Kodi Mukukaniza Mzimu wa Dziko?
“Sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma mzimu wa kwa Mulungu.”—1 AKORINTO 2:12.
1, 2. Kodi nditsoka lotani la mpweya waululu limene linachitika mu Bhopal, ku India, koma kodi ndi “mpweya” wakupha woposa wotani umene anthu akupuma padziko lonse?
USIKU wina wozizirira mu December 1984, panachitika chinthu china chowopsa mu Bhopal, ku India. Mumzindawo, muli fakitale ya mankhwala, ndipo usiku umenewo mu December, valavu inamasuka ku imodzi ya matanki osungira mpweya waululu. Mwadzidzidzi, matani a mpweya wa methyl isocyanate anayamba kutulukira mumpweya. Utatengedwa ndi mphepo, mpweya wakupha umenewo unaloŵa m’nyumba zambiri ndi kupuitsa mabanja amene anali gone. Awo amene anafa anali zikwizikwi, ndipo ambiri analemala. Imeneyo inali ngozi yoipa koposa m’mbiri ya maindasitale kufikira panthaŵiyo.
2 Anthu analira pamene anamva za Bhopal. Koma ngakhale kuti unali wakupha motero, mpweya waululuwo umene unatuluka kumeneko unapha anthu oŵerengeka kwambiri poyerekezera ndi amene amaphedwa mwauzimu ndi “mpweya” umene anthu padziko lonse amapuma masiku onse. Baibulo limautcha “mzimu wa dziko.” Ndiwo mpweya wakupha umene mtumwi Paulo anasiyanitsa ndi mzimu wa Mulungu pamene anati: “Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziŵe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.”—1 Akorinto 2:12.
3. Kodi “mzimu wa dziko” nchiyani?
3 Kodi kwenikweni “mzimu wa dziko” nchiyani? Malinga ndi kunena kwa The New Thayer’s Greek English Lexicon of the New Testament, tanthauzo lachisawawa la liwulo “mzimu” (Chigiriki, pneuʹma) ndilo “mkhalidwe wa maganizo kapena chisonkhezero chimene chimadzaza ndi kulamulira moyo wa munthu aliyense.” Munthu angakhale ndi mzimu kapena mkhalidwe wa maganizo wabwino kapena woipa. (Salmo 51:10; 2 Timoteo 4:22) Ndiponso gulu la anthu lingakhale ndi mzimu, kapena mkhalidwe wa maganizo wolamulira. Mtumwi Paulo analembera Filemoni bwenzi lake kuti: “Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu.” (Filemoni 25) Mofananamo—koma pamlingo wokulirapo—dziko lonse lili ndi mkhalidwe wa maganizo wolamulira, ndipo umenewu ndiwo “mzimu wa dziko” wotchulidwa ndi Paulo. Malinga ndi kunena kwa buku la Word Studies in the New Testament la Vincent, “mawuwo amatanthauza mkhalidwe wa kuipa umene umasonkhezera dziko losalapali.” Ndiwo chikhoterero chauchimo chimene chili chofala m’kalingaliridwe ka dziko ndi chimene mwamphamvu chimasonkhezera zochita za anthu.
4. Kodi magwero a mzimu wa dziko ndani, ndipo nchiyambukiro chotani chimene mzimu umenewu uli nacho pa anthu?
4 Mzimu umenewu ngwakupha. Chifukwa? Chifukwa chakuti umachokera kwa “wolamulira wa dziko ili,” Satana. Ndithudi, iye amatchedwa “mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga [“mpweya,” NW], wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Yohane 12:31; Aefeso 2:2) Nkovuta kupeŵa “mpweya” umenewu, kapena “mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” Uli paliponse m’chitaganya cha anthu. Ngati tiupuma, timayamba kutengera mkhalidwe wake, zolinga zake. Mzimu wa dziko umalimbikitsa ‘kukhala ndi moyo monga mwa thupi,’ kutanthauza kuti, mogwirizana ndi kupanda kwathu ungwiro kwauchimo. Kumeneko nkwakupha, “pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa.”—Aroma 8:13.
Kupeŵa Mzimu wa Dzikoli
5. Kodi ndimotani mmene Mboni ina inachitira mwanzeru mkati mwa tsoka ku Bhopal?
5 Mkati mwa tsoka la ku Bhopal, Mboni ina ya Yehova inadzutsidwa ndi mabelu ochenjeza ndi fungo loŵaŵa la mpweya waululuwo. Mosazengereza inagalamutsa banja lake ndi kulitulutsira kunja m’khwalala. Ikumaima kwakamphindi kuti imve kumene mphepo inali kuchokera, inalimbikira kudutsa m’piringupiringu wa anthu osokonezeka nitsogolera banja lake pamwamba pa phiri kunja kwa mzinda. Kumeneko anakhoza kupuma mpweya wabwino wochokera kunyanja ina yapafupi.
6. Kodi tingapite kuti kuthaŵa mzimu wa dziko?
6 Kodi kuli malo okwezeka kumene tingathaŵireko kupeŵa “mpweya” waululu wa dzikoli? Baibulo limati aliko. Akumayang’ana mtsogolo ku tsiku lathu, mneneri Yesaya analemba kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kumka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake; chifukwa m’Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mawu a Yehova kuchokera m’Yerusalemu.” (Yesaya 2:2, 3) Malo okwezeka a kulambira koyera, “phiri la nyumba ya Yehova” lokwezedwa, ndilo malo okha papulaneti lino amene alibe mzimu wopuitsa, waululu wa dzikoli. Ndikumeneko kumene mzimu wa Yehova umayenda mwatawatawa pakati pa Akristu okhulupirika.
7. Kodi ndimotani mmene ambiri apulumutsidwira ku mzimu wa dziko?
7 Ambiri amene kale anapuma mzimu wa dzikoli apeza mpumulo wofanana ndi uja wopezedwa ndi Mboni ija ku Bhopal. Atalankhula za “ana a kusamvera” amene amapuma mpweyawo, kapena mzimu, wa dzikoli, mtumwi Paulo akuti: “Amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo; koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, . . . anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu.” (Aefeso 2:3-5) Awo amene amangopuma mpweya waululu wa dongosolo ili la zinthu ali akufa mwauzimu. Komabe, mothandizidwa ndi Yehova, anthu mamiliyoni ambiri lerolino akuthaŵira kumalo okwezeka auzimu ndipo akupulumuka mkhalidwe wakupha umenewo.
Zisonyezero za “Mzimu wa Dziko”
8, 9. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti tiyenera kukhala ochenjera ndi mzimu wa dziko? (b) Kodi mzimu wa Satana ungatiipitse motani?
8 Mpweya wakupha wa Satana ukali kutizinga. Tiyenera kukhala osamala ndipo sitiyenera kutengedwa, kutsikiranso kudziko, kumene mwinamwake tingatsamwitsidwe mwauzimu. Zimenezi zimafuna kudikira kosalekeza. (Luka 21:36; 1 Akorinto 16:13) Mwachitsanzo, talingalirani mfundo iyi. Akristu onse amadziŵa bwino miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino ndipo sangavomereze konse kuti machitachita oipa onga chigololo, dama, ndi mathanyula ali ovomerezedwa. Komabe, chaka chilichonse pafupifupi anthu 40,000 amachotsedwa m’gulu la Yehova. Chifukwa? Kaŵirikaŵiri chifukwa cha machitachita oipa amodzimodzi ameneŵa. Kodi zimenezo zingachitike motani?
9 Chifukwa chakuti tonsefe tili opanda ungwiro. Thupi nlofooka, ndipo nthaŵi zonse tifunikira kulimbana ndi zikhoterero zoipa zimene zimabuka m’mitima yathu. (Mlaliki 7:20; Yeremiya 17:9) Komabe, zikhoterero zoipa zimenezo zimachirikizidwa ndi mzimu wa dziko. Ambiri m’dziko lino samaona cholakwa ndi chisembwere, ndipo lingaliro lakuti zilizonse nzololeka lili mbali ya chikhoterero cha maganizo cha dongosolo la zinthu la Satana. Ngati tilola kalingaliridwe kotero, pamenepo, kudzakhala kotheka ndithu kwa ife kuyamba kuganiza mofanana ndi dziko. Posapita nthaŵi, malingaliro oipa otero angadzutse zilakolako zoipa zimene zidzathera m’tchimo lalikulu. (Yakobo 1:14, 15) Tidzakhala titachoka paphiri la kulambira koyera kwa Yehova kutsikira kuzidikha zoipa za dziko la Satana. Aliyense amene modzifunira akhala kumeneko sadzalandira moyo wosatha.—Aefeso 5:3-5, 7.
10. Kodi chimodzi cha zisonyezero za mpweya wa Satana nchiyani, ndipo chifukwa ninji Akristu ayenera kuchipeŵa?
10 Mzimu wa dziko ukuonekera paliponse motizinga. Mwachitsanzo, pali mkhalidwe wa maganizo wonyozera, wopanda ulemu umene ambiri amaonera moyo. Poona chinyengo cha andale osawona mtima kapena olephera ndi atsogoleri achipembedzo aumbombo ndi achisembwere, iwo amalankhula monyoza ngakhale zinthu zofunika. Akristu amakaniza mkhalidwe umenewu. Pamene tingakhale wanthabwala moyenerera, timapeŵa kudzetsa mumpingo mzimu wonyodola wa kupanda ulemu. Kalankhulidwe ka Mkristu kamasonyeza kuwopa Yehova ndi chiyero cha mumtima. (Yakobo 3:10, 11; yerekezerani ndi Miyambo 6:14.) Kaya tikhale wachichepere kapena wachikulire, kalankhulidwe kathu nthaŵi zonse kayenera kukhala ‘m’chisomo, kokoleretsa, kuti tikadziŵe ife mayankhidwe athu a kwa yense akatani.’—Akolose 4:6.
11. (a) Kodi mbali yachiŵiri ya mzimu wa dziko ndiiti? (b) Kodi nchifukwa ninji Akristu ali osiyana ndi awo amene amasonyeza mbali imeneyi?
11 Chikhoterero china chofala chosonyeza mzimu wa dzikoli ndicho chidani. Dziko nlogaŵanika ndi maudani ndi mikangano yozikidwa pa kusiyana kwa fuko, manenedwe, mtundu, ndipo ngakhale maumunthu. Zinthu zili zabwinopo chotani nanga kumene mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito! Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW]. Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake. Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.”—Aroma 12:17-21.
12. Kodi nchifukwa ninji Akristu amapeŵa kukondetsa zinthu zakuthupi?
12 Mzimu wa dzikoli umasonkhezeranso kukondetsa zinthu zakuthupi. Polimbikitsidwa ndi dongosolo la malonda, ambiri amakhala otengeka maganizo ndi ziŵiya za mtundu watsopano, mafashoni atsopano, ndi galimoto zatsopano. Ali muukapolo wa “chilakolako cha maso.” (1 Yohane 2:16) Ochuluka amapima chipambano chawo m’moyo ndi ukulu wa nyumba yawo kapena unyinji wa ndalama zawo kubanki. Akristu, opuma mpweya wabwino wauzimu paphiri lokwezeka la kulambira koyera kwa Yehova, amakaniza chikhoterero chimenechi. Amadziŵa kuti kulondola motsimikiza mtima zinthu zakuthupi kungakhale kowononga. (1 Timoteo 6:9, 10) Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti: “Moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.”—Luka 12:15.
13. Kodi nziti zimene zili zisonyezero zina za mzimu wa dzikoli?
13 Pali zisonyezero zina za “mpweya” woipa wa dzikoli. China ndicho mzimu wa chipanduko. (2 Timoteo 3:1-3) Kodi mwaona kuti anthu ambiri sagwirizananso ndi olamulira? Kodi mwaona kuntchito kwanu chizoloŵezi chofala cha kusagwira ntchito ngati palibe munthu wina woyang’anira? Kodi ndianthu angati amene mudziŵa amene aswa malamulo—mwinamwake kunama pamsonkho wawo kapena kuba pantchito? Ngati mukali kupita kusukulu, kodi munalefulidwapo pakuchita zomwe mungathe chifukwa chakuti anzanu a m’kalasi amaipidwa ndi awo amene apambana mwa nzeru zawo zokha? Zonsezi ndizisonyezero za mzimu wa dziko umene Akristu ayenera kukaniza.
Mmene Tingakanizire Mzimu wa Dzikoli
14. Kodi ndimotani mmene Akristu alili osiyana ndi amene sali Akristu?
14 Komabe, kodi ndimotani mmene tingakanizire mzimu wa dziko pamene kuli kwakuti tikukhala m’dzikoli? Tiyenera kukumbukira kuti kulikonse kumene tingakhale mwakuthupi, mwauzimu sitili mbali ya dziko. (Yohane 17:15, 16) Zonulirapo zathu sindizo zonulirapo za dzikoli. Kaonedwe kathu ka zinthu nkosiyana. Ndife anthu auzimu, olankhula ndi kulingalira “si ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi mzimu; ndi kulinganiza [zinthu zauzimu ndi mawu auzimu, NW].”—1 Akorinto 2:13.
15. Kodi ndimotani mmene tingakanizire mzimu wa dziko?
15 Kodi nchiyani chimene munthu angachite ngati wapezeka m’malo oipitsidwa ndi mpweya waululu? Mwina angavale chopumira kumaso cholumikizidwa kumagwero a mpweya wabwino, kapena akhoza kuchoka m’malowo. Kupeŵa mpweya wa Satana kumaphatikiza pamodzi njira ziŵirizo. Monga momwe kungathekere, timayesa kudzipatula pa chilichonse chimene chingatheketse mzimu wa dziko kuyambukira kalingaliridwe kathu. Motero, timapeŵa mayanjano oipa, ndipo timapeŵa mtundu uliwonse wa zosangulutsa zimene zimachirikiza chiwawa, chisembwere, kukhulupirira mizimu, chipanduko, kapena ntchito iliyonse ya thupi. (Agalatiya 5:19-21) Komabe, popeza kuti tikukhala m’dziko, sitingathe kupeŵeratu zinthu zimenezi. Chotero timachita mwanzeru ngati tidzilumikiza kumagwero auzimu a mpweya wabwino. Tidzadzaza mpweya wabwino m’mapapu athu auzimu, titero kunena kwake, mwa kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse, phunziro laumwini, ntchito ndi mayanjano Zachikristu, ndi pemphero. Mwanjirayi, ngati mpweya uliwonse wa Satana uloŵa m’mapapu athu auzimu, mzimu wa Mulungu umatipatsa mphamvu ya kuutulutsa.—Salmo 17:1-3; Miyambo 9:9; 13:20; 19:20; 22:17.
16. Kodi tingapereke motani umboni wakuti tili ndi mzimu wa Mulungu?
16 Mzimu wa Mulungu umachititsa Mkristu kukhala wosiyana kwambiri ndi awo amene ali mbali ya dziko. (Aroma 12:1, 2) Paulo anati: “Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.” (Agalatiya 5:22, 23) Mzimu wa Mulungu umapatsanso Akristu chidziŵitso chozamirapo cha zinthu. Paulo anati: “Za Mulungu palibe wina azidziŵa, koma mzimu wa Mulungu.” (1 Akorinto 2:11) Mwachisawawa, “za Mulungu” zimaphatikizapo chowonadi chonena za nsembe yadipo, Ufumu wa Mulungu wolamuliridwa ndi Yesu Kristu, chiyembekezo cha moyo wosatha, ndi kuchotsedwa kwa dziko loipali komayandikira. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Akristu amadziŵa ndi kuvomereza zinthu zimenezi monga chowonadi, ndipo kuteroko kumasiyanitsa kaonedwe kawo ka moyo ndi kaja ka anthu a dziko. Ali okhutira kupeza chimwemwe chawo m’kutumikira Yehova tsopano, ndi chiyembekezo cha kumtumikira kuumuyaya wonse ulinkudza.
17. Kodi ndani amene anapereka chitsanzo chabwino koposa cha kukaniza mzimu wa dziko, ndipo motani?
17 Yesu anali chitsanzo chabwino koposa cha awo amene akaniza mzimu wa dzikoli. Yesu atangobatizidwa, Satana anayesa kumchotsa pakutumikira Yehova mwa kumdzetsera ziyeso zitatu. (Mateyu 4:1-11) Chomalizira chinali ndi kuthekera kwakuti Yesu akanalandira ulamuliro wa dziko lonse mwa kungogwadira Satana kamodzi basi. Yesu akanalingalira kuti: ‘Eya, ndidzangomgwadira, ndiyeno nditalandira ulamuliro wa dziko, ndidzalapa ndi kuyambanso kulambira Yehova. Monga wolamulira wa dziko, ndidzakhala wokhoza bwino lomwe kupindulitsa mtundu wa anthu kuposa mmene ndilirimu monga wopala matabwa wa ku Nazarete.’ Yesu sanalingalire motero. Anali wofunitsitsa kuyembekezera kufikira pamene Yehova akampatsa ulamuliro wa dziko. (Salmo 2:8) Panthaŵiyo, ndi panthaŵi zina zonse m’moyo wake, iye anakaniza chisonkhezero chaululu cha mpweya wa Satana. Motero, analaka dziko ili loipitsidwa mwauzimu.—Yohane 16:33.
18. Kodi ndimotani mmene kukaniza kwathu mzimu wa dziko kumadzetsera chitamando kwa Mulungu?
18 Mtumwi Petro anati tiyenera kutsatira mapazi a Yesu mosamalitsa. (1 Petro 2:21) Kodi pangakhale chitsanzo chabwino kuposa chimenechi? M’masiku ano otsiriza, mosonkhezeredwa ndi mzimu wa dziko, anthu akutitimira mopitiriza m’chithapwi cha makhalidwe onyansa. Nkwabwino chotani nanga kuti pakati pa dziko lotero, malo okwezeka a kulambira kwa Yehova ali oyera ndi audongo! (Mika 4:1, 2) Ndithudi, mphamvu ya mzimu wa Mulungu imasonyezedwa mwa anthu mamiliyoni amene akukwera kumalo olambirira a Yehova, akumakaniza mzimu wofala wa dziko lino ndi kudzetsa ulemu ndi chitamando kwa Yehova! (1 Petro 2:11, 12) Tonsefe titsimikizetu kukhalabe m’malo okwezeka amenewo kufikira Mfumu yodzozedwa ya Yehova itachotsa dziko loipali ndi kuponyera Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake m’phompho. (Chivumbulutso 19:19–20:3) Panthaŵiyo, mzimu wa dzikoli sudzakhalaponso. Imeneyo idzakhala nthaŵi yabwino chotani nanga!
Kodi Mungathe Kufotokoza?
◻ Kodi mzimu wa dziko nchiyani?
◻ Kodi nchiyambukiro chotani chimene mzimu wa dzikoli uli nacho pa munthu aliyense?
◻ Kodi pali zisonyezero zina ziti za mzimu wa dziko, ndipo tingazipeŵe motani?
◻ Kodi tingasonyeze motani kuti tili ndi mzimu wa Mulungu?
◻ Kodi ndimadalitso otani amene awo okaniza mzimu wa dziko amalandira?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Mzimu wa dziko umachokera kwa Satana
Kuti mupeŵe mzimu wa dziko, thaŵirani kumalo olambirira okwezeka a Yehova