Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/15 tsamba 4-7
  • Chifukwa Chake Mgonero wa Ambuye Uli ndi Tanthauzo kwa Inu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Mgonero wa Ambuye Uli ndi Tanthauzo kwa Inu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Chinayambitsidwa?
  • “Ndinalandira kwa Ambuye”
  • Kuchikumbukira Kaŵirikaŵiri Motani?
  • Tanthauzo la Zizindikiro
  • Kodi Ayenera Kudya Ndani?
  • Mmene Chimakuyambukirirani
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • ‘Kuzindikira Zimene Ife Tiri’—Panthawi ya Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/15 tsamba 4-7

Chifukwa Chake Mgonero wa Ambuye Uli ndi Tanthauzo kwa Inu

YESU KRISTU anayambitsa Mgonero wa Ambuye pa usiku womalizira wa moyo wake waumunthu. Panali pa madzulo a Lachinayi, March 31, ndipo Yesu anafa masana a Lachisanu, April 1. Popeza kuti masiku a kalenda Yachiyuda anayambira madzulo a tsiku lina mpaka madzulo a tsiku lotsatira, zonse ziŵiri Mgonero wa Ambuye umenewu ndi imfa ya Yesu zinachitika pa Nisani 14, 33 C.E.

Kodi nchifukwa ninji Yesu anayambitsa chakudya chimenechi? Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mkate ndi vinyo zimene iye anagwiritsa ntchito? Kodi ndani ayenera kudya? Kodi chakudya chimenechi chiyenera kusungidwa mwakaŵirikaŵiri chotani? Ndipo kodi ndimotani mmene chingakhalire ndi tanthauzo kwa inu?

Kodi Nchifukwa Ninji Chinayambitsidwa?

Ponena za Mgonero wa Ambuyewo, Yesu anauza atumwi ake kuti: ‘Pitirizani kuchita ichi pondikumbukira.’ Malinga ndi matembenuzidwe ena, iye anati: “Chitani ichi monga chikumbutso changa.” (1 Akorinto 11:24; The New English Bible) M’chenicheni, kaŵirikaŵiri Mgonero wa Ambuye umatchedwa Chikumbutso cha imfa ya Kristu.

Yesu anafa monga wosunga umphumphu wochirikiza ulamuliro wa Yehova ndipo chotero anatsimikizira Satana kukhala wotonza wonama chifukwa cha kuneneza kuti anthu owongoka anatumikira Mulungu nzolinga zadyera chabe. (Yobu 2:1-5) Imfa yake inapangitsa mtima wa Mulungu kukondwera.​—Miyambo 27:11.

Kupyolera mwa imfa yake monga munthu wangwiro, Yesu ‘anaperekanso moyo wake dipo mosinthana ndi ambiri.’ (Mateyu 20:28) Pochimwira Mulungu, munthu woyamba anataya moyo waumunthu wangwiro ndi ziyembekezo zake. Koma “Mulungu anakonda dziko lapansi [la anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Inde, ‘Mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.’​—Aroma 6:23.

“Ndinalandira kwa Ambuye”

Omveketsa kukumbukiridwa kwa imfa ya Kristu ndiwo mawu a mtumwi Paulo awa: ‘Ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate; ndipo mmene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa. Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthaŵi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa. Pakuti nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.’​—1 Akorinto 11:23-26.

Popeza kuti Paulo sanali limodzi ndi Yesu ndi atumwi 11 pa Nisani 14, 33 C.E., mwachiwonekere chidziŵitso chimenechi ‘anachilandira kwa Ambuye’ mwavumbulutso louziridwa. Yesu anayambitsa Chikumbutso “usiku uja anaperekedwa” ndi Yudase kwa adani achipembedzo Achiyuda, amene anasonkhezera Aroma kupachika Kristu. Awo oyeneretsedwa kudya zizindikiro za mkate ndi kumwa vinyo akatero momkumbukira.

Kuchikumbukira Kaŵirikaŵiri Motani?

Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mawu a Paulo akutiwo: ‘Nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye’? Akristu odzozedwa okhulupirika akadya zizindikiro za Chikumbukutso “nthaŵi zonse” kufikira imfa yawo, pambuyo pake kuukitsidwira ku moyo wakumwamba. Chotero iwo akalengeza nthaŵi zonse pamaso pa Mulungu ndi dziko chikhulupiriro chawo m’kakonzedwe ka Yehova ka nsembe ya Yesu. Kwa utali wotani? “Kufikira akadza iye,” anatero Paulo, mwachiwonekere kutanthauza kuti kusungidwa kumeneku kukapitirizabe kufikira kufika kwa Yesu kulandira otsatira ake odzozedwa kumwamba mwachiukiriro mkati mwa “kukhalapo kwake.” (1 Atesalonika 4:14-17) Zimenezi ziri zogwirizana ndi mawu a Kristu kwa atumwi okhulupirika 11: “Ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.”​—Yohane 14:3.

Kodi imfa ya Kristu iyenera kukumbukiridwa tsiku lirilonse kapena mwinamwake mlungu uliwonse? Eya, Yesu anayambitsa Mgonero wa Ambuye ndipo anaphedwa pa Paskha, amene anali wokumbukira chilanditso cha Aisrayeli mu ukapolo wa Igupto. M’chenicheni, iye akutchedwa ‘Kristu paskha wathu’ chifukwa chakuti iye ali Mwanawankhosa woperekedwera nsembe Akristu. (1 Akorinto 5:7) Paskha inachitidwa kamodzi kokha pachaka, pa Nisani 14. (Eksodo 12:6, 14; Levitiko 23:5) Izi zikupereka lingaliro lakuti imfa ya Yesu iyenera kukumbukiridwa monga momwe Paskha inachitidwira​—kamodzi pa chaka, osati tsiku lirilonse kapena mlungu uliwonse.

Kwa zaka mazana angapo ochuluka odzinenera kukhala Akristu anakumbukira imfa ya Yesu kamodzi pachaka. Chifukwa chakuti iwo anatero pa Nisani 14, anali kutchedwa a Quartodecimans, kutanthauza a “tsiku lakhumi ndi chinayi.” Ponena za iwo, wolemba mbiri J. L. von Mosheim analemba kuti: “Akristu a ku Asia Minor anali ndi chizoloŵezi chakuchita phwando lamadyerero lopatulika limeneli, lokumbukira kukhazikitsidwa kwa Mgonero wa Ambuye, ndi imfa ya Yesu Kristu, pa nthaŵi imodzimodzi imene Ayuda anadya mwana wankhosa wa Paskha, ndiko kuti pamadzulo a tsiku lakhumi ndi chinayi la mwezi woyamba [Nisani]. . . . Iwo analingalira chitsanzo cha Kristu monga lamulo loyenera kutsatiridwa.”

Tanthauzo la Zizindikiro

Paulo ananena kuti Yesu “anatenga mkate; ndipo mmene adayamika, ananyema.” Mtanda wa mkate wonga bisiketi umenewo wophikidwa ndi ufa ndi madzi popanda chotupitsa (kapena, chimera) unafunikira kunyemedwa kuti udyedwe. M’maphiphiritso a Baibulo, chotupitsa chimatanthauza uchimo kapena chisalungamo. Pamene anali kulimbikitsa Akristu a ku Korinto kuchotsa mwamuna wachisembwere mumpingo, Paulo anati: ‘Kodi simudziŵa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse? Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paskha wathu waphedwa, ndiye Kristu; chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuwona mtima, ndi chowonadi.’ (1 Akorinto 5:6-8) Monga momwe ntchintchi yaing’ono yotupitsidwa imatupitsa mtanda wonse, kapena ntchintchi yonse ya mkate, chotero mpingo ukakhala wodetsedwa m’maso mwa Mulungu ngati chisonkhezero choipitsa cha munthu wochimwayo sichinachotsedwe. Iwo anafunikira kuchotsa “chotupitsa” pakati pawo, monga momwedi Aisrayeli sakafunikira kukhala ndi chotupitsa m’nyumba zawo mkati mwa Phwando la Mikate Yopanda Chotupitsa limene linatsatira Paskha.

Ponena za mkate wopanda chotupitsa wa Chikumbutso, Yesu anati: ‘Ichi ndi thupi langa kaamba ka inu.’ (1 Akorinto 11:24) Mkate umaimira thupi laumunthu langwiro la Yesu, ponena za limene Paulo analemba kuti: ‘[Yesu] poloŵa m’dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera Ine. Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwera nazo; Pamenepo ndinati, Tawonani, ndafika, (Pamutu pake pa bukhu palembedwa za Ine) Kudzachita chifuniro chanu, Mulungu. . . . Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.’ (Ahebri 10:5-10) Thupi laumunthu langwiro la Yesu linali lopanda uchimo ndipo linatumikira monga nsembe ya dipo kwa anthu.​—Ahebri 7:26.

Pambuyo pakupempherera chikho cha vinyo wofiira wosakoleretsedwa, Yesu anati: ‘Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga.’ (1 Akorinto 11:25) Matembenuzidwe ena amati: “Chikho ichi chimatanthauza pangano latsopano lotsimikiziridwa ndi mwazi wanga.” (Moffatt) Monga momwe mwazi wa ng’ombe zoperekedwa nsembe ndi mbuzi unatsimikizira pangano la Chilamulo pakati pa Mulungu ndi mtundu wa Israyeli, chotero mwazi wotsanuliridwa mu imfa wa Yesu unachititsa kugwira ntchito kwa pangano latsopano. Kutchulidwa kwa pangano limenelo kumatithandiza kuti tidziŵe akudya zizindikiro za Chikumbutso ovomerezedwa.

Kodi Ayenera Kudya Ndani?

Atsatiri odzozedwa a Yesu, amene ali m’pangano latsopano, ali ndi kuyenera kwa kudya zizindikiro za Chikumbutso. Pangano limeneli lapangidwa pakati pa Mulungu ndi Israyeli wauzimu. (Yeremiya 31:31-34; Agalatiya 6:16) Koma pangano latsopano potsirizira pake lidzabweretsa madalitso kwa anthu onse omvera, ndipo inu mungathe kukhala pakati pa olandira madalitso amenewo.

Akudya zizindikiro za Chikumbutso ayenera kukhala m’pangano laumwini la Ufumu limene Yesu anapanga. Pamene anayambitsa chakudya ichi, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Ndikuchita pangano ndi inu, monga momwe Atate wanga wachitira pangano la Ufumu ndi ine.” (Luka 22:29, NW) Pangano la Ufumu lochitidwa ndi Mulungu ndi Mfumu Davide linasonya mtsogolo ku kufika kwa Yesu, amene akalamulira kosatha, mu Ufumu wakumwamba. Aisrayeli auzimu a 144,000 amene adzakhala ndi phande m’kulamulira limodzi naye afotokozedwa kukhala akuimirira pa Phiri la Ziyoni lakumwamba ndi Mwanawankhosa, Yesu Kristu. Ataukitsidwa, iwo adzalamulira ndi Kristu monga mafumu anzake ndi ansembe. (2 Samueli 7:11-16; Chivumbulutso 7:4; 14:1-4; 20:6) Ali awo okha amene ali m’pangano latsopano ndi pangano laumwini ndi Yesu amene moyenerera amadya zizindikiro za Mgonero wa Ambuye.

Mzimu wa Mulungu umachitira umboni ndi mzimu wa odzozedwawo kuti iwo ali ana Ake ndi oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu. Paulo analemba kuti: ‘Mzimu wokha uchita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.’ (Aroma 8:16, 17) Mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, umawapatsa odzozedwawo chitsimikiziro cha mtima chapadera cha moyo wakumwamba. Iwo amawona zonse zimene Malemba amanena ponena za moyo wakumwamba kukhala zolunjikitsidwa kwa iwo ndipo ngofunitsitsa kusiya pano zinthu zonse za padziko lapansi, kuphatikizapo moyo waumunthu ndi ziŵalo za banja. Ngakhale kuti moyo m’Paradaiso wapadziko lapansi udzakhala wokondweretsa, iwo samakhala ndi chiyembekezo chimenecho. (Luka 23:43) Chiyembekezo cha kumwamba chotsimikizirika ndi chosasinthika osati chozikidwa pa malingaliro achipembedzo chonyenga chimawachititsa kuyenerera kudya zizindikiro za Chikumbutso.

Yehova sakakondwera ngati munthu anadzinenera yekha monga woitanidwa kukakhala mfumu ndi wansembe wakumwamba pamene iye sanaitanidwe motero. (Aroma 9:16; Chivumbulutso 22:5) Mulungu anapha Kora chifukwa chakufunafuna monyada kukhala wansembe. (Eksodo 28:1; Numeri 16:4-11, 31-35) Chotero, bwanji ngati malingaliro amphamvu kapena ziganizo zakale za chipembedzo zinapangitsa munthuyo kudya molakwa zizindikiro za chikumbutso? Pamenepo iye ayenera kusiya kudya ndi kupempherera modzichepetsa kuti Mulungu amkhululukire.​—Salmo 19:13.

Mmene Chimakuyambukirirani

Munthu safunikira kudya zizindikiro za Chikumbutso kuti apindule ndi nsembe ya dipo la Yesu ndi kulandira moyo wosatha padziko lapansi. Mwachitsanzo, Baibulo silimasonyeza kuti anthu owopa Mulungu onga Abrahamu, Sara, Isake, Rebeka, Boazi, Rute, ndi Davide adzadyako zizindikiro zimenezi. Komatu iwo ndi ena onse okhumba moyo wopanda mapeto pa chiunda chino adzafunikira kusonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Kristu ndi m’kakonzedwe ka Yehova ka nsembe ya dipo la Yesu. (Yohane 3:36; 14:1) Kusungidwa kwa chaka ndi chaka kwa imfa ya Kristu kumatumikira monga chokumbutsa nsembe yaikulu imeneyo.

Kufunika kwa nsembe ya Yesu kunasonyezedwa pamene mtumwi Yohane anati: ‘Ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.’ (1 Yohane 2:1, 2) Akristu odzozedwa angathe kunena kuti Yesu “ndiye chiwombolo cha machimo [awo].” Komabe, iye alinso nsembe ya machimo a dziko lonse, akumapangitsa moyo wamuyaya kukhala wotheka kwa anthu omvera m’dziko lapansi la Paradaiso limene tsopano layandikira kwambiri!

Mwakufikapo pa chikumbutso cha imfa ya Kristu, mudzapindula ndi nkhani ya Baibulo yosonkhezera maganizo. Mudzakumbutsidwa za ukulu wa zimene Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu atichitira. Kudzakhala kopindulitsa mwauzimu kusonkhana ndi anthu amene amalemekeza kwambiri Mulungu ndi Kristu ndi nsembe ya dipo la Yesu. Chochitikacho chingalimbikitsedi chikhumbo chanu chakukhala wolandira chisomo cha Mulungu kukumatsogolera ku moyo wamuyaya. Tikukuitanani ndi mtima wonse kukasonkhana ndi Mboni za Yehova pambuyo pa kuloŵa kwa dzuŵa pa April 6, 1993, kukakumbukira imfa ya Yesu Kristu chifukwa chakuti Mgonero wa Ambuye ungakhale ndi tanthauzo lalikulu kwa inu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena