Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Akristu ayenera kukhala odera nkhawa kwambiri chotani kuti kaya nsanganizo za mwazi, zonga “plasma” woumitsidwa, zingakhale zitawonjezeredwa kuzakudya zanyama?
Ngati pali maziko enieni okhulupiririra kuti mwazi wanyama (kapena nsanganizo zake) mosakaikira umagwiritsiridwa ntchito m’malowo m’zakudya zopangidwa, Akristu ayenera kusamala moyenerera. Komabe, kukakhala kupanda nzeru kuvutika maganizo ndi kunyumwira chabe kapena kukhala ndi nkhawa zopanda maziko.
Kuchiyambiyambi m’mbiri ya munthu, Mlengi wathu analamulira kuti anthu sayenera kudya mwazi. (Genesis 9:3, 4) Iye anafotokoza kuti mwazi umaimira moyo, umene uli mphatso yochokera kwa iye. Mwazi wochotsedwa m’cholengedwa ukagwiritsiridwa ntchito kokha m’nsembe, monga paguwa lansembe. Apo ayi, mwazi wochokera m’cholengedwa unayenera kutsanulidwa pansi, m’lingaliro la kuubwezera kwa Mulungu. Anthu ake anafunikira kupewa kuchirikiza moyo mwa kudya mwazi. Iye analamulira kuti: “Musamadya mwazi wa nyama iriyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndimwazi wake; aliyense akaudya adzasadzidwa.” (Levitiko 17:11-14) Chiletso cha Mulungu cha kudya mwazi chinabwerezedwa kwa Akristu. (Machitidwe 15:28, 29) Chotero Akristu oyambirira anafunikira kupewa chakudya chokhala ndi mwazi, chonga nyama ya zinyama zopotoledwa kapena masoseji amwazi.
Komabe, m’zochitika zenizeni, kodi ndimotani mmene Akristu amenewo akachitira malinga ndi chitsimikizo chawo cha ‘kupewa mwazi’? (Machitidwe 21:25) Kodi iwo ayenera kokha kugwiritsira ntchito mawu a mtumwi Paulo akuti: “Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima”?
Ayi. Mawu a pa 1 Akorinto 10:25 amenewo akusonya kunyama imene ingakhale ya nyama yoperekedwa nsembe pakachisi wafano. Kalelo, nyama yotsala muakachisi inali kugulitsidwa kwa ochita malonda, amene angaphatikize ndi nyama yawo ina yogulitsidwa m’masitolo awo. Mfundo ya Paulo inali yakuti nyama ya m’kachisi siinali yoipa mwa iyo yokha kapena yoipitsidwa. Mwachiwonekere kunali kozoloŵereka kuchotsa ndi kugwiritsira ntchito pamaguwa ansembe achikunja mwazi wa nyama zoperekedwa nsembe kumeneko. Chotero ngati nyama ina yotsala inagulitsidwa pamsika, popanda mgwirizano wachiwonekere ndi kachisi kapena malingaliro olakwika a akunjawo, Akristu akatha kuigula monga nyama yogulitsidwa imene inali yoyera ndi imene mwazi wake unali utachotsedwa moyenerera.
Komabe, kukanakhala kosiyana, ngati Akristu amenewo anazindikira kuti nyama imene inachokera pa nyama zopotoledwa (kapena masoseji amwazi) inali kugulitsidwa paimodzi ya masitolo a m’malomo. Iwo akafunikira kukhala osamala posankha nyama yoti agule. Iwo akakhoza kuzindikira nyama zimene zinali ndi mwazi ngati zimenezo zinali ndi mawonekedwe osiyana (ngakhale monga momwe kaŵirikaŵiri soseji yamwazi ingadziŵikire m’maiko kumene ili yofala). Kapena Akristu angafunse kwa wogwira ntchito m’butchala wotchuka kapena wogulitsa nyama. Ngati analibe chifukwa chokhulupiririra kuti nyamayo inali ndi mwazi, iwo angagule ndi kudya.
Paulo analembanso kuti: ‘Kulingalira kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.’ (Afilipi 4:5, NW) Zimenezo zingagwire ntchito pankhani yogula nyama. Chilamulo cha Israyeli kudzanso lamulo la bungwe lolamulira la Akristu a m’zaka za zana loyamba sizinasonyeze kuti anthu a Mulungu anafunikira kuthera nthaŵi yaitali ndi kuyesayesa kufunsafunsa za nyama, ngakhale kufikira kukhala odya ndiwo zokha ngati panali chikaikiro chochepetsetsa cha kukhalamo kwa mwazi m’nyama imene iripo.
Mzimba Wachiisraeli amene anapha nyama ankachotsa mwazi wake. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 12:15, 16.) Ngati banja lake silinakhoze kudya nyama yonseyo, iye akatha kugulitsa ina. Ngakhale nyama yokhetsedwa mwazi bwino lomwe, mlingo waung’ono wa mwazi unkakhalabe m’nyamayo, koma palibe mawu m’Baibulo amene amasonyeza kuti Myuda wogula nyamayo anafunikira kuchita mopambanitsa m’kupeza maumboni onga chiŵerengero cha mphindi pakati pa kupha ndi kuchucha kwa magazi, kuti ndimtsempha uti kapena ndimnyewa uti umene unadulidwa kuti mwazi utuluke, ndi mmene nyamayo inalenjekedwera ndi kuti nkwautali wotani. Ndiponso, bungwe lolamuliralo silinalembe kuti Akristu anafunikira kupereka chisamaliro chopambanitsa ponena za zimenezi, monga ngati kuti anafunikira maumboni atsatanetsatane ndi otsimikizirika kotheratu asanadye nyama iriyonse.
M’maiko ambiri lerolino, lamulo, mwambo, kapena chizoloŵezi chachipembedzo zimafunikiritsa kuti nyama zonse (kusiyapo zinthu zina zapadera, zonga soseji yamwazi) zimachokera m’nyama zimene ziyenera kuchotsedwa mwazi pophedwa. Chotero, kaŵirikaŵiri Akristu m’madera amenewo safunikira kukhala ankhaŵa mopambanitsa ndi njira zophera kapena njira zochitira. Kunena mwachidule, iwo ‘ayenera kudya kokha nyama yogulitsidwa m’mabutcha ololedwa ndi lamulo kapena yodziŵika bwino maphedwe ake, popanda kufunsafunsa,’ ndipo angakhaletu ndi chikumbumtima choyera chakuti iwo akusala mwazi.
Komabe, mwakamodzikamodzi pakhala malipoti pazopangidwa, onena za kugwiritsira ntchito mwazi m’zamalonda amene avutitsa maganizo Akristu ena. Anthu ena mu indasitale ya nyama amalingalira kuti mlingo waukulu wa mwazi wochokera m’nyama zophedwa ungasonkhanitsidwe kaamba ka kugwiritsiridwa ntchito mopindulitsa, monga kupangira fataleza kapena chakudya cha zifuyo. Ofufuza apenda kuti adziŵe kaya mwazi woterowo (kapena mbali yake) ungagwiritsiridwe ntchito m’nyama ya m’zitini. Mafakitale azamalonda ochepekera apanga mlingo wochepa wa plasma yamadzi, youmikidwa ndi aisi, kapena yaufa (kapena maselo ofiira ochotseredwa mawonekedwe) imene ingalowedwe mmalo ndi peresenti yochepa ya nyama m’zinthu zonga masoseji kapena msanganizo wazakudya. Mapendedwe ena azikidwa pa kugwiritsira ntchito zinthu zochokera m’mwazi waufa monga zowonjezera kapena kukhuthalitsa madzi ndi mafuta m’nyama yogaidwa, m’zinthu zokazingidwa, kapena m’zakudya ndi zakumwa zina kuwonjezera protini kapena ma ayoni.
Komabe, nkoyenera kuzindikira kuti kupenda koteroko kwakhala kukuchitika kwazaka makumi ambiri. Komabe, kukuwonekera kuti m’maiko ochulukitsitsa kugwiritsiridwa ntchito kwa zinthu zoterozo kwakhala kochepa kwambiri, kapena kuti kulibeko. Malipoti ena otumikira monga chitsanzo amatithandiza kusonyeza chifukwa chake:
“Mwazi uli magwero a maprotini olimbikitsa thupi ndi othandiza. Komabe, mwazi wang’ombe wagwiritsiridwa ntchito kokha kumlingo wochepa kuti udyedwe mwachindunji ndi anthu chifukwa cha mawonekedwe ake owopsa ndi kamvekedwe kake kachilendo m’kamwa.”—Journal of Food Science, Voliyamu 55, Nambala 2, 1990.
“Maprotini a plasma yamwazi ali mikhalidwe yothandiza yonga kusungunuka mosavuta, kusanduliza ndi kusagwirizana ndi zamadzi . . . ndipo kugwiritsiridwa ntchito kwawo m’kukonzedwa kwachakudya kumapereka mapindu aakulu. Komabe, palibe dongosolo logwira mtima loyeretsera plasma, makamaka pambuyo pa kutha madzi, limene layambitsidwa m’Japan.”—Journal of Food Science, Voliyamu 56, Nambala 1, 1991.
Akristu ena mwakamodzikamodzi apenda malebulo pazakudya za m’zitini, popeza kuti maboma ambiri amafuna kuti zopanga chakudyazo zisanjidwe. Ndipo angasankhe kutero nthaŵi zonse pogula chakudya chirichonse chimene ali ndi chifukwa choganizira kuti mwina nchosanganizidwa ndi mwazi. Ndithudi, kukakhala kwabwino, kupewa zakudya zimene zinasanja zinthu zonga mwazi, plasma yamwazi, plasma, protini ya globin (kapena globulin), kapena ayoni ya hemoglobin (kapena globin). Chidziŵitso chotsatsa malonda cha kampani ina ya ku Ulaya pankhani imeneyi chinanena kuti: “Chidziŵitso chonena za kugwiritsiridwa ntchito kwa globin monga nsanganizo yopanga chakudya chiyenera kulembedwa papaketi lachakudyacho m’njira yakuti wakudyayo sakusokeretsedwa ponena za zophatikizdwa m’chakudyacho kapena phindu lake.”
Komabe, ngakhale popenda malebulo kapena pofunsa eni mabutchala, uchikatikati ngwofunika. Sikuli monga ngati kuti Mkristu aliyense padziko lonse ayenera kuyamba kupenda malebulo ndi zimene zapanga chakudyacho pa chakudya chonse cha m’pamapaketi kapena kuti ayenera kufunsisitsa antchito m’makantini kapena m’masitolo achakudya. Mkristu angayambe kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali umboni wotsimikizirika wakuti mwazi ndi zipangizo zake zimagwiritsiridwa ntchito m’zakudya zanthawi zonse za m’dera lino kapena dziko?’ M’malo ambiri yankho nlakuti ayi. Chotero, Akristu ambiri asankha kuti iwo eniwo sadzathera nthaŵi yochuluka ndi chisamaliro akumapenda zothekera zakamodzikamodzi kwambiri. Munthu amene samalingalira mwanjira imeneyi ayenera kuchita mogwirizana ndi chikumbumtima chake, popanda kuweruza ena amene angathetse nkhaniyo mwanjira ina koma ali ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu.—Aroma 14:2-4, 12.
Ngakhale ngati zakudya zokhala ndi mwazi zingapangidwe, kungachitikedi kuti zimenezi sizimachitika mofala chifukwa cha kukwera mtengo, malamulo, kapena zochititsa zina. Mwachitsanzo, Food Processing (September 1991) inati: “Kwa okonza amenewo amene ali ndi mavuto alionse ndi yosachepera pa 1% (m’nyama yokonzedwa) ya plasma ya nyama yang’ombe yowoletsedwa ndi kuwonjezeredwa mwazi mumsanganizowo, msanganizo woloŵa m’malo ndiwo zinthu za protini yamadzi ndipo ungatsimikiziridwe kukhala Woyenera.”
Kuyenera kugogomezeredwa kuti lamulo, mwambo, kapena kufuna m’maiko ambiri zimafunikiritsa kuti mwazi kawirikawiri uchotsedwe m’nyama yophedwa ndi kuti mwazi woterowo usagwiritsiridwe ntchito m’zakudya zina. Ngati palibe maziko olimba olingalilira kuti mkhalidwewo ngwosiyana m’malowo kapena kuti masinthidwe aakulu achitika posachedwapa, Akristu ayenera kupewa kuvutika maganizo ndi zothekera chabe kapena mphekesera. Komabe, pamene kuli kotsimikizirika kapena kothekera kwambiri kuti mwazi umagwiritsiridwa ntchito mofala—kaya ndim’chakudya kapena m’mankhwala—tiyenera kutsimikizira kumvera lamulo la Mulungu la kusala mwazi.