Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 9/15 tsamba 3-6
  • Kusiyanitsa Zinthu N’kothandiza Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusiyanitsa Zinthu N’kothandiza Kwambiri
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE MUNGACHITE KUTI KUSIYANITSA ZINTHU KUKUTHANDIZENI
  • Kulitsani Luso la Kuphunzitsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • “Pitirizanibe Kuyenda Monga Ana a Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake
    Nsanja ya Olonda—2012
  • ‘Kwaniritsani Utumiki Wanu’
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 9/15 tsamba 3-6
[Chithunzi patsamba 3]

Kusiyanitsa Zinthu N’kothandiza Kwambiri

Yesu anali Mphunzitsi wabwino kwambiri kuposa munthu aliyense padzikoli. Iye ankagwiritsa ntchito mafunso komanso mafanizo. Mwina inunso mumayesetsa kutsanzira kaphunzitsidwe kake. Koma kodi mukudziwa kuti iye ankakondanso kusiyanitsa zinthu pophunzitsa?

Anthu ambiri akamalankhula amakonda kusiyanitsa zinthu. Mwina nanunso mumachita zimenezi. Mwachitsanzo, mukhoza kunena kuti: “Aja anena kuti nthochi zonsezi ndi zakupsa koma izitu ndi zosapsa.” Kapena mukhoza kunena kuti: “Mtsikanayu ali wamng’ono anali wamantha koma pano ndi wolimba mtima.”

Posiyanitsa zinthu, timagwiritsa ntchito mawu ngati koma, m’malomwake, apo ayi kapena ngakhale zili choncho. Kusiyanitsa zinthu kumasangalatsa ndipo kumathandiza anthu kuti amvetse zimene tikunena.

N’zoona kuti m’zilankhulo zina anthu sakonda kugwiritsa ntchito mawu osiyanitsira zinthu, komabe tonsefe tiyenera kudziwa ubwino wa mawuwa. Tikutero chifukwa chakuti mawu amenewa amapezekapezeka m’Baibulo. Monga tanena kale, Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito mawu amenewa. Mwachitsanzo, iye ananena kuti: “Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale.” “Sindinabwere kudzaziwononga [Chilamulo kapena Zolemba za aneneri] koma kudzazikwaniritsa.” “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi . . . “ “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja, umutembenuzirenso linalo.”—Mat. 5:15, 17, 27, 28, 38, 39.

Mabuku ena a m’Baibulo amasiyanitsanso zinthu. Zimenezi zimathandiza kuti timvetse bwino mfundo inayake kapena tidziwe ubwino wochita zinthu zina. Ngati muli ndi ana, mungachite bwino kuganizira mawu akuti: “Inunso abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ngati mtumwi Paulo akanangolemba kuti atate (kapena amayi) ayenera kulera ana awo m’malangizo a Mulungu, zikanakhala zomveka komanso zoona. Koma mfundoyi imamveka bwino kwambiri chifukwa choti ananena kuti: ‘Musamawapsetse mtima, koma muwalere m’malangizo a Yehova.’

M’chaputala chomwechi, Paulo analembanso kuti: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi . . . makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aef. 6:12) Kalembedwe kameneka kamatithandiza kuona kuti tili pa nkhondo yoopsa kwabasi. Sikuti tikungolimbana ndi anthu koma makamu a mizimu yoipa.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI KUSIYANITSA ZINTHU KUKUTHANDIZENI

M’buku lomweli la Aefeso, timapeza malemba ena amene Paulo anagwiritsa ntchito mawu osiyanitsira zinthu. Tikamaganizira mawu amenewa timamvetsa bwino mfundo ya Paulo komanso kuona zoyenera kuchita.

Mungachite bwino kuwerenga tchati chimene chili patsamba 4 ndi 5 kuti muone malemba enanso a m’buku la Aefeso amene amasiyanitsa zinthu. Mukamawerenga malemba amenewa, muziganizira za moyo wanu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ineyo mtima wanga ndi wotani? Kodi nditakumana ndi zoterezi ndingatani? Kodi anthu ena angaone kuti ndili mbali iti pa zinthu ziwirizi?’ Ngati mukuona kuti pali zina zimene muyenera kusintha, yesetsani kusintha. Lolani kuti mawu osiyanitsa zinthuwo akuthandizeni.

Mwinanso mungagwiritse ntchito tchatichi pa kulambira kwanu kwa pabanja. Choyamba mungawerengere limodzi malemba onsewo. Kenako mmodzi anganene mbali yoyamba ya lemba lina, ndiyeno enawo ayese kukumbukira mfundo ya mbali yachiwiri ya lembalo. Zimenezi zingathandize kuti mukambirane mbali yachiwiriyo ndi kuona mmene mungaigwiritsire ntchito. Kukambirana mawu osiyanitsa zinthu m’njira imeneyi kungathandize ana ndi achikulire omwe kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

Ndani akukumbukira mbali yachiwiri?

Mukaona kufunika kwa mawu osiyanitsa zinthu mudzatha kuwazindikira mosavuta m’Baibulo, ndipo mudzaona kuti ndi othandiza mu utumiki. Mwachitsanzo, polalikira munganene kuti: “Anthu ambiri amanena kuti aliyense ali ndi mzimu umene suufa, koma onani zimene Mawu a Mulungu amanena.” Kapena pophunzira Baibulo ndi munthu, mungafunse kuti: “Anthu ambiri kwathu kuno amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu. Inu maganizo anu ndi otani? Koma kodi mukudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi?”

Apa taona kuti pali malemba ambiri amene amasiyanitsa zinthu ndipo angatithandize kuyenda m’njira ya Mulungu. Tingathenso kugwiritsa ntchito mawu osiyanitsa zinthu pothandiza anthu ena kuti adziwe mfundo za m’Baibulo.

Malemba Ena a M’buku la Aefeso Amene Amasiyanitsa Zinthu

Mungachite bwino kugwiritsa ntchito tchati chimenechi pochita Kulambira kwa Pabanja

“Tisakhalenso . . . otengeka kupita uku ndi uku ndi . . . chiphunzitso chonyenga cha anthu, mwa kuchenjera kwa anthu popeka mabodza.”​—4:14.

“Koma polankhula zoona, tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khristu.”​—4:15.

“[Anthu a mitundu ina] alinso mu mdima wa maganizo, . . . chifukwa cha . . . kukakala kwa mitima yawo.”​—4:18, 19.

“Koma inu simunaphunzire Khristu kukhala wotero, malinga ngati munamumvadi. Ndiponso, monga mmene choonadi chilili mwa Yesu, munaphunzitsidwa mwa iye.”​—4:20, 21.

“Simulinso anthu osadziwika kapena alendo m’dziko la eni.”​—2:19.

“Koma ndinu nzika zinzawo za oyerawo, ndipo ndinu a m’banja la Mulungu.”​—2:19.

“Wakubayo asabenso.”​—4:28.

“Koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino.”​—4:28.

“Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.”​—4:29.

“Koma alionse olimbikitsa.”​—4:29.

“Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.”​—4:31.

“Koma khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”​—4:32.

“Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.”​—5:3.

“M’malomwake, muziyamika Mulungu.”​—5:4.

“Poyamba munali mdima.”​—5:8.

“Koma tsopano ndinu kuwala mogwirizana ndi Ambuye.”​—5:8.

“Musamachite nawo ntchito zosapindulitsa za mu mdima.”​—5:11.

“M’malomwake, muzidzudzula ntchitozo.”​—5:11.

“Choncho samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru.”​—5:15.

“Koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—5:15, 16.

“Pa chifukwa chimenechi, lekani kukhala opanda nzeru.”​—5:17.

“Koma pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.”​—5:17.

“Musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa.”​—5:18.

“Koma khalanibe odzaza ndi mzimu.”​—5:18.

“[Khristu] alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zotero.”​—5:27.

“Koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.”​—5:27.

“Palibe munthu anadapo thupi lake.”​—5:29.

“Koma amalidyetsa ndi kulikonda, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.”​—5:29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena