Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 3/1 tsamba 7
  • Kuukitsidwa kwa Yesu Kudzapangitsa Anthu Kupeza Moyo Wosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuukitsidwa kwa Yesu Kudzapangitsa Anthu Kupeza Moyo Wosatha
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Timakhulupirira Kuti Anthu Amene Anamwalira Adzauka
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • “Akufa Adzaukitsidwa”
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Ndili ndi Chiyembekezo mwa Mulungu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 3/1 tsamba 7

Kuukitsidwa kwa Yesu Kudzapangitsa Anthu Kupeza Moyo Wosatha

KUUKITSIDWA kwa Yesu kuli ndi phindu lalikulu kwa ife. Mtumwi Paulo anafotokoza kufunika kwa nkhani imeneyi pamene analemba kuti: “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa. Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi. Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akorinto 15:20-22.

Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16 m’chaka cha 33 C.E. Pa tsikuli, Ayuda ankapereka kwa Yehova Mulungu zipatso zoyambirira m’kachisi ku Yerusalemu. Potchula Yesu kuti chipatso choyambirira, Paulo anasonyeza kuti palinso anthu ena amene adzaukitsidwe.

Kenako Paulo anatchula chinthu chimene chinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu. Iye anati: “Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi.” Anthufe timafa chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro zimene tinatengera kwa Adamu. Komabe pamene Yesu anapereka moyo wake wangwiro n’kuukitsidwa, anachititsa kuti anthu adzamasulidwe ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Pomveketsa mfundoyi, pa Aroma 6:23, Paulo analemba kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”

Yesu nayenso anafotokoza kufunika kwa imfa yake komanso kuukitsidwa kwake. Iye anati: “Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba, kuti aliyense wokhulupirira iye akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:14-16.

Tangoganizani, anthu adzakhala ndi moyo wosatha wopanda mavuto kapena chisoni. (Chivumbulutso 21:3, 4) Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri. Pofotokoza zimenezi katswiri wina wamaphunziro ananena kuti: “Tikaona manda timakumbukira kuti moyo ndi waufupi. Koma mfundo yoti akufa adzauka, imatikumbutsa kuti anthu sadzapitiriza kufa mpaka kalekale.” Kuukitsidwa kwa Yesu kudzachititsa kuti anthu apeze moyo wosatha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena