Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 3 tsamba 8-9
  • Muzizindikira Kuti Ena Amakuposani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzizindikira Kuti Ena Amakuposani
  • Galamukani!—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Limene Limakhalapo
  • Mfundo ya M’Baibulo
  • Zimene Mungachite
  • Mapeto a Tsankho
    Galamukani!—2004
  • Kodi Muli Ndi Mtima Watsankho?
    Galamukani!—2020
  • Kodi Tsankho Lidzatha Liti?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Tsankho Limayamba Bwanji?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 3 tsamba 8-9
Zithunzi: 1. Mwamuna ndi mkazi wake akufulumira ndipo zawanyansa kwambiri ataona mayi wina wosaona akuwadutsira kutsogolo. 2. Kenako, banja lomwe lija likusangalala kwambiri kuona mayi wosaona akuimba mwaluso ndi chida chake.

Muzizindikira Kuti Ena Amakuposani

Vuto Limene Limakhalapo

Kudzikonda kungachititse munthu kukhala watsankho. Munthu wodzikonda amadziona kuti ndi wofunika kwambiri kuposa anthu ena komanso amaona anthu osiyana ndi iyeyo kuti ndi otsalira. Aliyense akhoza kuyamba kukhala ndi maganizo amenewa. Buku lina linati: “Ngakhale kuti zimasiyanasiyana, koma anthu azikhalidwe zambiri amaona kuti moyo umene amakhala, zakudya zawo, zovala, zinthu zimene amakonda kuchita, zikhulupiriro zawo, mfundo zimene amayendera komanso zinthu zina, ndi zapamwamba kwambiri kuposa za anthu a zikhalidwe zina.” (Encyclopædia Britannica) Kodi tingatani kuti tichotse maganizo amenewa?

Mfundo ya M’Baibulo

Muzichita zinthu “modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”​—AFILIPI 2:3.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Kuti tipewe mtima wodzikuza, tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa. Tikakhala odzichepetsa timazindikira kuti pali zinthu zina zimene anthu azikhalidwe zina amachita bwino kuposa ifeyo. Si zoona kuti anthu achikhalidwe chinachake amachita bwino pa zinthu zonse.

Taganizirani chitsanzo cha Stefan. Iye anakulira m’dziko la Chikomyunizimu koma anasiya kuchitira tsankho anthu omwe amachokera m’mayiko amene satsatira Chikomyunizimu. Iye anati: “Zimene ndaona ndi zakuti kuona ena kukhala okuposa kumathandiza kuthetsa mtima watsankho. Ndimazindikira kuti sindingadziwe zonse, ndiye ndimaona kuti ndikhoza kuphunzira zinazake kwa munthu wina aliyense.”

Zimene Mungachite

Muziona zinthu moyenera komanso muzivomereza kuti nthawi zina mumalakwitsa. Muzivomerezanso kuti anthu ena amachita bwino kwambiri zinthu zimene inuyo mumalephera. Musamaganize kuti anthu onse a mtundu winawake ali ndi vuto lofanana.

M’malo mongothamangira kuganizira zolakwika zokhudza munthu wa mtundu winawake, mungachite bwino kudzifunsa kuti:

Muzivomereza kuti anthu ena amachita bwino kwambiri zinthu zimene inuyo mumalephera

  • ‘Kodi khalidwe limene silindisangalatsa mwa munthu ameneyu ndi loipadi kapena tangokhala kuti anthufe timachita zinthu mosiyana?’

  • ‘Kodi munthu ameneyu akhozanso kuona kuti ndili ndi makhalidwe enaake oipa?’

  • ‘Kodi munthu ameneyu amachita bwino zinthu ziti kuposa ineyo?’

Ngati mutayankha mafunso amenewa moona mtima, mukhoza kuthetsa mtima watsankho komanso mungayambe kuona makhalidwe abwino amene munthuyo ali nawo.

Zimene Zinachitikadi: Nelson (United States)

“Ndinakulira m’dera limene anthu ambiri ndi a mtundu umodzi komanso moyo wawo ndi wofanana. Koma ndili ndi zaka 19 ndinasamukira mumzinda waukulu komwe ndinakayamba kugwira ntchito pafakitale ina. Kumeneko ndinayamba kugwira ntchito komanso kukhala ndi anthu a mitundu, zikhalidwe komanso moyo wosiyanasiyana.

“Pamene ndinayamba kudziwana bwino ndi anthu amene ndinkagwira nawo ntchito, ndinapeza anzanga ocheza nawo. Kukhala ndi anthu amenewa kunandithandiza kuzindikira kuti mtundu wa munthu, chilankhulo chake komanso dziko limene amachokera sizingandithandize kudziwa ngati munthuyo ndi wolimbikira ntchito kapena wokhulupirika. Sizingandithandizenso kudziwa mmene amamvera mumtima mwake.

“Kenako ndinakwatira mkazi wochokera dziko lina komanso wamtundu wosiyana ndi wanga. Kwa ine zakhala zosangalatsa kwambiri kuphunzira kudya zakudya zosiyanasiyana komanso nyimbo zimene poyamba sindinkazidziwa. Zimene ndaphunzira pamoyo wanga ndi zakuti tonse timalakwitsa zinazake komanso tonse tili ndi makhalidwe abwino. Kunena zoona, panopa ndine munthu wabwino chifukwa chotengera makhalidwe abwino a anthu amene ndimasiyana nawo mtundu komanso chikhalidwe.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena