Kumvera Kwaumulungu M’banja la Zipembedzo Zosiyana
“KUMAPWETEKA kwambiri kuposa kumenyedwa kwa mtundu uliwonse. . . . Ndimamva monga ngati kuti ndili ndi mikwingwirima m’thupi monse, komabe palibe amene akuiona.” “Nthaŵi zina moyo umandigwetsa ulesi . . . ndipo ndimachita monga ngati kuti ndingachoke panyumba osadzabweranso.” “Kulingalira bwino kumandivuta nthaŵi zina.”
Mawu achisoni amenewo amasonyeza kutaya mtima ndi kusungulumwa. Anthu amene amawanena ndi aja ochitidwa chipongwe—kunenezedwa zinthu, kuwopsezedwa, kutchedwa maina onyoza, kusalankhuzidwa—ndiponso amene amamenyedwa ndi anzawo a muukwati ndi a m’banja lawo. Kodi nchifukwa ninji anthu ameneŵa amachitidwa moipa choncho? Chifukwa cha kusiyana chabe kwa zikhulupiriro za zipembedzo zawo. M’mikhalidwe imeneyi, kukhala m’banja la zipembedzo zosiyana kumachititsa kulambira Yehova kukhala kovuta kwambiri. Komabe, Akristu ambiri ovutitsidwa mwanjira imeneyo amakhoza kusonyeza kumvera kwaumulungu.
Ndi mwaŵi kuti si m’mabanja onse a zipembedzo zosiyana mmene nsautso ndi kupsinjika maganizo kumeneku kumapezeka. Komabe, iko kulipo. Kodi umenewu ndiwo mkhalidwe m’banja lanu? Pamenepo, kungakuvuteni kukhala waulemu kwa mnzanu wa muukwati kapena kwa makolo anu. Ngati ndinu mkazi amene muli mumkhalidwe umenewo kapena ana amene ali m’malo otero, kodi mungakhoze bwanji kusonyeza kumvera kwaumulungu m’banja la zipembedzo zosiyana? Kodi ena angachirikize motani? Ndipo kodi Mulungu amaiona motani nkhaniyi?
Kodi Nchifukwa Ninji Kumvera Kuli Kovuta Kwambiri?
Mzimu wa dziko wa kudzikonda ndi kusayamika umagwirizana ndi zikhoterero zanu zopanda ungwiro kuchititsa kumvera kwaumulungu kukhala nkhondo yanthaŵi zonse. Satana amadziŵa zimenezi, ndipo cholinga chake ndicho kufooketsa mzimu wanu. Nthaŵi zambiri iye amagwiritsira ntchito a m’banja amene samayamikira kapena kulemekeza kwenikweni miyezo yaumulungu kapena amene samatero nkomwe. Miyezo yanu yapamwamba yauzimu ndi yamakhalidwe nthaŵi zambiri imasiyana kwambiri ndi ija ya banja lanu losakhulupirira. Zimenezi zimachititsa kukhala ndi malingaliro osiyana pa khalidwe ndi zochita. (1 Petro 4:4) Chisonkhezero cha kukupambutsani pa muyezo Wachikristu chingakhale champhamvu kwambiri, popeza kuti mwamvera lamuloli: “Musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu.” (Aefeso 5:11) Kwa iwo zonse zimene muchita sizilinso zolondola. Zonsezo zili chifukwa cha chipembedzo chanu. Mayi wina, atatopa ndi ana odwala, anapempha mwamuna wake thandizo ndipo anamyankha motonza kuti, “Ngati nthaŵi ya chipembedzo chako uli nayo, sufunikira thandizo.” Mawu otero amangochititsa kumvera kukhala kovutirapo.
Ndiyeno pamakhala nthaŵi zimene mungatsutsane pa nkhani zina zimene sizimaombana mwachindunji ndi Malemba. Komabe, mumadziŵa kuti muli mbali ya banjalo ndipo chifukwa cha zimenezo muli ndi mathayo ena. “Ndimakwiya ndikaganiza mmene atate amatichitira chifukwa chakuti ndimazindikira kuti iwo amaganiza kuti timawanyalanyaza,” akutero Connie. “Nthaŵi zambiri ndimangokumbukira kusaipidwa ndi chitsutso cha atate wanga. Ndimadziuza kuti pali chifukwa chachikulu chimene iwo amaipidwira ndi kaimidwe kathu. Satana ali wolamulira wa dongosolo ili la zinthu.” Susan, wokwatiwa kwa wosakhulupirira, akuti: “Poyamba ndinkafuna kupatukana ndi mwamuna wanga—koma sindimateronso. Ndinadziŵa kuti Satana anali kumgwiritsira ntchito kundiyesa.”
Zoyesayesa za Satana za kukumvetsani kukhala wopanda pake zingaoneke kukhala zosatha. Pangapite masiku popanda kulankhulana ndi mnzanu wa muukwati. Moyo ungakhale wosungulumwa kwambiri. Zimenezi zimachotsa chidaliro ndi ulemu wanu ndipo zimayesa kumvera kwanu kwaumulungu. Nawonso ana amataya mtima natha mphamvu. Panthaŵi ina, ngakhale kuti makolo awo anawatsutsa, atumiki atatu a Mulungu achinyamata anapitirizabe kupezeka pa misonkhano Yachikristu. Mmodzi wa iwo, mtumiki wa nthaŵi yonse tsopano, anati: “Tinkamva kukhala opimbidzala ndi otopa; sitinali kuona tulo; mitima yathu inali yosweka.”
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Inu?
Kumvera Mulungu kumakhala koyamba nthaŵi zonse, ndipo kumvera mwamuna monga mutu kokhala ndi malire kuyenera kugwirizana ndi malangizo a Yehova nthaŵi zonse. (Machitidwe 5:29) Zimenezo zingakhale zovuta, koma nzotheka. Pitirizanibe kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka thandizo. Iye akufuna kuti ‘mumlambire mumzimu ndi m’choonadi’ nimumvere malangizo ake ndi kuwagonjera. (Yohane 4:24) Chidziŵitso cha m’Mawu a Mulungu, pamene chiloŵa mumtima wabwino, chimasonkhezera kumvera kodzifunira. Ngakhale mikhalidwe yanu ingasinthe, Yehova ndi Mawu ake sasintha. (Malaki 3:6; Yakobo 1:17) Yehova wapatsa mwamuna umutu. Zimenezi zili choncho kaya iye amavomereza kapena samavomereza umutu wa Kristu. (1 Akorinto 11:3) Ngakhale kuti zimenezi zingakuvuteni kuvomereza ngati mukuyang’anizana ndi nkhanza yosatha ndi kunyazitsidwa, mtumwi Yakobo akuti: ‘Nzeru yochokera kumwamba ili . . . yomvera bwino.’ (Yakobo 3:17) Kuzindikira umutu umenewu popanda kukayikira ndi kuuvomereza kumafuna mzimu wa Mulungu, makamaka chipatso chake cha chikondi.—Agalatiya 5:22, 23.
Pamene mukonda wina, nkwapafupi kusonyeza kumvera kwaumulungu kulinga ku ulamuliro woikidwa ndi Mulungu. Aefeso 5:33 amalangiza kuti: “Yense payekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziwopa mwamuna.”
Talingalirani za Yesu. Iye anachitidwa chipongwe ndi kumenyedwa, koma sanatukwane aliyense. Anasunga mbiri yabwino. (1 Petro 2:22, 23) Kuti Yesu apirire minyozo yaikulu yotero, anafunikira kulimba mtima kwambiri ndi chikondi chosagonja pa Atate wake, Yehova. Koma, chikondi “chipirira zinthu zonse.”—1 Akorinto 13:4-8.
Paulo anakumbutsa wantchito mnzake Timoteo, ndipo akukumbutsanso ife lerolino kuti: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.” (2 Timoteo 1:7) Chikondi chachikulu pa Yehova ndi Yesu Kristu chingakusonkhezereni pa kumvera kwaumulungu pamene mkhalidwe uoneka kukhala wosapiririka. Kudziletsa kudzakuthandizani kukhala ndi lingaliro loyenera ndi kumamatirabe pa unansi wanu ndi Yehova ndi Yesu Kristu.—Yerekezerani ndi Afilipi 3:8-11.
Amuukwati Amene Amakhoza Kusonyeza Kumvera Kwaumulungu
Nthaŵi zina muyenera kudikira nthaŵi yaitali kuti muone mmene Yehova adzasamalira mavuto anu. Komabe, dzanja lake silifupika. “Nthaŵi zonse chitani zimene Yehova akupatsani ufulu ndi mwaŵi wa kuzichita—kumlambira pamisonkhano yampingo ndi yaikulu, kuphunzira, kupita mu utumiki, ndi kupemphera,” akulangiza motero yemwe akukhoza kusonyeza kumvera kwaumulungu. Yehova samadalitsa zochita zanu zokha, komanso zoyesayesa zanu. Pa 2 Akorinto 4:17, mtumwi Paulo ananena kuti ‘chisautso nchakanthaŵi chichitira ife ulemerero wosatha.’ Sinkhasinkhani zimenezi. Zidzakuthandizani kukhazikika. Mkazi wina akunena kuti: “Moyo wa banja langa sukuwongokera, ndipo nthaŵi zina ndimakayikira ngati Yehova amakondwera nane. Koma chinthu chimodzi chimene ndimaona monga dalitso lake nchakuti ndimapyola m’mikhalidwe yovuta imeneyi bwinopo kuposa mwamuna wanga. Kudziŵa kuti zochita zathu zimakondweretsa Yehova kumachititsa kupirira konseko kukhala kopindulitsa.”
Yehova amalonjeza kuti sadzakulolani kuvutika kufikira pamene simukhoza kupirira. Mdalireni. Iye amadziŵa bwino kuposa inu, ndipo amakudziŵani bwino kuposa mmene mumadzidziŵira. (Aroma 8:35-39; 11:33; 1 Akorinto 10:13) Kupemphera kwa Yehova m’mikhalidwe yovuta kumathandiza. Pempherani kuti mzimu wake ukutsogolereni, makamaka pamene simukudziŵa chochita kapena mochitira ndi mkhalidwewo. (Miyambo 3:5; 1 Petro 3:12) Nthaŵi zonse m’pempheni kuleza mtima, kudziletsa, ndi kudzichepetsa kuti mumvere ulamuliro wa mutu wanu. Wamasalmo anati: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga.” (Salmo 18:2) Kukumbukira zimenezi kumalimbitsa a m’mabanja a zipembedzo zosiyana.
Makamaka, yesetsani zolimba kuchititsa ukwati wanu kukhala wachimwemwe. Inde, Yesu anaoneratu kuti uthenga wabwino unali kudzachititsa magaŵano. Ngakhale zili tero, pempherani kuti magaŵano alionse asakhale chifukwa cha mzimu wanu kapena khalidwe lanu. (Mateyu 10:35, 36) Ndi cholinga chimenechi, kugwirizana kumachepetsa mavuto a muukwati. Ngakhale ngati ndinu nokha amene mukusonyeza mzimu umenewu, uwo ungathandize kwambiri kuletsa mavuto kufika pa kukangana ndi kugaŵanikana kowopsa. Kuleza mtima ndi chikondi nzofunika kwambiri. “Khalani wodekha,” (NW) ndi “woleza” mtima.—2 Timoteo 2:24.
Mtumwi Paulo anakhala “zinthu zonse kwa anthu onse.” (1 Akorinto 9:22) Mofananamo, popanda kugonja pa mathayo Achikristu, nthaŵi zina mungafunikire kusintha programu yanu kuti mukhale ndi nthaŵi yochuluka yokhala ndi mnzanu wa muukwati ndi banja. Pezani nthaŵi yochuluka kwambiri yokhala ndi munthu amene munasankha kukhala naye. Sonyezani nkhaŵa Yachikristu. Kumeneku ndi kusonyeza kumvera kwaumulungu.
Mkazi wowopa Mulungu ndi wogonjera amene ali wokhoza kusintha ndi wachifundo kumamkhalira kwapafupi kusonyeza kumvera kwaumulungu. (Aefeso 5:22, 23) Mawu achisomo, “okoleretsa,” amathandiza kuchepetsa mikangano imene ingabuke.—Akolose 4:6; Miyambo 15:1.
Nzeru yaumulungu imakulangizani kuthetsa mikangano mwamsanga ndi kubwezeretsa mtendere mwa mawu abwino omangirira, m’malo mwa kukagona “muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26, 29, 31) Zimenezi zimafuna kudzichepetsa. Dalirani Yehova kwambiri kaamba ka nyonga. Mkazi wina Wachikristu anavomereza modzichepetsa kuti: “Pambuyo pa pemphero lakhama, mzimu wa Yehova umatukula mkono wanga kuti ndikumbatire mwamuna wanga.” Mawu a Mulungu amati: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ndi chabwino gonjetsani choipa.” (Aroma 12:17-21) Uphungu umenewu ngwanzeru ndipo uli njira ya kumvera kwaumulungu.
Ana Osonyeza Kumvera Kwaumulungu
Uphungu wa Yehova kwa inu ana amene muli m’mabanja a zipembedzo zosiyana ngwakuti: “Mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:20) Onani kuti Ambuye Yesu Kristu akutchulidwa pa nkhaniyi. Chotero, kumvera makolo sikuli kopanda malire. M’lingaliro lina uphungu wa Machitidwe 5:29, wa “kumvera Mulungu koposa anthu,” umakhudzanso Akristu achinyamata. Padzakhala nthaŵi zina pamene mudzafunikira kusankha chochita mogwirizana ndi zimene mudziŵa kukhala zabwino malinga ndi Malemba. Mwina zimenezi zingadzetse chilango chifukwa cha kukana kwanu kuchitako mbali ya kulambira konyenga. Pamene kuli kwakuti kuyembekezera zimenezi nkosakondweretsa, mungapeze chitonthozo ndipotu mungakondwe chifukwa chakuti mukuvutika kaamba ka kuchita chabwino pamaso pa Mulungu.—1 Petro 2:19, 20.
Popeza malingaliro anu amatsogozedwa ndi miyezo ya Baibulo, mungasemphane ndi makolo anu pa nkhani zina. Zimenezi sizimawakhalitsa adani anu. Ngakhale ngati saali atumiki odzipatulira a Yehova, ayenera kupatsidwa ulemu woyenera. (Aefeso 6:2) Solomo anati: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako.” (Miyambo 23:22) Yesani kumvetsetsa kupweteka mtima kumene iwo akumva chifukwa cha kutsatira kwanu chipembedzo chimene chikuoneka chosayenera kwa iwo. Lankhulanani nawo, ndipo “kufatsa kwanu kuzindikirike.” (Afilipi 4:5) Auzeni malingaliro ndi nkhaŵa zanu. Mamatirani zolimba pa miyezo yaumulungu, komabe, “ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) Kumvera kwanu ulamuliro wa makolo tsopano kumasonyeza Yehova kuti mukufuna kupitirizabe kukhala womvera monga nzika ya Ufumu.
Zimene Ena Angachite
Akristu amene ali m’mabanja a zipembedzo zosiyana afunikira chichirikizo ndi chifundo cha alambiri anzawo. Zimenezi zikusonyezedwa ndi mawu a wina yemwe anati: “Ndatayiratu mtima ndipo ndisoŵeratu chochita, pakuti palibe chimene aliyense angachite, ndipo palibe chimene ndingachite kuwongolera zinthu. Ndikudalira Yehova kuti achite chifuniro chake m’banja lathu, mulimonse mmene angachichitire.”
Kuyanjana ndi abale ndi alongo auzimu pa misonkhano Yachikristu ndiko linga. Munthu mmodzimodziyu anafotokoza moyo wake kukhala “wonga maiko aŵiri osiyana. Lina ndiyenera kukhalamo ndipo linalo ndimakonda kukhalamo.” Chikondi cha abale ndicho chimatheketsa ovutika ameneŵa kupirira ndiponso ndi kutumikira m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Atchuleni m’mapemphero anu. (Aefeso 1:16) Nthaŵi zonse, pa chochitika chilichonse, lankhulani nawo ndi mawu olimbikitsa, abwino, ndi otonthoza. (1 Atesalonika 5:14) Ngati kutheka ndipo nkoyenera, aphatikizeni m’zochita zanu zateokrase ndi m’macheza.
Madalitso ndi Mapindu a Kumvera Kwaumulungu
Sinkhasinkhani tsiku ndi tsiku madalitso ndi mapindu a kusonyeza kumvera kwaumulungu m’banja la zipembedzo zosiyana. Limbikirani pa kumvera. ‘Musaleme.’ (Agalatiya 6:9) Kupirira mikhalidwe yoipa ndi chisalungamo “chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu . . . ndiko chisomo” cha Mulungu. (1 Petro 2:19, 20) Mverani kumlingo uliwonse umene sungaswe miyezo ndi malamulo olungama a Yehova. Zimenezi zimasonyeza kukhulupirika ku makonzedwe a Yehova. Kumvera kwanu kwaumulungu mwina kungapulumutsenso mnzanu wa muukwati, ana, kapena makolo.—1 Akorinto 7:16; 1 Petro 3:1.
Pamene mukuyesayesa kukwaniritsa zofuna za banja la zipembedzo zosiyana ndi zimene limakuyembekezerani kuchita, kumbukirani kufunika kwa kusunga umphumphu kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Mungagonje pa zinthu zambiri, koma kugonja pa umphumphu ndiko kugonja pa zonse, kuphatikizapo moyo weniweniwo. Mtumwi Paulo anati: “Mulungu . . . pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika woloŵa nyumba wa zonse, mwa iyenso analenga maiko.” Kuzindikira “chipulumutso chachikulu chotero” kudzakulimbitsani pa kumvera.—Ahebri 1:1, 2; 2:3.
Kumvera kwanu kosagonja ndi kulimbikira kwanu pa makhalidwe ndi miyezo yabwino ndiko chitetezo chabwino kwa inu ndi mnzanu wa muukwati wosakhulupirira. Kukhulupirika kumakulitsa chikondi cholimba m’banja. Miyambo 31:11 imati ponena za mkazi wangwiro ndi wokhulupirika: “Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira.” Khalidwe lanu loyera ndi ulemu waukulu zingamtsegule maso mwamuna wanu wosakhulupirirayo. Zingamchititse kulandira choonadi cha Mulungu.
Kumvera kwaumulungu kulidi kwamtengo wapatali ndi kopulumutsa moyo. Kupempherereni m’moyo wanu wa banja. Kudzadzetsa mtendere wa maganizo ndi chitamando kwa Yehova.