-
Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Kodi munthu amene ali ndi mtima wofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzake angatani kuti azikondweretsa Mulungu?
Baibulo limati: “Musalole kuti thupi lanu lizikulamulirani. Chititsani ziwalo za thupi lanu kukhala zakufa ku chilakolako chofuna kugonana m’njira yolakwika.” (Akolose 3:5, Contemporary English Version) Kuti munthu achititse ziwalo zake kukhala zakufa ku zilakolako zolakwika, zimene zimachititsa munthu kuchita zinthu zoipa, munthuyo amafunika kulamulira maganizo ake. Ngati nthawi zonse mumaganizira zinthu zabwino, mukhoza kukwanitsa kuthana ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. (Afilipi 4:8; Yakobo 1:14, 15) N’zoona kuti poyamba mungavutike kulimbana ndi maganizo oipawo koma mukhoza kukwanitsa. Mulungu akukulonjezani kuti adzakuthandizani “kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.”—Aefeso 4:22-24.
-
-
Kodi N’kulakwa Kukambirana Zokhudza Kugonana pa Intaneti?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
“Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana.” (Akolose 3:5) M’malo mochititsa kuti chilakolako chogonana chikhale chakufa, kuonerera zolaula kumaonjezera chilakolako chimenechi. Kuonerera zolaula kumachititsa munthu kuti akhale wodetsedwa m’maso mwa Mulungu.
-