Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/1 tsamba 4-7
  • Kusintha Chibadwa cha Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusintha Chibadwa cha Anthu
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Muzu wa Vutolo
  • Chibadwa cha Anthu Kusinthidwa!
  • “Mdyerekezi wa M’malemba”
  • Kubwezeretsedwa
  • “Mawu a Mulungu Ngamoyo Ndipo Amapereka Mphamvu”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mdani wa Moyo Wosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • “Mawu a Mulungu Ngamoyo”
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Mzimu Wochirikiza Dongosolo Lakale Liripo’li
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/1 tsamba 4-7

Kusintha Chibadwa cha Anthu

“ANTHU samangokhala ndimoyo wolimbana ndi mavuto,” anatero wanthanthi Bwana Isaiah Berlin. “Amakhala ndimoyo ndi zonulirapo zabwino, zaumwini ndi zaonse.” Koma kodi ndiangati amene angapeze “zonulirapo zabwino” zoterozo? Kaŵirikaŵiri kwambiri chibadwa cha anthu chimayedzamira kuchinthu choipa ndi chowononga.

Mwachitsanzo, m’Briteni, maupandu achiwawa posachedwapa anawirikiza ndi 11 peresenti. “Ntchito yathu,” ikutero nduna yaikulu yaboma la Briteni, “ndiyakupeza zolepheretsa kotero kuti kutsungula kwakukulu kungapite patsogolo.” Koma kodi malamulo ndi chikakamizo cha ndale, mulimonse mmene zingakhalire ndi cholinga chabwino, zingasinthedi chikhoterero cha anthu chakuchita choipa? Chenicheni chakuti kusaweruzika kulipo ndipo kukuwonjezereka pamaso pa bungwe lamalamulo, ndipo ngakhale pamaso pa osungitsa malamulo aukatswiri, chimadzilankhulira chokha. Chinachake choposa kuletsa kwalamulo nchofunikira. Chibadwa cha anthu chenichenicho chiyenera kusintha.

Baibulo, polankhula za lingaliro lenileni la moyo, mowona mtima limalongosola mikhalidwe yoipa ya munthu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analembera Akristu anzake m’Galatiya ponena za “machitidwe achisembwere, achidetso, ndi oipa . . . Anthu amakhala adani namamenyana; amakhala ansanje, okwiya, ndi . . . osirira, kuledzera, njiru, amachita zinthu zina zonga zimenezi.” Mogwirizana ndi Today’s English Version, yogwidwa mawu panopa, machitachita oluluzika onsewa ndiwo “zimene chibadwa cha anthu chimachita.”​—Agalatiya 5:19-21.

Muzu wa Vutolo

Komabe, Today’s English Version ndiyo matembenuzidwe opanda tsankho ndipo mawu akuti “zimene chibadwa cha anthu chimachita” angokhala kunenera m’mawu ena zimene Paulo kwenikweni ananena. Liwu Lachigiriki limene Paulo anagwiritsira ntchito, sarx, limatanthauza “thupi,” osati “chibadwa cha anthu.” Kaamba ka chifukwa chimenechi, matembenuzidwe enieni amalankhula panopa za “ntchito za thupi” kupereka lingaliro la Paulo molongosoka m’chinenero chathu chamakono.a

Cholembedwa cha Baibulo chonena za kuloŵa kwa uchimo pakati pa anthu nchomvekera bwino lomwe ndichosavuta​—ndiiko komwe, nchosavuta kwenikweni kwakuti ochuluka amasankha kusachikhulupirira. Paulo anachifotokoza motere: ‘Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Paulo panopa akusonya ku Genesis, bukhu loyamba la Baibulo, ndi kuchilengedwe cha munthu woyambirira, Adamu, ndi mkazi wake, Hava. Kusamvera kwawo kodzifunira nkodziŵika bwino lomwe. Chifukwa cha chimenecho, iwo anaweruzidwa ku imfa. Ana awo anakhala ndi choloŵa cha kupanda ungwiro ndipo nawonso anafa. Chotero pamenepo, ‘onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.’ Kaamba ka chifukwa chachikulu chimenechi, chibadwa cha anthu lerolino chiridi chithunzi choipitsidwa cha mmene chinaliri pamene Mulungu poyambirira analenga munthu wangwiro.​—Aroma 3:23; Genesis, mitu 2 ndi 3.

Chibadwa cha Anthu Kusinthidwa!

Komabe, nkotheka kugonjetsa makhalidwe oipitsitsa a chibadwa cha anthu. Ndithudi, Baibulo limanena kuti tikhoza kusintha chibadwa chathu m’lingaliro lakusintha umunthu wathu. Motani? Mwathandizo la mzimu woyera wa Mulungu.​—Aroma 8:9.

Paulo, m’kalata yake kwa Akristu anzake ku Kolose, ananena motere: “Vulani umunthu wakale limodzi ndi zochita zake, ndi kudziveka umunthu watsopano, umene mwa chidziŵitso cholongosoka ulinkupangidwa kukhala watsopano mogwirizana ndi chifanefane cha Uyo amene anaulenga.” Pakati pa zochita za umunthu wakale, iye akundandalitsa ina ya mikhalidwe imene imachititsa anthu kukhoterera ku zinthu zowononga: chilakolako choipa, ukali, mkwiyo, ndi kuipa.​—Akolose 3:5-10, NW.

Polembera Akristu a ku Efeso mofananamo, Paulo akutchulanso kufunika kwa “umunthu watsopano,” (NW) umene akuwauza kuti “unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.” (NW) Iye akukulitsa kukambitsirana kwake mwakunena kuti: ‘Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo.’​—Aefeso 4:24, 31, 32.

Kodi mawu a Paulo anali onena zenizeni? Kodi maumunthu angasinthidwedi? Eya, umboni ngwakuti Akristu oyambirirawo anapanga masinthidwe aakulu m’maumoyo awo. Monga kagulu ka anthu, iwo anakhala osiyana ndi dziko lowazinga. Justin Martyr, wolemba mbiri wa m’nthaŵi Zachikristu zoyambirira, analemba kuti: “Ife amene tinadana nitiphana, ndipo, chifukwa cha kusiyana kwa makhalidwe, tinakana kukhala ndi anthu afuko losiyana, tsopano, chiyambire kubwera kwa Kristu, tikukhala nawo pamodzi pamaziko a zochita zofanana, ndikupempherera adani athu, ndikuyesayesa kuchititsa amene amatida popanda chifukwa chenicheni kukhala ndimoyo mogwirizana ndi malamulo angwiro a Kristu.”

Bwanji ponena za lerolino? Kodi nkothekerabe kupanga masinthidwe aakulu oterowo m’chibadwa cha munthu? Inde! Zitsanzo zikwi makumi ambiri zimasonyeza kuti masinthidwe aakulu oterowo akuchitikabe. Chotsatirachi nchimodzi chokha cha izo.

Stephen analeredwera muimodzi ya matauni a indasitale a ku Mangalande. Bambo wake anali wosakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu. Pamsinkhu wa 12, Stephen anaweruzidwa kukakhala zaka zitatu m’sukulu yophunzitsira makhalidwe. Iye anali ataulula milandu yothyola ndikuba yokwanira 64! Posapita nthaŵi anataya ulemu ku ulamuliro uliwonse, ndipo pamene ankakula, maupandu ake anakhala owopsa mowonjezereka. Anaphatikizapo uphyuta, uchidakwa, mkhalidwe wosalongosoka, ndi kuwukira apolisi, mlandu wotsirizira umene unapereka Stephen kundende. Chibadwa chake chinakhala chachiwawa kwambiri. “Palibe upandu umene munthu wosapembedza sadzachita ngati sozoŵa zake nzazikulu mokwanira,” iye anatero.

Kodi nchiyani chimene chingasinthe mpandu wokakala woteroyo? M’kupita kwanthaŵi Stephen analandira thandizo kuchokera kwa mbale wake amene adakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Ataphunzira Baibulo kwanthaŵi yochepa, Stephen anayamba kuvala “umunthu watsopano.” Masinthidwe amene anapanga analidi aakulu. Tsopano, zaka zisanu pambuyo pake, ali wokwatira wachimwemwe ndichiŵalo chathayo cha mpingo wa Mboni za Yehova, umene akutumikiramo monga mtumiki wotumikira.

Chotero chibadwa cha anthu chingasinthidwe m’zochitika zamunthu payekha. Koma kodi zifooko za anthu ndizo chifukwa chokha chimene ‘chikudodometsa kutsungula’ lerolino?

“Mdyerekezi wa M’malemba”

Mtumwi Paulo analemba ulosi wapadera wonena za “masiku otsiriza” ano. Mawu ake abwerezedwa m’kabokosi kali pamwambako. Onani kuti kuŵirikizika kwa chiwawa ndi kuipa kukudzetsa ‘nthaŵi zowawitsa.’ Kodi chibadwa cha anthu nchimene chiri ndi liŵongo lonse la zonsezi?​—2 Timoteo 3:1.

Ayi, pali chinachake, mphamvu yauchiŵanda yochititsa kuipa imene ikugwiritsira ntchito zifooko za anthu. Monga momwe anthu akukupezera kukhala kovuta kukhulupirira kuti munthu ali ndi tchimo lacholoŵa, momwemonso akukupeza kukhala kovuta kuvomereza kuti pali mphamvu yaikulu kuposa munthu imene imafunafuna kumsonkhezera. Koma Baibulo limanena kuti mphamvu yoteroyo iripo: Satana Mdyerekezi.

Liwu lakuti “Mdyerekezi” (lotanthauza, “woneneza”) limapezeka nthaŵi 33 m’Baibulo, ndipo “Satana” (lotanthauza, “wotsutsa”) limapezeka nthaŵi 52. Zambiri za zilozerozi zimakhudza munthu woipa wauzimu mmodzimodziyo. Ngakhale kuli choncho, ena amakana kukhalapo kwa Satana monga munthu, nakonda kunena kuti: “Chibadwa cha anthu ndi chikhoterero chake chachikulu ku uchimo ndicho mdyerekezi wa m’Malemba.”b Komabe, mosangalatsa, m’cholembedwa cha Yobu, mtumiki wokhulupirika wa Yehova, malemba Achihebri amagwiritsira ntchito liwu lakuti has·Sa·tanʹ, Satanayo, ndipo pa Luka 4:2, (NW) timaŵerenga kuti anali Mdyerekeziyo (Chigiriki, ho di·aʹbo·los) amene anayesa Yesu. (Yobu 1:6) M’zochitika zonse ziŵiri, munthu wakutiwakuti akuzindikiritsidwa mwamawu. Sizikunena za chibadwa cha anthu.

Mtumwi Paulo akukulitsa kumvetsetsa kwathu kwa mmene Satana aliri wamphamvu pamene, polembera Aefeso, akulankhula za “olamulira a dziko amdima uno, . . . mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6:12, NW) Limodzi ndi Satana Mdyerekezi, “olamulira a dziko” amenewo ndiwo ziŵanda, zolengedwa zauzimu zoipa zosaoneka. Izo ‘zikunyenga dziko lonse lapansi,’ kugwiritsira ntchito mkhalidwe wamunthu wopanda ungwiro kumlingo waukulu wothekera. (Chibvumbulutso 12:9) Ndi kaamba ka chifukwa chimenechi kuti Paulo akulangiza mwamphamvu Mkristu aliyense ‘kuchirimika pokana machenjero a Mdyerekezi.’ Iye ndiye wochititsa wamkulu wa kunyonyotsoka kwa mkhalidwe wa anthu wotizinga umene tikuwona.​—Aefeso 6:11.

Kubwezeretsedwa

Petro, wokhalako m’nthaŵi ya Paulo, akutitsimikizira kuti Satana ndi ziŵanda zake sadzakhalako kwamuyaya akumasaka anthu. Iye akuti: ‘Tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko lapansi latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Ndithudi, posachedwapa tsopano, kuipa kwa mtundu uliwonse sikudzakhalanso mbali ya anthu. Satana ndi ziŵanda zake adzawonongedwa. (Aroma 16:20; Chibvumbulutso 20:1-3) Pamenepo, ndithudi, chibadwa cha anthu chidzaunikira “ulemerero wa Mulungu,” ndi moyo wosatha chiyembekezo chotsimikizirika cha banja la anthu.​—Aroma 3:23.

“Ndanena nthaŵi zonse ndipo ndidzanenabe nthaŵi zonse,” anatsimikizira motero pulezidenti wa Amereka Thomas Jefferson, “kuti kupenda Bukhu Lopatulika mwakhama kudzapanga nzika zabwinopo . . . Baibulo limapanga anthu abwino koposa m’dziko.” Monga momwe tawonera, chibadwa chathu chingasinthidwe ngati tipatsa mpata uthenga wamphamvu wa m’Baibulo kusonkhezera miyoyo yathu. (Aroma 12:2) Tingasankhe kukalamira kupata chimene chiri cholemekezeka ndi chaumulungu. Ndipo kuti tilimbikitsidwe m’kuyesayesa kwathu kuwongokera, tingasankhe kumayanjana ndi amene mowona mtima amafuna kuchita mofananamo. (Ahebri 10:24, 25) Mboni za Yehova nzofunitsitsa kukuthandizani mwanjira iriyonse yothekera. Bwanji osakambitsirana nazo tsopano!

[Mawu a M’munsi]

a Yerekezerani ndi: New World Translation of the Holy Scriptures; The Holy Bible, lolembedwa ndi Robert Young; The Emphasised Bible, lolembedwa ndi Joseph B. Rotherham; The Holy Bible in Modern English, lolembedwa ndi Ferrar Fenton; The Modern Reader’s Bible, lolembedwa ndi Richard G. Moulton.

b Ndemanga yoperekedwa mwalamulo ya chikhulupiriro cha Christadelphianism, mpatuko wa Chikristu Chadziko.

[Bokosi patsamba 6]

“MASIKU OTSIRIZA” Kufotokoza kwa Baibulo

‘Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.’​—2 Timoteo 3:1-5.

[Chithunzi patsamba 7]

Posachedwapa, chibadwa cha anthu chidzaunikira ulemerero wa Mulungu mokwanira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena