-
Onetsani Kuti Mukupita PatsogoloNsanja ya Olonda—2001 | August 1
-
-
Onetsani “Chipatso cha Mzimu”
12. N’chifukwa chiyani kuonetsa chipatso cha mzimu kuli kofunika pamene tikuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu?
12 Pamene kusunga ‘umodzi wa chikhulupiriro ndi wa chidziŵitso cholondola’ kuli kofunika, tifunikanso kuonetsa chipatso cha mzimu wa Mulungu m’mbali iliyonse ya moyo wathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti malinga ndi mmene taonera, uchikulire si wobisika koma umaonekera bwino mwa makhalidwe amene angathandize ndi kulimbikitsa ena. Ndithudi, pamene tikuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu si cholinga chathu kuti tioneke otsogola kapena apamwamba ayi. Koma pamene tikukula mwauzimu ndi kutsata utsogoleri wa mzimu wa Mulungu, maganizo athu ndi zochita zathu zimasintha kwambiri. Mtumwi Paulo anati: “Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.”—Agalatiya 5:16.
13. Kodi ndi kusintha kotani kumene kuli umboni wosatsutsika wakuti munthu akupita patsogolo?
13 Ndiyeno Paulo anatchula “ntchito za thupi,” zimene zili zambiri komanso “zionekera.” Munthu asanadziŵe zimene Mulungu amafuna, amatsata njira za dziko pa moyo wake ndipo moyo wakewo ungakhale ndi zina mwa zinthu zimene Paulo anatchula: “Dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.” (Agalatiya 5:19-21) Koma pamene apita patsogolo mwauzimu, amayamba kugonjetsa “ntchito za thupi” zoipazi ndi kulola “chipatso cha Mzimu” kutenga malo. Kusintha kumeneku kooneka kwa onse ndi umboni wosatsutsika wakuti munthuyo akupita patsogolo kukhala Mkristu wachikulire.—Agalatiya 5:22.
14. Fotokozani ziganizo ziŵirizo, “ntchito za thupi” ndi “chipatso cha Mzimu.”
14 Tione ziganizo ziŵirizo, “ntchito za thupi” ndi “chipatso cha Mzimu.” “Ntchito” ndi zochita za munthu. Mwa mawu ena, zimene Paulo analemba kukhala ntchito za thupi ndi zinthu zimene munthu amachita dala kapena posonkhezeredwa ndi thupi lochimwa. (Aroma 1:24, 28; 7:21-25) Koma mawu akuti “chipatso cha Mzimu” akutanthauza kuti munthu amakhala ndi makhalidwe otchulidwawo chifukwa cha mphamvu ya mzimu wa Mulungu osati chifukwa choyesetsa kusintha khalidwe lake kapena kuwongola umunthu wake. Monga momwe mtengo umabalira zipatso pousamalira bwinobwino, munthunso amaonetsa chipatso cha mzimu pamene mzimu woyera ugwira ntchito mwaufulu pamoyo wake.—Salmo 1:1-3.
15. N’chifukwa chiyani tifunika kusamalira mbali zonse za “chipatso cha Mzimu”?
15 Mfundo ina yofunika kuiona ndi mmene Paulo anagwiritsira ntchito liwulo, “chipatso” pofotokoza makhalidwe onse abwino amene anatchula. Mzimuwo subala zipatso zosiyanasiyana kuti ife tisankhepo chimene tikufuna ayi. Makhalidwe onsewo omwe Paulo anatchula—chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso ndi chiletso—ndi ofunika ndipo onse pamodzi amatheketsa umunthu watsopano wachikristu. (Aefeso 4:24; Akolose 3:10) Chotero, pamene zingatheke kuti ena mwa makhalidwe ameneŵa angaonekere kwambiri pamoyo wathu chifukwa cha umunthu wathu ndi mtima wathu, tifunika kuonetsetsa kuti tikusamalira mbali zonse zimene Paulo anatchula. Tikatero, tidzaonetsa kwambiri umunthu ngati wa Kristu pamoyo wathu.—1 Petro 2:12, 21.
16. Kodi cholinga chathu n’chiyani tikamayesetsa kukhala Akristu achikulire, ndipo zimenezo zingatheke bwanji?
16 Phunziro lalikulu limene tikutengapo pa zimene Paulo anafotokoza ndi lakuti pamene tikuyesetsa kukhala Akristu achikulire, si cholinga chathu kukhala ndi chidziŵitso choposa kapena kukhala ophunzira kwambiri. Ndiponso sikuti tikhale ndi umunthu wonyaditsa ayi. Koma kuti mzimu wa Mulungu uzigwira ntchito mwaufulu pamoyo wathu. Timakhala achikulire mwauzimu malinga ndi mmene timalabadirira utsogoleri wa mzimu wa Mulungu m’maganizo athu ndi pa zochita zathu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Tiyenera kutsegula mtima ndi maganizo athu kuti mzimu wa Mulungu uzitilamulira. Zimenezi zimaphatikizapo kufika pamisonkhano yachikristu mokhazikika ndi kutenga nawo mbali. Tifunikanso nthaŵi zonse kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha, kulola mfundo zake zachikhalidwe kutitsogolera pochita zinthu ndi anthu ena ndiponso pa zosankha zathu. Pamenepo, kupita kwathu patsogolo kudzaonekera kwambiri.
-
-
Onetsani Kuti Mukupita PatsogoloNsanja ya Olonda—2001 | August 1
-
-
• Kodi uchikulire wauzimu umaonekera motani?
-