-
“Thawani Dama”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
3. Kodi cholinga cha Balamu chinakwaniritsidwa bwanji?
3 Kodi nyambo imeneyi inagwira ntchito? Inde, chifukwa amuna ambiri achiisiraeli anakopekadi ndipo “anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.” Anthuwa anayamba kulambira milungu yonyansa yachimowabu monga Baala wa ku Peori, amene anali mulungu wobereketsa kapena kugonana. Chifukwa cha zimenezi, Aisiraeli okwana 24,000 anafa atangotsala pang’onong’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Limenelitu linali tsoka lalikulu.—Numeri 25:1-9.
-
-
“Thawani Dama”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
4. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ambiri anachita chiwerewere?
4 Kodi chinabweretsa tsoka limeneli n’chiyani? Aisiraeli ambiri anali ndi mtima woipa chifukwa anamusiya Yehova, Mulungu amene anawatulutsa ku Iguputo, kuwapatsa chakudya ali m’chipululu ndiponso kuwayendetsa bwinobwino pa ulendo wawo wopita kudziko limene anawalonjeza. (Aheberi 3:12) Poganizira nkhani imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tisamachite dama, mmene ena mwa iwo anachitira dama, n’kufa 23,000 tsiku limodzi.”a—1 Akorinto 10:8.
-
-
“Thawani Dama”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
a Buku la Numeri limanena kuti anthu amene anaphedwa anali 24, 000. Chiwerengerochi ndi cha anthu 23, 000 amene anaphedwa ndi Yehova komanso cha ‘atsogoleri a anthuwo’ amene anaphedwa ndi oweruza ndipo n’kutheka kuti analipo 1,000.—Numeri 25:4, 5.
-