-
“Mtendere Ukhale Ndi Inu”Nsanja ya Olonda—1988 | February 15
-
-
4. Ndimotani mmene anthu a Yehova angasungirire mtendere wa maganizo ndi mtima m’nthaŵi zino zovuta?
4 Tikukhala m’nthaŵi ya mapeto, “m’nthaŵi zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1) Okwera pa akavalo onenedweratu mu Chivumbulutso akuyenda kupyola pa dziko lapansi—monga mmene mungawonere kuchokera ku nkhondo, kuperewera kwa chakudya, ndi imfa chifukwa cha matenda. (Chivumbulutso 6:3-8) Anthu a Yehova akuyambukiridwanso ndi mikhalidwe yowazinga iwo. Chotero ndimotani mmene mungasungire mtendere waumulungu wa m’maganizo ndi mtima? Mwa kukhala chifupi ndi magwero a akulu a chitonthozo ndi mtendere. Monga mmene nkhani yapitayi yasonyezera, ichi chimafunikira pemphero ndi pembedzero lobwerezabwereza. Mwanjira imeneyo “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
5. Nchifukwa ninji Paulo anali wotsimikizira kuti “mtendere wa Mulungu” ungachinjirize mitima yathu?
5 Mtumwi Paulo, yemwe analemba mawu amenewo, iyemwini anali atapirira matsoka ndi zovuta. Iye anaikidwapo m’ndende ndi kumenyedwa ndi Ayuda ndi Aroma. Iye anaponyedwa miyala ndi kusiidwa kuti afe. Kuyenda m’masiku amenewo kunali kuika moyo pangozi; Paulo anataika posweka chombo nthaŵi zitatu, ndipo kaŵirikaŵiri iye anali pa ngozi ya achifwamba. Iye anathera masiku ambiri osagona ndipo kaŵirikaŵiri anavutika ndi mphepo, njala, ndi ludzu. Kuwonjezera ku zonsezi, iye tsiku ndi tsiku anadzimva kukhala wa “chilabadiro cha mipingo yonse.” (2 Akorinto 11:24-28) Chotero Paulo anadziŵa kuchokera ku zokumana nazo zaumwini zochuluka mmene uliri wofunika “mtendere wa Mulungu” womwe ungachinjirize mitima yathu.
6. Nchifukwa ninji chiri chofunika kwambiri kukhazikitsa ndi kusunga chomangira chotentha, ndi chathithithi ndi Mlengi wathu?
6 “Mtendere wa Mulungu” ungalongosoledwe monga lingaliro la bata ndi kudekha, lowunikira unansi wabwino ndi Mulungu. Ichinso chiri chofunika kwambiri kaamba ka Akristu, makamaka pamene iwo ayang’anizana ndi chizunzo kapena chisautso. Nchifukwa ninji? Chabwino, tonsefe tiri opanda ungwiro; chotero, pamene tivutitsidwa ndi mavuto, kupsyinjika, chitsutso, kapena mitundu yosiyanasiyana ya zobweza m’mbuyo, mopepuka tingachite mantha. Chimenechi chingatsogolere ku kulephera kwathu kusunga umphumphu wathu. Zoterozo zingabweretse chitonzo pa dzina la Mulungu, zingatitaikiritse chiyanjo cha Yehova, ndipo chingatsogolere ku kutaya kwathu moyo wosatha. Chotero chiri chofunika chotani nanga kukalamira kupeza “mtendere wa Mulungu” womwe udzatithandiza ife kuyang’anizana ndi zitokoso zoterozo mwachipambano. Mtendere woterowo ndithudi uli umodzi wa ‘mphatso yabwino ndi chininkho changwiro’ choperekedwa ndi Atate wathu wa kumwamba.—Yakobo 1:17.
7, 8. (a) Ndi pa chiyani pamene “mtendere wa Mulungu” wazikidwa, ndipo ndimotani mmene iwo ‘umapambanira malingaliro’? (b) Ndimotani mmene mtendere woterowo unachitidwira chitsanzo m’nkhani ya mbale mmodzi wa ku Africa?
7 Mungakhale munawonapo kuti anthu ena amapyola m’moyo a bata ndi chidaliro. Kaŵirikaŵiri ichi chimachitika chifukwa cha kuthekera kwachibadwa, chisonkhezero cha banja, chuma, maphunziro, kapena nsonga zina zoterozo. “Mtendere wa Mulungu” uli wosiyana kotheratu. Iwo suli wozikidwa pa mikhalidwe yabwino, ndiponso suli chotulukapo cha kuthekera kwaumunthu kapena kulingalira. Uwo umachokera kwa Mulungu ndipo “umasunga maganizo onse.” Kalembedwe ka J. B. Phillips ka Afilipi 4:7 kali kakuti “mtendere wa Mulungu . . . umapitirira kumvetsetsa kwa munthu.” Anthu a kudziko kaŵirikaŵiri amadabwitsidwa panjira imene Akristu amayang’anizirana ndi mavuto a akulu, kupwetekedwa kwa kuthupi, kapena ngakhale imfa.
8 Chitsanzo chamakono cha ichi anali mmodzi wa Mboni za Yehova yemwe anali kutsogoza msonkhano Wachikristu m’dziko la ku Africa kumene Mboni, mokulira pa chisonkhezero cha Akatolika a kumaloko, zinasulizidwa kukhala zigaŵenga. Mwadzidzidzi, gulu la nkhondo la apolisi onyamula malupanga okonzekeretsedwa kale linawonekera. Iwo anatumiza akazi ndi ana kunyumba koma anayamba kumenya amunawo. Mboniyo ikukumbukira kuti: “Ndiribe mawu akulongosolera mtundu mu umene tinavutitsidwira. Mkulu wa apolisi wotsogolera analengeza mwapoyera kuti tidzamenyedwa kufikira imfa. Ndinalandira kumenyedwa koteroko ndi chibonga cha ndodo kotero kuti pambuyo pake ndinasanza mwazi kwa masiku 90. Koma kudera nkhaŵa kwanga kunali kaamba ka miyoyo ya anzanga, mu pemphero ndinafunsa Yehova kusamalira kaamba ka miyoyo ya awa, nkhosa zake,” onse omwe anapulumuka. Ndi chitsanzo chotani nanga cha kukhala wa bata m’nsautso yowopsya ndi cha kulingalira ena mwachikondi! Inde, Atate wathu wachikondi wakumwamba amayankha zopempha za atumiki ake okhulupirika, kuwapatsa iwo mtendere wake. Mmodzi wa asilikari odabwitsidwa m’nkhani imeneyo anachitira ndemanga kuti Mulungu wa Mboni “ayenera kukhala wowona.”
9. Ndi chotulukapo chotani chimene kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha pa ilo kungakhale nacho?
9 M’nthaŵi zino zovuta, Akristu ambiri ali ndi mavuto amene amawapangitsa iwo kudzimva okwiitsidwa ndi okhumudwitsidwa. Njira yabwino ya kusungira mtendere wa maganizo iri kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha pa ilo. Lingapatse wina mphamvu ndi kugamulapo kwa kupitirizabe ndi kuima nji. “Mawu a Mulungu ali amoyo amapereka mphamvu.”—Ahebri 4:12, NW.
10. Ndimotani mmene kukhala wokhoza kukumbukira malemba kungakhalire dalitso?
10 Komabe, bwanji ngati nsautso itipambana ife pamene Baibulo palibepo? Mwachitsanzo, Mkristu angagwidwe mwadzidzidzi ndi kumangidwa m’ndende wopanda Baibulo. M’chochitika chimenecho, likakhala dalitso lenileni kukhala wokhoza kukumbukira malemba onga ngati Afilipi 4:6, 7; Miyambo 3:5, 6; 1 Petro 5:6, 7; ndi Masalmo 23. Kodi inu simudzayamikira mozama kukhala wokhoza kukumbukira ndi kusinkhasinkha pa ndime zoterozo? M’malo a mdima andende, chingakhale ngati kuti Yehova iyemwini ali kulankhula ndi inu. Mawu a Mulungu angachiritse maganizo opwetekedwa, kulimbikitsa mitima yofooka, ndi kulowa m’malo chisautso cha maganizo ndi mtendere. (Onani Masalmo 119:165.) Inde, chiri chofunika kwambiri kuzamitsa malemba m’maganizo athu tsopano pamene tidakali ndi mwaŵi wa kuchita tero.
11. Ndimotani mmene mbale mu Netherlands anasonyezera chifuno kaamba ka chakudya chauzimu?
11 Arthur Winkler ali mmodzi amene anayamikira mozama Baibulo, makamaka mkati mwa kulamulira kwa chiNazi mu Netherlands, pamene Mboni zinayenera kuchita ntchito yawo ya Chikristu mobisa. A Gestapo anakhala akufunafuna kaamba ka Mbale Winkler. Pamene iwo pomalizira anamgwira iye, anayesera kumupanga iye kuti agonjere koma analephera. Iwo kenaka anamumenya iye kufikira atakomoka. Ndi mano ake atachotsedwa, chibwano cha m’munsi chitagululidwa, ndipo thupi lake litamenyedwa ali wamaliseke, iye anaikidwa m’ndende ya mdima. Koma wolindirira wake anali womvera chifundo ndi waubwenzi. Mbale Winkler anafuna chitsogozo cha Yehova m’pemphero. Iye anadzimvanso wosowa mozama kaamba ka chakudya chauzimu ndipo anapempha wolindirirayo kaamba ka thandizo. Pambuyo pake, chitseko cha kundende chinatsegulidwa, ndipo Baibulo linaponyeredwa mkatimo. “Chinali chimwemwe chotani nanga,” akukumbukira Mbale Winkler, “tsiku lirilonse kusangalala ndi mawu otonthoza a chowonadi . . . Ndinadzimva inemwini ndikupeza mphamvu mwauzimu.”a
Mtendere Waumulungu Udzakuchinjirizani
12. Nchifukwa ninji pali chifuno chapadera kwa ife kuchinjiriza mitima yathu ndi mphamvu zathu za kulingalira?
12 Yehova akulonjeza kuti mtendere wake “Udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afilipi 4:7) Ichi chiri chofunika koposa! Mtima uli maziko a zisonkhezero ndi malingaliro. M’masiku ano otsiriza, mitima yathu ingafooketsedwe mopepuka ndi mantha kapena kudera nkhaŵa, kapena kutinyenga ife kuti tichite cholakwa. Dongosolo la chisawawa la moyo likuipiraipirabe mofulumira. Tiyenera kudzichinjiriza mokhazikika. Kuwonjezera ku kufuna mitima ya mphamvu, tiyeneranso kukhala ndi “mphamvu zathu za kulingalira” zitalimbikitsidwa ndi kutsogozedwa ndi Mulungu kupyolera m’Mawu ake ndi mpingo wake.
13. Ndi mapindu otani amene angabwere kuchokera ku kuchinjiriza mphamvu zathu za kulingalira?
13 Mogwirizana ndi W. E. Vine, liwu la Chigriki noʹe·ma (lolembedwa monga “mphamvu za maganizo”) liri ndi lingaliro la “chifuno” kapena “chida.” (An Expository Dictionary of New Testament Words) Chotero, mtendere wa Mulungu ungalimbikitse chifuno chathu cha Chikristu ndi kutichinjiriza ife motsutsana ndi chikhoterero china chirichonse cha kufooketsa kapena kusintha malingaliro athu popanda chifukwa chenicheni. Chotero chokhumudwitsa kapena mavuto sizidzatha kutifooketsa ife mopepuka. Mwachitsanzo, ngati tapanga chifuno cha kutumikira Yehova m’thayo lina lake lapadera, monga ngati kukhala mtumiki wa chipainiya wokhazikika kapena kupita kukatumikira kumene atumiki akufunika kwambiri, “mtendere wa Mulungu” udzakhala thandizo lokulira kwa ife m’kuwumirira kulinga ku chonulirapo chimenecho. (Yerekezani ndi Luka 1:3; Machitidwe 15:36; 19:21; Aroma 15:22-24, 28; 1 Atesalonika 2:1, 18.) Kuti mulimbikitse mphamvu zanu za kulingalira mowonjezereka, perekani nthaŵi yokwanira kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kukhala ndi mayanjano Achikristu. Inu chotero mudzadyetsa malingaliro anu ndi mtima wanu ndi malingaliro oyera, omangilira. Kodi muli wokhoza kupereka nthaŵi yokwanira kudzilowetsa inu eni mu “zonena” zouziridwa ndi Mulungu? Kodi muyenera kuzipatsa izo chisamaliro chowonjezereka?
14. Ndi ku uphungu wouziridwa wotani umene tiyenera kupereka chilabadiro chosamalitsa, ndipo nchifukwa ninji?
14 Mungawone kuti ponse paŵiri mtima ndi maganizo, kapena mphamvu za kulingalira, zikuphatikizidwa m’kupeza ndi kupindula kuchokera ku “mtendere wa Mulungu.” Ichi chimasonyezedwa mu uphungu waumulunguwu: “Mwananga, tamvera mawu anga. Tchera makutu ku zonena zanga. Asachoke ku maso ako. Uwasunge mkati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa owapeza, nalamitsa thupi lawo lonse. Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga, pakuti magwero a moyo atulukamo.”—Miyambo 4:20-23.
15. Kodi ndi mbali yotani imene Yesu amaichita m’kukhala kwathu ndi “mtendere wa Mulungu”?
15 “Mtendere wa Mulungu” womwe umatulukapo kuchokera ku chomangira chotentha, chathithithi ndi Yehova umasungilira mitima yathu ndi mphamvu zathu za kulingalira “mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:7) Ndi mbali yotani imene Yesu ali nayo mu ichi? Paulo akulongosola kuti: “Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu. Amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m’nyengo ya pansi pano yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu.” (Agalatiya 1:3, 4) Inde, Yesu mwachikondi anapereka moyo wake kuti tikawomboledwe. (Mateyu 20:28) Chotero chiri “kupyolera mwa Kristu Yesu” mmene tingalandiridwe kwa Yehova monga atumiki ake odzipereka ndi kukhala mumkhalidwe wa kusangalala ndi mtendere waumulungu umene ungakhale chinjirizo lathu.
-
-
“Mtendere Ukhale Ndi Inu”Nsanja ya Olonda—1988 | February 15
-
-
20. Nchiyani chimene aliyense amene angachite cholakwa chachikulu ayenera kuchita?
20 Ngati wina aliyense akhala ndi liwongo la kuchita cholakwa chachikulu koma achibisa icho, iwo mwachiwonekera adzataya chivomerezo cha Yehova ndi “mtendere wa Mulungu” umene anali nawo. Iwo adzatayanso mtendere wawo wa maganizo. (Yerekezani ndi 2 Samueli 24:10; Mateyu 6:22, 23.) Mungawone, chotero, nchifukwa ninji chiri chofunika koposa kuti Mkristu aliyense yemwe wagwera m’cholakwa chachikulu achiwulule chimenecho kwa Yehova ndi kwa akulu achikondi, omwe angapititse patsogolo kuchiritsa kwauzimu. (Yesaya 1:18, 19; 32:1, 2; Yakobo 5:14, 15) Pamene munthu amene wataya kulinganizika kwake kwauzimu pamalo oterereka a chimo afunafuna thandizo kuchokera kwa abale achikulire, iye sadzapitiriza kukhala ndi chikumbumtima chovutitsidwa kapena kukhala wopanda mtendere waumulungu.
21. Ndi chifukwa chotani cha kuyamikira kozama kwa Yehova chimene tiri nacho lerolino, ndipo nchiyani chimene chiyenera kukhala kugamulapo kwathu?
21 Uli mwaŵi wotani nanga kukhala mmodzi wa Mboni zodzipereka za Yehova lerolino! Kuli konse kotizinga, dziko iri lausatana likusweka ndi kukhala malo osakazidwa. Ilo lidzapita posachedwapa. Anthu ambiri “akukomoka ndi mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza padziko lapansi.” Koma tingatukule mitu yathu chifukwa tikudziŵa kuti “chipulumutso chathu chayandikira.” (Luka 21:25-28) Kuti tisonyeze mmene tiriri oyamikira kwa Yehova kaamba ka “mtendere wake . . . womwe umapambana maganizo onse,” lolani kuti tichite zimene tingathe kutumikira mokhulupirika “Mulungu yemwe amapereka mtendere.”—Aroma 15:33; 1 Akorinto 15:58.
-