Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”
    Nsanja ya Olonda—2008 | September 1
    • ANTHUFE timakumana ndi mavuto ambiri m’moyo monga kuzunzika, kukhumudwa ndiponso kusungulumwa. Tikakumana ndi zimenezi timada nkhawa komanso kutaya mtima. Ndiye zikatero timadzifunsa kuti, ‘Kodi ndigwire mtengo wanji?’ Mawu a Mtumwi Paulo opezeka pa 2 Akorinto 1:3, 4 amatiuza kuti Yehova Mulungu yekha ndi amene angathe kutitonthoza.

      Pa vesi 3 Mulungu akutchedwa kuti “Tate wa chifundo chachikulu.” Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “chifundo chachikulu” angatanthauze kukhudzidwa mtima anthu ena akamavutika.a Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limati mawuwa tingawalembenso kuti “amamva chisoni” kapena kuti “amakonda kwambiri anthu.” Chifukwa chakuti Mulungu ndi wa chifundo chachikulu, amathandiza anthu pamavuto. Kudziwa khalidwe la Mulungu limeneli kumachititsa kuti timukonde kwambiri.

      Paulo ananenanso kuti Yehova ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse.” Buku lina linati mawu a Paulo palembali amatanthauzanso “kulimbikitsa, kutonthoza, kapena kupereka thandizo kwa munthu amene ali pa mavuto kapena pa chisoni.” Bukulo linapitiriza kuti “Munthu akamavutika timamutonthoza pomulimbitsa mtima kuti apirire mavuto akewo.”​—The Interpreter’s Bible.

      Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Mulungu amatitonthoza ndi kutilimbikitsa motani?’ Amatero makamaka pogwiritsa ntchito Mawu ake Baibulo komanso pemphero, lomwe ndi mphatso yomwe iye anatipatsa. Paulo ananena kuti Mulungu anatipatsa Mawu ake mwachikondi pofuna kuti “mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” Kuwonjezera pamenepo tikamapemphera mochokera pansi pamtima tingathe kupeza “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.”​—Aroma 15:4; Afilipi 4:7.

  • “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”
    Nsanja ya Olonda—2008 | September 1
    • a Mulungu amatchedwa “Tate [kapena kuti magwero] a chifundo chachikulu,” chifukwa choti iye ndi amene anayambitsa khalidwe la chifundo ndipo ndi mbali ya umunthu wake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena