Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/15 tsamba 16-20
  • Khalani Oleza Mtima pa Onse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Oleza Mtima pa Onse
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhala Woleza Mtima Ndi Abale Athu
  • M’banja
  • Ndi Akunja
  • Chikhulupiriro ndi Chiyembekezo Zimathandiza m’Kusonyeza Kuleza Mtima
  • Pemphero, Kudzichepetsa, ndi Chikondi Zidzathandiza
  • Kukhala Oleza Mtima ndi Chimwemwe?
  • ‘Valani Kuleza Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Lingalirani Zitsanzo za Kuleza Mtima
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Yehova Ndi Mulungu Woleza Mtima
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuleza Mtima
    Imbirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/15 tsamba 16-20

Khalani Oleza Mtima pa Onse

‘Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima, chilikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.’​—1 ATESALONIKA 5:14.

1. Kodi nkuti ndipo pansi pa mikhalidwe yotani kumene Mboni za Yehova zasonyeza kuleza mtima?

MBONI zamakono za Yehova zapereka chitsanzo chabwino chotani nanga cha kuleza mtima! Iwo apirira zovuta zambiri ndi chizunzo m’maiko akale a Chinazi ndi Chifascist ndi m’maiko onga ngati Malawi kufikira tsopano. Omwe akusonyezanso kuleza mtima ndi awo amene akukhala m’mabanja ogawikana mwachipembedzo.

2. Kodi ndi mfundo ziŵiri ziti zimene zimapangitsa paradaiso wauzimu amene anthu a Yehova akusangalala naye?

2 Mosasamala kanthu za chizunzo ndi zovuta zimene amakumana nazo, anthu odzipereka a Yehova akhala akusangalala ndi madalitso a paradaiso wauzimu. Ndithudi, zenizeni zimasonyeza kuti Akristu odzozedwa anayamba kusangalala nayo m’chaka cha 1919. Kodi nchiyani chimene chimapangitsa paradaiso wauzimu ameneyu? Choyamba, mikhalidwe yaparadaiso imeneyi imakhalapo pakati pa anthu a Yehova chifukwa chakuti Mulungu wabwezeretsa atumiki ake odzozedwa ku “dziko” lawo, kapena mkhalidwe, wa kulambira kowona. (Yesaya 66:7, 8) Paradaiso wauzimuyu amapitanso patsogolo chifukwa chakuti aliyense amasonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu. Kuleza mtima nchimodzi cha zipatsozi. (Agalatiya 5:22, 23) Kufunika kwa mkhalidwe umenewu mogwirizana ndi paradaiso wathu wauzimu kungawoneke kuchokera ku ndemanga iyi yoperekedwa ndi William Barclay: “Sipangakhale kugwirizana Kwachikristu popanda makrothumia [kuleza mtima]. . . . Ndipo chifukwa chake​—nchakuti makrothumia ndiyo mkhalidwe waukulu wa Mulungu (Aroma 2.4; 9.22).” (A New Testament Wordbook, tsamba 84) Inde, kuleza mtima nkofunika motero!

Kukhala Woleza Mtima Ndi Abale Athu

3. Kodi Yesu anampatsa Petro phunziro lotani lonena za kuleza mtima?

3 Kukuwoneka kuti mtumwi Petro anali ndi vuto m’kusonyeza kuleza mtima, popeza kuti nthaŵi ina anamfunsa Yesu kuti: ‘Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? kufikira kasanu ndi kaŵiri kodi?’ Yesu anampatsa uphungu uwu: ‘Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.’ (Mateyu 18:21, 22) Kunena m’mawu ena, palibe polekezera ponena za nthaŵi imene tingapirirane ndi kukhululukira winawake amene watichimwira. Ndiiko komwe, sitingalingalire konse kuti munthu angayambe kuŵerengera kufikira nthaŵi 77! Komabe, kukhala wokhululukira motero kumafunikira kuleza mtima.

4. Kodi nchifukwa ninji akulu makamaka ayenera kukhala oleza mtima?

4 Palibe chikaikiro kuti akulu mumpingo ayenera kukhala opereka chitsanzo m’kusonyeza kuleza mtima kwa abale auzimu. Kupirira kwawo kungayesedwe chifukwa chakuti okhulupirira anzawo ena angakhale osasamala kapena amphwayi. Ena angakhale ochedwa kuwongolera zizoloŵezi zoipa. Akulu ayenera kukhala osamala kusakwiyitsidwa msanga kapena kukhumudwa ndi zofooka za abale ndi alongo awo Achikristu. Mmalomwake, abusa auzimu ameneŵa ayenera kukumbukira uphungu uwu: ‘Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.’​—Aroma 15:1.

5. Kodi tikhoza kulakanji ngati ndife oleza mtima?

5 Ndiponso, kusemphana kwamaumunthu kungabuke chifukwa cha zofooka zaumunthu ndi zophophonya. Chifukwa cha zolakwa kapena zizoloŵezi zachilendo, timayambukira abale athu moipa, kunena kwake titero, ndipo nawonso angatichitire motero. Chotero, uphungu uwu ngoyenerera chotani nanga: ‘Kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso.’ (Akolose 3:13) ‘Kulolerana wina ndi mnzake’ kumatanthauza kukhala woleza mtima, ngakhale kuti tingakhale ndi zifukwa zenizeni zodandaulira motsutsana ndi munthu wina. Sitiyenera kubwezera kapena kulanga mbale wathu, osati ngakhale kumuusira moyo.​—Yakobo 5:9.

6. Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima kuli kwanzeru?

6 Wokhala ndi tanthauzo lofananalo uli uphungu wa pa Aroma 12:19 uwu: ‘Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].’ ‘Kupatuka pamkwiyo’ kumatanthauza kulekereza, kapena kuleza mtima. Kusonyeza mkhalidwe umenewu nkwanzeru, popeza kuti kumatipindulitsa ife limodzi ndi ena. Ngati pabuka vuto, ife enife timamva bwinopo popeza kuti mwakukhala oleza mtima, sitimapangitsa vutolo kukula. Ndiponso munthu amene timamlezera mtima amamva bwinopo popeza kuti sitikumlanga kapena kumbwezera mwanjira ina. Nzosadabwitsa kuti Paulo anachenjeza Akristu anzake kuti ‘limbikitsani amantha mtima, chilikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse’!​—1 Atesalonika 5:14.

M’banja

7. Kodi nchifukwa ninji anthu okwatira afunikira kukhala oleza mtima?

7 Kwanenedwa bwino lomwe kuti ukwati wachimwemwe nkugwirizana kwa okhululukira abwino aŵiri. Kodi zimenezo zimatanthauzanji? Zimatanthauza kuti anthu okwatirana mwachimwemwe amakhala oleza mtima m’kuchitirana zinthu. Kaŵirikaŵiri anthu amakopeka kwa wina ndi mnzake chifukwa cha kawonedwe kawo ka zinthu kosiyana. Kusiyana kumeneku kungakhale kosangalatsa, komabe kungakhalenso magwero a kukangana kumene kumawonjezera zipsinjo ndi nkhaŵa zimene zimapangitsa Akristu okwatira kukhala ndi ‘chisautso m’thupi.’ (1 Akorinto 7:28) Mwachitsanzo, talingalirani kuti mwamuna sakonda kupereka tsatanetsatane wa zinthu kapena amakhala wosasamala kapena wauve. Ichi chingakhale chopereka chiyeso kwa mkazi wake. Koma ngati malingaliro operekedwa bwino sakuphula kanthu, mkaziyo angangofunikira kupirira ndi zofooka za mwamunayo mwakukhala woleza mtima.

8. Kodi nchifukwa ninji amuna okwatira angafunikire kukhala oleza mtima?

8 Kumbali ina, mkazi angamafune tsatanetsane nakhala wokhoterera kuvutitsa mwamuna wake. Izi zingatikumbutse lemba lakuti: “Kukhala patsindwi nkwabwinopo kuposa kukhala nyumba imodzi ndi mkazi wovutitsa.” (Miyambo 25:24, Today’s English Version) M’chochitika chotero, kuleza mtima nkofunika kuti tigwirizane ndi uphungu wa Paulo uwu: “Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.” (Akolose 3:19) Amuna amafunikiranso kukhala oleza mtima kuti alabadire uphungu wa mtumwi Petro uwu: ‘Momwemonso amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.’ (1 Petro 3:7) Nthaŵi zina zofooka za mkazi wake zingapereke chiyeso kwa mwamuna, koma kuleza mtima kudzamthandiza kuzilaka.

9. Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima kuli kofunika kwa makolo?

9 Makolo afunikira kukhala oleza mtima ngati ati akhale achipambano m’kulera ana awo. Ana angapange zophophonya zimodzimodzizo mobwerezabwereza. Iwo angawoneke kukhala ouma mutu kapena osaphunzira zinthu msanga ndipo angamapitirize kuika makolo awo pachiyeso. Pansi pa mikhalidwe yoteroyo, makolo Achikristu afunikira kulekereza, osapsa mtima kapena kunyanyuka koma kukhala abata pamene akumamatira ku malamulo amakhalidwe abwino olungama. Atate ayenera kukumbukira kuti nawonso panthaŵi ina anali achichepere ndipo anapanga zophophonya. Iwo afunikira kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo uwu: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”​—Akolose 3:21.

Ndi Akunja

10. Kodi tiyenera kuchita motani pamalo athu antchito, monga momwe kwawonedwera ndi chokumana nacho chotani?

10 Chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthu ndi dyera, mikhalidwe yoipa ingabuke pamalo antchito a Mkristu. Nchithu chanzeru kukhala wochenjera ndi kupirira zolakwazo kuti pakhale mtendere. Chomwe chimasonyeza mmene ichi chingakhalire chanzeru ndi chokumana nacho cha Mkristu yemwe anali mnkhole wa kusamvana kochititsidwa ndi wantchito mnzake wanjiru. Chifukwa chakuti mbaleyo sanaikulitse nkhaniyo koma anali woleza mtima, m’kupita kwanthaŵi iye anali wokhoza kuyambitsa phunziro Labaibulo ndi wantchito yemwe anali wovutitsayo.

11. Kodi ndiliti makamaka pamene tifunikira kukhala oleza mtima, ndipo nchifukwa ninji?

11 Anthu a Yehova ayenera kukhala oleza mtima kwenikweni pochitira umboni kwa awo okhala kunja kwa mpingo Wachikristu. Kaŵirikaŵiri, Akristu amakumana ndi mayankho amwano kapena achipongwe. Kodi chikakhala choyenera kapena chanzeru kuyankha mofananamo? Ayi, popeza kutero sikukasonyeza kuleza mtima. Njira yanzeru ikakhala kukumbukira ndi kutsatira mwambi wanzeru uwu: ‘Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.’​—Miyambo 15:1.

Chikhulupiriro ndi Chiyembekezo Zimathandiza m’Kusonyeza Kuleza Mtima

12, 13. Kodi ndimikhalidwe yotani imene idzatithandiza kukhala oleza mtima?

12 Kodi chingatithandize nchiyani kusonyeza kuleza mtima, kupirira mikhalidwe yopweteka? Chinthu choyamba ndi chikhulupiriro m’malonjezo a Mulungu. Tiyenera kumkhulupirira Mulugu. Malemba amati: ‘Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.’ (1 Akorinto 10:13) Kunena m’mawu ena, monga momwe mkhalakale wina ananenera kuti: “Ngati Mulungu achilola, ndidzachichita.” Inde, tingachichite mwakukhala woleza mtima.

13 Chogwirizana thithithi ndi chikhulupiriro ndicho chiyembekezo cha Ufumu wa Mulungu. Pamene udzalamulira dziko lonse lapansi, mikhalidwe yonse yoipa imene imatipangitsa kukhala opsinjika idzachotsedwa. Posonya ku zimenezi, wamasalmo Davide anati: ‘Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa. Pakuti ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.’ (Salmo 37:8, 9) Chiyembekezo chotsimikizirika chakuti posachedwapa Mulungu adzachotsa mikhalidwe yonse yopereka chiyeso chimatithandiza kukhala oleza mtima.

14. Kodi nchokumana nacho chotani chimene chikusonyeza kuti tiyenera kukhala oleza mtima kwa wamuukwati wosakhulupirira?

14 Kodi tiyenera kuchita motani ngati wamuukwati wosakhulupirira ativutitsa? Pitirizanibe kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka thandizo, ndipo pitirizani kuyembekeza kuti wotsutsayo adzakhala mlambiri wa Yehova. Mkazi wa Mkristu wina nthaŵi zina ankakana kumphikira chakudya ndi kumchapira zovala. Ankagwiritsira ntchito chinenero chotukwana, ndipo sankamulankhulitsa kwa masiku ambiri, ndipo anafikira pa kuyesayesa kumchitira matsenga mwaufiti. “Koma,” anatero mwamunayo, “nthaŵi iriyonse ndinatembenukira kwa Yehova m’pemphero, ndipo ndinadalira pa Iye kuti andithandize kukulitsa mkhalidwe wabwino wa kuleza mtima kuti ndisataye kulinganizika kwanga Kwachikristu. Ndinayembekezanso kuti tsiku lina mkhalidwe wamtima wa mkaziyo ukasinthe.” Pambuyo pa zaka 20 za kuchitiridwa koteroko, mkazi wake anayamba kusintha, ndipo mwamunayo anati: “Ndine woyamikira chotani nanga kwa Yehova kuti anandithandiza kukulitsa chipatso cha mzimu, kuleza mtima, chifukwa tsopano ndikuwona chotulukapo chake: Mkazi wanga wayamba kuyenda pamsewu wopita ku moyo!”

Pemphero, Kudzichepetsa, ndi Chikondi Zidzathandiza

15. Kodi nchifukwa ninji pemphero lingatithandize kukhala oleza mtima?

15 Pemphero ndithandizo lina lalikulu koposa posonyeza kuleza mtima. Paulo anafulumiza kuti: ‘Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 4:6, 7) Kumbukiraninso kulabadira uphungu uwu: “Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Salmo 55:22.

16. Kodi kudzichepetsa kungatithandize motani kukhala woleza mtima?

16 Kudzichepetsa ndithandizo lina lalikulu m’kukulitsa chipatso cha mzimu cha kuleza mtima. Munthu wonyada ngosaleza mtima. Iye amachimwiridwa msanga, amakwiya mofulumira, ndipo sangapirire kuchitiridwa koipa kulikonse. Zonsezi nzosemphana ndi kuleza mtima. Koma munthu wodzichepetsa samadzitenga mosamalitsa. Iye adzadikirira Yehova, monga momwe anachitira Davide pamene ankasakidwa ndi Mfumu Sauli ndi kutukwanidwa ndi Simeyi Wachibenjamini. (1 Samueli 24:4-6; 2 Samueli 16:5-13) Chotero, tiyenera kukhumba kuyenda ‘ndi chifatso, ndi kuwonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi.’ (Aefeso 4:2) Kuwonjezerapo, tiyenera ‘kudzichepetsa pamaso pa [Yehova, NW].’​—Yakobo 4:10.

17. Kodi nchifukwa ninji chikondi chidzatithandiza kukhala oleza mtima?

17 Chikondi chopanda dyera chimatithandiza kwenikweni kukhala oleza mtima. Ndithudi, ‘chikondi chikhala chilezere,’ popeza kuti chimatipangitsa kukhala ndi zikondwerero za ena. (1 Akorinto 13:4) Chikondi chimatitheketsa kukhala olingalira ena, kudziika ife eni mmalo mwa ena, kunena kwake titero. Ndiponso, chikondi chimatithandiza kukhala oleza mtima chifukwa ‘chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.’ (1 Akorinto 13:7, 8) Inde, monga momwe nyimbo Yaufumu nambala 108 m’bukhu la “Kuyimba ndi Kutsagana ndi Nyimbo za Malimba m’Mitima Mwanu” imasonyezera, chikondi:

“Chimaona zabwino.

Chimangira ubale.

Chikondi kwa olakwa.

Chifunira ubwino.”

Kukhala Oleza Mtima ndi Chimwemwe?

18. Kodi nzotheka motani kukhala woleza mtima ndi chimwemwe?

18 Paulo anapemphera kuti akhulupiriri anzake m’Kolose akadzazidwe ndi chidziŵitso cholongosoka cha chifuniro cha Mulungu kuti iwo akayende koyenera Yehova, kumkondweretsa, ndikubala zipatso m’ntchito iriyonse yabwino. Mwakutero iwo akakhala ‘olimbikitsidwa m’chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.’ (Akolose 1:9-11) Chikhalirechobe, kodi ndimotani mmene munthu angakhalire ‘woleza mtima ndi chimwemwe’? Chimenecho sichosemphana, popeza kuti kukhala ndi chimwemwe chotchulidwa m’Malemba sikuli kokha kudzimva wokondwera kapena wosangalala. Chipatso cha mzimu cha chimwemwe chimaphatikizapo chikhutiro chozama chakuchita chabwino pamaso pa Mulungu. Icho chirinso chisonyezero cha chiyembekezo chakulandira mphotho yolonjezedwa monga chotulukapo cha kukhala woleza mtima. Chimenecho ndicho chifukwa chake Yesu anati: ‘Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zirizonse chifukwa cha ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m’mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.’​—Mateyu 5:11, 12.

19. Kodi nzitsanzo zotani zimene zikusonyeza kuti nkotheka kukhala ponse paŵiri woleza mtima ndi wachimwemwe?

19 Yesu anali ndi chimwemwe choterocho. Ndithudi, ‘chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi.’ (Ahebri 12:2) Chimwemwe chimenecho chinamtheketsa Yesu kukhala woleza mtima. Mofananamo, talingalirani zimene zinachitika pamene atumwi anakwapulidwa nalamulidwa kuti ‘asalankhule kutchula dzina la Yesu.’ Iwo ‘anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. Ndipo masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’ (Machitidwe 5:40-42) Ha, nchitsanzo chabwino chotani nanga chotsimikizira kuti atsatiri a Kristu angakhale oleza mtima ndi chimwemwe!

20. Ngati timasonyeza kuleza mtima, kodi chimenechi chingayambukire motani unansi wathu ndi ena?

20 Ndithudi, Mawu a Mulungu amapereka uphungu wanzeru pamene amatichenjeza kusabwezera, kukhala olekereza pamene tikuyembekezera zabwino koposa​—inde, kukhala oleza mtima! Tifunikira pemphero lokhazikika ndipo chipatso cha mzimu wa Mulungu chimenechi kuti tikhale bwino ndi abale ndi alongo athu mumpingo, awo a m’banja mwathu, ndi anthu kumalo athu antchito, ndi anthu amene timakumana nawo muuminisitala Wachikristu. Ndipo kodi nchiyani chimene chingatithandize kusonyeza kuleza mtima? Chikhulupiriro, chiyembekezo, kudzichepetsa, chimwemwe, ndi chikondi. Zowonadi, titakhala ndi mikhalidwe imeneyo tidzakhala oleza mtima pa onse.

Kodi Mumakumbukira?

◻ Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima kuli kofunika m’kukhalamo kwathu m’paradaiso wauzimu?

◻ Kodi nchifukwa ninji akulu makamaka ayenera kukhala oleza mtima?

◻ Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima kuyenera kukulitsidwa ndi amuna ndi akazi okwatira?

◻ Kodi ndimikhalidwe ina iti imene idzatithandiza kukhala oleza mtima?

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi ndi uphungu wotani wochokera kwa Yesu umene unathandiza Petro kukhala woleza mtima?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena