-
Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo LabwinoMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
3. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti abatizidwe?
Musanabatizidwe, muyenera kuphunzira zokhudza Yehova komanso kuyamba kumukhulupirira kwambiri. (Werengani Aheberi 11:6.) Mukapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova komanso kumukhulupirira, m’pamenenso mudzayambe kumukonda kwambiri. Kenako mudzayamba kufuna kulalikira zokhudza Yehova komanso kuchita zimene Iye amafuna pa moyo wanu. (2 Timoteyo 4:2; 1 Yohane 5:3) Munthu akangoyamba ‘kuyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti azimukondweretsa pa chilichonse,’ amasankha kupereka moyo wake kwa Mulungu kenako amabatizidwa.—Akolose 1:9, 10.a
-
-
Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo LabwinoMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
a Munthu ayenera kubatizidwanso ngakhale kuti anabatizidwa kale ku chipembedzo china. Tikutero chifukwa chipembedzocho sichinamuthandize kudziwa choonadi cha m’Baibulo.—Onani Machitidwe 19:1-5 ndi Phunziro 13.
-
-
Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
1. Kodi muyenera kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti mubatizidwe?
Kuti mubatizidwe, muyenera ‘kudziwa choonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti muyenera kudziwa yankho la funso lililonse limene anthu angafunse lokhudza Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale Akhristu amene anabatizidwa kalekale, amapitirizabe kuphunzira zinthu zina. (Akolose 1:9, 10) Komabe, kuti mubatizidwe mufunika kuyamba kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Akulu amumpingo adzakuthandizani kudziwa ngati mwadziwa zinthu zokwanira zokhudza Baibulo.
-