Kugaŵana Chitonthozo Chimene Yehova Amapereka
“Chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziŵa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.”—2 AKORINTO 1:7.
1, 2. Kodi zinali motani kwa ambiri amene akhala Akristu lerolino?
AMBIRI amene amaŵerenga Nsanja ya Olonda anakula opanda chidziŵitso cha choonadi cha Mulungu. Mwinamwake ndi mmene zilili kwa inunso. Ngati ndi choncho, takumbukirani mmene munamvera pamene maso anu akumvetsa zinthu anayamba kutseguka. Mwachitsanzo, pamene munamva kwa nthaŵi yoyamba kuti akufa samazunzika koma ali osadziŵa kanthu, kodi simunamve mpumulo? Ndipo pamene munaphunzira za chiyembekezo cha akufa, kuti mabiliyoni adzaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu, kodi simunatonthozedwe?—Mlaliki 9:5, 10; Yohane 5:28, 29.
2 Bwanji ponena za lonjezo la Mulungu la kuthetsa kuipa ndi kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso? Pamene munaphunzira zimenezi, kodi sizinakutonthozeni ndi kukupatsani chidwi cha chiyembekezo? Kodi munamva motani pamene munamva kwa nthaŵi yoyamba za kuthekera kwa kusafa koma kupulumuka kuloŵa m’Paradaiso wa padziko lapansi alimkudzayo? Ndithudi, zimenezo zinakusangalatsani kwabasi. Inde, munalandira uthenga wotonthoza wa Mulungu umene tsopano ukulalikidwa padziko lonse ndi Mboni za Yehova.—Salmo 37:9-11, 29; Yohane 11:26; Chivumbulutso 21:3-5.
3. Kodi nchifukwa ninji aja amene amagaŵana ndi ena uthenga wa chitonthozo wa Mulungu nawonso amakumana ndi chisautso?
3 Komabe, pamene munayesa kuuzako ena uthenga wa Baibulo, inunso munazindikira kuti “si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Mwinamwake ena a mabwenzi anu akale anakusekani posonyeza chikhulupiriro chanu m’malonjezo a Baibulo. Mwinamwake munazunzidwa chifukwa cha kupitiriza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mwinamwake chitsutsocho chinakula pamene munayamba kupanga masinthidwe m’moyo wanu kuugwirizanitsa ndi mapulinsipulo a Baibulo. Munayamba kuona chisautso chimene Satana ndi dziko lake amadzetsa pa anthu amene amalandira chitonthozo cha Mulungu.
4. Kodi okondwerera achatsopano angachite mosiyanasiyana motani pamene akumana ndi chisautso?
4 Mwachisoni, monga momwe Yesu ananeneratu, chisautso chimachititsa ena kupunthwa ndi kuleka kuyanjana ndi mpingo wachikristu. (Mateyu 13:5, 6, 20, 21) Ena amapirira chisautso mwa kusumika maganizo awo pa malonjezo otonthoza amene amaphunzira. M’kupita kwa nthaŵi amapatulira moyo wawo kwa Yehova ndi kubatizidwa monga ophunzira a Mwana wake, Yesu Kristu. (Mateyu 28:19, 20; Marko 8:34) Ndithudi, chisautso sichimaleka pamene Mkristu abatizidwa. Mwachitsanzo, kudzisungira bwino kungakhale nkhondo yaikulu kwa munthu amene kale anali wachisembwere. Ena amafunikira kulimbana ndi chitsutso cha abanja osakhulupirira. Mulimonse mmene chisautsocho chingakhalire, onse amene mokhulupirika amalondola moyo wa kudzipatulira kwa Mulungu angakhale otsimikizira za chinthu chimodzi. Mwa njira yapadera kwambiri, adzapeza chitonthozo cha Mulungu ndi chithandizo chake.
“Mulungu wa Chitonthozo Chonse”
5. Pokumana ndi mayesero ambiri, kodi Paulo anapezanso chiyani?
5 Munthu wina amene anayamikira kwambiri chitonthozo chimene Mulungu amapereka anali mtumwi Paulo. Atapyola m’nthaŵi ya mayesero aakulu mu Asiya ndi Makedoniya, anapeza chitonthozo chachikulu pamene anamva kuti mpingo wa Akorinto unalabadira bwino chidzudzulo cha m’kalata yake. Zimenezi zinamsonkhezera kuwalembera kalata yachiŵiri, imene ili ndi mawu achitamando otsatirawa: “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo [zachisoni, NW] ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
6. Kodi tikuphunziraponji pa mawu a Paulo opezeka pa 2 Akorinto 1:3, 4?
6 Mawu ouziridwa ameneŵa akutiuza zambiri. Tiyeni tiwapende. Pamene Paulo apereka chitamando kapena chiyamikiro kwa Mulungu kapena pamene apempha kwa iye m’makalata ake, kaŵirikaŵiri timapeza kuti amaphatikizaponso chiyamikiro chachikulu kwa Yesu, Mutu wa mpingo wachikristu. (Aroma 1:8; 7:25; Aefeso 1:3; Ahebri 13:20, 21) Chifukwa chake, Paulo akulankhula mawu achitamando awa kwa ‘Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.’ Ndiyeno, kwa nthaŵi yoyamba m’makalata ake, akugwiritsira ntchito nauni yachigiriki yotembenuzidwa “zifundo zachisoni.” Nauni imeneyi ikuchokera ku liwu logwiritsiridwa ntchito kusonyeza chisoni pa kuvutika kwa wina. Motero Paulo akulongosola chisoni cha Mulungu kwa mtumiki Wake wokhulupirika aliyense amene avutika m’nsautso—chisoni chimene chimasonkhezera Mulungu kuchitapo kanthu mwachifundo kaamba ka iwo. Chomalizira, Paulo anayang’ana kwa Yehova monga magwero a mkhalidwe wokhumbirika umenewu mwa kumutcha ‘Atate wa zifundo zachisoni.’
7. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova ali ‘Mulungu wa chitonthozo chonse’?
7 “Zifundo zachisoni” za Mulungu zimapereka mpumulo kwa munthu wokhala m’nsautso. Chifukwa chake, Paulo akupitiriza kulongosola Yehova kuti ali “Mulungu wa chitonthozo chonse.” Chotero, chitonthozo chilichonse chimene tingakhale nacho mwa kukoma mtima kwa okhulupirira anzathu, tiyenera kuchiona kukhala chochokera kwa Yehova. Palibe chitonthozo chenicheni ndi chokhalitsa chilichonse chosachokera kwa Mulungu. Ndiponso, iye ndiye analenga munthu m’chifanizo chake, akumatikhozetsa kukhala otonthoza. Ndipo ndi mzimu woyera wa Mulungu umene umasonkhezera atumiki ake kusonyeza chifundo chachisoni kwa aja ofunikira chitonthozo.
Ophunzitsidwa Kukhala Otonthoza
8. Ngakhale kuti Mulungu sindiye amadzetsa mayesero athu, kodi kupirira kwathu nsautso kungakhale ndi chiyambukiro chopindulitsa chotani pa ife?
8 Pamene kuli kwakuti Yehova Mulungu amalola mayesero osiyanasiyana amene amadza pa atumiki ake okhulupirika, sali iye amene amawapereka. (Yakobo 1:13) Komabe, chitonthozo chimene amapereka pamene tipirira nsautso chikhoza kutiphunzitsa kukhala ozindikira kwambiri zosoŵa za ena. Ndi chotulukapo chotani? “Kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.” (2 Akorinto 1:4) Motero Yehova amatiphunzitsa kugaŵana bwino chitonthozo chake ndi okhulupirira anzathu ndi aja amene tikumana nawo mu utumiki wathu pamene tikutsanzira Kristu ndi ‘kutonthoza onse akulira maliro.’—Yesaya 61:2; Mateyu 5:4.
9. (a) Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupirira mavuto? (b) Kodi ena amatonthozedwa motani pamene ife tipirira nsautso mokhulupirika?
9 Paulo anapirira mavuto ake ambiri chifukwa cha chitonthozo chachikulu chimene anachilandira kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu. (2 Akorinto 1:5) Ifenso tingapeze chitonthozo chachikulu mwa kusinkhasinkha pa malonjezo amtengo wapatali a Mulungu, mwa kupemphera kaamba ka chichirikizo cha mzimu wake woyera, ndi mwa kulandira mayankho a Mulungu pa mapemphero athu. Mwakutero tidzalimbitsidwa kuti tipitirizebe kuchirikiza uchifumu wa Yehova ndi kutsimikiziritsa Mdyerekezi kukhala wonama. (Yobu 2:4; Miyambo 27:11) Pamene tapirira mokhulupirika mtundu uliwonse wa nsautso, mofanana ndi Paulo, tiyenera kupereka thamo lonse kwa Yehova, amene chitonthozo chake chimakhozetsa Akristu kukhalabe okhulupirika poyang’anizana ndi chiyeso. Kupirira kwa Akristu okhulupirika kuli ndi chiyambukiro chotonthoza abale, kuchititsa ena kukhala okonzekera motsimikiza mtima za ‘kupirira masautso omwewo.’—2 Akorinto 1:6.
10, 11. (a) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zinachititsa mavuto mumpingo wa ku Korinto wakale? (b) Kodi Paulo anatonthoza motani mpingo wa Akorinto, ndipo ndi chiyembekezo chotani chimene iye anasonyeza?
10 Akorinto anakumana ndi mavuto amene amagwera Akristu onse oona. Ndiponso, anafunikira uphungu wa kuchotsa wadama wosalapa. (1 Akorinto 5:1, 2, 11, 13) Kulephera kuchita zimenezi ndi kulephera kuthetsa mikangano ndi mipatuko kunadzetsa chitonzo pa mpingowo. Koma potsirizira pake iwo anagwiritsira ntchito uphungu wa Paulo ndi kusonyeza kulapa kwenikweni. Chifukwa chake, iye anawathokoza kwambiri ndi kunena kuti kulabadira kwawo uphungu wa m’kalata yake kunamtonthoza. (2 Akorinto 7:8, 10, 11, 13) Zikuoneka kuti, wochotsedwayo nayenso anali atalapa. Chotero Paulo anawalangiza kuti ‘amkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo angamizidwe ndi chisoni chochulukacho.’—2 Akorinto 2:7.
11 Kalata yachiŵiri ya Paulo iyenera kuti inatonthozadi mpingo wa Akorinto. Ndipo chimenechi chinali chimodzi cha zolinga zake. Analongosola kuti: “Chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziŵa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.” (2 Akorinto 1:7) Pomaliza kalata yake, Paulo analimbikitsa kuti: “Mutonthozedwe; . . . ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.”—2 Akorinto 13:11.
12. Kodi nchosoŵa chotani chimene Akristu onse ali nacho?
12 Ndi phunziro lofunika chotani nanga limene tingatengepo pa zimenezi! Ziŵalo zonse za mpingo wachikristu zimafunikira ‘kuyanjana m’chitonthozo’ chimene Mulungu amapereka kupyolera m’Mawu ake, mzimu wake woyera, ndi gulu lake la padziko lapansi. Ngakhale ochotsedwa angafunikire chitonthozo ngati alapa ndi kuwongolera njira yawo yolakwa. Chotero, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka makonzedwe achifundo akuwathandiza. Kamodzi pachaka akulu aŵiri angachezere anthu ena ochotsedwa. Ameneŵa angakhale asakusonyezanso mzimu wachipanduko kapena kuchita tchimo lalikulu ndipo angafunikire chithandizo kuti atenge njira zofunikira kotero kuti abwezeretsedwe.—Mateyu 24:45; Ezekieli 34:16.
Chisautso cha Paulo mu Asiya
13, 14. (a) Kodi Paulo anailongosola motani nthaŵi ya masautso aakulu omwe anakumana nawo mu Asiya? (b) Kodi Paulo angakhale anali kukumbukira chochitika chiti?
13 Mtundu wa kuvutika umene mpingo wa Akorinto unakumana nawo pofika panthaŵiyi sukanayerekezeredwa ndi masautso ambiri amene Paulo anawapirira. Chotero, iye anakhoza kuwakumbutsa kuti: “Sitifuna abale, kuti mukhale osadziŵa za chisautso chathu tinakomana nacho m’Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhaŵa ngakhale za moyo wathu; koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa; amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene tiyembekezera kuti adzalanditsanso.”—2 Akorinto 1:8-11.
14 Akatswiri a Baibulo ena amakhulupirira kuti Paulo anali kunena za chipolowe cha m’Efeso, chomwe chikanatayitsa moyo wa Paulo limodzinso ndi miyoyo ya oyenda naye aŵiri a ku Makedoniya, Gayo ndi Aristarko. Akristu aŵiriŵa anawakhwekhweretsera m’bwalo lodzaza anthu amene ‘anafuula monga maola aŵiri, Wamkulu ndi Artemi [mlungu wamkazi] wa Aefeso’! Potsirizira pake, mdindo wa mumzinda anakhoza kukhalitsa bata khamulo. Ngozi imeneyi pa moyo wa Gayo ndi Aristarko iyenera kuti inamvutitsa maganizo kwambiri Paulo. Ndipo iye anafuna kuloŵa kuti akakambitsirane ndi khamu laukali limenelo, koma analetsedwa kuika moyo wake pangozi mwa njira imeneyi.—Machitidwe 19:26-41.
15. Kodi ndi mkhalidwe wowopsa kwambiri wotani umene ungakhale utalongosoledwa pa 1 Akorinto 15:32?
15 Komabe, Paulo angakhale anali kulongosola mkhalidwe wowopsa kwambiri kuposa chochitika chomwe chasimbidwacho. M’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, Paulo anafunsa kuti: “Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji?” (1 Akorinto 15:32) Izi zingatanthauze kuti moyo wa Paulo unaikidwa pangozi osati chabe ndi anthu onga zilombo komanso ndi zilombo zenizeni m’bwalo la maseŵero la ku Efeso. Nthaŵi zina apandu analangidwa mwa kukakamizidwa kumenyana ndi zilombo pamene anthu a ludzu la mwazi anali kupenyerera. Ngati Paulo anatanthauza kuti anayang’anizana ndi zilombo zenizeni, potsirizira penipeni ayenera kuti anapulumutsidwa mozizwitsa ku imfa yankhalwe, monga momwe Danieli anapulumutsidwira ku mikango yeniyeni.—Danieli 6:22.
Zitsanzo Zamakono
16. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zambiri zikhoza kumvetsetsa masautso amene Paulo anakumana nawo? (b) Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani ponena za aja omwe anafa kaamba ka chikhulupiriro chawo? (c) Kodi kupulumuka imfa kodabwitsa kwa Akristu kwakhala ndi chiyambukiro chabwino chotani?
16 Akristu ambiri amakono akhoza kumvetsetsa bwino masautso amene Paulo anakumana nawo. (2 Akorinto 11:23-27) Lerolinonso, Akristu “athodwa kwakukulu, koposa mphamvu [yawo],” ndipo ambiri akumana ndi mikhalidwe mmene ‘ada nkhaŵa ngakhale za moyo wawo.’ (2 Akorinto 1:8) Ena afa mwa kuphedwa kwa unyinji ndi mwa kuzunzidwa. Tiyenera kukhala otsimikizira kuti mphamvu ya Mulungu yopatsa chitonthozo inawakhozetsa kupirira ndi kuti iwo anafa ali osumika mitima ndi maganizo pa kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chawo, chiyembekezo cha kumwamba kapena padziko lapansi. (1 Akorinto 10:13; Afilipi 4:13; Chivumbulutso 2:10) M’zochitika zina, Yehova watsogolera zinthu m’njira yake, ndipo abale athu apulumutsidwa ku imfa. Mosakayikira, aja omwe apulumutsidwa mwa njira imeneyo akulitsa chidaliro chawo “pa Mulungu wakuukitsa akufa.” (2 Akorinto 1:9) Pambuyo pake, anakhoza kulankhula ndi chitsimikizo chokulirapo pamene anali kugaŵira ena uthenga wachitonthozo wa Mulungu.—Mateyu 24:14.
17-19. Kodi ndi zochitika zotani zimene zimasonyeza kuti abale athu m’Rwanda agaŵana m’chitonthozo cha Mulungu?
17 Posachedwapa abale athu okondedwa m’Rwanda anakumana ndi zimene Paulo ndi anzake anakumana nazo. Ambiri anataya miyoyo yawo, koma zoyesayesa za Satana zinalephera kuswa chikhulupiriro chawo. M’malo mwake, abale athu m’dzikolo apeza chitonthozo cha Mulungu m’njira zambiri zapadera. M’nthaŵi ya kuphana kwa Atutsi ndi Ahutu a m’Rwanda, panali Ahutu omwe anaika moyo wawo pangozi kuti atetezere Atutsi, ndi Atutsi kuti atetezere Ahutu. Pakati pa ameneŵa panali Mboni zachihutu zimene zinaphedwa ndi akuda mtundu wina opambanitsa kaamba ka kutetezera okhulupirira anzawo. Mwachitsanzo, Gahizi, Mboni yachihutu anaphedwa chifukwa chobisa mlongo Chantal wachitutsi. Mwamuna wa Chantal wachitutsi, Jean, anabisidwa kumalo ena ndi mlongo wachihutu, Charlotte. Masiku 40, Jean ndi mbale wina wachitutsi anakhala chibisalire m’tchumuni chachikulu, akumangotuluka kwa kanthaŵi pang’ono usiku. M’nthaŵi yonseyi, Charlotte anawapatsa chakudya ndi kuwatetezera, ngakhale kuti anali pafupi ndi msasa wa asilikali achihutu. Patsamba limeneli, mukuona chithunzi cha Jean ndi Chantal atapezananso, amene akuyamikira kwambiri kuti alambiri anzawo achihutu ‘anapereka makosi awo’ kaamba ka iwo, mofanana ndi Priskila ndi Akula kaamba ka mtumwi Paulo.—Aroma 16:3, 4.
18 Mboni ina yachihutu, Rwakabubu, inatamandidwa ndi nyuzipepala yotchedwa Intaremara chifukwa cha kutetezera okhulupirira anzake achitutsi.a Iyo inati: “Palinso Rwakabubu, mmodzi wa Mboni za Yehova, amene anapitiriza kubisa anthu uku ndi uku mwa abale ake (ndi mmene amatchera okhulupirira anzawo). Anali kuthera tsiku lonse akumawaperekera chakudya ndi madzi akumwa ngakhale kuti iye akudwala chifuŵa cha asima. Koma Mulungu anamlimbitsa modabwitsa.”
19 Talingaliraninso za okondwerera aŵiri okwatirana achihutu, Nicodeme ndi Athanasie. Kuphana kusanabuke, okwatirana ameneŵa ankaphunzira Baibulo ndi Mboni yachitutsi yotchedwa Alphonse. Mwa kuika moyo wawo pangozi, iwo anabisa Alphonse m’nyumba mwawo. Pambuyo pake anazindikira kuti nyumbayo siinali malo osungika chifukwa chakuti anansi awo achihutu anadziŵa za bwenzi lawo lachitutsilo. Chotero, Nicodeme ndi Athanasie anabisa Alphonse m’dzenje la m’bwalo la panyumba pawo. Kameneka kanali kachitidwe kanzeru chifukwa chakuti anansiwo anayamba kufika kudzafunafuna Alphonse pafupifupi tsiku lililonse. Pamene anali chigonere m’dzenjemo masiku 28, Alphonse anasinkhasinkha pa nkhani za m’Baibulo monga ya Rahabi, amene anabisa Aisrayeli aŵiri patsindwi la nyumba yake m’Yeriko. (Yoswa 6:17) Panthaŵi ino Alphonse akupitiriza ndi utumiki wake m’Rwanda monga mlaliki wa uthenga wabwino, zikumatheka chifukwa chakuti maphunziro ake a Baibulo achihutu aja anaika pangozi moyo wawo kaamba ka iye. Ndipo bwanji za Nicodeme ndi Athanasie? Tsopano ali Mboni za Yehova zobatizidwa ndipo akuchititsa maphunziro a Baibulo okwanira 20 kwa okondwerera.
20. Kodi ndi m’njira yotani imene Yehova watonthozera abale athu m’Rwanda, koma kodi ndi chosoŵa chotani chimene ambiri a iwo akupitiriza kukhala nacho?
20 Pamene kuphana m’Rwanda kunayambika, munali alaliki a uthenga wabwino 2,500 m’dzikomo. Ngakhale kuti mazana ambiri anafa kapena kukakamizidwa kuthaŵa m’dzikolo, chiŵerengero cha Mboni chawonjezeka kuposa pa 3,000. Umenewu ndi umboni wakuti Mulungu anaperekadi chitonthozo kwa abale athu. Bwanji nanga za ana amasiye ambiri ndi akazi amasiye pakati pa Mboni za Yehova? Mwachibadwa, ameneŵa akuvutikabe ndi nsautso ndipo amafunikira chitonthozo chopitiriza. (Yakobo 1:27) Misozi yawo idzapukutidwa kotheratu pa chiukiriro m’dziko latsopano la Mulungu. Komabe, ali okhoza kulimbana ndi moyo chifukwa cha chithandizo cha abale awo ndi chifukwa chakuti ali alambiri a “Mulungu wa chitonthozo chonse.”
21. (a) Kodi nkuti kwina kumene abale athu akufunikira kwambiri chitonthozo cha Mulungu, ndipo kodi ndi m’njira yotani imene tonsefe tingathandizire? (Onani bokosi lakuti “Chitonthozo Mkati mwa Zaka Zinayi za Nkhondo.”) (b) Kodi chosoŵa chathu cha chitonthozo chidzakwaniritsidwa liti modzala?
21 M’malo ena ambiri, monga Eritrea, Singapore, ndi dziko limene kale linali Yugoslavia, abale athu akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika mosasamala kanthu za masautso. Tiyeni tiwathandize abale oterowo mwa mapembedzero a nthaŵi zonse kuti apeze chitonthozo. (2 Akorinto 1:11) Ndipo tipiriretu mokhulupirika kufikira nthaŵi pamene Mulungu, kupyolera mwa Yesu Kristu ‘adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso [pathu]’ m’lingaliro lenileni. Pamenepo tidzapeza chitonthozo cha Yehova pamlingo wodzala chimene Yehova adzapereka m’dziko lake latsopano la chilungamo.—Chivumbulutso 7:17; 21:4; 2 Petro 3:13.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda ya January 1, 1995, tsamba 26, inasimba chokumana nacho cha mwana wamkazi wa Rwakabubu, Deborah, amene pemphero lake linalasa mtima gulu la asilikali achihutu ndipo linapulumutsa banjalo kuti lisaphedwe.
Kodi Mukudziŵa?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova amatchedwa ‘Mulungu wa chitonthozo chonse’?
◻ Kodi tiyenera kuwaona motani masautso?
◻ Kodi tingagaŵane chitonthozo ndi yani?
◻ Kodi ndi motani mmene chosoŵa chathu cha chitonthozo chidzakwaniritsidwira modzala?
[Chithunzi patsamba 17]
Jean ndi Chantal, ngakhale kuti anali Mboni zachitutsi, anabisidwa m’malo osiyana ndi Mboni zachihutu m’nthaŵi ya kuphana kwa m’Rwanda
[Chithunzi patsamba 17]
Mboni za Yehova zikupitiriza kugaŵira uthenga wa chitonthozo wa Yehova kwa anansi awo m’Rwanda