Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/1 tsamba 16-22
  • Akristu Onse Owona Ayenera Kukhala Alaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akristu Onse Owona Ayenera Kukhala Alaliki
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupita Patsogolo Chiyambire 1919
  • Chifukwa Chake Zakhala Zachipambano
  • Kuyesa Ena Monga Otiposa
  • Kufunitsitsa Kulepa Zoyenerera
  • Padakali Zambiri Zochita
  • ‘Chitani Ntchito ya Mlaliki wa Uthenga Wabwino’
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Dzanja la Yehova Linali Nawo”
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mboni za Yehova—Alaliki Enieni
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Ndani Amene Ali Alengezi Owona?
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/1 tsamba 16-22

Akristu Onse Owona Ayenera Kukhala Alaliki

“Chita ntchito ya mlaliki [kapena, mmishonale, NW, mawu amtsinde].”​—2 TIMOTEO 4:5.

1. Kodi nchiyani chinali mbiri yabwino imene inalalikidwa ndi alaliki m’zaka za zana loyamba?

KODI kumatanthauzanji lerolino kukhala mlaliki? Kodi ndinu mlaliki? Liwu lakuti “mlaliki” limachokera ku liwu Lachigiriki lakuti eu·ag·ge·li·stesʹ, limene limatanthuza “mlaliki wa mbiri yabwino.” Kuyambira pamene mpingo Wachikristu unakhazikitsidwa mu 33 C.E., mbiri yabwino Yachikristu inagogomezera njira ya Mulungu ya chipulumutso ndi kulengeza kuti Yesu Kristu akabweranso panthaŵi yamtsogolo kudzayambitsa ulamuliro wake wa Ufumu pa mtundu wa anthu.​—Mateyu 25:31, 32; 2 Timoteo 4:1; Ahebri 10:12, 13.

2. (a) Kodi uthenga wa mbiri yabwino walemeretsedwa motani m’tsiku lathu? (b) Kodi Ndithayo lotani limene liri pa Akristu owona onse lerolino?

2 Kuyambira 1914 kumka mtsogolo, umboni unayamba kuchuluka wakuti chizindikiro chimene Yesu anapereka cha kubweranso kwake ndi cha kukhalapo kwake kosawoneka chinali kukwaniritsidwa. (Mateyu 24:3-13, 33) Kachiŵirinso, mbiri yabwino ikaphatikizapo mawu akuti “ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:7, 31; Marko 1:14, 15) Ndithudi, nthaŵi inali itafika yakuti ulosi wa Yesu wolembedwa pa Mateyu 24:14 ukwaniritsidwe mwanjira yaikulu: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Chifukwa chake, kulalikira tsopano kumaphatikizapo kulengeza mwachangu Ufumu wokhazikitsidwawo wa Mulungu ndi madalitso amene udzabweretsa posachedwapa kwa anthu omvera. Akristu onse akulamulidwa kuchita ntchito imeneyi ndi “kupanga ophunzira.”​—Mateyu 28:19, 20; Chivumbulutso 22:17.

3. (a) Kodi liwu lakuti “mlaliki” liri ndi tanthauzo lina liti? (Wonani Insight on the Scriptures, Voliyamu 1, tsamba 770, danga 2, ndime 2.) (b) Kodi zimenezi zimadzutsa mafunso otani?

3 Kuwonjezera pakulalikira mbiri yabwino kwa onse, Baibulo limagwiritsira ntchito liwu lakuti “mlaliki” m’lingaliro lapadera kwa awo amene amasiya gawo lakwawo kukalalikira mbiri yabwino kumadera amene sanagwiridwemo ntchito chikhalire. M’zaka za zana loyamba, panali alaliki amishonale ambiri, monga Filipo, Paulo, Barnaba, Sila, ndi Timoteo. (Machitidwe 21:8; Aefeso 4:11) Koma bwanji ponena za nthaŵi yathu yapadera chiyambire 1914? Kodi anthu a Yehova lerolino adzipereka monga alaliki akumaloko ndi monga amishonale?

Kupita Patsogolo Chiyambire 1919

4, 5. Kodi panali ziyembekezo zotani za ntchito yolalikira mwamsanga pambuyo pa 1914?

4 Pamene Nkhondo Yadziko I inali pafupi kutha mu 1918, atumiki a Mulungu anayang’anizana ndi chitsutso chomakulakula chochokera kwa ampatulo ndi atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko ndi atsamwali awo andale zadziko. Kwenikweni, kulalikira kwa Akristu owona kunatsala pang’ono kulekekeratu mu June 1918 pamene akuluakulu otsogolera a Watch Tower Society mu United States anaweruzidwa zaka 20 m’ndende pazinenezo zonamizira. Kodi adani a Mulungu anapambana m’kuthetsa kulalikidwa kwa mbiri yabwino?

5 Mosayembekezereka, mu March 1919 akuluakulu a Sosaite anamasulidwa ndipo pambuyo pake anapezeka opanda mlandu pazinenezo zonamizirazo zimene zinawachititsa kuponyedwa m’ndende. Pokhala ndi ufulu wopezedwa watsopano, Akristu odzozedwa ameneŵa anazindikira kuti panali ntchito yochuluka yoti ichitidwe asanalandire mphotho yawo yakumwamba monga oloŵa nyumba mu Ufumu wa Mulungu.​—Aroma 8:17; 2 Timoteo 2:12; 4:18.

6. Kodi ntchito yakulalikira inapita patsogolo motani pakati pa 1919 ndi 1939?

6 Kalero mu 1919 opereka lipoti la kukhala kwawo ndi phande m’kufalitsa mbiri yabwino sanafike pa 4,000. M’zaka makumi aŵiri zotsatira, amuna angapo anadzipereka monga alaliki amishonale, ndipo ena anatumizidwa kumaiko a m’Afirika, Asia, ndi Ulaya. Podzafika mu 1939, pambuyo pazaka 20 zakulalikira Ufumu, Mboni za Yehova zinawonjezeka kufika oposa 73,000. Chiwonjezeko chapadera chimenechi, chofikiridwa mosasamala kanthu za chizunzo, chinafanana ndi zimene zinachitika m’zaka zoyambirira za mpingo Wachikristu.​—Machitidwe 6:7; 8:4, 14-17; 11:19-21.

7. M’chaka cha 47 C.E. ndi 1939, kodi ndimkhalidwe wofanana wotani umene unakhalapo wa ntchito yolalikira Yachikristu?

7 Komabe, Mboni za Yehova zochuluka panthaŵiyo zinali kwakukulukulu m’maiko Achiprotestanti olankhula Chingelezi. Kwenikweni, oposa 75 peresenti a olengeza Ufumu okwanira 73,000 anali mu Australia, Briteni, Canada, New Zealand, ndi United States. Monga momwe zinaliri pafupifupi 47 C.E., panafunikira chinthu cholimbikitsa alalikiwo kupereka chisamaliro chachikulu pamaiko adziko lapansi m’mene ntchito siinachitidwemo kwambiri.

8. Podzafika 1992, kodi Sukulu ya Gileadi inali itakwaniritsa chiyani?

8 Ziletso za m’nthaŵi yankhondo ndi mazunzo sizinathe kuletsa mzimu woyera wamphamvu wa Yehova kusonkhezera atumiki ake kukonzekera kaamba ka chiwonjezeko chokulirapo. Mu 1943, pamene Nkhondo Yadziko II inali pachimake, gulu la Mulungu linakhazikitsa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ndi cholinga chakufalitsa mbiri yabwino mokulira kwambiri. Pofika March 1992, sukuluyo inatumiza amishonale 6,517 ku maiko osiyanasiyana 171. Kuwonjezerapo, amuna anaphunzitsidwa kusamalira nthambi za Watch Tower Society m’maiko akutali. Pofika mu 1992 mwa ogwirizanitsa Komiti ya Nthambi 97, okwanira 75 anaphunzitsidwa ku Gileadi.

9. Kodi ndimaprogramu ophunzitsa otani amene athandiza kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira?

9 Kuwonjezera pa Sukulu ya Gileadi, maprogramu ena ophunzitsa akonzekeretsa anthu a Yehova kuwonjezereka ndi kuwongolera ntchito yawo yolalikira. Mwachitsanzo, Sukulu Yautumiki Wateokratiki imachitidwa m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi. Makonzedweŵa, limodzi ndi Msonkhano Wautumiki wa mlungu ndi mlungu, aphunzitsa mamiliyoni a ofalitsa Ufumu kukhala ogwira mtima muuminisitala wapoyera. Palinso Sukulu Yautumiki Waufumu, imene imaphunzitsa mopindulitsa akulu ndi atumiki otumikira kotero kuti asamalire bwinopo mipingo yomakulakulayo. Sukulu Yautumiki Waupainiya yathandiza alaliki anthaŵi zonse ambiri kukhala ogwira mtima koposerapo m’ntchito yawo yolalikira. Posachedwapa, Sukulu Yophunzitsa Aminisitala yachitidwa m’maiko osiyanasiyana kuthandiza atumiki otumikira ndi akulu osakwatira kukhala a Timoteo amakono.

10. Kodi nchiyani chakhala chotulukapo cha kuphunzitsa kwabwino konseko koperekedwa kupyolera m’gulu la Mulungu? (Phatikizanipo mawu a m’bokosi.)

10 Kodi nchiyani chakhala chotulukapo cha kuphunzitsa konseku? Mu 1991, Mboni za Yehova zinafikira chiŵerengero chapamwamba choposa mamiliyoni anayi a olengeza Ufumu okangalika m’maiko 212. Komabe, mosiyana ndi mkhalidwe wa mu 1939, oposa 70 peresenti a ameneŵa ali m’maiko Achikatolika, Chiorthodox, osakhala Achikristu, kapena maiko ena, kumene Chingelezi sichiri chinenero chachikulu.​—Wonani bokosi la “Chiwonjezeko Chiyambire 1939.”

Chifukwa Chake Zakhala Zachipambano

11. Kodi mtumwi Paulo anapereka kwa yani thamo la chipambano chake monga minisitala?

11 Mboni za Yehova sizimadzitama pakufutukuka kumeneku. Mmalomwake, zimawona ntchito yawo monga mmene mtumwi Paulo anachitira, monga momwe anafotokozera m’kalata yake kwa Akorinto. “Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa. Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa; Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.”​—1 Akorinto 3:5-7, 9.

12. (a) Kodi Mawu a Mulungu amachita mbali yanji m’kulalikira Kwachikristu kwachipambano? (b) Kodi ndani amene waikidwa monga Mutu wa mpingo Wachikristu, ndipo kodi ndinjira yofunika iti yosonyezera kugonjera kwathu ku umutu wake?

12 Sikokaikiritsa kuti kuwonjezeka kozizwitsa kwa Mboni za Yehova kuli kaamba ka dalitso la Mulungu. Iri ntchito ya Mulungu. Pozindikira mfundo imeneyi, izo mokhazikika zimayesayesa kuphunzira Mawu a Mulungu mosalekeza. Zonse zimene zimaphunzitsa m’ntchito yawo yolalikira zimachokera m’Baibulo. (1 Akorinto 4:6; 2 Timoteo 3:16) Chinthu china chochititsa chipambano m’kulalikira kwawo ndicho kuvomereza kwawo kotheratu Uyo amene Mulungu anamuika monga Mutu wa mpingo, Ambuye Yesu Kristu. (Aefeso 5:23) Akristu a m’zaka za zana loyamba anasonyeza zimenezi mwakugwirizana ndi awo oikidwa ndi Yesu monga atumwi. Amunaŵa, pamodzi ndi akulu ena a mpingo wa Yerusalemu, anapanga bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba. Ali kumwamba Ambuye Yesu Kristu anagwiritsira ntchito gulu limeneli la Akristu okula msinkhu kuthetsa mikangano ndi kupereka chitsogozo kuntchito yolalikira. Changu cha Paulo chakutsatira makonzedwe aumulungu ameneŵa chinatulukira m’ziwonjezeko m’mipingo imene anachezetsa. (Machitidwe 16:4, 5; Agalatiya 2:9) Mofananamo lerolino, mwakugwiritsitsa Mawu a Mulungu ndi kutsatira mwachangu chitsogozo chochokera ku Bungwe Lolamulira, chipambano nchotsimikizirika kwa alaliki Achikristu muuminisitala wawo.​—Tito 1:9; Ahebri 13:17.

Kuyesa Ena Monga Otiposa

13, 14. (a) Kodi mtumwi Paulo anapereka uphungu wotani monga kwalembedwa pa Afilipi 2:1-4? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukumbukira uphungu umenewu pamene tikukhala ndi phande m’ntchito yolalikira?

13 Mtumwi Paulo anasonyeza chikondi chopanda mpeni kumphasa kwa ofunafuna chowonadi ndipo sanasonyeze mzimu wodzikweza kapena tsankho la fuko. Chifukwa chake, iye anakhoza kupatsa uphungu okhulupirira anzake ‘kuyesa ena monga owaposa.’​—Afilipi 2:1-4.

14 Mofananamo, alaliki owona Achikristu lerolino sali ndi mzimu wodzikweza pamene akuchita ndi anthu a mafuko ndi ziyambi zosiyanasiyana. Mmodzi wa Mboni za Yehova wa ku United States, wogaŵiridwa kudzagwira ntchito monga mmishonale mu Afirika akunena kuti: “Ndingodziŵa kuti sitiri oposa ena. Mwina tiri ndi ndalama zambiri ndi chimene chimatchedwa maphunziro akusukulu, koma iwo [anthu akumakolo] ali ndi mikhalidwe imene imaposa yathu.”

15. Kodi ndimotani mmene awo ogaŵiridwa kukagwira ntchito m’maiko akutali angasonyezere ulemu woyenera kwa oyembekerezeredwa kukhala ophunzira?

15 Ndithudi, mwakusonyeza ulemu woyenera kwa amene tigaŵana nawo mbiri yabwino, tidzakupangitsa kukhala kosavuta kwa iwo kulandira uthenga wa Baibulo. Kumathandizanso pamene mlaliki mmishonale asonyeza kuti ali wachimwemwe kukhala pakati pa anthu amene wagaŵiridwa kuwathandiza. Mmishonale wachipambano yemwe wathera zaka 38 zapitazo m’Afirika akufotokoza kuti: “Ndimamva kukhutiritsidwa kozama mkati mwanga kuti kwathu nkunoko, ndipo aŵa a mpingo umene ndinagaŵiridwa ndiwo abale ndi alongo anga. Pamene ndibwerera ku Canada patchuthi, sindimamva kwenikweni kuti ndiri kwathu. Mlungu womalizira kapena kuposapo pang’ono ndiri ku Canada, ndimangolakalaka kubwerera. Ndimamva motero nthaŵi zonse. Ndimauza amene ndimaphunzira nawo Baibulo ndi abale ndi alongo mmene ndimakhalira wachimwemwe kuti ndabwereranso, ndipo amayamikira kuti ndimafuna kukhala nawo.”​—1 Atesalonika 2:8.

16, 17. (a) Kodi nchitokoso chotani chimene amishonale ambiri ndi alaliki akumaloko avomereza kotero kuti akhale ogwira mtima koposa muuminisitala wawo? (b) Kodi ndichokumana nacho chotani chimene mmishonale wina anakhala nacho chifukwa cha kulankhula chinenero chakumaloko?

16 Pamene apeza gulu lalikulu lolankhula chinenero chachilendo m’magawo akumakolo, ena achita kuyesayesa kwakuphunzira chinenerocho, mwakutero akumasonyeza kuti amalingalira ena kukhala oposa. “Kummwera kwa Afirika,” akutero mmishonale wina, “nthaŵi zina pamakhala malingaliro akukaikirana pakati pa anthu Akuda ndi Azungu. Koma kulankhula chinenero cha m’dzikomo mwamsanga kumachotsa malingaliroŵa.” Kulankhula chinenero cha awo amene tigaŵana nawo mbiri yabwino kumathandiza kwambiri kufikira mitima yawo. Kumafunikira kuyesayesa mwamphamvu ndi kudzichepetsa kosalekeza. Mmishonale m’dziko la ku Asia akufotokoza kuti: “Kuphophonya nthaŵi zonse ndi kumasekedwa kungakhale chiyeso. Kungawonekere kukhala kosavuta kungoleka.” Komabe, kukonda Mulungu ndi mnansi kunathandiza mmishonaleyu kupirira.​—Marko 12:30, 31.

17 Momvekera bwino, anthu amakondwa pamene mlendo amayesa kugaŵana nawo mbiri yabwino m’chinenero chawo. Nthaŵi zina zimatulukira m’madalitso osayembekezereka. Mmishonale wotumikira m’dziko la m’Afirika la Lesotho anali kulankhula m’Chisotho kwa mkazi wogwira nchito m’shopu ya makapeti ndi nsalu zina. Nduna yaboma yochokera ku dziko lina la m’Afirika inkayendera malowo ndipo inamva kukambitsiranako. Inadza pafupi ndi kumthokoza mkaziyo, amene anayamba kulankhula kwa nduna yabomayo m’chinenero chake. “Bwanji osafika [kudziko langa] ndi kugwira ntchito pakati pa anthu athu, popeza kuti mumadziŵanso Chiswahili?” anafunsa motero. Mwaluso, mmishonaleyo anayankha kuti: “Zimenezo zikakhala bwino kwambiri. Koma ndine mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo pakali pano ntchito yathu njoletsedwa ndi lamulo m’dziko mwanu.” “Chonde,” anayankha motero, “musaganize kuti tonsefe timatsutsa ntchito yanu. Ambiri a ife timayanja Mboni za Yehova. Mwinamwake tsiku lina mudzakhoza kuphunzitsa momasuka pakati pa anthu athu.” Nthaŵi ina pambuyo pake, mmishonaleyo anakondwa kumva kuti Mboni za Yehova zinapatsidwa ufulu wakulambira m’dziko limenelo.

Kufunitsitsa Kulepa Zoyenerera

18, 19. (a) Kodi ndimwanjira yofunika kwambiri yotani imene Paulo anayesayesera kutsanzira Mbuye wake, Yesu Kristu? (b) Simbani chokumana nacho (cha m’ndime kapena chanu) mukumasonyeza kufunika kwa kupeŵa chirichonse chokhumudwitsa anthu amene timagaŵana nawo mbiri yabwino.

18 Pamene mtumwi Paulo analemba kuti: “khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu,” anali atangolankhula kumene zakufunika kwa kupeŵa kukhumudwitsa ena, akumati: “Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse kuulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena mpingo wa Mulungu, monga inenso ndikondweretsa onse m’zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyinjiwo, kuti apulumutsidwe.”​—1 Akorinto 10:31-33; 11:1.

19 Alaliki onga Paul, amene ali ofunitsitsa kudzimana kuti apindulitse amene amawalalikira, amatuta madalitso. Mwachitsanzo, m’dziko lina la m’Afirika, amishonale okwatirana anapita ku hotela yakumaloko kuchakudya chokondwerera tsiku lawo laukwati. Poyamba analinganiza kugula vinyo ndi chakudya, popeza kuti kumwa zoledzeretsa kwachikatikati sikumaletsedwa m’Baibulo. (Salmo 104:15) Komano okwatiranaŵa anasankha kusatero kuwopera kuti kungakhumudwitse anthu akumaloko. “Panthaŵi ina pambuyo pake,” akukumbukira motero mwamunayo, “tinakumana ndi mwamuna amene anali wophika wamkulu m’hotela ija, ndi kuyamba naye phunziro Labaibulo. Pambuyo panthaŵi yaitali anatiwuza kuti: ‘Kodi mukukumbukira pamene munadza ku hotela kudzadya chakudya? Tonsefe tinali kukuwonererani tiri kumbuyo kwa chitseko cha kitchini. Mwawona nanga, amishonale a tchalitchi anatiuza kuti nkulakwa kwa ife kumwa. Komabe, pamene iwo abwera ku hotela, amagula vinyo momasuka. Chotero tinasankha kuti ngati inu mukagula vinyo, sitikakumvetserani pamene mubwera kudzatilalikira.’” Lerolino, wophika wamkulu ameneyo ndi ena amene ankagwira ntchito pahotelapo ali Mboni zobatizidwa.

Padakali Zambiri Zochita

20. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti tipirire monga alaliki achangu, ndipo ndimwaŵi wosangalatsa wotani umene ambiri akutenga?

20 Pamene mapeto a dongosolo ili la zinthu akufika mofulumira, ambiri akulakalakabe kumva mbiri yabwino, ndipo nkofunika mofulumira kuposa ndi kale lonse kuti Mkristu aliyense apirire monga mlaliki wokhulupirika. (Mateyu 24:13) Kodi mungawonjezere kukhala kwanu ndi phande m’ntchito imeneyi mwakukhala mlaliki m’lingaliro lapadera monga Filipo, Paulo, Barnaba, Sila, ndi Timoteo? Ambiri akuchita zofanana ndi zomwezo mwakuloŵa muupainiya ndi kudzipereka kukatumikira m’malo okhala ndi kusoŵa kokulirapo.

21. Kodi ndimotani mmene ‘khomo lalikulu lopita kuntchito’ latsegukira kwa anthu a Yehova?

21 Posachedwapa, minda yaikulu yolalikirako yatseguka m’maiko a m’Afirika, Asia, ndi Yuropu Wakummaŵa, kumene ntchito ya Mboni za Yehova kale inali yoletsedwa. Monga momwe zinachitikira kwa mtumwi Paulo, ‘khomo lalikulu lopita kuntchito latseguka’ kwa anthu a Yehova. (1 Akorinto 16:9) Mwachitsanzo, alaliki amishonale amene posachedwapa anafika m’dziko la Afirika la Mozambique satha kukwaniritsa unyinji wa anthu ofuna maphunziro Abaibulo. Ndife achimwemwe chotani nanga kuti ntchito ya Mboni za Yehova inaloledwa mwalamulo m’dzikolo kuyambira pa February 11, 1991!

22. Kaya gawo lathu limafoledwa bwino kapena ayi, kodi nchiyani chimene tonsefe tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita?

22 M’maiko amene nthaŵi zonse takhala ndi ufulu wakulambira, abale athu akusangalalanso ndi ziwonjezeko zopitirizabe. Inde, kulikonse kumene tikukhala, padakali ‘zochuluka m’ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Popeza kuti ziri choncho, tipitirizetu kugwiritsira ntchito mwanzeru nthaŵi yotsalayo pamene aliyense wa ife ‘akuchita ntchito ya mlaliki, kutsiriza kotheratu uminisitala wathu.’​—2 Timoteo 4:5; Aefeso 5:15, 16.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi mlaliki nchiyani?

◻ Kodi uthenga wa mbiri yabwino unalemeretsedwa motani pambuyo pa 1914?

◻ Kodi ntchito yolalikira yapita patsogolo motani chiyambire 1919?

◻ Kodi ndizinthu zazikulu ziti zimene zathandizira chipambano cha ntchito yolalikira?

[Bokosi patsamba 19]

Chiwonjezeko Chiyambire 1939

Talingalirani zitsanzo za m’makontinenti atatu kumene amishonale ophunzitsidwa ku Gileadi anatumizidwa. Kalero mu 1939 panali olengeza Ufumu 636 okha amene anachitira lipoti ku West Africa. Podzafika 1991 chiŵerengerochi chinawonjezereka kuposa 200,000 m’maiko 12 a ku West Africa. Amishonale athandiziranso chiwonjezeko chozizwitsa m’maiko a ku South America. Limodzi la iwo ndilo Brazil, limene linawonjezereka kuchokera pa olengeza Ufumu 114 mu 1939 kufika 335,039 mu April 1992. Panakhala chiwonjezeko chofananacho pambuyo pakufika kwa amishonale m’maiko a ku Asia. Mkati mwa Nkhondo Yadziko II, chiŵerengero chochepa cha Mboni za Yehova m’Japan chinazunzidwa mowopsa, ndipo ntchito yawo inaima. Ndiyeno, mu 1949, amishonale 13 anafika kukathandiza kulinganizanso ntchitoyo. M’chaka chautumiki chimenecho, ofalitsa akumaloko osakwanira khumi anachitira lipoti utumiki wakumunda m’Japan yense, pamene mu April 1992 chiwonkhetso chonse cha ofalitsa chinafika 167,370.

[Bokosi patsamba 21]

Chikristu Chadziko ndi Vuto la Chinenero

Amishonale ena a Chikristu Chadziko anachita kuyesayesa kwakuphunzira chilankhulo chachilendo, koma ambiri anayembekezera anthu akumakolo kulankhula chinenero chawo Chachizungu. Monga momwe Geoffrey Moorhouse akufotokozera m’bukhu lake la The Missionaries kuti:

“Vuto linali lakuti kudziŵa chinenero chakumaloko kaŵirikaŵiri kunawonedwa kukhala chabe njira yomasulirira Malemba. Panachitidwa kuyesayesa kwakung’ono chabe, kaya ndi anthuwo kapena ndi magulu owalemba ntchito, kutsimikizira kuti mmishonale akakhoza kulankhula kwa nzika yakumaloko m’chinenero cha eni dziko mwanjira yamyaa imene iyo yokha ikachititsa kumvetsetsa kozama pakati pa anthu aŵiri. Mmishonale aliyense ankaphunzira kulankhula kocholoŵanitsa mawu a chinenero chakumoloko . . . Kuposa apo, kulankhulana kunali kwakukulukulu m’Chingelezi chachilapalapa, kosonyeza lingaliro lakuti nzika ya m’Afirika inayenera kugonjera ku chinenero cha mlendo Wachingelezi. Moipitsitsa, zimenezi zinali chiwonetsero china cha kudzikweza kwaufuko.”

Mu 1992 School of Oriental and African Studies m’London inafalitsa lipoti pavuto la chinenero. “Tiganiza kuti,” linatero lipotilo, “mlingo wochepa wa amishonale wakukhoza kulankhula chinenero chakumaloko . . . ngwosayenera momvetsa chisoni ndipo ngakhale waupandu.”

Amishonale a Watch Tower Society nthaŵi zonse awona kuphunzira chinenero chakumaloko kukhala kofunikira, zimene zimasonyeza chifukwa chake akhala achipambano m’ntchito yaumishonale.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena