“Mtendere wa Mulungu Wakupambana Chidziŵitso Chonse”
M’MBIRI yonse, atumiki okhulupirika a Mulungu akumana ndi nyengo za kuvutika malingaliro kwakukulu. Zimenezi zili choncho kwambiri chotani nanga lerolino, popeza kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa”! (2 Timoteo 3:1) Mtumwi Paulo analangiza Akristu kutaya nkhaŵa zawo pa Yehova kupyolera mwa pemphero. Ndi chotulukapo chotani? “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:7.
Kodi nchiyani chimene chili “mtendere wa Mulungu” umenewu? Ndicho bata limene limakhalapo chifukwa cha kukhala ndi unansi wapafupi ndi Mlengi. Unansi wotero umatipatsa chidaliro chakuti, mosasamala kanthu za mavuto athu, Yehova “sadzasiya anthu ake; sadzathaŵa awo amene ali ake.”—Salmo 94:14, Today’s English Version.
Zimenezi sizitanthauza kuti tapatulidwa pa mavuto. “Masautso a wolungama mtima achuluka,” analemba motero wamasalmo. (Salmo 34:19) Koma mtendere wa Mulungu ungadzetse chitonthozo. Motani?
Mtendere wa Mulungu ‘upambana chidziŵitso chonse,’ analemba motero Paulo—kapena monga momwe Concordant Version imanenera, uli “wopambana mkhalidwe uliwonse wa maganizo.” Nkhaŵa ingatichititse kukumana ndi malingaliro osiyanasiyana ovutitsa. (Mlaliki 7:7) Komabe, mtendere wa Mulungu ungatilimbitse, makamaka pamene tifunikira “ukulu woposa wamphamvu.”—2 Akorinto 4:7; 2 Timoteo 1:7.
Ndiponso, mtendere wa Mulungu ndiwo chitetezero. Ungathe ‘kusunga mitima yanu ndi maganizo anu,’ monga momwe Paulo analembera kwa Afilipi. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “sunga” ndi liwu lankhondo limene mwachionekere linasonkhezera chithunzithunzi cha m’maganizo cha alonda olonda usana ndi usiku. M’njira yofananayo, mtendere wa Mulungu ungachite monga mlonda wolonda kwa maola 24 wa mitima yathu ndi maganizo athu.—1 Akorinto 10:13; yerekezerani ndi Aefeso 4:26.
Polingalira za mavuto osautsa amene timayang’anizana nawo lerolino, kodi mtendere wa Mulungu suli kanthu kena kamene tiyenera kukayamikira?—Salmo 18:2, yerekezerani ndi Eksodo 40:38.