Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova Amawerenga ‘Tsitsi Lonse la M’mutu Mwanu’
    Nsanja ya Olonda—2005 | August 1
    • 4. Kodi Paulo anayenera kupirira vuto lotani losatherapo, ndipo kodi vuto langati limeneli lingatikhudze motani ifeyo?

      4 Taganizirani zimene zinamuchitikira mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “Kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze.” Paulo anapitiriza kuti: “Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.” Yehova anamva pemphero la Paulo. Komabe, anauza Paulo kuti sathetsa vuto lakelo m’njira yozizwitsa. M’malo mwake, Paulo anayenera kudalira mphamvu za Mulungu kuti ndizo zimuthandize kuti alimbane ndi “munga m’thupi” mwake.b (2 Akorinto 12:7-9) Monga Paulo, n’kutheka kuti nanunso muli ndi vuto linalake limene silikukutherani. Ndiye mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi popeza zikuoneka kuti Yehova sanachitepo kanthu pa vuto langali ndiye kuti sakudziwa za vutoli kapena mwina sandiganizira?’ Ayi, sichoncho ngakhale pang’ono. Zimene Yesu anauza ophunzira ake atangowasankha kumene, zimagogomezera mfundo yakuti Yehova amaganizira kwambiri mtumiki wake aliyense wokhulupirika. Tiyeni tione mmene mawu ake angatilimbikitsire masiku ano.

  • Yehova Amawerenga ‘Tsitsi Lonse la M’mutu Mwanu’
    Nsanja ya Olonda—2005 | August 1
    • b Baibulo silinena kuti “munga m’thupi” umene Paulo anali nawowu unali chiyani makamaka. N’kutheka kuti mwina unali vuto linalake, monga vuto la maso. N’kuthekanso kuti mawu akuti “munga m’thupi” ankatanthauza atumwi onyenga ndi anthu enanso amene ankatsutsa kuti Paulo anali mtumwi weniweni, n’kumalimbana ndi utumiki wake.​—2 Akorinto 11:6, 13-15; Agalatiya 4:15; 6:11.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena