Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 23 tsamba 191-202
  • Gulu Lowoneka la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gulu Lowoneka la Mulungu
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • GULU LOWONEKA LA MULUNGU—LAKALE NDI LATSOPANO
  • CHITSANZO CHA M’ZAKA ZA ZANA LOYAMBA
  • CHILANGIZO CHATEOKRATIKI LEROLINO
  • KUTSOGOZA GULU LAPADZIKO LONSE LAPANSI
  • MISONKHANO MKATI MWA MIPINGO
  • KUTUMIKIRA MULUNGU LIMODZI NDI GULU LAKE
  • Kodi Yehova Amatsogolera Motani Gulu Lake?
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Khalani Otetezereka m’Gulu Lolinganizidwa la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Ndimotani Mmene Yehova Amatsogozera Gulu Lake?
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Yehova Akutsogolera Gulu Lake
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 23 tsamba 191-202

Mutu 23

Gulu Lowoneka la Mulungu

1. Kodi Baibulo limanenanji ponena za gulu losawoneka la Mulungu?

KODI NCHIFUKWA NINJI tingakhale otsimikizira kuti Mulungu ali ndi gulu lowoneka? Chifukwa chimodzi nchakuti iye ali ndi gulu losawoneka. Yehova analenga akerubi, aserafi ndi angelo ena ambiri kuti achite chifuniro chake kumwamba. (Genesis 3:24; Yesaya 6:2, 3; Salmo 103:20) Yesu Kristu ndiMkulu wa angelo woposa ndi wopitirira onsewa. (1 Atesalonika 4:16; Yuda 9; Chivumbulutso 12:7) Baibulo limafotokoza angelo kukhala akulinganizidwa kukhala “mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro.” (Akolose 1:16; Aefeso 1:21) Iwo onse amatumikira molamulidwa ndi Yehova, akumachita mogwirizana ntchito imene iye akuwauza kuchita.—Danieli 7:9, 10; Yobu 1:6; 2:1.

2. Kodi njira imene Mulungu analengera thambo lathu lowoneka imasonyeza motani kuti iye amaika chigogomezero chachikulu pa gulu?

2 Tikupezanso lingaliro la kufunika kumene Mulungu amaika pa gulu pamene tilingalira zolengedwa zake zowoneka. Mwa chitsanzo, pali mabiliyoni zikwi zambiri za nyenyezi m’thambo amene alinganizidwa m’magulu akulu otchedwa milalang’amba. Milalang’amba imeneyi imayenda m’mlengalenga m’njira yadongosolo, ndipo chomwechonso nyenyezi zosiyanasiyana ndi mapulaneti mkati mwa milalang’amba imeneyi. Mwa chitsanzo, pulaneti lathu Dziko Lapansi, chaka chirichonse limapanga ulendo wozungulira dzuwa, limene liri nyenyezi yathu yapafupi kwambiri, m’masiku 365, maola 5, maminitsi 48 ndi masekendi 45.51 zenizeni. Inde, thambo lowoneka nlolinganizidwa kwambiri!

3. Kodi kulinganizidwa bwino pakati pa zolengedwa zosawoneka za Mulungu ndi thambo lake lowoneka kumatiphunzitsa chiyani?

3 Kodi kulinganizidwa kodabwitsa kumeneku pakati pa zolengedwa zosawoneka za Mulungu ndi m’thanbo lake lowoneka kumatiphunzitsa kanthu kena? Inde, kumatiphunzitsa kuti Yehova ndiMulungu wa dongosolo. Ndithudi, pamenepa, Mulungu woteroyo sakasiya anthu padziko lapansi amene amamkondadi opanda chitsogozo ndi gulu.

GULU LOWONEKA LA MULUNGU—LAKALE NDI LATSOPANO

4, 5. Kodi tikudziwa motani kuti Mulungu anatsogoza anthu ake m’njira yolinganizidwa m’nthawi ya Abrahamu ndi ya mtundu wa Israyeli?

4 Baibulo limasonyeza kuti Yehova nthawi zonse watsogoza atumiki ake m’njira yolinganizidwa. Mwa chitsanzo, anthu a chikhulupiriro monga ngati Abrahamu anatsogoza mabanja awo ndi atumiki m’kulambira Yehova. Yehova analengeza chifuniro chake kwa Abrahamu mwa kulankhula naye. (Genesis 12:1) Ndipo Mulungu anamuuza kuti apitirize chidziwitso chimenechi kwa ena, akumati: “Ndamdziwa [Abrahamu] kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova.” (Genesis 18:19) Panopa panali kakonzedwe kadongosolo kakuti kagulu ka anthu kalambire Yehova moyenera.

5 Pambuyo pake, pamene Aisrayeli anawonjezeka m’kuchuluka nakhala mamiliyoni ambiri, Yehova sanalole aliyense kulambira m’njira yakeyake, yolekana ndi kakonzedwe kalikonse kolinganizidwa. Ayi, Aisrayeli anapangidwa kukhala mtundu wa alambiri olinganizidwa. Mtundu wa Israyeli unatchedwa “mpingo wa Yehova.” (Numeri 20:4; 1 Mbiri 28:8, NW) Ngati mukanakhala mlambiri wowona wa Yehova kale pa nthawi imeneyo, mukadafunikira kukhala mbali ya mpingo wa alambiri umenewo, osati wolekana nawo.—Salmo 147:19, 20.

6. (a) Kodi Mulungu anasonyeza motani kuti chiyanjo chake chinali pa atsatiri a Kristu? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti Akristu analinganizidwa kaamba ka kulambira?

6 Kodi mkhalidwe unali wotani m’zaka za zana loyamba? Baibulo limasonyeza kuti chiyanjo cha Yehova chinali pa atsatiri a Mwana wake Yesu Kristu. Yehova anatsanulira pa iwo mzimu wake woyera. Kuti asonyeze kuti iye tsopano anali kugwiritsira ntchito gulu Lachikristu limeneli koposa ndi mtundu wa Israyeli, iye anapatsa Akristu ena oyambirira mphamvu ya kuchiza odwala, kuukitsa akufa ndi kuchita zozizwitsa zina. Simungawerenge Malemba Achikristu Achigiriki popanda kukhutiritsidwa maganizo ndi chenicheni chakuti Akristu analinganizidwa kaamba ka kulambira. Kunena zowona, iwo analamulidwa kosankhana pamodzi kaamba ka chifuno chimenechi. (Ahebri 10:24, 25) Motero ngati mukanakhala mlambiri wowona wa Yehova m’zaka za zana loyamba, mukanafunikira kukhala mbali ya gulu Lachikristu.

7. Kodi tikudziwa motani kuti Yehova sanagwiritsire ntchito magulu ambiri m’nyengo ina iriyonse?

7 Kodi Yehova anagwiritsirapo ntchito magulu oposa limodzi mkati mwa nyengo ya nthawi iriyonse? M’nthawi ya Nowa, Nowa yekha ndi awo okhala naye mkati mwa chingalawa anali ndi tchinjirizo la Mulungu ndipo anapulumuka madzi achigumula. (1 Petro 3:20) Ndiponso, m’zaka za zana loyamba munalibe magulu Achikristu awiri kapena ambiri. Mulungu anachita mdi limodzi lokhalo. Kunali chabe “Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.” (Aefeso 4:5) Momwemonso m’nthawi yathu Yesu Kristu ananeneratu kuti kukakhala magwero amodzi okha a chilangizo chauzimu kaamba ka anthu a Mulungu.

8. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti kukakhala gulu limodzi lokha lowoneka la Mulungu padziko lapansi m’nthawi yathu?

8 Posimba kukhalapo kwake mu ulamuliro Waufumu, Yesu anati: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indethu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) Pa kubweranso kwake mu ulamuliro Waufumu m’chaka cha 1914, kodi Kristu anapeza kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kakupereka “chakudya” chauzimu, kapena chidziwitso? Inde, iye anapeza “kapolo” woteroyo wopangika ndi otsalira padziko lapansi a “abale” ake 144,000. (Chivumbulutso 12:10; 14:1, 3) Ndipo chiyambire 1914 mamiliyoni ambiri a anthu alandira “chakudya” chimene iwo akupereka, ndipo ayamba kutsatira chipembedzo chowona limodzi nawo. Gulu la atumiki a Mulungu limeneli likudziwika monga Mboni za Yehova.

9. (a) Kodi nchifukwa ninji atumiki a Mulungu ali ndi dzinalo Mboni za Yehova? (b) Kodi nchifukwa ninji amatcha malo awo a kulambira Nyumba Zaufumu?

9 Mboni za Yehova zimayang’ana kwa Mulungu ndi Mawu ake kaamba ka chilangizo m’zonse zimene izo zimachita. Dzina lawo lenilenilo Mboni za Yehova limasonyeza kuti ntchito yawo yaikulu ndiyo kuchitira umboni dzina ndi ufumu wa Yehova Mulungu, monga momwedi Kristu anachitira. (Yohane 17:6; Chivumbulutso 1:5) Ndiponso, izo zimatcha malo kumene zimasonkhanira kulambira kukhala Nyumba Yaufumu chifukwa chakuti ufumu wa Mulungu wochitidwa ndi Mesiya, kapena Kristu, ndiwo mutu wankhani wa Baibulo lonse. Popeza kuti nkwachiwonekere kuti Chikristu cha m’zaka za zana loyamba chinali ndi chivomerezo cha Mulungu, Mboni za Yehova zimapanga gulu lawo mochitsanzira. Tiyeni tiyang’ane mwachidule gulu Lachikristu loyambirira limenelo ndi kuwonano zofanana ndi gulu lowoneka la Mulungu lerolino.

CHITSANZO CHA M’ZAKA ZA ZANA LOYAMBA

10. Kodi mbali zina za gulu Lachikristu la m’zaka za zana loyamba zinali zotani?

10 Kulikonse kumene kunali Akristu m’zaka za zana loyamba, iwo anasonkhana pamodzi m’timagulu kaamba ka kulambira. Mipingo imeneyi inasonkhana nthawi ndi nthawi kaamba ka utsamwali ndi kuphunzira. (Ahebri 10:24, 25) Ntchito yawo yaikulu inali kulalikira ndi kuphunzitsa ponena za ufumu wa Mulungu, monga momwedi Kristu anachitira. (Mateyu 4:17; 28:19, 20) Ngati chiwalo cha mpingo chinatembenukira ku njira yoipa ya moyo, icho chinali kuchotsedwa mu mpingo.—1 Akorinto 5:9-13; 2 Yohane 10, 11.

11, 12. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti mpingo Yachikristu yoyambirira inalandira chitsogozo ndi chilangizo kuchokera kwa atumwi ndi “akulu” m’Yerusalemu? (b) Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi chilangizo “chateokratiki”? (c) Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo cha kulandira kwa mipingo chilangizo choterocho?

11 Kodi mipingo Yachikristu imeneyo m’zaka za zana loyamba inali yosadalirana, uliwonse ukamapanga zosankha zakezake pa zinthu? Ayi, Baibulo limasonyeza kuti iyo inagwirizana m’chikhulupiriro chimodzi Chachikristu. Mipingo yonse inalandira chitsogozo ndi chilangizo kuchokera pamagwero amodzi. Motero, pamene mkangano unabuka pa nkhani ya mdulidwe, mpingo kapena munthu aliyense payekha sanadzisankhire chochita. Ayi, koma, m’malo mwake, mtumwi Paulo, Barnaba ndi ena anauzidwa “akwere kumka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.” Pamene amuna achikulire amenewa, mothandizidwa ndi Mawu a Mulungu ndi ‘mzimu wake woyera,’ anapanga chosankha chawo, iwo anatumiza amuna okhulupirika kukauza mipingoyo.—Machitidwe 15:2, 27-29.

12 Kodi nchiyani chimene chinatulukapo mwa kulandira kwa mipingoyo chitsogozo ndi chilangizo chateokratiki, kapena choperekedwa ndi Mulungu chimenechi? Baibulo limati: “Pamene [mtumwi Paulo ndi atsamwali ake] anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu. Kotero mipingoyo inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiwerengo chawo tsiku ndi tsiku.” (Machitidwe 16:4, 5) Inde, mipingo yonse inagwirizana ndi zimene bungwe la akulu limenelo m’Yerusalemu lidagamula, ndipo iyo inakhala yamphamvu kwambiri m’chikhulupiriro.

CHILANGIZO CHATEOKRATIKI LEROLINO

13. (a) Kodi gulu lowoneka la Mulungu lerolino limalandira chitsogozo kuchokera pamalo otani padziko lapansi ndipo kupyolera mwa bungwe la amuna lotani? (b) Kodi bungwe lolamulira liri ndi chigwirizano chotani ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

13 Gulu lowoneka la Mulungu lerolino limalandiranso chitsogozo ndi chilangizo chateokratiki. Pamalikulu a Mboni za Yehova m’Brooklyn, New York, pali bungwe lolamulira la amuna achikulire Achikristu ochokera m’mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi amene akupereka uyang’aniro wofunika ku za zochita-padziko lonse lapansi za anthu a Mulungu. Bungwe lolamulira limeneli lapangika ndi ziwalo za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Limatumikira monga mneneri wa “kapolo” wokhulupirika ameneyo.

14. Kodi bungwe lolamulira la anthu a Mulungu limadalira pa chiyani m’kupanga zosankha zake?

14 Amuna a bungwe lolamulira limenelo, mofanana ndi atumwi ndi akulu m’Yerusalemu, ali ndi zaka zambiri za kudziwa m’ntchito ya Mulungu. Koma iwo samadalira pa nzeru yaumunthu m’kupanga zosankha. Ayi, pokhala olamuliridwa mwateokratiki, iwo amatsatira chitsanzo cha bungwe lolamulira loyambirira m’Yerusalemu, limene zosankha zake zinazikidwa pa Mawu a Mulungu ndipo zinapangidwa motsogozedwa ndi mzimu woyera.—Machitidwe 15:13-17, 28, 29.

KUTSOGOZA GULU LAPADZIKO LONSE LAPANSI

15. Kodi nchifukwa ninji mawu a Yesu pa Mateyu 24:14 amasonyeza kuti Mulungu akakhala ndi gulu lalikulu padziko lapansi mkati mwa nthawi ya mapeto?

15 Yesu Kristu anapereka lingaliro la ukulu wa gulu limene Mulungu akakhala nalo padziko lapansi mkati mwa nthawi ya mapeto ino pamene iye anati: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Taganizirani kuchuluka kwambiri kwa ntchito yofunika kuuza anthu a dziko lapansi mamiliyoni zikwi zambiri ponena za ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa. Kodi gulu Lachikristu lamakono, limene limayang’ana ku bungwe lake lolamulira kaamba ka chitsogozo ndi chilangizo, nlokonzekera kuchita ntchito yaikulu imeneyi?

16. (a)Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zakhazikitsa mafakitale ambiri aakulu osindikizira? (b) Kodi nchiyani chimene chikupangidwa m’mafakitale amenewa?

16 Mboni za Yehova tsopano zikulalikira uthenga Waufumu m’maiko oposa 200 ndi zisumbu za m’nyanja padziko lonse lapansi. Kuti athandize ofalitsa Aufumu opitirira 3,500,000 (mu 1988) kuchita ntchito imeneyi, mafakitale aakulu osindikizira akhazikitsidwa m’maiko ambiri. Munomo Mabaibulo ndi mabukhu ofotokoza Baibulo amapangidwa ochuluka kwambiri. Tsiku lirilonse logwira ntchito, pa averaji, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! oposa mamiliyoni awiri amasindikizidwa ndi kutumizidwa kuchokera pamafakitale amenewa.

17. (a)Kodi nchifukwa ninji mabukhu ofotokoza Baibulo amenewa akukonzedwa? (b) Kodi mukupemphedwa kuchitanji?

17 Mabukhu ofotokoza Baibulo onsewa amakonzedwa kuti athandize anthu kukula m’kudziwa zifuno zabwino kwambiri za Yehova. Kunena zowona, mawuwo “Yolengeza Ufumu wa Yehova” ali mbali ya dzina la magaziniwo Nsanja ya Olonda. Mukupemphedwa kukhala ndi phande m’kugawira mabukhu ofotokoza Baibulo amenewa ndi kufotokozera ena chowonadi Chabaibulo chimene chirimo. Mwachitsanzo, kodi pali munthu wina amene mungamuuze chidziwitso chofunika chimene mwaphunzira m’bukhu lino, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi?

18. (a) Kodi gulu la Mulungu lerolino ndigulu lamtundu wotani? (b)Kodi nchifukwa ninji anthu a Mulungu tsopano akufunikira chilimbikitso chochuluka?

18 Mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, gulu la Mulungu lerolino ndigulu la olalikira Ufumu odzipatulira ndi obatizidwa. Ndipo lakhazikitsidwa kuti lithandize ziwalo zake zonse kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira imeneyi. Anthu amenewa amafuna chisonkhezero chambiri ndi chilimbikitso chauzimu, popeza kuti Satana ndi awo amene iye ali wokhoza kukopa amatsutsa uthenga Waufumu. Otsutsa oterowo anachititsa Yesu kuphedwa chifukwa cha kuulalikira, ndipo Baibulo limachenjeza kuti atsatiri ake akazunzidwanso.—Yohane 15:19, 20; 2 Timoteo 3:12.

19. (a) Kodi ndani amene aperekedwa tsopano kuthandiza ndi kulimbikitsa anthu a Mulungu? (b) Kodi mpingo ukutetezeredwa motani ku ziyambukiro zoipa zimene zikatha kuuipitsa?

19 Monga nomwe kunaliri m’zaka za zana loyamba chomwechonso lerolino “amuna achikulire,” kapena akulu, amaikidwa kuti athandize ndi kulimbikitsa mpingo uliwonse. Iwo angakuthandizeninso ndi uphungu Wabaibulo kuti mulimbane ndi mavuto osiyanasiyana. Akulu amenewa amatetezeranso “gulu lankhosa la Mulungu.” Motero, ngati chiwalo cha mpingo chitembenukira kunjira yoipa ya moyo ndipo chikukana kusintha, “amuna achikulire” amalinganiza kuti munthu woterowo akutulutsidwa, kapena kuchotsedwa, mu mpingo. Motero mpingo wathanzi ndi woyera mwauzimu umasungidwa.—Tito 1:5; 1 Petro 5:1-3; Yesaya 32:1, 2; 1 Akorinto 5:13.

20. (a) Kodi ndani m’zaka zazana loyamba anatumizidwa ndi bungwe lolamulira m’Yerusalemu, ndipo kaamba ka chifukwa chotani? (b) Kodi ndani akutumizidwa ndi bungwe lolamulira lerolino?

20 Momwemonso, monga momwedi bungwe lolamulira m’Yerusalemu linatumizira oimira apadera, monga ngati Paulo ndi Sila, kukapereka malangizo ndi kupereka chilimbikitso kwa anthu a Mulungu, chomwechonso bungwe lolamulira la lerolino m’nthawi ya mapeto ino. (Machitidwe 15:24-27, 30-32) Kawiri pachaka minisitala wodziwa, wotchedwa woyang’anira dera, amauzidwa kutha sabata limodzi ndi mpingo uliwonse m’dera lake.

21. Kodi woyang’anira dera amathandiza motani mipingo ya anthu a Mulungu?

21 Pali mipingo ya Mboni za Yehova yopitirira kwambiri 60,000 padziko lonse lapansi, ndipo imeneyi yagawidwa kukhala madera opangika ndi mipingo yokwanira 20 lirilonse. Pochezetsa mipingoyo m’dera lake, woyang’anira dera amalimbikitsa mboni Zaufumu mwa kutsagana nazo m’ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa. Kuphatikiza pa kuzisonkhezera m’njira imeneyi, iye amapereka malingaliro kuti azithandize kuchita bwino muuminisitala wawo.—Machitidwe 20:20, 21.

22. (a) Kodi ndikakonzedwe kowonjezereka kotani kolimbikitsira anthu a Mulungu kamene kamapangidwa kawiri pachaka? (b) Kodi chiitano chimene chikuperekedwa kwa inu nchotani?

22 Chisonkhezero ndi chilimbikitso chowonjezereka chimaperekedwa pamene, kawirikawiri kawiri pachaka, mipingo m’dera lirilonse imasonkhana pamodzi kaamba ka msonkhano wa tsiku limodzi kapena wamasiku awiri. Panthawi zimenezi pangakhale anthu ochokera pamazana awiri kapena atatu kufikira ku 2,000 kapena kupitirirapo ofikapo. Mukupemphedwa kufika pa wotsatirapo m’dera lanu. Tikutsimikizira kuti mudzawona msonkhanowo kukhala wolimbikitsa mwauzimu ndi wopindulitsa kwa inu.

23. (a) Kodi ndimisonkhano ina yotani imene imachitidwa kamodzi pachaka? (b) Kodi umodzi wa misonkhano imeneyi unali waukulu motani?

23 Ndiyeno, kamodzi pachaka, msonkhano wokulirapo kwambiri wotchedwa Msonkhano Wachigawo ungachitidwe kwamasiku angapo. Bwanji osapanga kuyesayesa kwenikweni kuti mufikepo ndi kudziwonera mmene msonkhano woterowo ungakhalire wokondweretsa ndi wopindulitsa mwauzimu? Zaka zingapo, mmalo mwa misonkhano yachigawo, pakhala misonkhano yokulirapo ya mtundu kapena yamitundu yonse. Waukulu koposa wochitidwa chiyambire m’malo amodzi unali mu Yankee Stadium ndi Polo Grounds ya Mzinda wa New York kwa masiku asanu ndi atatu mu 1958. Panthawi imeneyo anthu 253,922 anasonkhanira nkhani yapoyerayo “Ufumu wa Mulungu Ukulamulira —Kodi Mapeto a Dziko Ayandikira?” Kuyambira panthawi imeneyo palibe malo alionse amene akhala akulu mokwanira kukwana khamu lalikulu loterolo, motero makonzedwe apangidwa kaamba ka malo m’mizinda yambiri yaikulu oti agwiritsidwe ntchito kaamba ka misonkhano yaikulu.

MISONKHANO MKATI MWA MIPINGO

24. Kodi ndimisonkhano isanu yamlungu ndi mlungu yotani imene imachitidwa ndi mipingo ya anthu a Mulungu?

24 Bungwe lolamulira la Mboni za Yehova limalinganizanso programu yogwirizanitsidwa ya chilangizo Chabaibulo imene imachitidwa m’mipingo yonse ya anthu a Yehova. Mpingo uliwonse umakhala ndi misonkhano isanu pamlungu. Imeneyi ndiyo Sukulu Yautumiki Wateokratiki, Msonkhano Wautumiki, Msonkhano Wapoyera, Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi phunziro labukhu lampingo. Popeza kuti inu kufikira tsopano mungakhale musanadziwe misonkhano imeneyi, tidzaifotokoza mwachidule.

25, 26. Kodi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Msonkhano Wautumiki zimatumikira chifuno chotani?

25 Sukulu Yautumiki Wateokratiki yalinganizidwa kuthandiza ophunzira kukhala ogwira mtima kwambiri m’kulankhula kwa ena ponena za ufumu wa Mulungu. Nthawi ndi nthawi, awo olembetsa amakamba nkhani zazifupi pa nkhani Zabaibulo ku kagulu konse. Ndiyeno mkulu wachidziwitso amapereka malingaliro kaamba ka kupita patsogolo.

26 Kawirikawiri pamadzulo amodzimodziwo Msonkhano Wautumiki umachitidwanso. Autilaini ya msonkhano umenewu imafalitsidwa mu Utumiki Wathu Waufumu, kope lamwezi ndi mwezi la masamba awiri kapena kupitirirapo lolembedwa ndi bungwe lolamulira. Mkati mwa msonkhano umenewu malingaliro ndi zitsanzo zopindulitsa zonena za msonkhano umenewu malingaliro ndi zitsanzo zopindulitsa zonena za njira zabwino zolankhulira ndi ena ponena za uthenga Waufumu zimaperekedwa. M’njira yofonanayo, Kristu analimbikitsa atsatiri ake ndi kuwapatsa malangizo a kuchita kwake uminisitala wawo.—Yohane 21:15-17; Mateyu 10:5-14.

27, 28. Kodi Msonkhano Wapoyera, phunziro la Nsanja ya Olonda ndi phunziro la bukhu lampingo ndimisonkhano ya mtundu wotani?

27 Msonkhano Wapoyera ndiponso phunziro la Nsanja ya Olonda kawirikawiri zimachitidwa pa Sande. Zoyesayesa zapadera zimachitidwa kuitanira anthu okondwerera chatsopano ku Msonkhano Wapoyera, umene uli nkhani Yabaibulo yokambidwa ndi minisitala woyeneretsedwa. Phunziro la Nsanja ya Olonda ndilo kukambitsiridwa kwamafunso ndi mayankho kwa nkhani Yabaibulo yoperekedwa m’kope laposachedwapa la magazini a Nsanja ya Olonda.

28 Pamene mpingo wonse ungasonkhane pa Nyumba Yaufumu kaamba ka misonkhano yondandalikidwa pamwambapoyo, timagulu tocheperapo timasonkhana m’nyumba za anthu kaamba ka phunziro labukhu lampingo lamlungu ndi mlungu. Chothandizira kuphunzira Baibulo, chonga ngati bukhu lino limene mukuwerenga, chimagwiritsidwa ntchito monga maziko a kukambitsirana Baibulo kumeneko, kumene kungafikire ku ola limodzi.

29. (a) Kodi ndichikumbutso chotani chimene Akristu owona amasunga chaka chirichonse? (b) Kodi ndani amene moyenerera amadya mkati ndi vinyo?

29 Kuphatikiza pa misonkhano yamasiku onse imeneyi, Mboni za Yehova zimachita msonkhano wapadera chaka chirichonse pa deti la imfa ya Yesu. Polinganiza choyamba kaamba ka chikumbutso cha imfa yake chimenechi, Yesu anati: “Chitani ichi chikumbukilo changa.” (Luka 22:19, 20) Mkati mwa dzoma lopanda zambiri Yesu anagwiritsira ntchito vinyo ndi mkate wosatupitsidwa monga zizindikiro za moyo umene iye anali pafupi kuperekera nsembe anthu. Motero pa chakudya Chokumbutsa chachaka ndi chaka chimenechi otsala padziko lapansi a atsatiri odzozedwa 144,000 a Kristu amasonyeza chiyembekezo chawo chakumwamba mwa kudya mkate ndi vinyo.

30. (a) Kodi ndaninso amene moyenerera amafika pa Chikumbutso, ndipo kodi ziyembekezo zawo nzotani? (b) Kodi anthu oterowo akufotokozedwa ndi Yesu motani?

30 Mamiliyoni ambiri a ena amene amafika pa Chikumbutso chimenechi m’Nyumba Zaufumu padziko lonse lapansi amakhala okondwa kukhala openyerera. Iwo nawonso amakumbutsidwa zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anachita kutheketsa kupulumutsidwa kwawo ku uchimo ndi imfa. Koma m’malo mwa kuyembekezera moyo wakumwamba, iwo amakondwera ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi. Iwo ali ngati Yohane Mbatizi, amene anadzitcha kukhala “mnzake wa mkwatiyo” koposa ndi mbali ya mkwatibwi wachiungwe wa Kristu wa ziwalo 144,000. (Yohane 3:29) Mamiliyoni ambiri a anthu amenewa ndiwo mbali ya “nkhosa zina” zimene Yesu anatchula. Izo siziri ziwalo za “kagulu kankhosa.” Komabe, monga momwe Yesu ananenera, iwo akutumikira mogwirizana ndi awo a “kagulu kankhosa,” kotero kuti onse ‘akukhala gulu limodzi.’—Yohane 10:16; Luka 12:32.

KUTUMIKIRA MULUNGU LIMODZI NDI GULU LAKE

31.Kodi pali umboni wotani wakuti Mulungu samavomereza awo amene akukhalabe mbali ya chipembedzo chonyenga ndipo chikhalirebe akuyesanso kukhala mbali ya gulu lake?

31 Nkwachiwonekere chotani nanga mmene kuliri kuti, mofanana ndi m’nthawi zakale, Yehova Mulungu ali ndi gulu lowoneka lerolino! Iye tsopano akuligwiritisira ntchito kuphunzitsa anthu kaamba ka moyo m’dongosolo lake latsopano lolungama. Komabe, sitingakhale mbali ya gulu la Mulungu ndipo, pa nthawi imodzimodziyo, kukhala mbali ya chipembedzo chonyenga. Mawu a Mulungu amati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuwunika kuyanjana bwanji ndi mdima”? . . . Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira?” Motero Mulungu akulamula kuti: “Chifukwa chake, tulukani pakati pawo, ndipo patukani.”—2 Akorinto 6:14-17.

32. (a) Ngati titi ‘tituluke pakati pawo,’ kodi tiyenera kuchitanji? (b) Kodi tidzalandira dalitso lotani ngati titsatira kachitidwe kotsimikizirika ka kutumikira Mulungu limodzi ndi gulu lake lowoneka lateokratiki?

32 Kodi kukutanthauzanji ‘kutuluka pakati pawo’? Eya, sitikakhala tikumvera lamulo limenelo mwa kukhalabe mbali ya, kapena kupereka chichirikizo ku, gulu lina lachipembedzo losiyana ndi limene Yehova Mulungu akugwiritsira ntchito. Motero ngati aliyense wa ife ali chikhalirebe wa gulu lina lachipembedzo loterolo, tifunika kupereka chidziwitso chakuti ife tikuchokamo. Ngati ife tsopano tituluka pakati pa awo amene akutsatira chipembedzo chonyenga ndi kuchitapo kanthu kotsimikizirika kutumikira Mulungu limodzi ndi gulu lake lateokratiki lowoneka, tidzakhala pakati pa awo amene Mulungu akuti: “Ndidzakhala pakati pawo ndi kuyenda pakati pawo, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”—2 Akorinto 6:16, NW.

[Chithunzi patsamba 192]

Pa nthawi ya Chigumula, Kodi Mulungu anali ndi magulu ambiri?

[Zithunzi patsamba 196]

MALIKULU ADZIKO LONSE LA A MBONI ZA YEHOVA

MAOFESI OYENDETSA NTCHITO

Makompyuta

OFESI YOSINDIKIZA YA KU BROOKLYN

Makina Osindikizira

Komangira Mabukhu

Kotumizira

[Zithunzi patsamba 197]

ENA A MAOFESI ENA AMBIRI OSINDIKIZA A WATCH TOWER

Brazil

England

South Africa

Wallkill, New York

Canada

[Zithunzi patsamba 198]

Ena a 253,922 pamsonkhano wa Mboni za Yehova mu New York

Polo Grounds

Yankee Stadium

[Chithunzi patsamba 201]

Programu ya chilangizo Chabaibulo imalandiridwa pamisonkhano ya Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena