-
Kulera Ana M’maleredwe a MulunguGalamukani!—2004 | November 8
-
-
Tanthauzo Lenileni la Kulera Mwana
Baibulo limafotokoza bwinobwino udindo wa makolo wolera ana awo. Mwachitsanzo, lemba la Aefeso 6:4 limati: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Lemba limeneli likutchula makamaka atate kuti ndi amene ayenera kutsogolera pa ntchito yolera ana. Komabe, amayi amathandizana ndi amuna awo pantchito imeneyi.
Mawu oyambirira a Chigiriki amene anawamasulira kuti “m’maleredwe” pa Aefeso 6:4 amaphatikizapo zambiri osati kuphunzitsa, kulangiza, ndi kudziŵitsa kokha. Amaphatikizaponso kudzudzula, kuwongolera, ndi kulanga. Choncho kulera ana kumaphatikizapo kuwalanga komanso kuwaphunzitsa zinthu zonse zimene amafunikira kuti akule bwino. Koma kodi makolo angatani kuti asakwiyitse ana awo?
Khalani Womvetsetsa
Kodi n’chiyani chimene chimakwiyitsa mwana? Tayerekezerani izi. Muli ndi mnzanu wa kuntchito amene sachedwa kupsa mtima ndiponso ndi wosaleza mtima. Palibe chimene amakonda mwa inu. Amaoneka kuti sasangalala ndi chilichonse chimene mumanena ndi kuchita. Nthaŵi zambiri mukagwira ntchito amati simunaigwire bwino ndipo amakuchititsani kumva kuti ndinu munthu wolephera. Kodi zimenezo sizingakukwiyitseni ndi kukugwetsani ulesi?
Zimenezo zingachitikenso kwa mwana ngati makolo ake nthaŵi zonse amangokhalira kumudzudzula ndi kumuwongolera mokwiya. N’zoona kuti ana amafunika kuwawongolera nthaŵi ndi nthaŵi ndiponso kuti makolo anapatsidwa mphamvu yochita zimenezo m’Baibulo. Komabe, kukwiyitsa mwana chifukwa chomuchitira zinthu mwankhanza ndiponso mopanda chikondi kungamuvulaze m’maganizo, pa moyo wake wauzimu, ndiponso thupi lake.
-
-
Kulera Ana M’maleredwe a MulunguGalamukani!—2004 | November 8
-
-
[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]
“CHILANGIZO CHA AMBUYE”
Lemba la Aefeso 6:4 limanena za “chilangizo cha Ambuye.” Mawu oyambirira a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chilangizo,” m’mabaibulo ena anawamasulira kuti “kalingaliridwe,” “kuchenjeza,” ndi “uphungu.” Mawu onseŵa akusonyeza kuti mabanja ayenera kuchita zambiri osati kungoŵerenga Baibulo kapena mabuku ofotokoza za m’Baibulo nthaŵi ndi nthaŵi basi. Makolo ayenera kuonetsetsa kuti ana awo akumvetsa bwino tanthauzo la Mawu a Mulungu, akumvetsa kufunika komvera, ndiponso akumvetsa mmene Yehova amawakondera, ndi mmene amawatetezera.
Kodi angachite bwanji zimenezi? Judy, mayi wa ana atatu, anaona kufunika kochita zambiri m’malo momangokhalira kukumbutsa ana ake mfundo za Mulungu. “Ndinaona kuti sankasangalala ndikamangowauza zinthu zimodzimodzi m’njira yomweyomweyo nthaŵi zonse. Ndinayamba kufunafuna njira zatsopano zowaphunzitsira. Njira imodzi yomwe ndinatsatira inali yofufuza nkhani m’magazini a Galamukani! zimene zinkafotokoza zinthu zomwezo m’njira ina. Choncho ndinaphunzira kukumbutsa ana anga zinthu zimene ankafunikira kudziŵa popanda kuwakwiyitsa.”
Angelo, amene banja lake linakumana ndi mavuto aakulu, akufotokoza mmene anaphunzitsira ana ake aakazi anayi kusinkhasinkha za Mawu a Mulungu. Iye akuti: “Tinkaŵerengera limodzi mavesi a m’Baibulo, ndiyeno ndinkasankhapo mawu ena n’kufotokoza mmene ankagwirizanirana ndi zimene zinali kuchitika pa moyo wawo. Kenaka, akamaŵerenga okha Baibulo, ndinkawaona akuganiza kwambiri, akusinkhasinkha za tanthauzo la zimene ankaŵerengazo kwa iwo.”
-