-
Kugonjetsa Kufooka KwaumunthuNsanja ya Olonda—2001 | March 15
-
-
4. Ndi chenjezo lotani lomwe Paulo anapereka pa 1 Akorinto 10:12, 13?
4 Paulo polembera Akristu okhala ku Korinto—mzinda wodziŵika ndi mikhalidwe yake yoipa—anapereka chenjezo loyenerera lokhudza chiyeso ndi mphamvu ya tchimo. Iye anati: “Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe. Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:12, 13) Tonsefe—mwana kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi—timakumana ndi ziyeso zambiri kusukulu, kuntchito, kapena kwinakwake. Chotero, tiyeni tipende mawu a Paulowa ndi kuona tanthauzo lomwe alinalo kwa ife.
-
-
Kugonjetsa Kufooka KwaumunthuNsanja ya Olonda—2001 | March 15
-
-
7. N’chifukwa chiyani kudziŵa kuti ena apambana pokana chiyeso kuli kolimbikitsa?
7 Tikupezatu chitonthozo champhamvu m’mawu a Paulo akuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu”! (1 Akorinto 10:13) Mtumwi Petro analemba kuti: “Mumkanize [Mdyerekezi], okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” (1 Petro 5:9) Inde, ena akumanapo ndi mayesero ngati amenewo ndipo chifukwa cha thandizo la Mulungu, awapirira mwachipambano, nafenso tingatero. Komabe, monga Akristu oona okhala m’dziko loipali, tonsefe tingayembekezere kuyesedwa nthaŵi iliyonse. Tsono tingatsimikizire motani kuti tidzagonjetsa kufooka kwaumunthu ndi chiyeso chakuti tichite tchimo?
-