-
Pitirizani Kuyenda M’njira ya YehovaNsanja ya Olonda—1999 | May 15
-
-
6, 7. Ngakhale kuti Aisrayeli anali olambira Yehova Mulungu, ndi pazochitika ziti pamene iwo anagwa, ndipo chifukwa chiyani?
6 Zimenezi zinawachitikira Aisrayeli akale, monga momwe Paulo anasonyezera. Iye analemba kuti: “Zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakelake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka. Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kuseŵera. Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.”—1 Akorinto 10:6-8.
7 Choyamba Paulo akunena za nthaŵi pamene Aisrayeli analambira mwana wa ng’ombe wa golide m’munsi mwa Phiri la Sinai. (Eksodo 32:5, 6) Kumeneku kunali kusamvera lamulo la Mulungu limene anavomera kuti adzalimvera milungu yochepa poyambapo. (Eksodo 20:4-6; 24:3) Kenako, Paulo akunena za nthaŵi pamene Aisrayeli anagwadira Baala ndi ana aakazi a Moabu. (Numeri 25:1-9) Polambira mwana wang’ombe, anthuwo anali kukhutiritsa zilakolako zawo mopambanitsa, ‘kuseŵera.’a Polambira Baala anthuwo anali kuchita zachiwerewere zosaneneka. (Chivumbulutso 2:14) N’chifukwa chiyani Aisrayeli anachita machimo ameneŵa? Chifukwa analola mitima yawo ‘kulakalaka zoipa’—kaya kulambira mafanoko kapena miyambo yonyansa imene anali kuichita polambira.
8. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinachitikira Aisrayeli?
8 Paulo anati tiyenera kuphunzirapo pa zochitika zimenezi. Kuphunzirapo chiyani? Mosakayikira Mkristu sangagwadire mwana wang’ombe wagolide kapena mulungu wakalekale wa Amoabu. Koma bwanji za chiwerewere kapena kukhutiritsa zilakolako mosadziletsa? Zimenezi n’zofala lerolino, ndipo ngati tilola chikhumbo cha kuchita zimenezi kukula m’mitima yathu, zidzakhala chopinga pakati pa ifeyo ndi Yehova. Chotsatira chake chidzakhala chofanana ndi kuti talambira mafano—kupatutsidwa kwa Mulungu. (Yerekezani ndi Akolose 3:5; Afilipi 3:19.) Ndiye chifukwa chakedi Paulo anamaliza nkhani yake yofotokoza zochitikazo mwa kulimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Thaŵani kupembedza mafano.”—1 Akorinto 10:14.
-
-
Pitirizani Kuyenda M’njira ya YehovaNsanja ya Olonda—1999 | May 15
-
-
a Ponena za mawu achigiriki otembenuzidwa panopo kuti “kuseŵera,” womasulira mawu wina ananena kuti mawuwo amatanthauza magule amene anali kuchitika pamapwando achikunja ndipo anawonjezera kuti: “Ambiri mwa magule ameneŵa, monga momwe timadziŵira bwino lomwe, anakonzedwa kwenikweni kuti azinyanyula anthu kuti akhale ndi zilakolako zonyansa kotheratu.”
-