Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kumvera—Kodi Ndi Phunziro Lofunika Paubwana?
    Nsanja ya Olonda—2001 | April 1
    • “Kuti Kukhale Bwino ndi Iŵe”

      Paulo anatchula ubwino wina wa kumvera pamene analemba kuti: “Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iŵe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:2, 3; Eksodo 20:12) Kodi ndi motani mmene kumvera makolo kungabweretsere munthu zinthu zokoma?

      Choyamba, kodi si zoona kuti makolo anakhalapo kale ndiponso amadziŵa zinthu zambiri? Ngakhale kuti sangadziŵe zambiri pankhani za kompyuta kapena maphunziro ena a kusukulu, iwo amadziŵa zambiri pankhani za moyo ndiponso mmene tingathetsere mavuto m’moyo. Pamene, achinyamata salingalira bwinobwino chifukwa nzeru zoterozo zimadza mwa kukhala wokhwima m’maganizo. Motero, iwo amakhala opupuluma posankha zinthu zoti achite, nthaŵi zambiri anzawo amawasonkhezera kuti achite zinthu zoopsa, ndipo zimangowavulaza. Moyenerera, Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” Kodi mankhwala ake n’chiyani? “Nthyole yom’langira idzauingitsira kutali.”​—Miyambo 22:15.

      Mapindu a kumvera sikuti amangothera pa unansi wa kholo ndi mwana. Kuti anthu agwire ntchito mopanda zopinga komanso mwaphindu, payenera kukhala mgwirizano, womwe umafuna kumvera. Mwachitsanzo, mu ukwati, kukhala wokonzeka kugonja ndiko kumabweretsa mtendere, mgwirizano, ndi chimwemwe, kusiyana ndi kukhala munthu wolamulira ndi wosaganizira za ufulu ndi zolingalira za ena. Pantchito, m’pofunika kuti wolembedwa ntchito akhale wogonjera pofuna kuti ntchito iliyonse iyende bwino. Pa za malamulo a boma, kumvera sikuti kumangom’pulumutsa munthu kuti asalandire chilango koma kumadzetsanso chitetezo.​—Aroma 13:1-7; Aefeso 5:21-25; 6:5-8.

      Achinyamata omwe samvera olamulira kaŵirikaŵiri sagwirizana ndi ena. Mosiyana ndi zimenezi, phunziro la kumvera lolandiridwa paubwana lingakhale lopindulitsa kwa moyo wonse wa munthu. Ndi mwayi waukulu kwambiri kuphunzira kumvera paubwana!

  • Kumvera—Kodi Ndi Phunziro Lofunika Paubwana?
    Nsanja ya Olonda—2001 | April 1
    • Kumbukirani kuti, malinga ndi momwe mtumwi Paulo analembera, lamulo la kumvera makolo lili ndi lonjezo la mbali ziŵiri, lomwe ndi ‘kuti kukhale bwino ndi iŵe ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaitali padziko.’ Chitsimikizo cha lonjezo limeneli timachipeza pa Miyambo 3:1, 2: “Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.” Mphoto yaikulu ya anthu omvera ndiyo kukhala pa unansi ndi Yehova lerolino ndiponso moyo wosatha m’dziko latsopano la mtendere.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena