Kodi Ndinu Fano la Inumwini?
Mosadziŵa, anthu ena amapanga mafano a iwo eni. Baibulo pa Aefeso 5:5 (NW) limalongosola kuti: “Pakuti inu muchidziŵa ichi, mukumadzidziŵira nokha, kuti palibe wadama kapena munthu wauchisi kapena munthu waumbombo—zimene zimatanthauza kukhala wopembedza mafano—ali ndi choloŵa chiri chonse mu ufumu wa Kristu ndi wa Mulungu.” (Akolose 3:5; yerekezerani ndi Agalatiya 5:19-21.) Zikhumbo zakuthupi zingabwere pakati pa munthu ndi Mulungu. Paulo akunena za zimenezo kuti “mulungu wawo ndiyo mimba yawo.” (Afilipi 3:18, 19) M’mawu ena, iwo ali ndi “mulungu” wina pambali pa Yehova, namaika zikhumbo zawo zakuthupi m’malo oyamba. Mkhalidwe woterowo ungalepheretse munthu kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10) Chotero, pali chifukwa chabwino, kulabadira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Chifukwa chake, okondedwa anga, thaŵani kupembedza mafano.”—1 Akorinto 10:14.