-
Zimene Zachitika M’zaka 100 Zimene Ufumu Wakhala UkulamuliraNsanja ya Olonda—2015 | November 15
-
-
2. (a) Kodi n’kutheka kuti panali anthu angati pamene Yesu anapereka lamulo la pa Mateyu 28:19, 20? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti ambiri mwa anthuwa anadzakhala Akhristu?
2 Tsiku lina Yesu ataukitsidwa, anakumana ndi anthu oposa 500. (1 Akor. 15:6) N’kutheka kuti pa nthawiyi m’pamene anapereka lamulo lakuti otsatira ake azikalalikira “anthu a mitundu yonse.”a Koma ntchito imene anawauza kuti agwireyi sinali yophweka. Iye ananeneratu kuti ntchito yolalikirayi idzachitika mpaka “m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Choncho tikamagwira nawo ntchito imeneyi timathandiza kuti ulosiwu ukwaniritsidwe.—Mat. 28:19, 20.
-
-
Zimene Zachitika M’zaka 100 Zimene Ufumu Wakhala UkulamuliraNsanja ya Olonda—2015 | November 15
-
-
a Zikuoneka kuti ambiri mwa anthuwa anadzakhala Akhristu. Tikutero chifukwa chakuti m’kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Korinto, ananena kuti anthu oposa 500 aja tsopano anali “abale.” Iye ananenanso kuti: “Ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero, koma ena anagona mu imfa.” Choncho zikuoneka kuti Paulo ankadziwana ndi ena mwa Akhristu amene analipo pamene Yesu ankapereka lamulo loti ophunzira ake azilalikira.
-