“Kuchititsa Kwanu Sikuli Chabe”
1 Ndi mawu olimbikitsa bwanji! Kuchititsa kwanu muutumiki wa Yehova sikuli chabe. (1 Akor. 15:58) Mosiyana ndi zimenezo, lingalirani mmene anthu amavutikira kugwira ntchito molimbika kuti asinthe umoyo wawo kapena kuti apeze ndalama. Iwo angachite maphunziro apamwamba kwa zaka zambiri kapena kugwira ntchito ngati akapolo kuti akhale opeza bwino m’zachuma. Komabe, chifukwa cha “zom’gwera m’nthaŵi mwake,” mwina sangapeze ulemerero umene amafuna, kapena angakakamizike kukhutira ndi zinthu zakuthupi zochepa kwambiri zimene ali nazo osati zimene amafuna. Monga zinthu ‘zongosautsa mtima,’ ntchito zawo zonse zili chabe. (Mlal. 1:14; 9:11) Chotero, n’kopindulitsa kwambiri kuti tili ndi zochita zambiri mu ntchito yokhayo imene siili chabe popeza ili ndi phindu losatha!
2 Ntchito Imene Ili Yaphindudi: Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiyo ntchito yofunika kwambiri padziko lapansi. Ndi ntchito imene iyenera kuchitidwa kaya anthu amvetsere kapena ayi. Tikufuna kuti tithe kunena monga ananenera Paulo kuti: “Ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse. Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.”—Mac. 20:26, 27.
3 Anthu akamvetsera ndi kulabadira uthenga wa Ufumu, timasangalala kwambiri! Mayi wina wachitsikana anaferedwa azakhali ake. Ankadzifunsa kuti kodi azakhali akewo apita kumwamba kapena kuhelo? Mogwiritsa ntchito dzina la Yehova, monga mmene mchemwali wake anam’phunzitsira, anapemphera kwa Mulungu kuti am’thandize. Mosakhalitsa, anayamba kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu. Zimenezi zinam’pangitsa kuona moyo mwanjira yatsopano ndipo analeka kuyanjana ndi magulu aupandu a mumsewu. Mayi wachitsikanayu analeka kusuta, kumwa mankhwala osokoneza bongo, ndiponso kuba. Mayiyu akuti: “Chikondi cha Yehova chokha ndicho chinandisiyitsa moyo woipa umenewu. Yehova yekha mwa chifundo chake chachikulu anandipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha.” Sakutayiranso nthaŵi ya moyo wake pa zinthu zachabechabe.
4 Ngakhale anthu akane kumvetsera, mumakwaniritsabe china chake chaphindu. Amadziŵa kuti Mboni za Yehova zinawafikira. Umphumphu, kukhulupiririka, ndi chikondi chanu zimakhala zotsimikizika. Choncho, kodi kuchititsa kwathu mu ntchito ya Ambuye kuli chabe? N’zosatheka!