Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 1/15 tsamba 13-18
  • Pitirizani Kuyenda ndi Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kuyenda ndi Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyendabe Osabwerera Mmbuyo
  • Peŵani Msampha wa Kudzidalira Kopambanitsa
  • Musachite Zinthu Chifukwa Choopa Anthu
  • Peŵani Kupeputsa Uphungu
  • Kulaka Nkhaŵa za m’Moyo
  • Yendani mwa Chikhulupiriro Osati mwa Zooneka Ndi Maso
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mapindu a Kuwopa Mulungu Woona
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Pitirizani Kuyenda M’njira ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kuyenda ndi Mulungu—Masitepe Oyambirira
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 1/15 tsamba 13-18

Pitirizani Kuyenda ndi Mulungu

“Muyendeyende ndi mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.”​—AGALATIYA 5:16.

1. (a) Kodi Enoke anayenda ndi Mulungu pamikhalidwe yotani, nanga anayenda ndi iye kwa nthaŵi yaitali motani? (b) Kodi Nowa anayenda ndi Mulungu kwa nthaŵi yaitali motani, ndipo kodi ndi maudindo olemetsa ati amene iye anali nawo?

BAIBULO limatiuza kuti Enoke “anayendabe ndi Mulungu.” Mosasamala kanthu za mawu okwiyitsa ndi makhalidwe oipa a anthu a m’dziko lake, iye anapitirizabe kuyenda ndi Mulungu mpaka mapeto a moyo wake pamsinkhu wazaka 365. (Genesis 5:23, 24; Yuda 14, 15) Nayenso Nowa “anayendabe ndi Mulungu.” Iye anatero pamene anali kusamalira banja lake, pamene anali kupirira kukhala m’dziko losonkhezeredwa ndi angelo opanduka pamodzi ndi ana awo achiwawa, ndiponso pamene anali kusamalira malongosoledwe atsatanetsatane a kamangidwe ka chingalawa chachikulu chimene chinali chachikulu kuposa chombo chilichonse cha m’nthaŵi zakale. Chigumula chitapita, iye anapitirizabe kuyenda ndi Mulungu, ngakhale pamene anaona ena akupandukira Yehova pa Babele. Ndithudi, Nowa anapitiriza kuyenda ndi Mulungu mpaka imfa yake pamsinkhu wazaka 950.​—Genesis 6:9; 9:29.

2. Kodi ‘kuyenda ndi Mulungu’ kumatanthauzanji?

2 Likamanena kuti amuna ameneŵa ‘anayenda’ ndi Mulungu, Baibulo likugwiritsira ntchito mawuwo mophiphiritsira. Limatanthauza kuti Enoke ndi Nowa anali ndi makhalidwe amene anasonyeza kuti iwo anali ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. Iwo anachita monga momwe Yehova anawalamulira ndipo miyoyo yawo inali yogwirizana ndi zimene anadziŵa ponena za iye malinga ndi mmene amachitira ndi mtundu wa anthu. (Yerekezerani ndi 2 Mbiri 7:17.) Iwo sanangotsimikiza chabe m’malingaliro mwawo zimene Mulungu ananena ndi kuchita koma anachita mogwirizana ndi chilichonse chimene iye anafuna​—osati zoŵerengeka chabe koma zonse monga momwe akanathera monga anthu opanda ungwiro. Choncho, Nowa, mwachitsanzo, anachita zonse zimene Mulungu anamlamulira. (Genesis 6:22) Nowa sanali kuchita zinthu mosemphana ndi malangizo amene anapatsidwa, ndiponso sanali kuzengereza kuchita zimenezo. Chifukwa chakuti anali paunansi wathithithi ndi Yehova, nakhala womasuka kupemphera kwa Mulungu ndiponso chifukwa chakuti anali kutsogozedwa ndi Mulungu, iye anali kuyenda ndi Mulungu. Kodi inuyo mukutero?

Kuyendabe Osabwerera Mmbuyo

3. Kodi nchiyani chimene chili chofunika kwambiri kwa atumiki a Mulungu odzipatulira ndi obatizidwa?

3 Ndi chinthu chosangalatsa kwambiri kuona mmene anthu amayambira kuyenda ndi Mulungu. Pamene asintha miyoyo yawo kuti igwirizane ndi chifuniro cha Yehova, iwo amapereka umboni wakuti ali ndi chikhulupiriro, popeza kuti popanda chimenechi munthu sangathe kukondweretsa Mulungu. (Ahebri 11:6) Timakhala osangalala chotani nanga poona kuti chaka chilichonse, pa avareji ya zaka zisanu zapitazo, anthu oposa 330,000 anadzipatulira kwa Yehova ndipo anadzipereka ku ubatizo wa m’madzi! Komatu nkofunikanso kwa iwo ndiponso kwa tonsefe kuti tipitirizebe kuyenda ndi Mulungu.​—Mateyu 24:13; Chivumbulutso 2:10.

4. Ngakhale kuti nthaŵi zina anali kusonyeza chikhulupiriro, kodi nchifukwa ninji Aisrayeli ambiri amene anatuluka ku Igupto sanaloŵe nawo m’Dziko Lolonjezedwa?

4 M’tsiku la Mose, mabanja achiisrayeli anasonyeza chikhulupiriro pamene anachita Paskha ku Igupto, napaka mwazi pamphuthu za m’mbali ndi pamwamba pachitseko m’nyumba zawo. (Eksodo 12:1-28) Komabe, chikhulupiriro cha ambiri a iwo chinagwedera pamene anaona gulu lankhondo la Farao lili pafupi kuwapeza pamene anali pa Nyanja Yofiira. (Eksodo 14:9-12) Salmo 106:12 likusonyeza kuti pamene iwo anawoloka bwinobwino pakati pa nyanja pouma napenya madzi oŵinduka akumiza ankhondo a ku Igupto, iwo anayambanso ‘kuvomereza mawu [a Yehova].’ Komabe, patangopita nthaŵi yochepa pamene anafika m’chipululu, Aisrayeliwo anayamba kudandaula za madzi akumwa, chakudya, ndi uyang’aniro. Malipoti oopsa a azondi 10 mwa azondi 12 amene anabwerako kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa anawachititsa mantha. Nthaŵi imeneyo, monga momwe Salmo 106:24 likunenera, iwo ‘sanavomereze mawu [a Mulungu].’ Anafuna kubwerera ku Igupto. (Numeri 14:1-4) Chikhulupiriro chimene anali nacho chinali kusonyezedwa pokhapokha ataona zozizwitsa zochitidwa mwa mphamvu ya Mulungu. Iwo sanapitirizebe kuyenda ndi Mulungu. Chotsatirapo chake, Aisrayeli amenewo sanaloŵe nawo m’Dziko Lolonjezedwa.​—Salmo 95:10, 11.

5. Kodi 2 Akorinto 13:5 ndi Miyambo 3:5, 6 ikufotokozanji ponena za kuyenda ndi Mulungu?

5 Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.” (2 Akorinto 13:5) Kukhala “m’chikhulupiriro” kumatanthauza kumamatira ku zikhulupiriro zachikristu. Zimenezi nzofunika kwambiri chifukwa chakuti zimatithandiza kuyenda ndi Mulungu tsiku lililonse la moyo wathu. Kuti tiyende ndi Mulungu, tiyenera kusonyeza chikhulupiriro chathu mwa kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse. (Miyambo 3:5, 6) Pali misampha ndi mbuna zambiri zimene zingagwire amene amalephera kuchita zimenezo. Kodi ina mwa misamphayi ndi mbunazi nchiyani?

Peŵani Msampha wa Kudzidalira Kopambanitsa

6. Kodi Akristu onse amadziŵanji ponena za dama ndi chigololo, ndipo kodi machimo ameneŵa amawaona motani?

6 Aliyense amene anaphunzira Baibulo, kupereka moyo wake kwa Yehova, nabatizidwa amadziŵa kuti Mawu a Mulungu amaletsa dama ndi chigololo. (1 Atesalonika 4:1-3; Ahebri 13:4) Anthu otero amavomereza kuti kuletsaku nkwabwinodi. Iwo amafuna kuti azitsatira mawu amenewo. Ngakhale zili choncho, chisembwere chikupitirizabe kukhala umodzi mwa misampha yamphamvu kwambiri ya Satana. Chifukwa chiyani?

7. Ku Zidikha za Moabu, kodi amuna achiisrayeli anadziloŵetsa motani m’makhalidwe amene anadziŵa kuti anali oipa?

7 Poyambirira, amene amachita makhalidwe oipa ameneŵa angakhale asakufuna kutero. Mwinamwake zimenezi nzimene zinachitikiranso Aisrayeli ku Zidikha za Moabu. Chifukwa cha kutopa ndi moyo wa m’chipululu, amuna achiisrayeli anakopeka ndi akazi achimoabu ndi achimidyani amene mwinamwake poyambirira anaoneka ngati akazi achikondi ndi ochereza alendo. Koma kodi chinachitika nchiyani pamene Aisrayeli analola kuyanjana ndi anthu amene anali kulambira Baala osati Yehova, anthu amene anali kulola ana awo aakazi (ngakhale ochokera m’mabanja olemekezeka) kuti azigonana ndi amuna amene sanakwatirane nawo? Pamene amuna ochokera mumsasa wa Israyeli anayamba kuona kuti mayanjano amenewo anali osangalatsa, iwo ananyengedwa nachita zinthu zimene anadziŵa kuti zinali zoipa, ndipo zimenezi zinawatayitsa miyoyo yawo.​—Numeri 22:1; 25:1-15; 31:16; Chivumbulutso 2:14.

8. M’tsiku lathu, kodi nchiyani chimene chingasonkhezere Mkristu kuchita chisembwere?

8 Kodi nchiyani chimene chingagwetsenso munthu mumsampha wofananawo m’tsiku lathu? Ngakhale kuti iye angadziŵe kuopsa kwa chisembwere, ngati iyeyo salingaliranso za kuopsa kwa kudzidalira kopambanitsa, iye angadziloŵetse mumkhalidwe umene ungamsonkhezere kuchita zoipa mosazindikira.​—Miyambo 7:6-9, 21, 22; 14:16.

9. Kodi ndi machenjezo a m’Malemba ati amene angatithandize kupeŵa chisembwere?

9 Kunena mosapita m’mbali, Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti tisanyengedwe mwa kulingalira kuti ndife anthu olimba amene sitingaipsidwe ndi mayanjano oipa. Zimenezi zimaphatikizapo kuonerera maprogramu a pawailesi yakanema amene amaonetsa makhalidwe a anthu achisembwere ndiponso kuŵerenga magazini amene amasonkhezera zilakolako zachisembwere. (1 Akorinto 10:11, 12; 15:33) Ngakhale kuyanjana ndi okhulupirira anzathu pamalo oipa kungachititse mavuto aakulu. Pali kukopeka kwamphamvu pakati pa mwamuna ndi mkazi. Mwachikondi, gulu la Yehova lakhala likutichenjeza kuti mwamuna ndi mkazi sayenera kukhala kwaokha kobisika ngati si okwatirana kapena ngati si pachibale. Kuti tipitirize kuyenda ndi Mulungu, tiyenera kupeŵa msampha wa kudzidalira kopambanitsa ndipo tiyeneranso kutsatira machenjezo amene iye amatipatsa.​—Salmo 85:8.

Musachite Zinthu Chifukwa Choopa Anthu

10. Kodi “kuopa anthu” kumatchera msampha motani?

10 Msampha wina wafotokozedwa pa Miyambo 29:25 kuti: “Kuopa anthu kutchera msampha.” Nthaŵi zambiri msampha wa mlenje umakhala ndi gango limene limakola pakhosi kapena zingwe zimene zimakola miyendo ya nyama. (Yobu 18:8-11) Kuopa anthu kungalepheretsenso munthu kulankhula momasuka ndi kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Chikhumbo cha kusangalatsa anthu ena nchachibadwa, ndipo kusasamala za zimene anthu ena akulingalira nkosemphana ndi Chikristu. Koma kusapambanitsa nkofunika. Ngati munthu achita zinthu zimene Mulungu amaletsa kapenanso kulephera kuchita zimene Mawu a Mulungu amalamulira chifukwa choopa zimene anthu ena angachite, ndiye kuti munthu ameneyo wakodwa mumsampha.

11. (a) Kodi nchiyani chimene chingathandize munthu kupeŵa kuchita zinthu chifukwa choopa anthu? (b) Kodi Yehova anathandiza motani atumiki ake amene anali kulimbana ndi vuto la kuopa anthu?

11 Chimene chingatitetezere ku msampha umenewo si malingaliro athu achibadwa ayi, koma ‘kukhulupirira Yehova.’ (Miyambo 29:25b) Mwa kukhulupirira Mulungu, ngakhale munthu wamanyazi mwachibadwa angalimbe mtima ndipo sangagonje. Malinga ngati tikhalabe pakati pa zisonkhezero za m’dongosolo lino la Satana, tidzafunikira kupeŵa kuopa anthu kumene kungatigwetsere mumsampha. Ngakhale kuti mneneri Eliya anali wolimba mtima mu utumiki wake, pamene Yezebeli anamuopseza kuti adzamupha, iye anachita mantha nathaŵa. (1 Mafumu 19:2-18) Atamuopseza, mtumwi Petro anakana mwamantha kuti sanali kumdziŵa Yesu Kristu, ndipo patapita zaka iye anachita zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chake chifukwa cha mantha. (Marko 14:66-71; Agalatiya 2:11, 12) Komabe, onse aŵiriwo Eliya ndi Petro analandira chithandizo chauzimu ndipo, mwa kudalira Yehova, iwo anapitiriza kutumikira Mulungu movomerezeka.

12. Kodi ndi zitsanzo zamakono ziti zimene zikusonyeza mmene anthu anathandizidwira kuti asalole mantha kuwalepheretsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu?

12 Nawonso atumiki ambiri a Yehova lerolino aphunzira mmene angalakire msampha wa mantha. Mboni ina yazaka zosakwana 20 ku Guyana inavomereza kuti: “Kuti ulake chitsenderezo cha ausinkhu wako kusukulu, pamafunikira kumenyera nkhondo zolimba.” Koma iye anawonjezera kuti: “Nchimodzimodzinso ndi chikhulupiriro changa mwa Yehova.” Pamene mphunzitsi wake anamnyoza pakati pa anzake a m’kalasi chifukwa cha chikhulupiriro chake, iye anapemphera kwa Yehova chamumtima. Kenaka iye anachitira umboni mochenjera kwa mphunzitsi wakeyo pamene enawo panalibe. Atakacheza kutauni yakwawo ku Benin, mnyamata wina amene anali kuphunzira za zifuno za Yehova anaganiza zotaya fano limene atate ake anamkonzera. Mnyamatayu anadziŵa kuti fanolo linali lopanda moyo, ndipo sanaliope, koma iye anadziŵanso kuti mwina anthu a m’mudzimo angakwiye ndi kumupha. Iye anapemphera kwa Yehova, ndipo anatenga fanolo usiku napita nalo kuthengo kukalitaya. (Yerekezerani ndi Oweruza 6:27-31.) Pamene mkazi wina ku Dominican Republic anayamba kutumikira Yehova, mwamuna wake anamfunsa kuti asankhepo pakati pa iye ndi Yehova. Mwamunayo anamuopseza kuti adzamsudzula. Kodi iye akanasiya chikhulupiriro chake chifukwa cha mantha? Iye anayankha kuti: “Zikanakhala kuti zinali zokhudza kusakhulupirika m’banja, ndikanachita manyazi, koma kutumikira Yehova Mulungu sikundichititsa manyazi!” Iye anapitirizabe kuyenda ndi Mulungu, ndipo m’kupita kwa nthaŵi mwamuna wakeyo anagwirizana naye pakuchita chifuniro cha Yehova. Mwa kukhulupirira kotheratu Atate wathu wa kumwamba, ifenso sitingalole mantha kutiletsa kuchita zinthu zimene tikudziŵa kuti zidzasangalatsa Yehova.

Peŵani Kupeputsa Uphungu

13. Kodi 1 Timoteo 6:9 akutichenjeza za msampha wanji?

13 Ngakhale kuti misampha ina ya alenje imakonzedwa kuti igwire nyama iliyonse yodutsa pamalopo, misampha ina imakhala ndi nyambo yonyengerera nyamazo. Chuma chili ngati nyambo imeneyo kwa anthu ambiri. (Mateyu 13:22) Pa 1 Timoteo 6:8, 9, Baibulo likutilimbikitsa kuti tizikhala okhutira ndi zakudya ndi zofunda. Kenaka likuchenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.”

14. (a) Kodi nchiyani chimene chingalepheretse munthu kugwiritsira ntchito uphungu wakuti tiyenera kukhutira ndi zakudya ndi zofunda? (b) Kodi malingaliro opotoka ponena za chuma angasonkhezere bwanji munthu kunyalanyaza uphungu wolembedwa pa 1 Timoteo 6:9? (c) Kodi “chilakolako cha maso” chingapangitse bwanji ena kuti asaone msampha umene ukuwayembekezera?

14 Ngakhale kuti pali chenjezo limeneli, ambiri amagwa mumsamphawu chifukwa chakuti sagwiritsira ntchito uphunguwo. Chifukwa chiyani? Kodi tinganene kuti kunyada ndiko kumawapangitsa kulimbikirabe kutsata njira ya moyo imene imafuna zambiri kuposa “zakudya ndi zofunda” zimene Baibulo limanena kuti tiyenera kukhutira nazo? Kodi mwina amapeputsa chenjezo la m’Baibuloli chifukwa chakuti amaganiza kuti chuma ndicho kukhala ndi zambiri monga momwe anthu achuma amachitira? Baibulo limasonyeza kuti kungofuna kukhala wachuma nkosemphana ndi uphungu wa kukhala wokhutira ndi zakudya ndi zofunda. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:5.) Kodi “chilakolako cha maso”​—kufuna kukhala ndi zinthu zimene amaona, ngakhale kusiya zinthu zauzimu chifukwa cha zimenezo​—ndicho chimawapangitsa kuika pambuyo kulambira koona? (1 Yohane 2:15-17; Hagai 1:2-8) Ndi chimwemwe chachikulu chotani nanga chimene chimakhala ndi anthu amene amatsatira uphungu wa m’Baibulowo napitiriza kuyenda ndi Mulungu mwa kupanga kutumikira Yehova kukhala chinthu chofunika kwambiri pamoyo wawo!

Kulaka Nkhaŵa za m’Moyo

15. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene imapangitsadi anthu a Yehova kukhala ndi nkhaŵa, ndipo kodi tiyenera kupeŵa msampha wanji pamene tikumana ndi mavuto ameneŵa?

15 Nkhaŵa ya kufunitsitsa kupeza zinthu zofunika pamoyo njaikulu kwambiri kuposa kufuna kukhala wachuma. Ambiri mwa atumiki a Yehova ali ndi zinthu zochepa. Amagwira ntchito zolimba kwa maola ambiri pofuna kukhala chabe ndi zovala, malo ogona a banja lawo, ndi chakudya cha patsikulo. Ena akulimbana ndi mavuto ena monga matenda kapena ukalamba wawo kapena wa apabanja awo. Kungakhale kosavuta chotani nanga kusiya zinthu zauzimu pamoyo wawo chifukwa cha mavuto amenewo!​—Mateyu 13:22.

16. Kodi Yehova amatithandiza motani polaka zitsenderezo za m’moyo?

16 Mwachikondi, Yehova akutiuza za mpumulo umene udzakhalapo mu ulamuliro wa Ufumu Waumesiya. (Salmo 72:1-4, 16; Yesaya 25:7, 8) Iye amatithandizanso kulaka zitsenderezo za m’moyo lerolino mwa kutipatsa uphungu wa mmene tingaikire zinthu zofunika pamalo oyamba. (Mateyu 4:4; 6:25-34) Kupyolera m’nkhani zonena za mmene anathandizira atumiki ake m’nthaŵi zakale, Yehova akutitsimikizira kuti adzateronso kwa ife. (Yeremiya 37:21; Yakobo 5:11) Iye amatilimbikitsa kuzindikira kuti, ngakhale tikumane ndi zothetsa nzeru zotani, chikondi chake kwa atumiki ake okhulupirika sichidzatha. (Aroma 8:35-39) Yehova akuuza amene amamkhulupirira kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

17. Perekani zitsanzo za mmene anthu ena anapitirizirabe kuyenda ndi Mulungu ngakhale kuti anakomana ndi zothetsa nzeru zina.

17 Mwa kulimbikitsidwa ndi chidziŵitso chimenechi, Akristu oona amapitirizabe kuyenda ndi Mulungu m’malo moyamba kuchita zinthu zakudziko. Lingaliro lakudziko lofala kwambiri pakati pa anthu osauka nlakuti kutenga zinthu kwa munthu wolemera ncholinga choti udyetse banja lako sikuba. Koma amene amayenda ndi chikhulupiriro amakana lingaliro limenelo. Iwo amaona kuti chiyanjo cha Mulungu nchofunika kwambiri kuposa chinthu chilichonse ndipo amayang’ana kwa iye kuti awapatse mphotho kaamba ka kuona mtima kwawo. (Miyambo 30:8, 9; 1 Akorinto 10:13; Ahebri 13:18) Mkazi wina wamasiye ku India anaona kuti kugwira ntchito mwakhama ndiponso kukhala wanzeru kunamthandiza kulaka vutolo. M’malo mokwiya ndi mavuto akewo, iye anazindikira kuti, ngati atenga Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake kukhala zinthu zoyamba pamoyo, Yehova angathe kudalitsa khama lake pofunafuna kupeza zosoŵa zake ndi za mwana wake wamwamuna. (Mateyu 6:33, 34) Anthu zikwi zambiri padziko lonse amachita zimenezo, mosasamala kanthu za zothetsa nzeru zimene angakumane nazo, Yehova ndiye pothaŵirapo pawo ndi linga lawo. (Salmo 91:2) Kodi ndi mmenenso zilili kwa inu?

18. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kupeŵa misampha ya m’dziko la Satana?

18 Malinga ngati tipitirizabe kukhala m’dongosolo la zinthu lilipoli, padzakhalabe misampha imene tidzafunikira kupeŵa. (1 Yohane 5:19) Baibulo limatiuza za iyo ndipo limatiuzanso mmene tingaipeŵere. Amene amakondadi Yehova nakananso kumkwiyitsa angalake misampha imeneyo. Ngati ‘ayendayenda ndi Mzimu,’ iwo sadzakopeka ndi zinthu zakudziko. (Agalatiya 5:16-25) Onse amene alidi paunansi weniweni ndi Yehova ali ndi chiyembekezo chachikulu cha kuyenda ndi Mulungu, kukhala paunansi wathithithi ndi iye mpaka muyaya.​—Salmo 25:14.

Kodi Mukutipo Bwanji?

◻ Kodi kudzidalira kopambanitsa kungakhale msampha motani?

◻ Kodi nchiyani chimene chingatithandize kupeŵa kuchita zinthu chifukwa choopa anthu?

◻ Kodi nchiyani chimene chingatilepheretse kugwiritsira ntchito uphungu wochenjeza za ngozi ya kufunafuna chuma?

◻ Kodi nchiyani chimene chingatithandize kupeŵa kugwera mumsampha wa nkhaŵa za m’moyo?

[Chithunzi pamsamba 16, 17]

Anthu ambiri amapitirizabe kuyenda ndi Mulungu moyo wawo wonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena