Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Kutengeka ndi Zithunzi Zolaula Kulibe Vuto Lililonse?
    Galamukani!—2002 | July 8
    • Kutengeka maganizo ndi nkhani za kugonana kumatisokoneza kulambira Mulungu. N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo . . . dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.”—Akolose 3:5.

      Palembali Paulo akuti chilakolako cha kugonana n’chimodzimodzi ndi kusirira koipa, kumene kuli kulakalaka kwambiri chinthu chimene munthuwe ulibe.a Kusirira koipa ndi mbali ina ya kupembedza mafano. Chifukwa chiyani? N’chifukwa chakuti kwa munthu amene akusirira chinthu chinachake amaona chinthucho kukhala chofunika kwambiri kuposa chinthu china chilichonse, ngakhale kuposa Mulungu amene. Zithunzi zolaula zimam’pangitsa munthu kumangolakalaka kugonana ndi mkazi kapena mwamuna amene si wako. Wolemba zachipembedzo wina ananena kuti: “Umangofuna mkazi kapena mwamuna amene si wako. . . . M’maganizo mwako mumangodzaza zimenezo basi. . . . Komatu chilichonse chimene timachilakalaka motere ndiye kuti tikuchilambira.”

  • Kodi Kutengeka ndi Zithunzi Zolaula Kulibe Vuto Lililonse?
    Galamukani!—2002 | July 8
    • a Pa lembali sikuti Paulo anali kunena za chilakolako choyenera chimene munthu amakhala nacho chofuna kugonana ndi munthu amene anakwatirana naye.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena