Imbirani Yehova Zitamando
“Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu.”—EKSODO 15:1.
1. Kodi ndi mikhalidwe yotani ya Yehova imene imatipatsa chifukwa chomtamandira?
KWA nthaŵi 13, Salmo 150 limalamula kutamanda Yehova kapena Ya. Vesi lotsiriziralo limalengeza kuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.” Monga Mboni za Yehova, timadziŵa kuti Yehova ali woyenerera chitamando chathu. Iye ndiye Wolamulira Wachilengedwe Chonse, Wam’mwambamwamba, Mfumu yamuyaya, Mlengi wathu, Wotifupa. Iye alibe wolingana naye, ali wapadera, wosayerekezereka, wosasanthulika m’njira zambiri. Ali mwininzeru, mwinimphamvu, wangwiro m’chilungamo, ndi chitsanzo changwiro cha chikondi. Iye aposa aliyense muubwino; ali wokhulupirika. (Luka 18:19; Chivumbulutso 15:3, 4) Kodi ali woyenerera chitamando chathu? Ndithudi alidi wotero!
2. Kodi tili ndi zifukwa zotani zosonyezera chiyamikiro kwa Yehova?
2 Yehova ali woyenerera osati chabe kulambira kwathu ndi chitamando komanso chiyamikiro ndi chithokozo chathu pa zonse zimene watichitira. Iye ali Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Iye ali Kasupe, Magwero a moyo wonse. (Salmo 36:9) Zinthu zonse zimene timasangalala nazo monga ziŵalo za fuko la anthu zinachokera kwa iye, pakuti ali Mlengi wathu Wamkulu. (Yesaya 42:5) Iye alinso Mpatsi wa madalitso onse auzimu amene amadza kwa ife kupyolera mwa mzimu wake, gulu lake, ndi Mawu ake. Timakhululukidwa machimo athu pamaziko a Mwana wake amene anampereka monga dipo lathu. (Yohane 3:16) Tili ndi chiyembekezo cha Ufumu cha ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene mudzakhala chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Tili ndi mayanjano abwino pamodzi ndi Akristu anzathu. (Aroma 1:11, 12) Tili ndi ulemu ndi madalitso a kukhala Mboni zake. (Yesaya 43:10-12) Ndipo tili ndi mwaŵi wamtengo wapatali wa pemphero. (Mateyu 6:9-13) Ndithudi, tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira Yehova!
Njira Zimene Tingatamandire Yehova
3. Kodi ndi m’njira zosiyanasiyana zotani zimene tingatamandire Yehova ndi kusonyeza chiyamikiro chathu kwa iye?
3 Kodi ndimotani mmene ifeyo, monga atumiki odzipereka a Yehova, tingamtamandire ndi kusonyeza chiyamikiro chathu? Tingachite zimenezo mwa kukhala ndi mbali muutumiki Wachikristu—tikumachitira umboni kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, kuchititsa maphunziro a Baibulo, ndi kuchita umboni wa m’khwalala. Tikhozanso kumtamanda mwa kuchitira umboni wamwamwaŵi pamene mpata upezeka. Ndiyenonso, tingatamande Yehova mwa makhalidwe athu olungama, ngakhalenso mwa kavalidwe ndi kapesedwe kathu kaudongo ndi kodekha. Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zatamandidwa kaamba ka kuchita bwino koposa m’mbali zimenezi. Ndiponso, tikhoza kutamanda Yehova ndi kumyamikira mwa pemphero.—Onani 1 Mbiri 29:10-13.
4. Kodi ndi iti imene ili imodzi ya njira zabwino koposa zimene tingatamandire Atate wathu wachikondi wakumwamba?
4 Kuwonjezerapo, imodzi ya njira zabwino koposa zimene tingatamandire Atate wathu wakumwamba wachikondi ndiyo mwa kumkweza iye ndi mikhalidwe yake mwa nyimbo za Ufumu. Oimba nyimbo ndi opeka nyimbo ambiri amavomereza kuti chiŵiya choimbira chabwino koposa ndicho liwu la munthu. Akatswiri a nyimbo za classic anasonkhezeredwa kulemba maseŵero a kuimba ndi mawu chifukwa cha chikhutiro chachikulu chimene chili m’kumvetsera liwu la munthu poimba.
5. Kodi nzifukwa zotani zimene tiyenera kuonera kuimba kwathu nyimbo za Ufumu kukhala kofunika kwambiri?
5 Ha, Yehova ayenera kusangalala chotani nanga kumvetsera anthu akuimba, makamaka pamene akuimba nyimbo za chitamando ndi za chiyamikiro! Chifukwa chake, tiyenera kuona kuimba kwathu nyimbo za Ufumu kukhala kofunika kwambiri pamisonkhano yathu yosiyanasiyana—misonkhano yampingo, misonkhano yadera, misonkhano yapadera ya tsiku limodzi, misonkhano yachigawo, ndi misonkhano yamitundu. Buku lathu lanyimbo lili ndi nyimbo zokoma zochuluka, ukoma umene wathokozedwa kaŵirikaŵiri ndi anthu akunja. Pamene tiloŵa kwambiri mumzimu wa kuimba nyimbo za Ufumu, ndi pamenenso timasangalatsa ena ndi kudzipindulitsa ife eni.
Kuimbira Yehova Zitamando m’Nthaŵi za Baibulo
6. Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anasonyezera chiyamikiro kaamba ka chilanditso chawo pa Nyanja Yofiira?
6 Mawu a Mulungu amatiuza kuti Mose ndi Aisrayeli onse anaimba nyimbo yachilakiko pamene anapulumutsidwa ku gulu lankhondo la Farao pa Nyanja Yofiira. Nyimbo yawo inayamba ndi mawu akuti: “Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza.” (Eksodo 15:1, 2) Tikhoza kuyerekezera bwino lomwe chisangalalo ndi chimwemwe chimene Aisrayeli anali nacho poimba mawu amenewo pambuyo pa kulanditsidwa kwawo kozizwitsa!
7. Kodi nzochitika zodziŵika zina ziti zolembedwa m’Malemba Achihebri zonena za Aisrayeli akutamanda Yehova m’nyimbo?
7 Pa 1 Mbiri 16:1, 4-36, timaŵerenga kuti Yehova anatamandidwa ndi nyimbo zapakamwa ndi zamalimba pamene Davide anabweretsa Likasa ku Yerusalemu. Imeneyo inalidi nthaŵi ya chisangalalo chachikulu. Panalinso kuimba chitamando kwa Yehova motsagana ndi nyimbo zamalimba panthaŵi imene Mfumu Solomo anapatulira kachisi ku Yerusalemu. Timaŵerenga pa 2 Mbiri 5:13, 14 kuti: “Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mawu amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mawu awo pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova; ndipo ansembe sanakhoza kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.” Kodi zimenezo zimasonyezanji? Zimasonyeza kuti Yehova anali kumvetsera chitamando cha mang’ombe okoma chimenechi ndipo anakondwera nacho, monga kunasonyezedwa ndi kufika kwa mtambo wozizwitsawo. Pambuyo pake, panali kuimba kwa magulu aŵiri potsegulira malinga a Yerusalemu m’masiku a Nehemiya.—Nehemiya 12:27-42.
8. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti kuimba kunaonedwa kukhala kofunika kwambiri kwa Aisrayeli?
8 Kwenikweni, kuimba kunali mbali yofunika kwambiri ya kulambira pakachisi kwakuti Alevi 4,000 anapatulidwa kaamba ka utumiki wa zamaimbidwe. (1 Mbiri 23:4, 5) Iwoŵa ankatsagana ndi oimba. Nyimbo, makamaka oimba, anali ndi mbali yaikulu m’kulambira, osati kwenikweni kuti amveketse nkhani zofunika kwambiri za Chilamulo, koma kuti adzutse mzimu woyenerera wa kulambira. Kunathandiza Aisrayeli kulambira Yehova m’njira yosonkhezereka maganizo. Taonani kukonzekera ndi chisamaliro chimene chinaikidwa pa mbali imeneyi: “Chiŵerengo chawo, pamodzi ndi abale awo ophunzitsidwa aimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana aŵiri mphambu makumi asanu ndi atatu.” (1 Mbiri 25:7) Onani mmene iwo anaonera kuimba chitamando kwa Yehova kukhala kofunika kwambiri. Anaphunzitsidwa kuimba ndipo anali akatswiri!
9. Kodi ndi chigogomezero chotani chimene chikuikidwa pakuimba m’Malemba Achigiriki Achikristu?
9 Ponena za m’zaka za zana loyamba la nyengo yathu, kodi timapeza chiyani? Yesu, pa usiku wa kuperekedwa kwake, ali ndi nkhani zovutitsa kwenikweni m’maganizo, anaonabe kufunika kwa kumaliza kuchita kwake phwando la Paskha ndi kuyambitsa Chikumbutso cha imfa yake mwa kuimba zitamando kwa Yehova. (Mateyu 26:30) Ndiponso, timaŵerenga kuti “ngati pakati pa usiku,” Paulo ndi Sila, pambuyo pa kumenyedwa ndi kuponyedwa m’ndende, “analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m’ndendemo analinkuwamva.”—Machitidwe 16:25.
Kuimba Zitamando—Mbali Yofunika ya Kulambira Kwathu
10. Kodi ndi malamulo otani amene Mawu a Mulungu amatipatsa a kumtamanda m’nyimbo?
10 Kodi mwinamwake mumaona kuimba nyimbo za Ufumu kusakhala kofunika kwambiri kwakuti mukupatse chisamaliro cha mtima wonse? Ngati zili motero, kodi simufunikira kupendanso nkhaniyo, kaamba ka kufunika kumene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu amaika pakuimba zitamando? Eya, Mawu a Mulungu ali odzaza ndi malangizo olamula kutamanda Yehova ndi kuimba zitamando kwa iye! Mwachitsanzo, pa Yesaya 42:10, timaŵerenga kuti: “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili mmenemo, zisumbu ndi okhala mommo.”—Onaninso Salmo 96:1; 98:1.
11. Kodi ndi chilangizo chotani chimene mtumwi Paulo anapereka ponena za kuimba?
11 Mtumwi Paulo anadziŵa kuti kuimba kungadzutse mwa ife mzimu wachisangalalo, motero anatilangiza kaŵiri pa nkhaniyi. Timaŵerenga pa Aefeso 5:18, 19, kuti: ‘Mudzale nawo mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira [Mulungu, NW] ndi kuimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu.’ Ndiponso pa Akolose 3:16, timaŵerenga kuti: “Mawu a Kristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.”
12. Kodi ndi zitsanzo zotani zimene tili nazo zosonyeza kuti nyimbo zathu zimatithandiza kuphunzitsana ndi kulangizana?
12 Onani kuti pa iliyonse ya nthaŵizo Paulo akubwereza kunena za kuimba, pamene atchula ‘masalmo, mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.’ Ndiponso, iye akuyamba mawu ake kwa Akolose mwa kunena kuti mwa zimenezi tikhoza “kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha.” Ndipo timachitadi zimenezo, monga momwe tingaonere mwa mitu ya nyimbo zathu—“Chilengedwe Chonse, Tamandani Yehova!” (nambala 5), “Khalani Okhazikika, Osasunthika!” (nambala 10), “Kondwererani Chiyembekezo Chaufumu!” (nambala 16), “Musawaope!” (nambala 27), “Tamani Yehova Mulungu Wathu!” (nambala 100), kungopereka zitsanzo zoŵerengeka zokha.
13. Kodi ndimotani mmene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wasonyezera kufunika kwa kuimba monga mbali ya kulambira kwathu?
13 Mogwirizana ndi malamulo ameneŵa, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” walinganiza kuti misonkhano yathu—misonkhano yampingo, misonkhano yadera, misonkhano yapadera ya tsiku limodzi, misonkhano yachigawo, ndi misonkhano yamitundu—iyenera kuyamba ndi kutha ndi kuimba nyimbo za Ufumu. (Mateyu 24:45) Ndiponso, nyimbo zimandandalikidwa zoimba panthaŵi zina pamisonkhano imeneyi. Popeza kuti misonkhano yathu kaŵirikaŵiri imayamba ndi kuimba nyimbo ya Ufumu, kodi sitiyenera kutsimikizira kuti tidzifika panthaŵi yake, mwamsanga kuti tigaŵanemo m’mbali imeneyo ya kulambira kwathu? Ndipo popeza kuti misonkhano imamalizidwa ndi kuimba, kodi sitiyenera kukhalapobe kufikira nyimbo yotsirizira ndi pemphero limene limatsatirapo?
14. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene tili nazo za nyimbo zosankhidwa zoyenerera maprogramu athu?
14 Nyimbo za pamisonkhano yathu zimasankhidwa mosamalitsa kuti zigwirizane ndi programuyo. Mwachitsanzo, pa Misonkhano Yachigawo ya “Chiphunzitso Chaumulungu” mu 1993, nyimbo nambala 70, “Tetezera Mtima Wako!,” imene imalimbikitsa Akristu kulimbana ndi Satana, dziko, ndi thupi lochimwa, inatsatira nkhani zitatu zimene zinafotokoza adani ameneŵa. Nyimbo nambala 39, “Khalani Monga Yeremiya!,” inatsatiridwa ndi tsatanetsatane wa nkhani zozikidwa pa maulosi a Yeremiya. Ndipo pambuyo pa nkhani yosiirana yonena za mbali zosiyanasiyana za utumiki wathu wa Ufumu panabwera nyimbo nambala 68, “Kufesa Mbewu za Ufumu,” nyimbo yosonkhezera kwambiri utumiki. Chisamaliro chofananacho chimachitidwa posankha nyimbo za Phunziro la Nsanja ya Olonda, Msonkhano Wautumiki, ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Ndiponso akulu akamapereka nkhani zapoyera ndi kusonyeza nyimbo yoyambira programu, ayenera kusankha nyimbo imene imayenerera mutu wa nkhani yawo.
15. Kodi ndimotani mmene tcheyamani wa msonkhano angakulitsire chiyamikiro cha nyimbo yoti iimbidwe?
15 Polengeza nyimbo yoti iimbidwe, tcheyamani angakulitse chiyamikiro cha nyimboyo mwa kutchula mutu wake. Sitimaimba manambala koma mitu yankhani ya Malemba. Ndiponso kukakhala kothandiza mpingo kumvetsetsa kwambiri nyimboyo ngati lemba loperekedwa pansi pa mutu wake litchulidwa. Ndiyeno, mawu angapo angakhale oyenera, onga akuti onse ayenera kuloŵa mumzimu wa nyimboyo.
Sonyezani Chiyamikiro Kaamba ka Ubwino wa Yehova mwa Kuimba
16. Kodi ndimotani mmene tingaloŵere mumzimu wa nyimbo zathu?
16 Popeza kuti mawu a nyimbo zathu za Ufumu ngodzaza ndi matanthauzo, tifunikira kusumika maganizo pa mawuwo pamene tikuimba. Timafuna kuloŵa mumzimu wa nyimbo iliyonse. Zina, monga zija zonena za chikondi, chipatso cha mzimu, zimakhudza mtima. (Agalatiya 5:22) Zimenezi timaziimba motenthedwa maganizo ndi mwachikondi. Zina nzachisangalalo, ndipo tiyenera kuyesayesa kuziimba mwachimwemwe. Komabe zina nzamphamvu, nyimbo zogubira, ndipo zimenezi ziyenera kuimbidwa ndi chikondwerero ndi chidaliro champhamvu. Mu Sukulu yathu Yautumiki Wateokratiki, timalangizidwa kusonyeza ubwenzi ndi mzimu wa nkhani limodzinso ndi chisangalalo pokamba nkhani zathu. Kusonyeza ubwenzi, mzimu wa nyimbo, ndi chisangalalo poimba nyimbo zathu kuli kofunika kwambiri.
17. (a) Kodi ndi chidzudzulo chotani choperekedwa kwa Aisrayeli osakhulupirika chimene sitikafuna kuti chikhale pa kaimbidwe kathu? (b) Kodi pangakhale chotulukapo chotani ngati titenga mosamalitsa chilangizo chopezeka m’nyimbo zathu?
17 Ngati tikaimba nyimbo zathu za Ufumu maganizo athu ali pazinthu zina, ndi kusazindikira mokwanira tanthauzo la mawuwo, kodi mwanjira ina sitikakhala ofanana ndi Aisrayeli osakhulupirika amene anadzudzulidwa chifukwa chakuti, ngakhale kuti anatamanda Mulungu ndi milomo yawo, mitima yawo inali yotalikirana kwambiri ndi iye? (Mateyu 15:8) Sitikufuna kuti chidzudzulo chotero chikhalenso pa kaimbidwe kathu ka nyimbo za Ufumu, sichoncho kodi? Mwa kuchita ndi nyimbo zathu za Ufumu mwanjira yofunikira, tidzasonkhezera osati ife eni chabe komanso awo ali pambali pathu, kuphatikizapo achichepere. Inde, ngati onse oimba pa Nyumba zathu Zaufumu asamalira kwenikweni chilangizo chokhala m’nyimbo zimenezi, zikakhala chilimbikitso champhamvu chokhalira achangu muutumiki ndi kupeŵa misampha ya kuchita zolakwa.
18. Kodi kuimba nyimbo za Ufumu kunayambukira motani mkazi wina?
18 Nthaŵi ndi nthaŵi, akunja amachita chidwi ndi maimbidwe athu a nyimbo za Ufumu. Panthaŵi ina Nsanja ya Olonda inafalitsa nkhani yakuti: “Kuti maimbidwe [athu] akhozanso kupatsa anthu chidziŵitso cha Yehova Mulungu kunasonyezedwa ndi mkazi wina amene anabatizidwa pa Msonkhano wa ‘Chilakiko Chaumulungu,’ ku Yankee Stadium, mumzinda wa New York. Iye anapita kwa nthaŵi yoyamba ku Nyumba Yaufumu ali yekha ndipo anakhalapo pamisonkhano yonse iŵiri. Pamene mpingo unaimba . . . ‘Yang’ananibe Maso Anu Pamphotho!,’ anachita chidwi kwambiri ndi mawuwo ndi mmene anaimbidwira kwakuti anagamula kuti kunoko ndi kumene anafuna kukhalako. Pambuyo pake anafikira mmodzi wa Mbonizo ndi kupempha phunziro la Baibulo, ndipo anapita patsogolo nakhala mboni Yachikristu ya Yehova.”
19. Kodi ndi chilimbikitso chotsirizira chotani chimene chikuperekedwa pa kuimba nyimbo zathu za Ufumu ndi moyo wonse?
19 Pamisonkhano yathu yambiri, pamakhala mipata yoŵerengeka yokha yakuti omvetserawo afotokoze malingaliro awo ndi chiyamikiro. Koma tonsefe tikhoza kusonyeza mmene timamverera ponena za ubwino wa Yehova mwa kugwirizana ndi mtima wonse kuimba nyimbo za Ufumu. Ndiponso, pamene tisonkhana pamodzi kodi sitimakhala ndi mzimu wachisangalalo? Motero tiyenera kukhala ofunitsitsa kuimba! (Yakobo 5:13) Ndithudi, pamlingo umene timayamikira ubwino wa Yehova ndi chisomo chake, tidzaimba ndi moyo wonse zitamando kwa iye.
Kodi Mukuyankha Motani?
◻ Kodi nzifukwa zazikulu ziŵiri ziti zotamandira Yehova?
◻ Kodi ndi m’njira zosiyanasiyana ziti zimene tingatamandire Yehova?
◻ Kodi ndi iti imene ili imodzi ya njira zabwino koposa zimene tingatamandire Yehova?
◻ Kodi tili ndi zitsanzo za Malemba zotani za kutamanda Yehova m’nyimbo?
◻ Kodi ndimotani mmene tingachitire mofunikira ndi maimbidwe a nyimbo zathu za Ufumu?
[Bokosi patsamba 11]
Sangalalani ndi Nyimbozo!
Zikuoneka kuti ena anali ndi vuto pang’ono pophunzira zina za nyimbo. Komabe, mipingo ina sinakhale ndi vuto lalikulu la kuimba zochuluka za nyimbo zimenezi. Mwinamwake mungofunikira kulimbikira pang’ono kuyesa kuphunzira zimene poyamba zimaoneka kukhala zachilendo. Mpingo utazoloŵera nyimbozo, kaŵirikaŵiri umaziyamikira kwambiri kuposa zija zimene zinaphunziridwa mosavuta. Ndiyeno onse mumpingo akhoza kuimba mwachidaliro. Inde, akhoza kusangalala ndi nyimbozo!
[Bokosi patsamba 12]
Imbani Nyimbo za Ufumu pa Misonkhano Yocheza
Kuimba kwathu nyimbo za Ufumu sikuyenera kukhala kwa pa Nyumba Yaufumu pokha. Paulo ndi Sila anaimba zitamando kwa Yehova pamene anali m’ndende. (Machitidwe 16:25) Ndipo wophunzira Yakobo anati: “Kodi pali aliyense amene ali ndi mzimu wosangalala? Aimbetu zitamando kwa Mulungu.” (Yakobo 5:13, NW, mawu amtsinde) Pa misonkhano yocheza aliyense amakhala ndi mzimu wosangalala. Chotero bwanji osaimba nyimbo za Ufumu? Zimenezi zingakhale zosangalatsa kwambiri makamaka ngati kuimbako kutsagana ndi piyano kapena gitala. Ngati sichoncho, pali matepi a piyano a nyimbo zathu za Ufumu; mabanja ambiri a Mboni ali ndi alubamu ya matepi ameneŵa. Samangotsagana bwino ndi kuimba komanso ali abwino monga nyimbo zomvetsera pocheza.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Atalanditsidwa pa Nyanja Yofiira, Aisrayeli anasonyeza chisangalalo chawo m’nyimbo
[Chithunzi patsamba 10]
Kuimba mwachisangalalo kuli mbali ya kulambira Kwachikristu lerolino