Chachiyuda cha Paulo ndi kufunitsitsa kwake kwa kuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino kunamukonzekeretsa kuthandiza Ayuda odzichepetsa kulandira Yesu monga Mesiya. Mwachitsanzo, lingalirani zimene mtumwiyo anachita pamene anasankha Timoteo monga mnzake woyenda naye. Timoteo, amene atate ake anali Mgriki, sanali wodulidwa monga mmene ana aamuna Achiyuda analiri. (Levitiko 12:2, 3) Paulo anadziŵa kuti Ayuda angakhumudwe ngati mwamuna wachichepere wosadulidwa anayesera kuŵathandiza kuti ayanjanitsidwe kwa Mulungu. Chotero, kotero kuti Ayuda owona mtima asatsekerezedwe kulandira Yesu, kodi Paulo anachitanji? Iye “anamtenga [Timoteo] namdula chifukwa cha Ayuda.” Izi zinachitidwa ngakhale kuti kudulidwa sikunali chiyeneretso Chachikristu.​—Machitidwe 16:1-3.

4. Molingana ndi 1 Akorinto 9:20, kodi nchiyani chimene chinali cholinga cha Paulo?

4 Chotero chinali chifukwa chakuti Paulo anali kuchita zinthu chifukwa cha uthenga wabwino pamene anasonyeza kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka Ayuda anzake. Iye analemba kuti: “Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo.” (1 Akorinto 9:20) Inde, monga mmene zasonyezedwera mu nkhani ya Timoteo, Paulo anachita zomwe akanatha kuti apindule Ayuda, kuwathandiza iwo kukhala Akristu. Koma kodi iye anachita mofananamo ndi Akunja?

Kufuna Kupindula Akunja

5. Kodi Paulo analalikira kwa yani mu Korinto, ndipo ndi chotulukapo chotani?

5 Pambuyo pa kufika kwa Paulo mu mzinda wa Korinto chifupifupi m’chirimwe cha 50 C.E., iye anapereka nkhani za mlungu ndi mlungu m’sunagoge ku khamu la atembenuki Achiyuda ndi Achigriki otembenukira ku chikhulupiriro Chachiyuda. Koma kulalikira kwake kwachangu kunadzutsa chitsutso kotero kuti anauza adani ake kuti: “Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.” Yehova anadalitsa kachitidwe kameneka, popeza kuti “Akorinto ambiri anamva, nakhulupira, nabatizidwa” monga Akristu. Ndithudi, m’masomphenya, Ambuye anachenjeza Paulo kumamatira ku gawo limenelo, akumamuuza kuti: “Ndiri nawo anthu ambiri m’mudzi muno.”​—Machitidwe 18:1-10.

6. Kodi nchiyani chimene chinadzutsa chikondwerero cha Paulo mwa awo amene chiyambi chawo chinali chosiyana ndi chake?

6 Chikhumbo chowona mtima cha Paulo cha kupeza Akunja kuwatembenuzira ku Chikristu chinamfulumiza kukhalanso ndi chikondwerero chaumwini mwa anthu amene chiyambi chawo chinali chosiyana kotheratu ndi chake. “Kwa iwo opanda lamulo [Akunja] monga wopanda lamulo, wosati wokhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.” (1 Akorinto 9:21) Kodi ndimotani mmene mtumwiyo anafunira kupindula Akunja?

7. Ponena za kudulidwa, kodi nchifukwa ninji mkhalidwe wa Tito unali wosiyana ndi uja wa Timoteo?

7 Pamene Paulo anapita ku Yerusalemu chifupifupi mu 49 C.E. kukapezekapo pa msonkhano wofunika kwambiri wa bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu, iye anapita ndi wophunzira Wachigriki Tito. Kwa abale osonkhanawo, Paulo anapereka ripoti la ntchito yake yolalikira pakati pa anthu amitundu, ndipo pambuyo pake analemba kuti: “Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mhelene, sanamkakamiza adulidwe.” (Agalatiya 2:1-3) Mosiyana ndi Timoteo, Tito anachita uminisitala wake choyambirira pakati pa anthu amitundu osadulidwa. Ndicho chifukwa chake nkhani ya mdulidwe sinabuke kwa iye.​—2 Akorinto 8:6, 16-18, 23; 12:18; Tito 1:4, 5.

8. Kodi Paulo anapereka motani umboni mu Atene?

8 Akumapereka umboni mu Atene, Paulo anasonyezanso kuti anachita zonse chifukwa cha uthenga wabwino. Akumalingalira kuganiza kwa nzika za likulu la Grisi, iye anawauza ponena za Mulungu wosadziŵika kwa iwo ndipo anagwira mawu olemba ndakatulo awo Aratus ndi Cleanthes, omwe ananena kuti: “Pakuti ifenso tiri mbadwa zake.” Chotero mtumwiyo anafuna kuwathandiza amvetseri ake kumvetsetsa kuti iwo sayenera “kulingalira kuti umulungu uli wofanana . . . kapena mwala wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.” Kuwonjezerapo, Paulo analingalira kuti: “Nthaŵi za kusadziŵako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima.” Iye analunjikitsa chidwi mokhutiritsa kwa “Mwini kumwamba ndi dziko lapansi,” Yehova. Ndipo kodi chotulukapo chinali chotani? “Ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira.” (Machitidwe 17:22-34) Inde, njira za Paulo zinali zachipambano!

9. Kodi Paulo anakhala bwanji ‘wofooka kwa ofooka,’ ndipo nchifukwa ninji?

9 “Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka,” anatero Paulo. (1 Akorinto 9:22a) Ngakhale kuti nkhani yake inali yamphamvu, mtumwiyo analingalira zikumbumtima zofooka za Ayuda ndi Akunja ena mu mpingomo. Iye anafulumiza Akristu Achiroma kuti: “Ndipo iye amene ali wofooka m’chikhulupiriro, mumlandire, koma sikuchita naye makani otsutsana ayi.” M’malo mokhala oweruza, Paulo anati: “Tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.” (Aroma 14:1, 13, 19) Iye anachenjeza kuti: “Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.” (Aroma 15:1) Akumazindikira thayo lake la kuwongolera njira ya kalankhulidwe ndi kachitidwe kake kotero kuti athandize ena, iye analemba kuti: “Ndakhala zonse kwa anthu onse.”​—1 Akorinto 9:22b; Agalatiya 3:28.

Ongolerani Maluso Anu a Kulalikira

10. Kodi ife lerolino tingamutsanzire motani Paulo?

10 Lerolino Mboni za Yehova zimafunikira kutsanzira Paulo monga mmene iye anatsanzirira Kristu. (1 Akorinto 11:1) Mtumwiyo anali wolalikira waluso yemwe anali ndi mzimu waumishonale. Zofananazo zingakhale zowona mu nkhani yathu, ngakhale kuti mikhalidwe yathu singatilole kutumikira m’maiko akunja. Mofanana ndi Paulo, tiyenera ‘kuchita zonse chifukwa cha uthenga wabwino kuti tikakhale oyanjana nawo.’ (1 Akorinto 9:23) Koma kodi nchiyani chimene chingawongolere maluso athu monga alaliki a Ufumu ndi opanga ophunzira?​—Mateyu 28:19, 20.

11. Monga minisitala, kodi nchifukwa ninji muyenera kukulitsa mphamvu zanu za kukhala watcheru?

11 Gwirirani ntchito pa kuwongolera mphamvu zanu za kukhala watcheru. Mwa kukhala watcheru, mungaphunzire zambiri zomwe zidzakuthandizani kusinthira kaperekedwe kanu ka uthenga wabwino kwa eninyumba osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ngati mukuchitira umboni kwa munthu wokhala mu mzinda, onani maloko pa chitseko, zokometsera zachipembedzo, ndi masilogani pa zomamatiza pamazenera. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kupereka umboni umene ungakhudze mitima ya anthu okhala m’nyumba zoterozo. Ndithudi Paulo anali watcheru. Mu Atene iye anagwiritsira ntchito guwa lansembe la “Kwa Mulungu Wosadziŵika” monga mbali imodzi ya umboni wake wabwino kulinga kwa “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo.” (Machitidwe 17:22-25) Nanunso mungachite zinthu zofananazo mu uminisitala wanu.

12. Kodi ndi mbali yotani imene kuzindikira kumachita mu uminisitala wathu?

12 Gwiritsirani ntchito kuzindikira mu uminisitala. Musakhumudwitsidwe ndi kunyinyirika koyamba kwa munthuyo potsegula chitseko ndi kulankhula kwa inu. M’malo modzilola inu eni kufooketsedwa ndi nkhope yopanda chisangalalo, sonyezani chikondi ndipo gwiritsirani ntchito kuzindikira. Yesetsani kusinthira umboni wanu ku mikhalidweyo. Ndi kulingaliradi kwapemphero kwachidule, mungakhale wokhoza kunena chinachake chimene chidzadzutsa chikondwerero mu mtima mwa munthuyo.​—Yerekezani ndi Nehemiya 2:4-6.

13. Kodi tingasonyeze motani kulingalira kwa awo amene timachitirako umboni?

13 Khalani wolingalira. Pa nsongayi, zinthu zosiyanasiyana zingachitidwe chifukwa cha uthenga wabwino. Mwachitsanzo, kulingalira kudzakuletsani kulola okalamba kapena odwala kuimirira pakhomo kwa nthaŵi yaitali. Mungapereke lingaliro lakuti mulankhule nawo mkati mwa nyumba, mmene angakhale omasuka. Kapena mungasankhe kuti pansi pa mikhalidweyo chikakhala chabwino kupanga ulendo wanu kukhala wachidule. Mwanjira iriyonse, khalani wolingalira. Sonyezani kuti mumasamala!​—Mateyu 9:35, 36.

14. Pamene tikuchitira umboni, kodi ndimotani mmene amvetseri angapumitsidwire?

14 Lankhulani m’njira imene ikapanga mwininyumba wanu kukhala womasuka. Yambani umboni wanu ndi moni waubwenzi amene ali wolandirika m’dera lanu. (Mateyu 10:12) Lingalirani mantha ndi kunyada kothekera. Pangani ndemanga zanu mwaulemu ndipo zokhala ndi ubwenzi wopanda mpeni kumphasa. Izi zikathandiza kutsimikizira eninyumba anu kuti mwabwera kudzathandiza ndipo mulibe zolinga zoipa.

15. Kodi nchifukwa ninji muyenera kupereka chidziŵitso chokwanira ponena za inu eni ndi chifukwa cha kufikira kwanu panyumbayo?

15 Eninyumba amafuna kudziŵa amene akufikirayo ndi chifukwa chake. Chotero, perekani chidziŵitso chokwanira ponena za inu eni. M’madera ena, makamaka mu Afirika ndi Asia, anthu ali okondweretsedwa kwabasi mwa alendo kotero kuti amakhala ofunitsitsa kumva mayankho ku mafunso onga ngati: Kodi ndinu yani? Kodi mumakhala kuti? Kodi ndinu wokwatira? Kodi muli ndi banja? Kuti muthandizireko ku kusangalatsa kwa chochitikacho, mwambo umafuna kuti muyankhe mafunsoŵa musanayambe kunena chifukwa chimene mwabwerera. Musawone moni woterowo kukhala wosayenerera, koma gwiritsirani ntchito nthaŵiyo kusanthula munthuyo ndi kumangilira kuwonana maso kwaulemu.

16. Kodi ndimotani mmene mafunso abwino angakhalire othandiza m’kusungabe kulankhulana ndi mwininyumba?

16 Gwiritsirani ntchito mafunso abwino kuti mupitirizebe kulankhula ndi mwininyumba. Ngakhale kuti nkhope ya munthuyo ingavumbule chinachake, maganizo ndi malingaliro ake ayenera kumvetsetsedwa. Izi pokhala tero, mungagwiritsire ntchito mwaluso mafunso kuti mudzutse mwininyumba kuti alongosole malingaliro ake ndi ziganizo. Kuti tichitire chitsanzo: Mkazi wina wopanda mwana yemwe anapereka chisamaliro chachikulu ku zinyama ananena izi ponena za kuchezera kwa Mboni: “Chimene ndimakumbukira ponena za nkhope yake yomwetulira ndi mtendere. Ndinadabwitsidwa. Mkazi ameneyu anandifunsa chomwe chinali chodera nkhaŵa changa chachikulu ponena za mikhalidwe pa dziko lapansi. Ndinanena kuti ndinali wodera nkhaŵa ponena za njira imene munthu amachitira ndi nyama, ndipo anandisonyeza Yesaya 11:6-9 ponena za nyama zikukhala mu mtendere weniweni. Ndinafuna kudziŵa zochuluka.”

17. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala amaso ku ndemanga zimene mwininyumba angapange ku mikhalidwe yake?

17 Khalani wamaso ku ndemanga zimene mwininyumba angapange ponena za mikhalidwe yake, makamaka m’gawo logwiridwa ntchito mobwerezabwereza. Mwanjira imeneyi, ngakhale mkati mwa kukambirana kwachidule, mwinamwake mungaphunzire zinazake zofunika ponena za munthuyo. Pambuyo pochoka pakhomopo, mwachidule lembani chidziŵitso choterocho pa cholembera cha kunyumba ndi nyumba. Koma bwanji ngati mwininyumba afunsa mafunso amene simungathe kuwayankha? Pamenepo chitani kufufuza m’mabukhu a Watch Tower Society kuti mupeze njira yabwino koposa yoperekera uthenga wabwino kwa munthuyo nthaŵi yotsatira imene mukamufikira.

Chitsanzo kwa Amishonale

18. Kodi nchiyani chimene amishonale ndi ena angaphunzire kuchokera kwa Paulo?

18 Pakati pa awo amene akuchita zonse chifukwa cha uthenga wabwino ali amishonale ophunzitsidwa pa Sukulu ya Giliadi ya Baibulo ya Watchtower. Iwo angaphunzire kwa Paulo, yemwe anali ndi mzimu wabwino waumishonale. Mwachitsanzo, iye sanafune kukhala ndi thayo la zokhumudwitsa zomwe zikanapangitsa Ayuda ndi Akunja kusalandira chowonadi. Chotero, mtumwiyo anali wosamala ponena za zimene anadya ndipo anachenjeza Akristu a ku Korinto kuwona kuti kusonyeza kuyenera kwawo kwa kudya zakudya zinazake sikunakhumudwitse ena. (1 Akorinto 8:8, 9) Mu New Century Bible, Profesa F. F. Bruce analongosola kuti: “Mu zinthu zonse zosiyana (zonga ngati chakudya chimene chinali kukambidwapo pa [1 Akorinto] chaputala 8), [Paulo] akugwirizana ndi miyambo ya awo amene ali nawo pa nthaŵiyo, kotero kuti asaike chokhumudwitsa m’njira ‘yowapindulira’ iwo ku uthenga wabwino.” (Aroma 14:21) Mofananamo, amishonale pakati pa Mboni za Yehova samayesera kusintha miyambo ya anthu m’magawo awo ogawiridwa, ngakhale kuti achatsopano amapatsidwa thandizo lauzimu la kupanga masinthidwe ofunikira kuti akondweretse Mulungu.​—Aroma 12:1, 2.

19. Popanga ophunzira, kodi ndi masinthidwe otani amene angakhale oyenerera kaamba ka (a) awo amene ali mu ntchito yaumishonale? (b) ofalitsa onse a Ufumu?

19 Awo oyamba ntchito yaumishonale ayenera kuphunzira ponena za njira ndi miyambo ya anthuwo. Ichi ndi chokumana nacho cholemeretsa ndipo chingathandize amishonalewo kukhala okhutiritsa kwambiri mu ntchito yawo yolalikira. Kwenikwenidi, kuti apeŵe kukhumudwitsa ena, iwo angafunikire kupanga masinthidwe m’nkhani zonga ngati kavalidwe ndi kapesedwe. Mwachitsanzo, pamene mlongo wina wachimishonale anafika choyamba Kumadzulo kwa Afirika, anapeza kuti njira imene ankagwiritsira ntchito zokometsera ikampangitsa iye kuzindikiridwa ndi akazi a makhalidwe achiŵereŵere m’chigawocho. Chotero, kotero kuti asakaikiritse ena, mwamsanga anasintha kagwiritsidwe kake ka zokometsera. Ndithudi, Mboni zonse za Yehova ziyenera kugwiritsira ntchito chiweruzo chabwino m’kavalidwe ndi kapesedwe kotero kuti athandize ena mwauzimu. Akristu, amene akulangizidwa ‘kusaika chokhumudwitsa pamaso pa ena’ ndi kulondola zinthu zomangirirana, ndithudi samafuna kukhumudwitsa aliyense.​—Aroma 14:13, 19.

20. (a) Mwachidule, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza ‘kuchita zonse chifukwa cha uthenga wabwino’? (b) Kodi ndi mafunso otani amene atsala kuti ayankhidwe?

20 Chipambano monga alengezi a Ufumu kwakukulukulu chimadalira pa dalitso la Yehova. (1 Akorinto 3:6, 7) Komabe, timafunikiranso kupanga kuyesayesa. Chotero khalani atcheru, monga mmene Paulo analiri mu uminisitala wake. Gwiritsirani ntchito kuzindikira, khalani wolingalira, pangitsani eninyumba kukhala pa mpumulo, ndipo funsani mafunso abwino kuti musungebe kukambitsirana ndi iwo. Sinthirani ku miyambo imene ingawoneke kukhala yachilendo koma sili yosemphana ndi malemba. Inde, tiyeni ‘tichite zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti tikakhale oyanjana nawo.’ (1 Akorinto 9:23) Koma kodi nchiyani chimene chimachitika ngati ena ali kale mbali ya ubale wathu Wachikristu? Kodi timachita nawo motani?

Kodi Mukayankha Motani?

◻ Kodi nchiyani chimene Paulo anachita kuti athandize Ayuda kukhala Akristu?

◻ Kodi ndimotani mmene Paulo anafunira kuthandiza Akunja?

◻ Kodi ndi ziti zimene ziri njira zina zowongolera maluso athu a kulalikira?

◻ Kodi Paulo anakhazikitsa chitsanzo chotani kaamba ka amishonale ndi alengezi ena a Ufumu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena