Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 10/1 tsamba 15
  • Muzikhululuka Ndi Mtima Wonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikhululuka Ndi Mtima Wonse
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Pitirizani Kukhululukirana Eni Okha’
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Kukhululuka Kumatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nkukhaliranji Wokhululukira?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 10/1 tsamba 15

MFUNDO ZAKALE KOMA ZOTHANDIZABE MASIKU ANO

Muzikhululuka Ndi Mtima Wonse

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”—Akolose 3:13.

Mzimayi wakhumudwa ndi mnzake ndipo akuchoka

Kodi mfundoyi imatanthauza chiyani? Baibulo limayerekezera tchimo ndi ngongole ndiponso kukhululuka ngati kuuza munthu kuti asabwezenso ngongoleyo. (Mateyu 18:21-27) Buku lina limanena kuti mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “kukhululuka” amatanthauza “kusakumbutsanso ngongole, n’kuiiwaliratu.” Choncho, ngati takhululukira munthu wina amene watilakwira, timakhala kuti taiwaliratu zimene munthuyo watichitira. Komatu kukhululukira munthu wina sikutanthauza kuti zimene munthuyo watichitira sizinatipweteke kapena kuti tikuchepetsa choipa chimene watichitira. Koma zimangotanthauza kuti sitikufuna kusunga zifukwa ngakhale titakhala ndi ‘chifukwa chomveka chodandaulira.’

Kodi mfundoyi ndi yothandiza masiku ano? Tonsefe si angwiro ndipo timalakwitsa nthawi zonse. (Aroma 3:23) Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizikhululukira anzathu chifukwa ifenso nthawi ina tidzafuna kuti anzathu atikhululukire. Komanso pali phindu lina ngati timakhululukira anzathu.

Azimayi awiri akukumbatirana

Timadzipweteka tokha tikamasunga zifukwa komanso tikamalephera kukhululukira anzathu. Kuchita zimenezi kungachititse kuti tisamasangalale, tizikhala opanikizika komanso tizisowa mtendere wamumtima. Zingachititsenso kuti tidwale matenda oopsa. Lipoti lina lomwe linalembedwa pakoleji ina yoona za matenda a mtima linanena kuti: “Zikuoneka kuti anthu ambiri aukali komanso omwe amakonda kukwiya, amadwala matenda a mtima.”—Journal of the American College of Cardiology.

Koma tikamakhululuka, timakhala pa mtendere ndi ena ndipo zimatithandiza kuti tizigwirizana ndi anzathu. Komanso tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikutsanzira Mulungu amene amakhululukira munthu amene walapa. Ndipotu Mulungu amafuna kuti ifenso tizikhululukira anzathu.—Maliko 11:25; Aefeso 4:32; 5:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena