Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 74-tsamba 77 ndime 2
  • Khalani Womapitabe Patsogolo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Womapitabe Patsogolo
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa Zinthu ndi Kusintha
  • Gwiritsani Ntchito Mphatso Yanu
  • Mmene Kudziŵa Zambiri Kumathandizira
  • Pitanibe Patsogolo
  • Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Achinyamata, Yesetsani Kuti Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Chititsani Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kupita Kwanu Patsogolo Kuzionekera
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 74-tsamba 77 ndime 2

Khalani Womapitabe Patsogolo

PAMENE munaphunzira kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo, maganizo anu ozama akale, malankhulidwe anu ndi khalidwe lanu, zinayamba kusintha pang’onopang’ono. Mbali yaikulu ya kusintha kumeneku inachitika musanalembetse n’komwe m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Munapita patsogolo mpaka munapereka moyo wanu kwa Yehova. Kodi izi zikutanthauza kuti tsopano simufunikiranso kupita patsogolo? Kutalitali! Ubatizo wanu unali chiyambi chabe.

Wophunzira Timoteo anali kale mkulu wachikristu pamene Paulo anam’langiza ‘kusamalira’ uphungu umene anam’patsa ndi mwayi wa utumiki woikizidwa kwa iye—kuti ‘akhale’ m’zinthu zimenezi—kotero kuti ‘kupita patsogolo kwake kuonekere kwa anthu onse.’ (1 Tim. 4:12-15, NW) Kaya mwangoyamba kumene kuyenda m’njira ya choonadi kapena ndinu mkhalakale m’moyo wachikristu, muyenera kukhala ndi chidwi chofuna kumapitabe patsogolo.

Kudziŵa Zinthu ndi Kusintha

Pa Aefeso 3:14-19, timaŵerenga kuti mtumwi Paulo anapemphera kuti okhulupirira anzake akakhoze kuzindikira . . . “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera” kwa choonadi. Pachifukwa chimenecho, Yesu anapereka mphatso za amuna kuti aphunzitse, kuwongolera, ndi kumangirira mpingo. Kusinkhasinkha nthaŵi zonse Mawu a Mulungu ouziridwa, limodzi ndi chithandizo chochokera kwa aphunzitsi odziŵa zambiri, zikhoza kutithandiza ‘kukula’ mwauzimu.—Aef. 4:11-15.

Kukula kumeneko kumaphatikizapo ‘kukhala atsopano m’mphamvu yoyendetsa maganizo.’ Zimenezi zimatanthauza kukhala ndi maganizo otengera Mulungu ndi Kristu. Kumafuna kumva za maganizo awo nthaŵi zonse, kotero kuti ‘tivale umunthu watsopano.’ (Aef. 4:23, 24) Pamene muŵerenga nkhani za Mauthenga Abwino anayi, kodi mumaziona kukhala zochitikadi m’moyo wa Kristu zimene muyenera kutengera monga chitsanzo? Kodi mumayesetsa kuzindikira makhalidwe amene Yesu anaonetsa ndi kulimbikira kuti muwatsanzire pamoyo wanu?—1 Pet. 2:21.

Mtundu wa nkhani zimene mumakambirana ndi anthu ungasonyeze mlingo umene mwapita patsogolo. Anthu amene avala umunthu watsopano salankhula zinthu zachinyengo, zonyoza, zolaula, kapena zongofuna kutsutsa basi. M’malo mwake, malankhulidwe awo amakhala ‘abwino ndi omangirira . . . kuti apatse chisomo kwa iwo akumva.’ (Aef. 4:25, 26, 29, 31; 5:3, 4; Yuda 16) Malankhulidwe awo mseri ndi pamisonkhano yampingo amaonetsa kuti choonadi chikusintha miyoyo yawo.

Ngati simulinso ‘otengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso,’ ndi umboni wina wakuti mukupitabe patsogolo. (Aef. 4:14) Mwachitsanzo, kodi mumatani pamene dziko likusonyezani maganizo atsopano osiyanasiyana, kapena mitundu yosiyanasiyana ya zosangalatsa? Kodi mumalakalaka kupatulako nthaŵi ya maudindo anu auzimu kuti mukasangalale ndi zinthu zimenezo? Kuchita zimenezo kungasokoneze kupita patsogolo kwauzimu. Chinthu chanzeru chingakhale kupatulira nthaŵi zinthu zauzimu.—Aef. 5:15, 16.

Mmenenso mumachitira ndi anthu ena ungakhalenso umboni wina wa kupita patsogolo mwauzimu. Kodi mwaphunzira kukhala “a mtima wachifundo, akukhululukirana” kulinga kwa abale ndi alongo anu?—Aef. 4:32.

Kupita kwanu patsogolo pa kuchita zinthu m’njira ya Yehova kuyenera kuonekera mbali zonse, kumpingo ndi kunyumba. Kuyenera kuonekeranso kusukulu, m’malo opezekako anthu onse, ndi kuntchito kwanu. (Aef. 5:21–6:9) Ngati m’mikhalidwe yonseyi mumasonyeza bwino lomwe makhalidwe aumulungu, ndiye kuti kupita kwanu patsogolo kukuonekera.

Gwiritsani Ntchito Mphatso Yanu

Yehova anatipatsa maluso a mtengo wapatali. Amatiyembekezera kuwagwiritsa ntchito kuthandizira ena, kotero kuti kupyolera mwa ife, aonetse chisomo chake. Pamfundo imeneyi mtumwi Petro analemba kuti: “Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha Mulungu.” (1 Pet. 4:10) Kodi inuyo mukuusamalira motani udindo wanu?

Petro akupitiriza kuti: “Akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu.” (1 Pet. 4:11) Vesi imeneyi ikuunika makamaka udindo wolankhula zinthu mogwirizana kwathunthu ndi Mawu a Mulungu, kuti Mulungu akalemekezeke. Choncho, malankhulidwe athu ayeneranso kulemekeza Yehova. Maphunziro operekedwa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu akhoza kukuthandizani kugwiritsa ntchito mphatso yanu m’njira imeneyo—kulemekeza Mulungu ndi njira imene mumathandizira ena. Ndi cholinga chimenecho, kodi mungapime motani kupita kwanu patsogolo m’sukuluyo?

M’malo moyang’ana pa mfundo zimene mwakhala mukukhoza pafomu yanu yolangizira kalankhulidwe kapena mtundu wa nkhani zimene mumapatsidwa, yang’anani mmene sukuluyo ikuwongolera mtundu wa nsembe yanu ya chitamando. Sukuluyi imatiphunzitsa kukhala aluso mu utumiki wa kumunda. Choncho, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakonzekeradi zoti ndikanene mu utumiki wa kumunda? Kodi ndaphunzira kuonetsa chidwi chenicheni kwa anthu amene ndimawalalikira? Kodi ndimayala maziko a maulendo obwereza mwa kusiya funso kwa munthu loti tikakambirane ulendo wotsatira? Ngati ndimaphunzira Baibulo ndi munthu wina, kodi ndikuyesetsa kukhala mphunzitsi amene amafika munthu pamtima?’

Kupita kwanu patsogolo musamakuonere chabe m’mwayi wa utumiki umene mumapatsidwa. Kupita kwanu patsogolo sikuonekera kwenikweni mu nkhani imene mwapatsidwa, koma mmene mumaikambira. Ngati mwapatsidwa nkhani yophunzitsa, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndagwiritsadi ntchito luso la kuphunzitsa? Kodi nkhani ija ndaikamba m’njira imene idzathandiza omvera pamiyoyo yawo?

Langizo lakuti gwiritsani ntchito mphatso yanu limatanthauza kugwiritsa ntchito nzeru. Kodi mumanyamuka nokha kuti mukagwire ntchito yakumunda pamodzi ndi ena? Kodi mumafunafuna mipata yoti muthandize atsopano mumpingo wanu, ang’onoang’ono, kapena olemala? Kodi mumadzipereka pantchito yokayeretsa ku Nyumba ya Ufumu kapena kuthandiza m’njira zosiyanasiyana pamisonkhano ikuluikulu? Kodi mukhoza kumalembetsa nthaŵi ndi nthaŵi upainiya wothandiza? Kodi mungatumikire ngati mpainiya wokhazikika kapena kukathandiza kumpingo wosoŵa? Ngati muli mbale, kodi mukukalamira kuti mukafikire ziyeneretso za m’Malemba za atumiki otumikira ndi akulu? Kudzipereka kwanu kuti muthandize ndi kulandira udindo kuli umboni wa kupita patsogolo.—Sal. 110:3.

Mmene Kudziŵa Zambiri Kumathandizira

Ngati mukudziona kukhala wopereŵera chifukwa chosadziŵa zambiri m’moyo wachikristu, musataye mtima. Mawu a Mulungu amapatsa nzeru munthu wosadziŵa zambiri. (Sal. 19:7; 119:130; Miy. 1:1-4) Kugwiritsa ntchito uphungu wa m’Baibulo kumatilola kupindula ndi nzeru yangwiro ya Yehova, imene imapindulitsa koposa nzeru ina iliyonse imene munthu angaipeze payekha. Komabe, pamene tikupita patsogolo mu utumiki wathu kwa Yehova, timakhala ndi nzeru yothandiza kwambiri. Kodi nzeru imeneyo tingaigwiritse ntchito motani m’njira yopindulitsa?

Munthu akaona zambiri m’moyo, angalingalire kuti: ‘Zimenezi sizachilendo kwa ine. Ndikudziŵa zochita.’ Kodi imeneyi ingakhale nzeru? Miyambo 3:7 imachenjeza kuti: “Usadziyese wekha wanzeru.” Inde, kudziŵa zambiri kuyeneradi kutithandiza kuona mbali zosiyanasiyana pochita ndi mikhalidwe ina m’moyo. Koma ngati tikupita patsogolo mwauzimu, kudziŵa kwathu zambiri kuyenera kuthandizanso maganizo athu ndi mitima yathu kudziŵa kuti tifunikira thandizo la Yehova kuti tipambane. Choncho, taona kuti kupita kwathu patsogolo kumaonekera osati mwa kudzidalira tokha pochita ndi mikhalidwe, koma mwa kutembenukira kwa Yehova mwachangu kuti atitsogolere m’miyoyo yathu. Kumaonekera mwa kukhala ndi chidaliro chakuti palibe chingatheke popanda chilolezo chake. Kumaonekeranso mwa kusunga unansi wathu wokhulupirira Atate wathu wakumwamba ndi kumukonda.

Pitanibe Patsogolo

Ngakhale kuti mtumwi Paulo anali Mkristu wodzozedwa ndi wokhwima mwauzimu, anazindikira kuti anafunikira kupitabe patsogolo kuti akapeze cholinga cha moyo. (Afil. 3:13-16) Kodi inunso muli ndi maganizo amenewo?

Kodi mwapita patsogolo kufika pati? Pimani msinkhu wa kukula kwanu kwauzimu mwa kuona ngati mwavala umunthu watsopano mokwanira, ngati mwagonjera ulamuliro wa Yehova kwathunthu, komanso ngati mukugwiritsa ntchito mphatso zanu kulemekezera Yehova mokhulupirika. Pamene mukupindula ndi maphunziro a Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, makhalidwe otchulidwa m’Mawu a Mulungu ayenera kumaonekerabe m’malankhulidwe ndi kaphunzitsidwe kanu. Nthaŵi zonse kumbukirani mbali zimenezi za kupita patsogolo. Inde, sangalalani nazo, ndipo kupita kwanu patsogolo kudzaonekera.

KODI ZOLINGA ZANU ZAUZIMU N’ZOTANI?

Kodi mwaika zolinga zotheka zotani zimene mukufuna kuzikwaniritsa chaka chamaŵa?

  1. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

  2. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

Kodi ndi zolinga zam’tsogolo zotani za mtengo wapatali zimene mwatsimikiza mtima kuti mulimbikire mpaka mukazikwaniritse?

  1. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

  2. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

  3. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena