Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 15-20
  • Mmene Miseche Yovulaza Ingathetsedwere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Miseche Yovulaza Ingathetsedwere
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yamikirani Maganizo Anu Operekedwa ndi Mulungu
  • Lemekezani Mulungu ndi Mawu Ake
  • Mmene Pemphero Lingathandizire
  • Chikondi Chimathetsa Miseche
  • Ulemu Umagonjetsa Miseche
  • Ntchito Zabwino Zimachepetsa Miseche Yovulaza
  • Chenjerani ndi Miseche Yovulaza!
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kujeda—Nchiyani Chomwe Chiri Chivulazo mu Iko?
    Galamukani!—1989
  • Miseche Kodi Nchifukwa Ninji Imasangalatsa?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Ndingapewe Bwanji Miseche?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 15-20

Mmene Miseche Yovulaza Ingathetsedwere

“Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.”​—SALMO 141:3.

1. Kodi ubongo wathu woperekedwa ndi Mulungu uli ndi ukulu wotani?

YEHOVA anatipatsa ubongo, ndipo ngwodabwitsa chotani nanga! Bukhu lotchedwa The Incredible Machine limati: “Ngakhale makompyutala ocholoŵana koposa amene tingayerekezere ngosapangidwa mokwanira atayerekezeredwa ndi kucholoŵana kwapafupifupi kopanda malire ndi luso la kukhoza kusintha la ubongo wa munthu . . . Zizindikiro mamiliyoni ambiri zoyenda mofulumira mkati mwa ubongo wanu pa mphindi iriyonse zimanyamula mtolo wadzawoneni wa chidziŵitso. Zimabweretsa mauthenga onena za malo a mkati ndi akunja a thupi lanu . . . Pamene zizindikiro zina zichitika ndi kupenda chidziŵitsocho, zimatulutsa malingaliro akutiakuti, zikumbukiro, ziganizo, kapena zolinganiza zimene zimatsogolera ku chosankha. Pafupifupi mwadzidzidzi, zizindikiro zochokera ku ubongo wanu zimauza mbali zina za thupi lanu zofunikira kuchita . . . Pa nthaŵiyo ubongo wanu ukuyang’aniranso kapumidwe kanu, nsanganizo za mwazi wanu, kutentha ndi kuzizira, ndi zochitika zina zofunika popanda inu kuzindikira.”​—Tsamba 326.

2. Kodi ndi funso lotani limene tsopano lifunikira kupendedwa?

2 Ndithudi, mphatso yodabwitsa yotero yochokera kwa Mulungu siyenera kugwiritsiridwa ntchito monga chotengera chotairako zinyalala kapena kudzala. Komabe, tingathe kugwiritsira ntchito molakwa ubongo mwa kumvetsera ndi kufalitsa miseche yovulaza. Kodi tingapeŵe motani nkhani zotero ndi kuthandiza ena kupeŵa kuphatikizidwamo?

Yamikirani Maganizo Anu Operekedwa ndi Mulungu

3. Kodi nchifukwa ninji Mkristu wowona sangaphatikizidwe m’nkhani yovulaza?

3 Kuyamikira maganizo athu operekedwa ndi Mulungu kudzatithandiza kupeŵa kumvetsera miseche yovulaza ndi kusaifalitsa. Mzimu wa Yehova sungasonkhezere munthu aliyense kudzaza maganizo ake ndi malingaliro otero ndi kugwiritsira ntchito lilime lake kuvulaza munthu aliyense. M’malomwake, Mawu a Mulungu amati: “Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake.” (Yesaya 55:7) Maganizo a munthu woipa ngodzazidwa ndi ziganizo zoipa, ndipo iye amafulumira kusinjirira wolungamayo. Koma sitikanayembekezera konse mawu otero kuti achokere kwa awo oyamikira maganizo awo operekedwa ndi Mulungu.

4. Ngati tiyamikira ubongo wathu ndi luso lathu la kulankhula, kodi tidzagwiritsira ntchito motani maganizo athu ndi lilime lathu?

4 Kuyamikira koyenerera kudzatithandiza kupeŵa kugwiritsira ntchito maganizo athu ndi lilime kuthandizira thupi lathu lauchimo. M’malomwake, tidzasunga maganizo athu ndi kalankhulidwe pa muyezo wapamwamba. Tingathe kupeŵa miseche yovulaza mwa kudalira mwapemphero pa Uyo amene maganizo ake ali apamwamba kwambiri kuposa athu. Mtumwi Paulo anapereka uphungu wakuti: “Zinthu zirizonse zowona [osati zonama kapena zosinjirira], zirizonse zolemekezeka [osati zamkutu], zirizonse zolungama [osati zoipa ndi zovulaza] zirizonse zoyera [osati kusinjirira kodetsedwako kapena kunyumwira koipako], zirizonse zokongola [osati za udani ndi zonyozerana], zirizonse zimveka zokoma [osati zolalatira]; ngati kuli chokoma mtima china [osati kuipa] kapena chitamando [osati chotsutsidwa] china, zilingirireni izi.”​—Afilipi 4:8.

5. Kodi okhulupirira anzake anawona ndi kumva chiyani ponena za Paulo?

5 Paulo anawonjezera kuti: “Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuziwona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wamtendere adzakhala pamodzi ndi inu.” (Afilipi 4:9) Kodi nchiyani chimene ena adawona ndi kumva ponena za Paulo? Zinthu zimene zinali zoyera ndi zolimbikitsa mwauzimu. Iye sanadzaze makutu awo ndi miseche yaposachedwapa ponena za Lidiya kapena Timoteo. Mungathe kutsimikizira kuti Paulo sanamvetsere ndi kuwanditsa mphekesera zonena za akulu m’Yerusalemu.a Mwachiwonekere, kuchitira ulemu maganizo ake operekedwa ndi Mulungu kunathandiza Paulo kupeŵa kuphatikizidwa m’miseche yovulaza. Tidzatsanzira chitsanzo chake ngati tiyamikiradi maganizo ndi lilime zimene Yehova anatipatsa.

Lemekezani Mulungu ndi Mawu Ake

6, 7. (a) Kodi Yakobo anasonyeza motani ziyambukiro za lilime losalamulirika? (b) Kodi nchiyani chimene sichidzachitika ngati tilemekeza Mulungu ndi Mawu ake?

6 Kuchitira ulemu Mulungu ndi Mawu ake Opatulika wochokera mu mtima kudzatithandizanso kuthetsa miseche yovulaza. Ndithudi, ulemu wotero udzatisonkhezera kulabadira uphungu wa wophunzira Yakobo, amene anasonyeza ntchito ya lilime. (Yakobo 3:2-12) Ngati munthu ali wokhoza kulamulira lilime, akakhoza kulamulira thupi lake lonse, monga momwedi chogwirira m’kamwa mwa kavalo chingalamulirire choŵetacho. Monga momwedi kamoto kakang’ono kangayatsire nkhalango yonse, choteronso lilime laling’ono lingakhale moto umene umakoleza gudumu lamoyo. Munthu angathe kuŵeta nyama zakuthengo, mbalame, zinthu zokwawa, ndi zamoyo za m’nyanja, “koma lilime palibe munthu akhoza kulizolowetsa,” anatero Yakobo. Chikhalirechobe, zimenezo sindizo zodzikhululukira kusapangira kuyesayesa kuthetsa miseche yovulaza.

7 Yakobo ananenanso kuti lilime limatulutsa dalitso ndi temberero kuchokera mkamwa mmodzimodzimo. Zimenezi siziri zoyenera, pakuti kasupe wa madzi samatulutsa ponse paŵiri madzi abwino ndi owawa. Mtengo wa mkuyu sungatulutse zipatso za azitona, ndipo madzi amchere sangatulutse madzi abwino. Ndithudi, malinga ngati Akristu ali opanda ungwiro, lilime lidzakhala losalamulirika kotheratu. Zimenezi ziyenera kutipangitsa kukhala okoma mtima kwa otilakwira olapa, komabe kutero sikumapangitsa miseche yovulaza kukhala yolungama. Malinga ngati zidalira pa ife, kugwiritsidwa ntchito kovulaza kotero kwa lilime sikudzapitirizabe kuchitika ngati tilemekezadi Mulungu ndi Mawu ake.

Mmene Pemphero Lingathandizire

8. Kodi pemphero lingatithandize motani kuthetsa miseche yovulaza?

8 Chiyeso cha kumvetsera miseche yovulaza ndiyeno kuiwanditsa chingakhale champhamvu kwambiri. Chotero ngati inu munagonjera kale kuchiyeso choterocho, kodi simuyenera kupempha Mulungu kaamba ka chikhululukiro ndi chithandizo? Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Akristu amene amapemphera kwamphamphu kuti Mulungu asawasiye kuphatikizidwa m’nkhani yopereka chiyeso koma yoipa yotero sadzagonjera ku machitachita amenewa a Satana; adzawomboledwa kwa wosinjirira wamkulu.

9. Ngati tiyesedwa kusinjirira munthu wina, kodi tingapemphere motani?

9 Ngati tiyesedwa kuti tisinjirire munthu aliyense, tingapemphere kuti: “Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.” (Salmo 141:3) Tikakhoza kuwononga ziyembekezo zathu za moyo wamuyaya mwakugonjera kuchiyeso ndi kutsanzira Mdyerekezi monga wosinjirira wambanda, wa udani, ndi wabodza. (Yohane 8:44) Mtumwi Yohane adalemba kuti: “Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziŵa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.”​—1 Yohane 3:15.

Chikondi Chimathetsa Miseche

10. M’malo mwa kuchita miseche ponena za ena, kodi tiri nawo mangawa achiyani?

10 Tonsefe tiri ndi mangawa a kanthu kena kwa ena, koma sitiri ndi mangawa a udani umene umasonkhezera miseche yovulaza. “Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko,” analemba motero Paulo. (Aroma 13:8) Tiyenera kulipira mangawa amenewo tsiku lirilonse m’malo mwa kulankhula motsutsana ndi ena ndi kuwononga mbiri yawo. Ngati tinena kuti tikonda Yehova, sitingathe kusinjirira wolambira mnzathu, “pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuwona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuwona.”​—1 Yohane 4:20.

11. Kodi fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi lingatipatse motani mfundo za kuzilingalira ponena za miseche yovulaza?

11 Talingalirani fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. Anthu onga mbuzi anawuzidwa kuti zimene anachitira abale a Kristu zinaŵerengeredwa kukhala zitachitiridwa kwa iye. Kodi inu mukanachita miseche ponena za Kristu? Ngati simukanalankhula motsutsana ndi Mbuye wanu ndi Ambuye, musachitire abale ake odzozedwa mwanjirayo. Musachite cholakwa chochitidwa ndi mbuzi, zimene “zidzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse.” Ngati mukonda abale a Yesu, sonyezani mwa zimene mumanena ponena za iwo.​—Mateyu 25:31-46.

12. Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la Miyambo 16:2, ndipo kodi ndimotani mmene chingayambukirire maganizo athu, ntchito, ndi mawu?

12 Popeza kuti tonsefe ndife ochimwa ndipo tifunikira nsembe ya dipo la Yesu, ngati munthu wina anafuna kulankhula mawu osayenerera ponena za ife, akanapeza zambiri za kuzinena. (1 Yohane 2:1, 2) Ndithudi, ife tingalingalire kuti tikuchita bwino lomwe. “Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu.” Sikelo ya Mulungu sinalemerere mbali imodzi chifukwa cha kukondera kapena tsankho. (Miyambo 16:2; Machitidwe 10:34, 35) Iye amapima mzimu wathu, nawona mkhalidwe wathu ndi lingaliro zimene zimatisonkhezera kuganiza, kuchita, ndi kulankhula. Pamenepa, ndithudi, sitikanafuna kuti Mulungu apeze kuti tikudzilingalira molakwa kukhala woyera ndipo ena kukhala alitsiro ndi oyenera kuneneredwa mawu ovulaza. Mofanana ndi Yehova, tiyenera kukhala osasankha, achifundo, ndi achikondi.

13. (a) Kodi ndimotani mmene chenicheni chakuti “chikondi chiri choleza mtima ndi chachifundo” chingatithandizire kuthetsa miseche yovulaza? (b) Kodi nchiyani chimene chidzatitetezera kusalankhula motsutsana ndi munthu amene walandira mwaŵi wa utumiki umene ife tiribe?

13 Kugwiritsira ntchito zimene Paulo adanena pa 1 Akorinto 13:4-8 kungathe kutithandiza kuthetsa miseche yovulaza. Iye adalemba kuti: “Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima.” Mlongo wina amene akuvutika ndi chizunzo m’banja logawanika angalephere kutilonjera mwachimwemwe. Kapena ena angakhale osafulumirirapo mwakuthupi, mwinamwake chifukwa cha matenda. Kodi chikondi sichiyenera kutisonkhezera kuleza mtima ndi kukhala achifundo kwa anthu otero m’malo mwa kuwapanga minkhole ya miseche yosuliza? ‘Chikondi sichichita nsanje, sichidzikuza, sichidzitukumula.’ Motero, ngati Mkristu wina alandira mwaŵi wautumiki umene ife tiribe, chikondi chidzatitetezera kusalankhula motsutsana naye ndi kupereka lingaliro lakuti iye ngwosayenerera ntchitoyo. Chikondi chidzatitetezeranso kusadzitamandira ponena za zipambano zathu, nkhani zimene zikanalefula okhala ndi mwaŵi wocheperako.

14. Kodi palinso chiyani ponena za chikondi zimene zingayambukire zomwe tinena ponena za ena?

14 Paulo ananenanso kuti ‘chikondi sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsya mtima, kapena kulingalira zoipa.’ M’malo mwa kulankhula monyansa zinthu zosagwirizana ndi Chikristu, tiyenera kulola chikondi kutisonkhezera kulankhula bwino ponena za ena ndi kulingalira zabwino zawo. Kumatitetezera kukwiyitsidwa ndi kulankhula motsutsana ndi anthu kaamba ka zivulazo zenizeni kapena zongoyerekezera. Popeza ‘chikondi sichikondwera ndi chisalungamo koma ndi chowonadi,’ chimatitetezera pa kusaphatikizidwa m’miseche yovulaza ngakhale ponena za otsutsa amene akuchitiridwa mosalungama.

15. (a) Kodi tiyenera kuyambukiridwa motani ndi chenicheni chakuti ‘chikondi chimakhulupirira ndi kuyembekeza zinthu zonse’? (b) Kodi ndi mbali ziti zachikondi zimene zingatithandize kumamatira ku gulu la Yehova ngakhale ngati ena alankhula motsutsana nalo?

15 Chikondi ‘chikhulupirira ndi kuyembekeza zinthu zonse’ zopezedwa m’Mawu a Mulungu ndipo chimatisonkhezera kuyamikira chakudya chauzimu choperekedwa ndi kagulu ka ‘kapolo wokhulupirika,’ m’malo mwa kumvetsera ku mawu osinjirira a ampatuko abodza. (Mateyu 24:45-47; 1 Yohane 2:18-21) Popeza kuti ‘chikondi chipirira zinthu zonse ndipo sichimalephera konse,’ chimatithandizanso kukhalabe okhulupirika ku gulu la Mulungu ngakhale ngati “abale onyenga” kapena anthu ena alankhula motsutsana nalo kapena ziŵalo zake.​—Agalatiya 2:4.

Ulemu Umagonjetsa Miseche

16. Kodi Paulo anachitiridwa motani ndi abale onyenga m’Korinto?

16 Kuchitira ulemu okhulupirira anzathu nakonso kumathandiza kuthetsa miseche yovulaza. Popeza iwo ngovomerezeka kwa Mulungu, ife ndithudi sitiyenera kuwasinjirira. Tisakhale konse ofanana ndi “abale onyenga” amene Paulo anakumana nawo. Mosakaikira, iwo ananena zinthu zoipa ponena za iye. (2 Akorinto 11:26) Nawonso ampatuko ayenera kukhala atamsinjirira. (Yerekezani ndi Yuda 3, 4.) M’Korinto anthu ena adati: “Akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma mawonekedwe a thupi lake ngofoka, ndi mawu ake ngachabe.” (2 Akorinto 10:10) Anthu samanena mawu otero kwa anthu amene amawakonda.

17. Kodi ndi mawu amtundu wanji amene Diotrefe anali kulankhula ponena za mtumwi Yohane?

17 Talingalirani mtumwi Yohane, amene analankhulidwa mosayanja ndi Diotrefe. “Ndalemba kanthu kwa mpingo,” anatero Yohane, “komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu kwa iwo, satilandira ife. Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, za kunena zopanda pake pa ife ndi mawu oipa.” (3 Yohane 9, 10) Kunena zopanda pake zotero kunali nkhani yowopsya kwambiri, ndipo ngati tikumvetsera kapena kuwanditsa nkhani zofananazo lerolino, tiyenera kuleka kuchita motero mwamsanga ndithu.

18. Kodi Demetriyo anasiyana motani ndi Diotrefe, ndipo kodi kusiyana kumeneku kungayambukire motani mkhalidwe wathu?

18 Akumalimbikitsa kuchitira ulemu wolungamayo, Yohane anawuza Gayo kuti: “Usatsanza chiri choipa, komatu chimene chiri chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuwona Mulungu. Demetriyo, adamchitira umboni anthu onse, ndi chowonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziŵa kuti umboni wathu uli wowona.” (3 Yohane 1, 11, 12) Aliyense wa ife ayenera kudzifunsa kuti: Kodi ndine Diotrefe kazitapeyo, kapena kodi ndine Demetriyo wokhulupirika? Ngati tichitira ulemu okhulupirira anzathu, sitidzalankhula mawu owaneneza, tikumapereka kwa ena chifukwa cha kutiwonera kukhala akazitape.

19. Kodi abale onyenga anafunafuna motani kuipitsa mbiri ya C. T. Russell?

19 Abale onyenga sanali kokha m’zaka za zana loyamba. Mkati mwa ma 1890, anthu ena achabechabe osonkhana ndi gulu la Mulungu anayesa kutenga ulamuliro wa Watch Tower Society. Iwo anachita chiwembu motsutsana ndi Charles Taze Russell, akumafunafuna kuthetsa kukhala kwake prezidenti woyamba wa Sosaite. Pambuyo pa kubwatama kwapafupifupi zaka ziŵiri, chiwembucho chinaulika mu 1894. Kwakukulukulu zinenezo zonyenga zinasumikidwa pa kunamizira Russell kuti anali wosawona mtima mu bizinesi. Zina za zinenezo zazing’onozo zinasonyeza cholinga cha onenezawo​—kuipitsa mbiri ya C. T. Russell. Akristu opanda tsankhu anafufuza nkhanizo nampeza kukhala wolondola. Motero, chiŵembu ichi cha “kuwulutsitsa A Russell ndi ntchito yawo m’mlengalenga” chinalephera. Chotero, mofanana ndi Paulo, Mbale Russell anawukiridwa ndi abale onyenga, koma kuimbidwa mlandu uku kunadziŵika kukhala machenjera a Satana. Pambuyo pake achiŵembuwo analingaliridwa kukhala osayenerera kusangalala ndi mayanjano Achikristu.

Ntchito Zabwino Zimachepetsa Miseche Yovulaza

20. Kodi ndi liwongo lotani limene Paulo analipeza ndi akazi amasiye achicheperepo ena?

20 Paulo anadziŵa kuti kaŵirikaŵiri miseche yovulaza inali yogwirizana ndi kukhala manjalende, osati kuchita ntchito zabwino zochuluka. Iye sanakondwere kuti akazi amasiye ena achicheperepo adaphunzira “kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, anachita mwina ndi mwina, kulankhula zosayenera.” Kodi mankhwala ake anali chiyani? Kuchita ntchito zabwino. Chotero, Paulo adalemba kuti: “Chotero ndingakonde kuti achicheperepowo akwatiwe, nabale ana, nasunge nyumba, kuti asapatse mdaniyo mpata uliwonse wakulankhula molalata.”​—1 Timoteo 5:11-14, Byington.

21. Kodi 1 Akorinto 15:58 ali ndi chigwirizano chanji ndi kupeŵa misampha ya miseche yovulaza?

21 Ngati akazi ayang’anira banja, kuphunzitsa ana mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu, naphatikizidwa mu ntchito zina zoyenera, iwo adzakhala ndi nthaŵi yochepa ya kuchita ukazitape umene ungatsogolere ku miseche yovulaza. Nawonso amuna adzakhala ndi nthaŵi yocheperapo kaamba ka nkhani zotero ngati ali otanganitsidwa ndi ntchito zabwino. ‘Kuchuluka m’ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse’ kudzathandiza tonsefe kupeŵa misampha ya miseche yovulaza. (1 Akorinto 15:58) Makamaka kuphatikizidwa kwa mtima wonse mu uminisitala Wachikristu, misonkhano ya mpingo, ndi zochitika zina zaumulungu zidzachititsa maganizo athu kukhala pa zinthu zauzimu kotero kuti sitikukhala ochita miseche otanganitsidwa ndi oloŵerera m’nkhani za ena.

22. Kodi Miyambo 6:16-19 imanena chiyani ponena za mmene Mulungu amawonera osinjirira?

22 Ngati titanganitsidwa m’ntchito zaumulungu ndi kufunafuna kudalitsa ena mwauzimu, tidzakhala mabwenzi okhulupirika, osati onyamula zam’kutu osakhulupirika. (Miyambo 17:17) Ndipo ngati tipeŵa miseche yosakaza, tidzakhala ndi Bwenzi labwino koposa onse​—Yehova Mulungu. Tiyeni tikumbukire kuti zinthu zisanu ndi ziŵiri zonyansa kwa iye ndizo “maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira [zolinga] zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu; Mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.” (Miyambo 6:16-19) Akazitape amakuza zinthu ndi malovu ndi kuzipotoza, ndipo osinjirira ali ndi lilime lonyenga. Mawu awo amayendetsa mapazi a ofunitsitsa kunyamula zamkutu. Pafupifupi nthaŵi zonse, chotulukapo chimakhala mkangano. Koma ngati tida zimene Mulungu amada, tidzakana miseche yovulaza imene ingavulaze wosalakwa ndi kubweretsa chikondwerero chachikulu kwa wosinjirira wamkulu, Satana Mdyerekezi.

23. Ponena za mawu athu, kodi tingapangitse motani mtima wa Yehova kukondwera?

23 Chifukwa chake, tiyeni tipangitse mtima wa Yehova kukondwera. (Miyambo 27:11) Tiyeni tipeŵe mawu amene iye amada, tikane kumvetsera ku kusinjirira, ndi kuchita zothekera kuthetsa miseche yovulaza. Ndithudi, tingatero mwachithandizo cha Mulungu wathu woyera, Yehova.

[Mawu a M’munsi]

a Ngakhale lerolino sikukuvomerezedwa kumvetsera ndi kuwanditsa mphekesera wamba (zimene kaŵirikaŵiri ziribe maumboni alionse) ponena za zimene ziŵalo za Bungwe Lolamulira kapena oimira awo ayerekezeredwa kukhala atanena kapena kuchita.

Kodi Mukanayankha Bwanji?

◻ Kodi pemphero lingatithandize motani kupeŵa kusinjirira ena?

◻ Kodi kugwiritsira ntchito 1 Akorinto 13:4-8 kungatithandize motani kuthetsa miseche yovulaza?

◻ Kodi ndimotani mmene kudzichitira ulemu kungatithandizire kulaka chiyeso chirichonse cha kudyera miseche okhulupirira anzathu?

◻ Kodi 1 Akorinto 15:58 ali ndi kugwirizana kotani ndi kupeŵa misampha ya miseche yovulaza?

[Mawu a Chithunzi patsamba 17]

U.S. Forest Service photo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena