Yesu Kristu—Mwana Wokondedwa wa Mulungu
“Ndipo onani, mawu akuchokera kumiyamba akuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.’”—MATEYU 3:17.
1, 2. (a) Kodi ndi chowonadi chosavuta chotani chimene Baibulo limaphunzitsa ponena za Mulungu wamphamvuyonse ndi Yesu Kristu? (b) Kodi nchiyani chimene zipembedzo za Chikristu cha Dziko zimaphunzitsa?
YESU KRISTU anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 30 mwa kumizidwa m’madzi. Pamene anatuluka m’madzi, liwu lochokera kumwamba linanena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Liwu limenelo linali liwu la Mulungu. Pa chochitika china, m’pemphero kwa Mulungu, Yesu ananena kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.” Ndipo pamene Yesu ananena chimenecho, “adadza mawu a Mulungu kuchokera kumwamba: ‘Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.’”—Yohane 12:28.
2 Kuchokera ku zolembedwa zimenezi, ngakhale mwana angamvetsetse kuti unansi pakati pa Mulungu Wamphamvuyonse ndi Yesu Kristu unali uja wa atate ndi mwana wake wokondedwa, anthu aŵiri osiyana. Komabe, chowonadi chopepuka cha Baibulo chimenechi chimakanidwa ndi zipembedzo za Chikristu cha Dziko. Zimawumirira kuti Yesu Kristu ndi Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini, munthu wachiŵiri wa Utatu, munthu wachitatu akumakhala mzimu woyera.
3. Ndimotani mmene kusokonezeka kwa chiphunzitso cha Utatu kukusonyezedwera?
3 Chiphunzitso chimenecho chapangitsa msokonezo wokulira pakati pa anthu a m’zipembedzo za Chikristu cha Dziko, chimene chiri chifukwa chimodzi chimene New Catholic Encyclopedia imatchera Utatu kukhala chinsinsi. Ndithudi, icho chimapangitsa msokonezo ngakhale pakati pa atsogoleri a chipembedzo, popeza encyclopedia imanenanso kuti: “Pali aphunzitsi oŵerengeka a ukatswiri wa Utatu m’masukulu ophunzira zaumulungu a Roma Katolika omwe sanafunsidwepo nthaŵi imodzi kapena ina ndi funso lakuti, ‘Koma kodi ndimotani mmene wina angalalikire Utatu?’ Ndipo ngati funsolo liri chizindikiro cha kusokonezeka ku mbali ya ophunzirawo, mwinamwake ilo siliri lochepera chizindikiro cha kusokonezeka kofananako kumbali ya aphunzitsi awo.”
4. Kodi nchiyani chimene chiri chiphunzitso cha lamulo cha matchalitchi ponena za Utatu?
4 Chiphunzitso chosokoneza chimenecho chiri chikhulupiriro chofunika cha zipembedzo za Chikatolika ndi chiProtestanti. The Catholic Encyclopedia imalongosola kuti: “Utatu liri liwu logwiritsiridwa ntchito kusonyeza chiphunzitso chokulira cha chipembedzo cha Chikristu . . . Chotero, m’mawu a Chiphunzitso cha Athanasi: ‘Atate ali Mulungu, Mwana ali Mulungu, ndipo Mzimu Woyera uli Mulungu, ndipo komabe palibe Milungu itatu koma Mulungu mmodzi.’” Mofananamo, m’mlandu wa m’bwalo la milandu wokhudza Mboni za Yehova m’Grisi, Tchalitchi cha Griki Orthodox chinanena kuti: “Maziko a chiphunzitso cha Chikristu, m’chimene Akristu onse amadzinenera kukhala okhulupirira . . . mosasamala kanthu za mpatuko kapena kusiyana, chiri . . . Utatu, kuti Mulungu ali Mmodzi mwa anthu atatu.” Tchalitchi cha Griki Orthodox chinanenanso kuti: “Akristu ali awo amene amalandira Kristu monga Mulungu.” Icho chinanena kuti awo omwe samalandira Utatu sali Akristu koma owukira chipembedzo.
5, 6. Nchifukwa ninji chiri chofunika kudziŵa chowonadi ponena za nkhaniyi?
5 Ngakhale kuli tero, ngati “maziko” a chiphunzitso cha Utatu amenewa a Chikristu cha Dziko sali owona, ngati ali bodza, chotero chosiyanako chikakhala nkhani. Akristu owona akachikana icho. Awo omwe apatuka kuchokera ku Chikristu angamamatire ku icho. Ndi chotulukapo chotani ku gulu lomwe langotchulidwa kumenelo? M’bukhu lotsirizira la Baibulo, “chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu [anamupatsa],” timaŵerenga ponena za awo omwe sanalinge ku moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu: “Kunja kuli agalu ndi anyanga, achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.”—Chivumbulutso 1:1; 22:15.
6 Chifukwa cha kufunika kwake, tifunikira kudziŵitsidwa ponena za kumene chiphunzitso cha Utatu chimenechi chinayambira ndi chifukwa chimene chinayambikira. Ndani kwenikweni yemwe ali kumbuyo kwake? Kodi ndimotani mmene ophunzira amakono a Baibulo akunenera ponena za icho? Koma tisanakambitsirane nkhanizi, tiyeni tifufuze mowonjezereka chimene Mawu a Mulungu owuziridwa enieniwo amanena.—2 Timoteo 3:16, 17.
Osati ‘Mulungu Mwana’ koma “Mwana wa Mulungu”
7. Kodi nchiyani chimene kuphunzira kopanda tsankho kwa Baibulo kumavumbula ponena za Yesu?
7 Yesu sanadzinenerepo ndi kale lonse kukhala Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini. Kuŵerenga Baibulo kulikonse kosasankha popanda lingaliro losungidwiratu m’maganizo ponena za Utatu kudzatsimikizira chimenecho. Mwachitsanzo, pa Yohane 3:16, Yesu ananena kuti: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti, anapatsa Mwana wake wobadwa yekha.” Kokha maversi aŵiri pambuyo pake, Yesu kachiŵirinso ananena kuti iye anali “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Yohane 3:18) Pamene Ayuda anampatsa Yesu mlandu wa kuchita mwano, iye anayankha kuti: “Kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko lapansi, ‘Uchita mwano,’ chifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?” (Yohane 10:36) Yesu sananene kuti iye anali ‘Mulungu Mwana’ koma kuti iye anali “Mwana wa Mulungu.”
8. Kodi ndi umboni wotani umene nduna ya nkhondo ndi omwe anali nayo anapereka?
8 Pamene Yesu anafa, ngakhale asilikali Achiroma oimirira pafupi naye anadziŵa kuti Yesu sanali Mulungu: “Pamene mkulu wa asilikali, ndi iwo anali nawo akudikira Yesu anawona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitika, anawopa kwambiri, nanena: ‘Indedi uyu ndiye Mwana wa Mulungu.’” (Mateyu 27:54) Iwo sananene kuti, ‘uyu anali Mulungu’ kapena ‘uyu anali Mulungu Mwana’ chifukwa chakuti Yesu ndi ophunzira ake anaphunzitsa kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, osati Mulungu Wamphamvuyonse mu mkhalidwe waumunthu.
9, 10. Ndi umboni wamphamvu wotani womwe ukupatsidwa mu Mauthenga Abwino ponena za unansi pakati pa Mulungu ndi Yesu?
9 Mulungu iyemwini anachitira umboni kuti Yesu anali Mwana wake wokondedwa, monga mmene wolemba Baibulo Mateyu anadziŵitsira pamene Yesu anabatizidwa. (Mateyu 3:17) Malemba ena a Baibulo anadziŵitsa mofananamo. Marko analemba kuti: “Mawu anatuluka m’mthambo: ‘Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa iwe ndikondwera bwino.’” (Marko 1:11) Luka ananena kuti: “Ndipo munatuluka mawu m’thambo kuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga, wokondedwa; mwa iwe ndikondwera.’” (Luka 3:22) Ndipo Yohane Mbatizi, yemwe anabatiza Yesu, anachitira umboni kuti: “Ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu [Yesu] ndi yemweyo.” (Yohane 1:34) Chotero Mulungu iyemwini, olemba Mauthenga Abwino anayi onsewo, ndi Yohane Mbatizi analongosola mowonekera bwino kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu. Ndipo pa nthaŵi ina pambuyo pake, pa mawalitsidwe a Yesu, chinthu chofananacho chinachitika: “Ndipo munatuluka mawu mumtambo [a Mulungu], nanena: ‘Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo. Mverani iye.’”—Luka 9:35.
10 Mu zolembera zimenezi, kodi Mulungu anali kunena kuti iyemwiniyo anali mwana wake wamwamuna, kuti anadzituma iyemwini, ndi kuti anadzivomereza iyemwini? Ayi, Mulungu Atate, Mlengi, anali kunena kuti anatumiza Mwana wake Yesu, munthu wosiyana, kudzachita ntchito ya Mulungu. Chotero, kupyola m’Malemba a Chigriki onse mawu akuti “Mwana wa Mulungu” akugwiritsiridwa ntchito kulozera kwa Yesu. Koma palibe ndi pamodzi pomwe pamene timawona mawu akuti ‘Mulungu Mwana,’ popeza Yesu sanali Mulungu Wamphamvuyonse. Iye anali Mwana wa Mulungu. Iwo ali anthu aŵiri osiyana, ndipo palibe “chinsinsi” cha maphunziro a zaumulungu chomwe chingasinthe chowonadi chimenecho.
Atate ali Wamkulu pa Mwana
11. Ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti Mulungu anali wokulira pa iye?
11 Yesu anadziŵa kuti iye sanali wofanana ndi Atate wake koma m’njira iriyonse iye anali m’malo otsika. Iye anadziŵa kuti anali Mwana wokondedwa yemwe anali ndi chikondi chozama kaamba ka Atate wake. Chimenecho ndicho chifukwa chake, nthaŵi ndi nthaŵi, Yesu anapanga ndemanga zonga zotsatirazi: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha koma chimene awona Atate achichita, ndicho.” (Yohane 5:19) “Pakuti ndinatsika kumwamba, sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha iye amene anandituma ine.” (Yohane 6:38) “Chiphunzitso changa sichiri changa, koma cha iye amene anandituma ine.” (Yohane 7:16) “Ine ndimdziwa iye [Mulungu], chifukwa ndiri wochokera kwa iye, nandituma ine Iyeyu.” (Yohane 7:29) Yemwe anatumiza ali wamkulu. Yemwe anatumizidwa ali wochepera, mtumiki. Mulungu ndiye wotumiza. Yesu ali yemwe anatumizidwa. Iwo sali olingana. Monga mmene Yesu anachilongosolera icho: “Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake, kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye.”—Yohane 13:16.
12. Ndi fanizo lotani limene limasonyeza malo otsika a Yesu kwa Atate?
12 Ichi chapangidwanso kukhala chomvekera mu fanizo limene Yesu anapereka. Iye anayerekeza Atate wake, Yehova Mulungu, ndi mwini wa munda wa mpesa yemwe anapita kutali ndi kusiya munda wa mpesa m’manja mwa olima—omwe mwachiwonekere anachitira chithunzi atsogoleri achipembedzo Achiyuda. M’kupita kwa nthaŵi, mwiniwake anatumiza kapolo kutenga zina za zipatso kuchokera m’munda wa mpesa, koma olimawo anamumemya kapoloyo ndi kumtumiza iye wopanda kanthu. Kenaka mwiniwake anatumiza kapolo wachiŵiri, ndipo chinthu chofananacho chinachitika. Iye anatumiza kapolo wachitatu, yemwe anapezanso kachitidwe kofananako. Kenaka mwiniwake (Mulungu) ananena kuti: “Ndidzatumiza Mwana wanga [Yesu] amene ndikondana naye. Kapena akamchitira iye ulemu.” Koma olima oipawo ananena kuti: “‘Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.’ Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha.” (Luka 20:9-16) Kachiŵirinso, ichi chimachipangitsa icho kukhala chowonekera kuti Yesu ali wogonjera kwa Atate, wotumizidwa ndi Atate kudzachita chifuniro cha Atate.
13. Ndi ndemanga zowonekera bwino zotani za Baibulo zomwe zimasonyeza kuti Mulungu anali wokulira pa Yesu?
13 Yesu iyemwini ananena kuti: “Atate ali wamkulu pa ine.” (Yohane 14:28, NW) Tifunikira kukhulupirira Yesu, popeza kuti iye motsimikizirika anadziŵa chowonadi ponena za unansi wake kwa Atate wake. Mtumwi Paulo anadziŵanso kuti Mulungu anali wokulira pa Yesu, ndipo iye ananena kuti: “Mwana yemwe [Yesu] adzagonjetsedwa kwa . . . Mulungu.” (1 Akorinto 15:28) Ichi chikuwonedwa mowonjezereka m’ndemanga ya Paulo pa 1 Akorinto 11:3: “Mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” Yesu anavomereza kuti iye anali ndi Mulungu wokulira pamene ananena kwa ophunzira ake kuti: “Ndikwera kunka kwa Atate wanga ndi Atate wanu ndi Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.”—Yohane 20:17.
14. Ndi zitsanzo zina ziti za m’malemba zomwe zimasonyeza kuti Yesu sanali Mulungu Wamphamvuyonse?
14 Yesu anatchula ukulu wa Mulungu pamene amayi wa aŵiri a ophunzirawo anamfunsa iye kuti ana ake akakhale mmodzi kulamanja ndi wina kulamanzere kwa Yesu pamene akadza mu Ufumu wake. Iye anayankha kuti: “Kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere sikuli kwanga kupatsa.” (Mateyu 20:23) Ngati Yesu anali Mulungu Wamphamvuyonse, kukanakhala kwake kupatsa. Koma sizinali tero. Kupatsa kunali kwa Atate wake. Mofananamo, pamene ankalongosola ulosi wake wonena za mapeto a dongosolo iri la zinthu, Yesu ananena kuti: “Koma za tsiku ilo, kapena nthaŵi yake sadziŵa munthu, ngakhale angero m’mwamba, ngakhale Mwana, koma Atate ndiye.” (Marko 13:32) Ngati Yesu anali Mulungu Wamphamvuyonse, iye akanadziŵa tsiku limenelo ndi ora. Koma sanadziwe chifukwa chakuti sanali Mulungu wodziŵa Zonse. Iye anali Mwana wa Mulungu ndipo sanadziŵe chirichonse, chimene Atate wake anadziŵa.
15. Pamene Yesu anali pafupi kufa, ndimotani mmene iye anasonyezera kugonjera kwa Mulungu?
15 Pamene Yesu anali pafupi kufa, iye anasonyeza chigonjero kwa Atate wake m’kupemphera kuti: “Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine; koma si kufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.” (Luka 22:42) Ndi kwandani kumene Yesu anali kupemphera? Kwa iyemwini? Ayi, iye anali kupemphera kwa Atate wake wakumwamba. Ichi chimveketsedwa bwino mwa kunena kwake kuti: “Koma si kufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitidwe.” Ndipo kenaka, pa imfa yake, Yesu anafuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiiranji ine?” (Marko 15:34) Kodi nkwa ndani kumene Yesu ankalirira? Kwa iyemwini? Ayi, iye ankalirira kwa Atate wake omwe anali m’mwamba.
16. Ndimotani mmene imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu zimasonyezera kuti iye sakanakhala Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini?
16 Pambuyo pa kufa kwa Yesu, iye anali m’manda chifupifupi kwa masiku atatu. Kodi ndani yemwe anamuukitsa? Popeza kuti anali wakufa, iye sakanakhoza kudziwukitsa iyemwini. Ndipo ngati iye sanali wakufa kwenikweni, kenaka iye sakanakhoza kulipira dipo kaamba ka Adamu. Koma iye anafadi ndipo sanakhalepo kwa chifupifupi masiku atatu. Mtumwi Petro akutiwuza ife yemwe anaukitsa Yesu: “Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa.” (Machitidwe 2:24) Wokulira, Mulungu Wamphamvuyonse, anawukitsa wotsikayo, Mwana wake wokondedwa, Yesu, kuchokera kwa akufa. Kuchitira chitsanzo: Pamene Yesu anawukitsa Lazaro kuchokera kwa akufa, kodi ndani anali wokulira? Yesu anali wokulira popeza kuti anali wokhoza kuwukitsa Lazaro kuchokera kwa akufa. (Yohane 11:41-44) Chinali chofananacho pamene Mulungu anaukitsa Yesu. Mulungu anali wokulira popeza kuti anali wokhoza kuwukitsa Yesu kuchokera kwa akufa.
17. Ndi umboni wina wotani womwe ulipo wakuti Yesu sanali Mulungu?
17 Yesu mothekera sakanakhala Mulungu iyemwini popeza Yesu analengedwa ndi Mulungu. Onani mmene Benjamin Wilson’s Emphatic Diaglott imaikira Apocalypse (Chivumbulutso) mutu 3, versi 14: “Zinthu izi ananena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yowona [Yesu], chiyambi cha chilengedwe cha Mulungu, (NW).” Mofananamo, Akolose 1:15, 16 amanena za Yesu kuti: “Amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko . . . Zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.” Chotero m’mwamba Mulungu Wamphamvuyonse analenga mwachindunji Mwana wake ndipo kenaka “mwa iye,” kapena “kupyolera mwa iye,” analenga zinthu zina, mokulira monga mmene munthu wa luso la zopangapanga angakhale ndi wolembedwa ntchito wophunzitsidwa bwino kuchita ntchito kaamba ka iye. Zinthu zimenezo zimene zinalengedwa “kupitira mwa iye” sizinaphatikizepo Yesu iyemwini, popeza kuti Mulungu anali atamulenga kale. Chotero, iye akutchedwa “woyamba kubadwa,” “wobadwa yekha.” Pamene mwana ali woyamba kubadwa, wobadwa yekha, sichimatanthauza ndi pang’ono pomwe kuti mwanayo ali wofanana ndi atate wake. Chimatanthauza nthaŵi zonse kuti pali maumunthu aŵiri osiyana olowetsedwamo, atate ndi mwana.
Mzimu Woyera—Munthu kapena Mphamvu Yogwira Ntchito?
18. Nchiyani chomwe Baibulo limaphunzitsa ponena za mzimu woyera?
18 Bwanji ponena za woyerekezedwa kukhala munthu wachitatu wa Utatu, mzimu woyera, wonenedwa kukhala wofanana mu mphamvu, m’kulingana, ndi kusafa kwa Atate ndi Mwana? Kulibe kulikonse m’Baibulo kumene mzimu woyera unatchulidwa ndi Mulungu ndi Kristu kukhala wolingana ndi iwo. Mwachitsanzo, chochitika chimodzi cha ubatizo wa Yesu, Marko 1:10 amasonyeza kuti mzimu woyera unadza pa Yesu “monga nkhunda,” osati mu mkhalidwe waumunthu. Mzimu woyera sunali munthu winawake yemwe anadza kwa Yesu koma unali mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Mphamvu imeneyo yochokera kwa Mulungu inamtheketsa Yesu kuchiritsa odwala ndi kuwukitsa akufa. Pa Luka 5:17 pamanena mu Diaglott: “Mphamvu Yokulira ya Ambuye [Mulungu] inali pa iye [Yesu] kuchiritsa.” Pambuyo pake, pa Pentekoste, atumwi anapatsidwanso mphamvu kuchokera kwa Mulungu kuchiritsa odwala ndi kuwukitsa akufa. Kodi chimenecho chinawapangitsa iwo kukhala mbali ina ya “mutu wa mulungu”? Ayi, iwo anangopatsidwa kokha mphamvu kuchokera kwa Mulungu, kudzera mwa Kristu, kuchita chimene anthu mwachibadwa sakanakhoza kuchita.
19. Nchifukwa ninji chiri chosathekera kaamba ka mzimu woyera kukhala munthu wachitatu wa Utatu?
19 Mphamvu yogwira ntchito imodzimodziyo ikutchulidwa pa Aefeso 5:18, pamene Paulo akulangiza kuti: “Mudzale naye mzimu.” Mofananamo, Machitidwe 7:55 amanena kuti Sitefano “anadzazidwa ndi mzimu woyera.” Ndipo pa Pentekoste, otsatira a Yesu “onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 2:4) Kodi munthu angakhoze kudzala ndi munthu wina? Ayi, koma iye angakhoze kudzazidwa ndi mphamvu imene imadza kuchokera kwa Mulungu. Mzimu woyera umenewo uli magwero ofananawo amene Mulungu anagwiritsira ntchito kulenga chilengedwe. Monga mmene Genesis 1:2 amanenera: “Ndipo mzimu wa Mulungu unali kufungatira pamwamba pa madzi.”
20. Kodi ndi masomphenya otani amene Sitefano anawona amene mowonjezereka amachitira chitsanzo kuti Utatu suli chowonadi?
20 Pambuyo pa kuwukitsidwa kwa Yesu, Sitefano anali ndi masomphenya am’mwamba ndipo “anawona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu ali kuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.” (Machitidwe 7:55) Chotero, anthu aŵiri osiyana anawonedwa m’mwamba: (1) Mulungu ndi (2) Yesu Kristu wowukitsidwa. Palibe mzimu woyera umene ukutchulidwa m’masomphenya amenewa chifukwa chakuti siunali munthu wachitatu aliyense wa Utatu. Mzimu woyera, pokhala mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, ukachokera kwa Mulungu koma osati monga munthu wokhalako wosiyana. Chimenecho ndicho chifukwa chake Sitefano anangowona kokha anthu aŵiri, osati atatu.
21, 22. (a) Kodi ndi kuvomereza kotani kumene encyclopedia ya chipembedzo imapanga ponena za mzimu woyera? (b) Kodi ndi nsonga zotani zimene nkhani yathu yotsatira idzaphatikiza?
21 Ponena za mzimu woyera, New Catholic Encyclopedia yavomereza kuti: “C[hipangano] C[hakale] mwachiwonekere sichimasonyeza mzimu wa Mulungu monga munthu, ngakhale m’lingaliro la nthanthi losamalitsa, kapena m’lingaliro la zinenero za kum’mwera cha kumadzulo kwa Asia. Mzimu wa Mulungu uli kokha mphamvu ya Mulungu. Ngati iwo nthaŵi zina umaimiridwa monga wosiyana kuchokera kwa Mulungu, icho chiri chifukwa chakuti mpweya wa Yahweh umagwira ntchito cha kunja.” Iyo inalongosolanso kuti: “Ochulukira a malemba a mu C[hipangano] C[hatsopano] amavumbula mzimu wa Mulungu kukhala chinachake, osati winawake; ichi chikuwoneka makamaka m’kulingana pakati pa mzimu ndi mpamvu ya Mulungu.”
22 M’kayang’anidwe ka nsonga zonsezi, “magwero” amenewa a chiphunzitso cha Utatu wa Chikristu cha Dziko sangakhale owona. Mawu a Mulungu enieniwo amatsutsa kudzinenera kumeneko. Iwo amasonyeza mowonekera bwino kuti Yehova Mulungu ali Atate wachikondi ndi kuti Yesu Kristu ali Mwana wake wokondedwa, Mwana yemwe anali ndi chikondi choterocho kaamba ka Atate wake kotero kuti anali wofunitsitsa kukhala womvera kufikira imfa. Ngakhale kuli tero, ena amatsutsa kuti pali malemba omwe amawoneka kukhala akusonyeza kuchirikiza kaamba ka Utatu, chotero m’nkhani yathu yotsatira, tidzalingalira ena a iwo. Ndiponso, tidzakambitsirana chifukwa chimene chiphunzitso chimenechi chakhala mbali yofunika yotero ya Chikristu cha Dziko ndi kumene chinachokera.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchiyani chimene Baibulo limaphunzitsa ponena za Mulungu ndi ponena za Yesu?
◻ Ndimotani mmene Malemba amasonyezera unansi wa Atate ndi Mwana?
◻ Ndi malemba ena ati amene amasonyeza kuti Mulungu anali wokulira pa Yesu?
◻ Nchifukwa ninji mzimu woyera sungakhale mbali ya Utatu?
[Chithunzi patsamba 13]
Yesu analengeza kuti: “Atate ali wokulira pa ine”