Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/1 tsamba 8-13
  • Khalani Osandulika M’maganizo ndi Ounikiridwa Mumtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Osandulika M’maganizo ndi Ounikiridwa Mumtima
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Mmene Amitundu Ayendera’
  • Maganizo Osapindulitsa ndi Amdima
  • Mitima Yopulukira ndi Youma
  • ‘Osazindikiranso Kanthu Konse’
  • “Pitirizanibe Kuyenda Monga Ana a Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Musakhale Mumdima, Koma Khalanibe M’kuwala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Pitirizani Kuyenda M’njira ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kuunika kwa Mulungu Kumachotsa Mdima!
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/1 tsamba 8-13

Khalani Osandulika M’maganizo ndi Ounikiridwa Mumtima

“Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda.”​—AEFESO 4:17.

1. Kodi nchiyani chimene maganizo athu ndi mitima zimatichitira?

MAGANIZO ndi mtima ndizo mphamvu ziŵiri mwa mphamvu zodabwitsa koposa zimene anthu ali nazo. Ngakhale kuti izo ziri ndintchito zosaŵerengeka, ziri zosiyana kwa munthu aliyense. Umunthu wathu, kalankhulidwe, mayendedwe, malingaliro, ndi makhalidwe zonse zimayambukiridwa kwambiri ndi njira imene maganizo athu ndi mitima zimagwirira ntchito.

2, 3. (a) Kodi Baibulo limagwiritsira ntchito motani mawu akuti “mtima” ndi “maganizo”? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kudziŵa ponena za ziŵirizo, mtima ndi maganizo?

2 M’Baibulo, “mtima” kwakukulukulu umasonya ku chisonkhezero cha mtima, malingaliro, ndi kumva kwamkati, ndipo “maganizo” amasonya ku luntha ndi maluso akulingalira. Komabe, ziŵirizo sizimalekanitsika. Mwachitsanzo, Mose anafulumiza Aisrayeli kuti: ‘Mukumbukire mumtima mwanu [mawu amtsinde, NW, “mukumbukire m’maganizo mwanu”] kuti Yehova ndiye Mulungu wowona.’ (Deuteronomo 4:39) Kwa alembi amene anali kumlinganizira chiwembu, Yesu anati: ‘Chifukwa ninji mulinkuganizira zoipa m’mitima yanu?’​—Mateyu 9:4; Marko 2:6, 7.

3 Izi zimasonyeza kuti maganizo ndi mtima nzogwirizana kwambiri. Zimagwira ntchito moloŵerana, nthaŵi zina zikumachirikizana ndi kugwirira ntchito pamodzi, komabe kaŵirikaŵiri zimakangana kufuna kulamulirana. (Mateyu 27:37; yerekezerani ndi Aroma 7:23.) Kaamba ka chimenechi, kuti tipeze chiyanjo cha Yehova, sitingoyenera kukhala otsimikizira za mkhalidwe wa maganizo athu ndi mitima, koma tiyeneranso kuziphunzitsa kugwirira ntchito pamodzi mogwirizana, kuti ziyende m’njira imodzi. Tiyenera kukhala osandulika m’maganizo ndi ounikiridwa mumtima.​—Salmo 119:34; Miyambo 3:1.

‘Mmene Amitundu Ayendera’

4. Kodi ndimotani mmene Satana wasonkhezerera maganizo ndi mitima ya anthu, ndipo kodi chotulukapo nchiyani?

4 Satana ndiye wonyenga ndi wosonkhezera wamkulu. Amadziŵa kuti, kuti apeze ulamuliro pa anthu, ayenera kuukira maganizo awo ndi mitima. Kuyambira pachiyambi penipeni pa mbiri ya anthu, iye wakhala akugwiritsira ntchito zipangizo zosiyanasiyana kuyesa kukwaniritsa cholinga chake chimenecho. Monga chotulukapo, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kunena zowona, Satana wapeza chipambano kwambiri m’kusonkhezera mitima ndi maganizo a anthu akudziko kwakuti Baibulo limawafotokoza kukhala “mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka.” (Afilipi 2:15) Mtumwi Paulo akufotokoza momvekera bwino mkhalidwe wa mtima ndi maganizo wa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka umenewo, ndipo mawu ake akukhala chenjezo kwa tonsefe lerolino. Mwachitsanzo, chonde taŵerengani Aefeso 4:17-19, ndipo yerekezerani ndi mawu a Paulo pa Aroma 1:21-24.

5. Kodi nchifukwa ninji Paulo analemba uphungu wamphamvu kwa Aefeso?

5 Tikhoza kuzindikira chifukwa chake Paulo analembera Akristu mu Efeso mawu amphamvu oterowo pamene tikumbukira kuti mzindawo unali woluluzika koipitsitsa m’makhalidwe ake onyansa ndi kulambira mafano. Ngakhale kuti Agirikiwo anali ndi amuna otchuka anzeru ndi anthanthi, kukuwonekera kuti maphunziro Achigiriki anapatsa ambiri a anthuwo kuthekera kwakukulu kwakuchita zoipa, ndipo mwambo wawo unangowakhwimitsa m’zoipa zawo. Paulo anadera nkhaŵa kwambiri Akristu anzake okhala m’malo oterowo. Iye anadziŵa kuti ambiri a iwo kale anali anthu amitundu ndipo ‘adayenda monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino.’ Koma tsopano anali atalandira chowonadi. Maganizo awo anali atasandulika, ndipo mitima yawo inali itaunikiridwa. Chofunika koposa, Paulo anafuna kuti iwo ‘ayende koyenera maitanidwe.’​—Aefeso 2:2; 4:1.

6. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kufuna kudziŵa tanthauzo la mawu a Paulo?

6 Mkhalidwewo ngwofanana ndi lerolino. Nafenso tikukhala m’dziko la mikhalidwe yokhotakhota, zizoloŵezi zoluluzika, ndi machitachita onyenga achipembedzo. Ambiri pakati pathu anali ndi moyo wogwirizana ndi dongosolo la zinthu la dziko lino. Ena a ife timakakamizika kuyanjana ndi anthu adziko tsiku ndi tsiku. Ena amakhala m’mabanja m’mene mzimu wadziko uli waukulu. Chotero, nkofunika kwambiri kuti timvetsetse tanthauzo la mawu a Paulo ndi kupindula ndi uphungu wake.

Maganizo Osapindulitsa ndi Amdima

7. Kodi Paulo anatanthauzanji ndi mawu akuti ‘kusapindulitsa kwa maganizo awo’?

7 Kuti achirikize mwamphamvu uphungu wake wakuti Akristu ‘sayendanso monga amitundu angoyenda,’ Paulo choyamba anatchula “kusapindulitsa kwa maganizo awo.” (Aefeso 4:17, NW) Kodi zimenezo zitanthauzanji? Liwu lotembenuzidwa “kusapindulitsa,” malinga ndi The Anchor Bible, “limapereka lingaliro la kupanda pake, kugodomala, chinthu chachabechabe, kupusa, kupanda chifuno, ndi kugwiritsa mwala.” Chotero, Paulo anali kusonyeza kuti kutchuka ndi ulemerero wa dziko la Agiriki ndi Aroma zingakhale zinawoneka zokondweretsa koma kuzilondola kunalidi kopanda pake, kupusa, ndi kopanda chifuno. Awo amene anasumika mitima yawo pa kutchuka ndi ulemerero m’kupita kwanthaŵi sanapeze kanthu koma kukhumudwa ndi kugwiritsidwa mwala. Zirinso motero ponena za dziko la lerolino.

8. Kodi zolondola zadziko nzosapindulitsa m’njira zotani?

8 Dziko liri ndi amuna ake ophunzira ndi anzeru kwa amene anthu amayang’anako kupeza mayankho a mafunso ofunika monga onena za magwero ndi chifuno cha moyo ndi mtsogolo mwa mtundu wa anthu. Koma kodi ndichidziŵitso chotani ndi chitsogozo zimene angapereke? Ndizo kusakhulupirira kukhalako kwa Mulungu, kukaikira kukhalako kwa Mulungu, chisinthiko, ndi malingaliro ndi nthanthi zina zochuluka zosokoneza ndi zotsutsana zimene sizimaunikira konse mofanana ndi madzoma ndi kukhulupirira malaulo kwakale. Zolondola zadziko zambiri zimawonekeranso kukhala zopatsa mlingo wakutiwakuti wa chikhutiro ndi kukwanira. Anthu amalankhula za kupita patsogolo ndi chipambano m’sayansi, umisiri, nyimbo, maseŵera, ndale zadziko, ndi zina zotero. Amasangalala ndi ulemerero wawo wosakhalitsa. Ngakhale ndichoncho, zolembedwa zachaka ndi chaka za mbiri za lerolino ndi mabuku a zipambano za anthu nzodzala ndi ngwazi zoiŵalika. Zonsezi siziri kanthu koma zopanda pake, zosapindulitsa, zachabechabe, zopusa, zopanda chifuno, ndi zogwiritsa mwala.

9. Kodi ndizolondola zosapindulitsa zotani zimene ambiri atembenukirako?

9 Pozindikira kusapindulitsa kwa zipambano zoterozo, ambiri amatembenukira pakulondola zinthu zakuthupi​—kukundika ndalama ndi kupeza zinthu zimene ndalama zingagule​—ndi kuyesa zinthu zimenezi kukhala chonulirapo chawo m’moyo. Iwo ali okhutiritsidwa kuti chimwemwe chimachokera m’chuma, katundu, ndi kufunafuna zokondweretsa. Samangosumika maganizo awo pazimenezo koma ali ofunitsitsa kutairapo chirichonse​—thanzi, banja, ndipo ngakhale chikumbumtima. Kodi chotulukapo nchiyani? Mmalo mwakukhala okhutiritsidwa, ‘adzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.’ (1 Timoteo 6:10) Mposadabwitsa kuti Paulo anafulumiza Akristu anzake kuleka kuyenda monga amitundu ayendera chifukwa cha kusapindulitsa kwa njira yakulingalira kwawo.

10. Kodi ndimotani mmene anthu adziko aliri “mu mdima wamaganizo”?

10 Kusonyeza kuti dziko liribe chopatsa chirichonse choyenera kukhumbiridwa kapena kutsanziridwa, Paulo anapitiriza kunena kuti “iwo ali mumdima wamaganizo.” (Aefeso 4:18, NW) Ndithudi, dziko liri ndi anthu aluntha ndi achidziŵitso pafupifupi m’mbali zonse za moyo. Komabe, Paulo ananena kuti iwo ali mumdima wamaganizo. Chifukwa chiyani? Mawu ake sakunena za chidziŵitso chawo ndi maluso amaganizo. Liwu lakuti “maganizo” likhoza kutanthauzanso phata la kulingalira kwa munthu, maziko a kuzindikira, munthu wamkati. Iwo ali mumdima chifukwa chakuti alibe kuunika kowatsogolera kapena lingaliro lakukhala ndi wowatsogoza m’zochita zawo. Izi zikhoza kuwonedwa m’lingaliro lawo loluluzidwa la choipa ndi chabwino. Anthu angaganize kuti kalingaliridwe kamakono kosadziletsa, kakuti chirichonse chimene munthu anena kapena kuchita nchololedwa, kali kuunikiridwa, komabe ndikodi maganizo amdima, malinga nkunena kwa Paulo. Mwauzimu, iwo akudzandiradzandira mumdima wa ndiwe yani.​—Yobu 12:25; 17:12; Yesaya 5:20; 59:6-10; 60:2; yerekezerani ndi Aefeso 1:17, 18.

11. Kodi nchiyani chimene chimachititsa mdima wamaganizo m’dziko?

11 Kodi nchifukwa ninji kuli kwakuti anthu akhoza kukhala achidziŵitso, ngakhale aluntha m’zinthu zambiri komabe ali mumdima wauzimu? Pa 2 Akorinto 4:4, Paulo anatipatsa yankho kuti: ‘Mwa amene mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu chisaŵaŵalire.’ Ndidalitso lamtengo wapatali chotani nanga kuti awo amene analandira mbiri yabwino ya ulemerero asandulike m’maganizo ndi kuunikiridwa mu mtima!

Mitima Yopulukira ndi Youma

12. Kodi ndimotani mmene dziko lapatukira pa “moyo wa Mulungu”?

12 Kutithandiza kuwona bwino chifukwa chake tiyenera kusandulika m’maganizo ndi kuunikiridwa mumtima, Paulo akutiuza chenicheni chakuti njira ya dziko ili “yopatuka pa moyo wa Mulungu.” (Aefeso 4:18, NW) Sikuti anthu sakukhulupiriranso Mulungu kapena kuti akhala osapembedza kotheratu. Wolemba m’danga la nyuzipepala wina ananena motere: “Mmalo mwa liwu lakuti osapembedza, tiyeni tipange latsopano: Mulungu-pang’ono. Anthu a Mulungu-pang’ono amafuna kutamandidwa ndi kuzindikiridwa kaamba ka kukhulupirira mulungu, ngakhale kuti panthaŵi imodzimodziyo amamsunga Iye m’bokosi, titero kunena kwake, akumamlola kutuluka pa Sande pokha mmaŵa ndi kusamlola konse Iye kusonkhezera malingaliro awo andale zadziko kapena miyoyo yawo mkati mwa mlungu. [Iwo] kaŵirikaŵiri amakhulupirira Mulungu koma amalingalira kuti Iye alibe chochita kwenikweni ndi chitaganya chamakono.” Paulo ananena motere m’kalata yake kwa Aroma: ‘Ngakhale anadziŵa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika.’ (Aroma 1:21) Tsiku lirilonse timawona anthu amene amakhala ndi moyo wosalingalira za Mulungu mpang’ono ponse. Ndithudi, iwo samamlemekeza Mulungu kapena kumyamikira.

13. Kodi “moyo wa Mulungu” nchiyani?

13 Mawu akuti ‘moyo wa Mulungu’ ngofunika kwambiri. Amasonyezanso mmene mdima wamaganizo ndi wauzimu umaluluzira lingaliro la anthu la makhalidwe abwino. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “moyo” (life) panopa sindilo biʹos (limene kumachokera mawu onga “biology” [sayansi ya thupi la chinthu chamoyo], “biography” [mbiri ya munthu]), limene limatanthuza njira ya moyo, kapena umoyo. Mmalo mwake, liwulo ndilo zo·eʹ (limene kumachokera mawu onga “zoo” [mosungira zinyama], “zoology” [sayansi yophunzira zinyama]). Limatanthauza “moyo monga chinthu chenichenicho, moyo m’lingaliro lake lenileni, moyo monga umene Mulungu ali nawo. . . . Pa moyo umenewu, munthu wapatutsidwa chifukwa cha [kuchimwa kwa Adamu],” malinga nkunena kwa Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words. Chotero, Paulo anali kutiuza kuti mdima wamaganizo ndi wauzimu sunangotsogolera anthu a dziko m’chivundi cha thupi komanso kuwapatutsa pachiyembekezo cha moyo wosatha umene Mulungu walonjeza. (Agalatiya 6:8) Chifukwa ninji ziri motero? Paulo anapitiriza kutiuza zifukwazo.

14. Kodi nchifukwa chimodzi chiti chimene dziko lapatukira pa moyo wa Mulungu?

14 Choyamba, iye anati nchifukwa cha ‘chipulukiro chiri mwa iwo.’ (Aefeso 4:18) Mawu akuti ‘chiri mwa iwo’ amagogomezera kuti kupulukirako sikuli chifukwa cha kusapeza mwaŵi koma kukanira dala chidziŵitso cha Mulungu. Matembenuzidwe ena a mawu ameneŵa amati: “Kukana kwawo kwachibadwa kudziŵa Mulungu” (The Anchor Bible); “opanda chidziŵitso chifukwa chakuti anachitsekera mitima yawo” (Jerusalem Bible). Chifukwa chakuti iwo amatsutsa, kapena kukanira dala chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu, alibe maziko opezera mtundu wa moyo umene Yehova walonjeza awo osonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wake, amene anati: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.’​—Yohane 17:3; 1 Timoteo 6:19.

15. Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera kupatuka kwa dzikoli pa moyo wa Mulungu?

15 Chifukwa china chimene dziko kwakukulukulu linapatukira pa moyo wa Mulungu, malinga nkunena kwa Paulo, ndicho ‘kuumitsa kwa mitima yawo.’ (Aefeso 4:18) “Kuumitsa” panopa kwakukulukulu kumatanthauza kulimbitsa, monga kuphimbidwa ndi khungu lokakala. Tonsefe timadziŵa mmene kukakala khungu kumachitikira. Khungulo poyamba lingakhale lofeŵa ndi lokhoza kumva msanga kukhudzidwa, koma ngati likanikizidwa mobwerezabwereza kapena kupereseka, limalimba ndi kuchindikala, nilikhala lokakala. Silimamvanso kukhudzidwa. Mofananamo, anthu samabadwa ndi mtima wouma kapena wokakala moti mwachibadwa amakhala opanda lingaliro lirilonse kulinga kwa Mulungu. Koma chifukwa chakuti tikukhala m’dzikoli ndipo tikuwona mzimu wake, sikumatenga nthaŵi yaitali kuti mtima ukhale wokakala ndi wouma ngati sutetezeredwa. Nchifukwa chake Paulo anachenjeza kuti: ‘Tapenyani, . . . kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjero la uchimo.’ (Ahebri 3:7-13; Salmo 95:8-10) Chotero, nkofulumira chotani nanga, kuti tikhalebe osandulika m’maganizo ndi ounikiridwa mumtima!

‘Osazindikiranso Kanthu Konse’

16. Kodi nchiyani chiri chotulukapo cha mdima wadziko wamaganizo ndi kupatuka kwake pa moyo wa Mulungu?

16 Chotsatirapo cha mdima ndi kupatuka koteroko chikufotokozedwa m’mawu achidule a mtumwi Paulo kuti: ‘Popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse ndi umbombo.’ (Aefeso 4:19) Mawu akuti ‘sazindikiranso kanthu konse’ kwenikweni amatanthauza “kusamvanso kupweteka,” kupweteka kwa makhalidwe abwino. Ndimo mmene mtima wokakala umakhalira. Pamene uleka kumva kupweteka kwa chikumbumtima ndi lingaliro la kuŵerengeredwa mlandu kulinga kwa Mulungu, sipamakhalanso choletsa chirichonse. Chifukwa chake, Paulo ananena kuti ‘anadzipereka okha’ ku mayendedwe osadzisungira ndi ku chidetso. Kali kachitidwe kadala, kodzifunira. Mawu akuti ‘mayendedwe osadzisungira,’ monga momwe agwiritsidwira ntchito m’Baibulo, amapereka lingaliro la mkhalidwe wamaganizo wolotchedwa, wonyansidwa ndi lamulo ndi olamulira. Mofananamo, ‘chidetso chonse’ chimaphatikizapo osati kokha zilakolako zakugonana komanso zinthu zonyansa zochitidwa m’dzina la chipembedzo, zonga ngati madzoma ndi miyambo yakubala yochitidwa pakachisi wa Artemi mu Efeso, zimene oŵerenga makalata a Paulo ankazidziŵa bwino lomwe.​—Machitidwe 19:27, 35.

17. Kodi nchifukwa ninji Paulo ananena kuti anthu amene sazindikira kanthu amachimwa ‘ndi umbombo’?

17 Kuwonjezera pakumwerekera m’zonyansa ndi chidetso cha mtundu uliwonse, Paulo akunenanso kuti anthu oterowo amachita ‘ndi umbombo.’ Pamene anthu amene adakali pang’ono ndi lingaliro la makhalidwe abwino achimwa, iwo akhoza kuipidwa ndi kuyesa zolimba kusabwerezanso. Koma awo amene ‘sazindikiranso kanthu konse’ amachimwa ‘ndi umbombo’ (“ndipo amafunabe zowonjezereka,” The Anchor Bible). Woulutsa pawailesi panthaŵi ina anagwiritsira ntchito mwambi wonga wakuti: “Udzu wobiriŵira unapha mbuzi.” Iwo amamira mofulumira kufikira pansi penipeni pa chithaphwi cha zonyansa​—ndipo samawonapo cholakwa chirichonse. Ndimalongosoledwe olondola chotani nanga a ‘chifuniro cha amitundu’!​—1 Petro 4:3, 4.

18. Kunena mwachidule, kodi ndichithunzi chotani chimene Paulo anapereka cha mkhalidwe wa dziko wa maganizo ndi wauzimu?

18 Chotero, m’mavesi atatu okha, Aefeso 4:17-19, Paulo akuvumbula makhalidwe enieni ndi mkhalidwe wauzimu wa dzikoli. Iye akusonyeza kuti malingaliro ndi nthanthi zopititsidwa patsogolo ndi anzeru adziko ndi kulondola chuma ndi zosangulutsa kosalekeza ziri zosapindulitsa mpang’ono pomwe. Iye akumveketsa bwino kuti chifukwa cha mdima wamaganizo ndi wauzimu, dziko liri m’kuthedwa nzeru, likumaipiraipira nthaŵi zonse. Chotsirizira, chifukwa cha kupulukira kodzichititsa okha ndi kukakala mtima, dziko lapatuka kotheratu pa moyo wa Mulungu. Ndithudi, tiri ndi zifukwa zabwino zakukanira kuyenda monga amitundu akuyendera!

19. Kodi ndimafunso ofunika otani amene ayenerabe kulingaliridwa?

19 Popeza kuti uli mdima wamaganizo ndi mtima umene umachititsa dziko kupatuka kwa Yehova Mulungu, kodi ndimotani mmene tingachotsere mdima wonse m’maganizo ndi m’mitima yathu? Inde, kodi tiyenera kuchitanji kuti tipitirizebe kuyenda monga ana a kuunika ndi kupeza chiyanjo cha Mulungu? Izi zidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi nchiyani chinasonkhezera Paulo kupereka uphungu wake wa pa Aefeso 4:17-19?

◻ Kodi nchifukwa ninji njira za dziko ziri zosapindulitsa ndi zamdima?

◻ Kodi mawu akuti ‘opatutsidwa pa moyo wa Mulungu’ amatanthauzanji?

◻ Kodi zotulukapo za maganizo amdima ndi mtima wouma nzotani?

[Zithunzi patsamba 9]

Efeso anali womwerekera m’makhalidwe ake onyansa ndi kulambira mafano

1. Mroma wamaseŵera akumenyana kwa wafawafa ku Efeso

2. Bwinja la kachisi wa Artemi

3. Nyumba ya maseŵero ku Efeso

4. Artemi wa Aefeso, mlungu wamkazi wa kubala

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi ndichidziŵitso chotani chimene ophunzira adziko angapereke?

Nero

[Mawu a Chithunzi]

Musei Capitolini, Roma

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena