Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/15 tsamba 17-22
  • Lolani Kudziletsa Kwanu Kukhalepo Nikusefukire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lolani Kudziletsa Kwanu Kukhalepo Nikusefukire
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kofunika Kwambiri Koma Kovuta
  • Kulamulira Maganizo Athu Opweteka
  • Maganizo Anu Opweteka Ndi Abale Anu
  • Nkotheka!
  • Kudziletsa—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kofunika Motero?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kukulitsa Chipatso cha Kudziletsa
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Wonjezerani Kudziletsa pa Chizindikiritso Chanu
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/15 tsamba 17-22

Lolani Kudziletsa Kwanu Kukhalepo Nikusefukire

“Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . kudziletsa.”​—2 PETRO 1:5, 6, NW.

1. Kodi ndipachochitika chachilendo chotani pamene Mkristu angapereke umboni?

YESU anati: “Adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala mboni ya kwa iwo.” (Mateyu 10:18) Ngati muitanidwa kukaonekera pamaso pa kazembe, woweruza, kapena prezidenti, kodi munganene za chiyani? Mwinamwake mungayambe ndi chifukwa chimene mwapitira kumeneko, mlandu umene mwapatsidwa. Mzimu wa Mulungu ukhoza kukuthandizani kuchita zimenezo. (Luka 12:11, 12) Koma kodi mungalingalire kukamba za kudziletsa? Kodi mumakuona kukhala mbali yofunika kwambiri muuthenga wathu Wachikristu?

2, 3. (a) Kodi zinachitika motani kuti Paulo anachitira umboni kwa Felike ndi Drusila? (b) Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kunali nkhani yoyenera kwa Paulo yoikamba mumkhalidwewo?

2 Talingalirani chitsanzo cha chochitika chenicheni. Mmodzi wa Mboni za Yehova anamangidwa ndi kukazengedwa mlandu. Pamene anapatsidwa mwaŵi wakulankhula, iye anafuna kufotokoza zikhulupiriro zake monga Mkristu, monga Mboni. Mukhoza kupenda cholembedwa chake ndipo mudzaona kuti iye anapereka umboni wogometsa ‘wonena za chilungamo ndi kudziletsa ndi chiweruziro chilinkudza.’ Tikunena za chokumana nacho cha mtumwi Paulo m’Kaisareya. Kumeneko kunali kufunsidwa mlandu koyamba. “Atapita masiku ena, anadza Felike ndi Drusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Kristu Yesu.” (Machitidwe 24:24) Mbiri yakale imasimba kuti Felike “anachita nkhanza ndi chilakolako chonyansa za mtundu uliwonse, akumalamulira ndi mphamvu yachifumu mwaukapolo wosautsa.” Iye anali atakwatirapo kaŵiri pamene ananyengeza Drusila kuti asudzule mwamuna wake (akumaswa lamulo la Mulungu) ndipo anakhala mkazi wake wachitatu. Mwinamwake anali iye mkaziyo amene anafuna kumva za chipembedzo chatsopano, Chikristu.

3 Paulo anapitiriza ‘kufotokoza za chilungamo, ndi kudziletsa, ndi chiweruziro chilinkudza.’ (Machitidwe 24:25) Zimenezi ziyenera kukhala zinaonetsa kusiyana kokhala pakati pa miyezo ya Mulugu ya chilungamo ndi nkhanza ndi kupanda chilungamo kwa Felike ndi Drusila. Mwinamwake Paulo anaganiza kuti akasonkhezera Felike kusonyeza chilungamo pamlandu wake. Koma kodi anatchuliranji za ‘kudziletsa ndi chiweruzo chilinkudza’? Okwatirana amakhalidwe oipa ameneŵa anafuna kudziŵa zimene ‘kukhulupirira Yesu Kristu’ kunaloŵetsamo. Chotero anafunikira kudziŵa kuti kumtsatira iye kumafuna kulamulira maganizo, mawu, ndi machitidwe, zimene kudziletsa kumatanthauza. Anthu onse ali ndi chodziyankhira kwa Mulungu kaamba ka kulingalira kwawo, mawu ndi machitidwe. Motero, chofunika kwambiri kuposa chiweruzo chilichonse cha Felike pamlandu wa Paulo chinali chiweruzo chimene kazembeyo ndi mkazi wake anayang’anizana nacho kwa Mulungu. (Machitidwe 17:30, 31; Aroma 14:10-12) Momvekera bwino, atamva uthenga wa Paulo, “Felike anagwidwa ndi mantha.”

Kofunika Kwambiri Koma Kovuta

4. Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kuli mbali yofunika ya Chikristu chowona?

4 Mtumwi Paulo anazindikira kuti kudziletsa kunali mbali yofunika kwambiri ya Chikristu. Mtumwi Petro, mmodzi wa atsamwali apamtima a Yesu, anatsimikiziranso zimenezi. Polembera awo odzakhala “oyanjana nawo umulungu” kumwamba, Petro anasonkhezera kusonyeza mikhalidwe imene inali yofunika, monga ngati chikhulupiriro, chikondi, ndi kudziletsa. Chifukwa chake, kudziletsa kunali koloŵetsedwamo m’lonjezo lotsimikizirika lakuti: “Ngati zinthu zimenezi zikhala mwa inu nizisefukira, zidzakutetezerani kuti musakhale ofooka kapena osabala zipatso m’chidziŵitso cholongosoka cha Ambuye wathu Yesu Kristu.”​—2 Petro 1:1, 4-8, NW.

5. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusamala kwambiri za kudziletsa?

5 Komabe, mumadziŵa kuti kungonena kuti tiyenera kusonyeza kudziletsa kumakhala kopepuka kuposa kukuchita m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Chifukwa chimodzi nchakuti kudziletsa sikowanda. Pa 2 Timoteo 3:1-5 Paulo anafotokoza mikhalidwe yamaganizo imene ikafalikira m’nthaŵi yathu, mu “masiku otsiriza.” Mkhalidwe umodzi umene ukawanda m’nyengo yathu ndiwo wakuti ambiri akakhala “osadziletsa.” Tikuona zimenezi kukhala zowona kulikonse, sichoncho nanga?

6. Kodi kupanda kudziletsa kumaonekera motani lerolino?

6 Anthu ambiri amakhulupirira kuti sikulakwa “kusonyeza maganizo opweteka kosadziletsa” kapena “kuzazuka kapenanso kukalipa kuti upume.” Lingaliro lawo limalimbikitsidwa ndi zimene amaona kwa anthu otchuka amene amaonekera kuti amanyalanyaza kudziletsa kwa mtundu uliwonse, amene amangochita malinga ndi mmene amverera. Tichitire chitsanzo: Ambiri amene amakonda akatswiri azamaseŵera akhala ozoloŵera kusonyeza mkwiyo, ngakhale kukhala achiwawa. Kodi simungakumbukire, mwa nkhani zoulutsidwa, zochitika za maseŵera pamene panabuka kuukirana ndi kumenyana kwankhalwe? Komabe, cholinga chathu sichakuti titaye nthaŵi yambiri tikukambitsirana zitsanzo za kusadziletsa. Mukhoza kundandalika mbali zambiri m’zimene tifunikira kusonyeza kudziletsa​—m’zakudya ndi zakumwa, makhalidwe athu kwa osiyana naye chiŵalo, ndi nthaŵi ndi ndalama zowonongera pa maseŵera. Koma m’malo mwakupenda mwachisawawa mbali zambiri zoterozo, tiyeni tipende mbali imodzi yaikulu mwa imene tiyenera kusonyeza kudziletsa.

Kulamulira Maganizo Athu Opweteka

7. Kodi ndimbali iti ya kudziletsa imene imafunikira chisamaliro chapadera?

7 Ambiri a ife takhala ndi chipambano m’kulamulira kapena kuletsa machitidwe athu. Sitimaba, kuchita chisembwere, kapena kupha; timadziŵa lamulo la Mulungu ponena za zolakwa zimenezi. Komabe, kodi tili achipambano motani m’kulamulira maganizo athu opweteka? M’kupita kwa nthaŵi, awo amene amalephera kukulitsa kudziletsa m’maganizo opweteka amalepheranso kudziletsa m’zochita zawo. Chotero, tiyeni tiyang’ane pa maganizo athu opweteka.

8. Kodi Yehova akufuna kuti tichitenji ponena za maganizo athu opweteka?

8 Yehova Mulungu samatiyembekezera kukhala monga maroboti, kotero kuti sitimasonyeza maganizo opweteka aliwonse. Kumanda a Lazaro, Yesu “anadzuma mumzimu navutika mwini.” Kenako “Yesu analira.” (Yohane 11:32-38) Iye anasonyeza maganizo opweteka a mtundu wina pamene, mwakudziletsa bwino lomwe m’machitidwe ake, anathamangitsa ochita malonda m’kachisi. (Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:14-17) Ophunzira ake okhulupirika anasonyeza maganizo amphamvu opweteka ndi akusangalala. (Luka 10:17; 24:41; Yohane 16:20-22; Machitidwe 11:23; 12:12-14; 20:36-38; 3 Yohane 4) Komabe, iwo anazindikira kufunika kwa kudziletsa kotero kuti maganizo awo opweteka sanawatsogolere kuuchimo. Lemba la Aefeso 4:26 limamveketsa chimenechi bwino lomwe kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiire.”

9. Kodi nchifukwa ninji kulamulira maganizo athu opweteka kuli kofunika kwambiri?

9 Pali upandu wakuti Mkristu angaonekere kukhala wosonyeza kudziletsa, pemene kwenikweni, maganizo ake opweteka akukula mosalamulirika. Kumbukirani chimene chinachitika pamene Mulungu anavomereza nsembe ya Abele: “Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake. Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake.” (Genesis 4:5-7) Kaini analephera kulamulira maganizo ake opweteka, amene anamchititsa kupha Abele. Maganizo opweteka osalamulirika anatsogolera ku kachitidwe kosalamulirika.

10. Kodi timaphunziranji pachitsanzo cha Hamani?

10 Talingaliraninso chitsanzo cha m’masiku a Moredekai ndi Estere. Nduna yotchedwa Hamani inakwiya kwambiri pamene Moredekai sanaigwadire. Pambuyo pake Hamani analingalira molakwa kuti zinthu zikamuyendera bwino. “Ndipo Hamani anatuluka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Moredekai ku chipata cha mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Moredekai. Koma Hamani anadziletsa, namuka kwawo.” (Estere 5:9, 10) Iye anafulumira kusangalala. Komabe anafulumiranso kukwiya atangoona munthu amene anadana naye. Kodi muganiza kuti pamene Baibulo limanena kuti Hamani “anadziletsa” limatanthauza kuti iye anali chitsanzo chabwino cha kudziletsa? Kutalitali. Panthaŵi imeneyo, Hamani analamulira machitidwe ake ndi kusaonetsa maganizo ake opweteka, koma analephera kulamulira mkwiyo wake wansanje. Maganizo ake opweteka anamchititsa kulinganiza chiwembu cha mbanda.

11. Mumpingo wa Filipi, kodi ndivuto lanji limene linalipo ndipo liyenera kukhala linachititsidwa ndi chiyani?

11 Mofananamo lerolino, kulephera kulamulira maganizo opweteka kungawononge Akristu kwambiri. ‘Koma,’ ena angaganize motero, ‘zimenezo sizingakhale vuto mumpingo.’ Koma zakhaladi vuto. Akristu aŵiri odzozedwa m’Filipi anali ndi vuto lalikulu pakati pawo, limene Baibulo silimatchula. Tayerekezerani kuti izi nzimene zinachitika: Euodiya anaitanira abale ena ndi alongo kuchakudya kapena kaphwando ka mayanjano. Suntuke sanaitanidwe, ndipo chimenecho chinampweteka. Mwinamwake nayenso anabwezera mwakusaitanira Euodiya kuchochitika chofananacho chimene analinganiza pambuyo pake. Ndiyeno onse aŵiri anayamba kufunirana zolakwa; m’kupita kwanthaŵi, analeka kulankhuzana. M’chochitika chonga chimenecho, kodi vuto lenileni lingakhale kusaitanirana kuchakudya? Ayi. Chimenecho chingangokhala choyambitsa chabe vutolo. Pamene alongo aŵiri odzozedwa ameneŵa analephera kulamulira maganizo awo opweteka, mbaliŵaliyo inakoleza thengo lonse. Vutolo linapitirizabe ndi kukula kwakuti mtumwi anafunikira kuloŵererapo.​—Afilipi 4:2, 3.

Maganizo Anu Opweteka Ndi Abale Anu

12. Kodi Mulungu akutipatsiranji uphungu wa pa Mlaliki 7:9?

12 Ndithudi, sikuli kopepuka kulamulira maganizo opweteka pamene munthu anyalanyazidwa, kukhumudwitsidwa, kapena kuchitiridwa mwatsankho. Yehova amadziŵa zimenezo, popeza kuti waona maunansi aumunthu kuyambira pachiyambi cha munthu. Mulungu amatilangiza kuti: “Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuŵa cha zitsiru.” (Mlaliki 7:9) Onani kuti Mulungu choyamba amasamala za maganizo osati machitidwe. (Miyambo 14:17; 16:32; Yakobo 1:19) Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndifunikira kuika chisamaliro chachikulu pakulamulira maganizo anga opweteka?’

13, 14. (a) M’dziko lino, kodi kulephera kulamulira maganizo opweteka kumachititsa chiyani? (b) Kodi nzinthu zotani zimene zingapangitse Akristu kukhala ndi maganizo audani?

13 Anthu ambiri m’dziko amene amalephera kulamulira maganizo awo opweteka amayamba chidani​—chamkwiyo, ngakhale chachiwawa kaamba ka kulakwa kwa wina kwenikweni kapena kongolingalira kochitidwa pa iwo kapena wachibale. Pamene maganizo opweteka akhala osalamulirika, akhoza kukhala ndi ziyambukiro zoipa kwa nthaŵi yaitali. (Yerekezerani ndi Genesis 34:1-7, 25-27; 49:5-7; 2 Samueli 2:17-23; 3:23-30; Miyambo 26:24-26.) Akristu mwachionekere, mosasamala kanthu za mtundu kapena fuko lawo, ayenera kuona nkhanza zoterozo ndi maudani kukhala zolakwa, zoipa zoyenera kuzipeŵa. (Levitiko 19:17) Kodi mumaona kupeŵa udani kukhala mbali ya kudziletsa kwanu kwa maganizo opweteka?

14 Monga momwe zinaliri kwa Euodiya ndi Suntuke, kulephera kulamulira maganizo opweteka kukhoza kutsogolera ku mavuto tsopano. Mlongo angaone kukhala wonyalanyazidwa posaitanidwa kuphwando laukwati. Kapena mwina anali mwana wake kapena msuwani wake amene sanaitanidwe. Kapena mwinamwake mbale anagula galimoto lakale kwa Mkristu mnzake, ndiyeno pasanapite nthaŵi nkufa. Chilichonse chimene chingakhale chifukwacho, zimenezo zingachititse maganizo opweteka, amene angakhale osalamulirika, ndipo oloŵetsedwamowo amakwiya. Kodi chingachitike nchiyani?

15. (a) Kodi nzotulukapo zotani zimene zakhalapo chifukwa cha maudani pakati pa Akristu? (b) Kodi ndiuphungu wa Baibulo uti umene umachenjeza za kusunga zakukhosi?

15 Ngati munthu wokwiyayo salimbikira kulamulira maganizo ake opweteka ndi kubwezeretsa mtendere ndi mbale wakeyo, padzakhala chidani. Zimachitika kuti Mboni ikana kugaŵiridwa ku Phunziro Labuku Lampingo lina chifukwa chakuti “samafuna” Mkristu wina kapena banja lina limene limapita kumeneko. Nzachisoni chotani nanga! Baibulo limanena kuti kumakhala kudzichititsa manyazi kwa Akristu kuperekana ku makhoti akudziko, koma kodi sikulinso kudzichititsa manyazi ngati tipeŵa mbale chifukwa cha kunyalanyazidwa kumene kunachitidwa pa ife kapena wachibale wathu? Kodi maganizo athu opweteka amasonyeza kuti timaika chibale patsogolo pa mtendere wathu ndi abale ndi alongo athu? Kodi timanena kuti tikakhala ofunitsitsa kufera mlongo wathu, chikhalirechobe maganizo athu opweteka amatilepheretsa kulankhula naye tsopano? (Yerekezerani ndi Yohane 15:13.) Mulungu akutiuza mosabisa kuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo.”​—Aroma 12:17-19; 1 Akorinto 6:7.

16. Kodi nchitsanzo chabwino chotani chimene Abrahamu anapereka m’kuchita ndi maganizo opweteka?

16 Njira yothandiza kulamulira maganizo opweteka ndiyo kubwezeretsa mtendere kapena kuthetsa chifukwa chochititsa kudandaula, m’malo mwakulola maganizo audani kupitiriza. Kumbukirani pamene malo anakhala ochepa kwa ziweto zambiri za Abrahamu ndi za Loti, ndipo antchito awo anayamba kukangana. Kodi Abrahamu analola maganizo ake opweteka kumgonjetsa? Kapena kodi anasonyeza kudziletsa? Mwanzeru, iye anapereka njira yothetsera vutolo mwamtendere; kuti aliyense wa iwo akhale ndi malo akeake. Ndipo anauza Loti kuyamba kusankha. Kutsimikizira kuti Abrahamu sanali ndi mkwiyo ndi kuti sanasunge chakukhosi, pambuyo pake anapita kunkhondo yolanditsa Loti.​—Genesis 13:5-12; 14:13-16.

17. Kodi ndimotani mmene Paulo ndi Barnaba analepherera pachochitika china, koma kodi nchiyani chinachitika pambuyo pake?

17 Tikhoza kuphunziranso kudziletsa mwa chochitika cha pakati pa Paulo ndi Barnaba. Atagwirira ntchito pamodzi kwa zaka zambiri, iwo anakangana ponena za kutenga Marko paulendo wawo. “Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnaba anatenga Marko, naloŵa m’ngalawa, nanka ku Kupro.” (Machitidwe 15:39) Kulephera kulamulira maganizo awo opweteka kwa amuna ameneŵa kuyenera kukhala chenjezo kwa ife. Ngati zinachitika kwa iwo, zikhoza kuchitika kwa ife. Komabe, iwo sanalole kusamvana kupitirizabe kapena chidani kukula. Cholembedwa chimatsimikizira kuti abalewo anakhozanso kulamulira maganizo awo opweteka ndiyeno pambuyo pake anagwirira ntchito pamodzi mwamtendere.​—Akolose 4:10; 2 Timoteo 4:11.

18. Ngati pakhala maganizo opweteka, kodi Mkristu mkulu msinkhu ayenera kuchitanji?

18 Tidziŵa kuti pangakhale maganizo opweteka, ndipo ngakhale maudani pakati pa anthu a Mulungu. Zimenezi zinalipo m’nthaŵi ya Ahebri ndi m’masiku a atumwi. Zachitikanso pakati pa atumiki a Yehova m’nthaŵi yathu, chifukwa chakuti tonsefe tili opanda ungwiro. (Yakobo 3:2) Yesu anafulumiza otsatira ake kuthetsa mavutowo mwamsanga pakati pa abale. (Mateyu 5:23-25) Koma kumakhala bwinopo kuŵatsekereza mwa kukulitsa kudziletsa kwathu. Ngati muona kuti mwanyalanyazidwa kapena mwakwiitsidwa ndi kanthu kakang’ono kamene mbale wanu kapena mlongo wanena, bwanji osalamulira maganizo anu opwetekawo ndi kungoiŵala? Kodi kulidi kofunikira kuti mpaka mukambitsirane ndi winayo, monga ngati kuti simungakhutiritsidwe kufikira atavomereza kuti ali wolakwa? Kodi mumalamulira maganizo anu opweteka kumlingo wotani?

Nkotheka!

19. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuti kukambitsirana kwathu kunali makamaka pakulamulira maganizo athu opweteka?

19 Takambitsirana makamaka za mbali imodzi ya kudziletsa, kulamulira maganizo athu opweteka. Ndipo imeneyo ndiyo mbali yofunika kwambiri chifukwa chakuti kulephera kulamulira maganizo athu kungatsogolere kukulephera kulamulira lilime lathu, zilakolako zathu zakugonana, zizolowezi zathu za kadyedwe, ndi mbali zina zambiri za moyo m’zimene tifunikira kusonyeza kudziletsa. (1 Akorinto 7:8, 9; Yakobo 3:5-10) Komabe, limbikani mtima popeza kuti mukhoza kuwongokera m’kudziletsa.

20. Kodi tingatsimikizire motani kuti kuwongokera kuli kothekera?

20 Yehova ali wofunitsitsa kutithandiza. Kodi tingatsimikizire motani zimenezo? Eya, kudziletsa kuli chimodzi cha zipatso za mzimu wake. (Agalatiya 5:22, 23) Chifukwa chake, mlingo umene timalimbikira kuti tiyenerere kulandira mzimu woyera kuchokera kwa Yehova ndi kusonyeza zipatso zake, ndiwo mlingo umene tidzakhala wokhoza kudziletsa. Tisaiŵale konse chitsimikiziro cha Yesu chakuti: “Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye?”​—Luka 11:13; 1 Yohane 5:14, 15.

21. Kodi ndinu wotsimikiza mtima kuchita chiyani mtsogolo ponena za kudziletsa ndi maganizo opweteka?

21 Musalingalire kuti kudzakhala kosavuta. Ndipo kungakhale kovutirapo kwambiri kwa ena amene analeredwa ndi anthu osalamulira maganizo awo opweteka, ndi kwa ena amtima wa pachala, kapena kwa ena amene sanayesepo kusonyeza kudziletsa. Kwa Mkristu woteroyo, kudziletsa ndi kukukulitsa kungakhale kovuta kwambiri. Komabe kuli kotheka. (1 Akorinto 9:24-27) Pamene tikuyandikira nthaŵi zonse kumapeto a dongosolo la zinthu lilipoli, zipsinjo ndi zotsendereza zidzawonjezereka. Tidzafunikira kudziletsa, osati kochepa koma kowonjezereka kwambiri! Pendani kudziletsa kwanu. Ngati muona mbali zimene mufunikira kuwongolera, limbikirani pa zimenezo. (Salmo 139:23, 24) Pemphani Mulungu mzimu wake wowonjezereka. Adzakumvani nadzakuthandizani kotero kuti kudziletsa kwanu kukhalepobe ndi kusefukira.​—2 Petro 1:5-8.

Mfundo Zoyenera Kukumbukira

◻ Kodi nchifukwa ninji kulamulira maganizo anu opweteka kuli kofunika kwambiri?

◻ Kodi mwaphunziranji pachitsanzo cha Hamani ndi cha Euodiya ndi Suntuke?

◻ Kodi mudzayesayesa kuchitanji mowona mtima ngati mulakwiridwa?

◻ Kodi kudziletsa kungakuthandizeni motani kupeŵa kusunga chidani chilichonse?

[Chithunzi patsamba 18]

Pamene anali pamaso pa Felike ndi Drusila, Paulo analankhula za chilungamo ndi kudziletsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena