-
4 | Mulungu Angakuthandizeni Kuthetsa Mtima WachidaniNsanja ya Olonda (Yogawira)—2022 | Na. 1
-
-
Baibulo Limati:
“Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”—AGALATIYA 5:22, 23.
Zimene Lembali Limatanthauza:
Mulungu angatithandize kuthetsa chidani. Mzimu wake woyera ungatithandize kukhala ndi makhalidwe amene patokha sitingakwanitse kukhala nawo. Choncho, m’malo moyesetsa kulimbana ndi kuthetsa mtima wachidani patokha, tingachite bwino kudalira Mulungu kuti atithandize. Tikachita zimenezi tidzafanana ndi Paulo yemwe analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Komanso tidzanena kuti: “Thandizo langa lichokera kwa Yehova.”—Salimo 121:2.
-