Nkhondo Yothetsa Ndhondo
NDEGE ya nkhondo yaikulu ya chiGerman inamira mkati mwa mtambo wa usiku. Inali kubwerera kwawo pambuyo pa kuwukira pa London, ndipo pamene inadutsa pa mudzi wa Essex, mabomba anaponyedwa. Limodzi la iwo linapha namwino wa patchuthi wochokera ku nkhondo mu France.
Ichi chinali chochitika chaching’ono cha Nkhondo ya Dziko ya I, koma chinali ndi zizindikiro zokulira. Chinali chitsanzo cha mmene zana la 20, kutalitali ndi kukhala lowberetsa nthaŵi pamene munthu ‘sadzaphunziranso nkhondo,’ lawona kukula kodabwitsa ponse paŵiri mu zida ndi njira zomenyera nkhondo. (Yesaya 2:2-4) Kwa zaka zikwi zingapo, nkhondo zakhala zikumenyedwa pa mtunda ndi pamwamba pa nyanja. Koma mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya I, kumenyanako kunafalikira mumlengalenga ndi pansi pa nyanja. Monga chotulukapo chake, anthu wamba omwe anali makilomita mazana angapo kuchokera ku malire omenyanirana anaphedwa ndi mabomba, ndipo masitima ambiri a pamadzi anatumizidwa pansi pa nyanja ndi masitima ankhondo oyenda pansi pa madzi osawoneka.
Ndithudi, mkati mwa nkhondo ya dziko yoyamba yowopsya imeneyo, asilikali 8 miliyoni anafa m’kumenyanako, ndipo chiŵerengero choyerekezera cha 12 miliyoni cha anthu wamba anafa ndi zochititsa zomwe zinaphatikizapo njala ndi kuwunikiridwa. “Tsoka la Nkhondo Yaikulu [Nkhondo ya Dziko ya I],” mogwirizana ndi katswiri wa mbiri yakale H. A. L. Fisher, “linali lakuti inamenyedwa pakati pa anthu otsungula koposa mu Europe pa nkhani imene anthu ochepera osaphunzira kwambiri akanaithetsa mopepuka.” Kuti alungamitse kupha kopanda chifundoko, iyo inatchedwa “nkhondo yothetsa nkhondo.” Koma mawu amenewo mwamsanga anafikira kumveka opanda pake.
Gulu la Mtendere
Mwamsanga mtendere utalengezedwa mu 1918, mbadwo wowawidwa mtima unakakamiza kuti miyezo itengedwe kutsimikizira kuti nkhondo yoteroyo siikachitikanso kachiŵiri. Chotero, Chigwirizano cha Mitundu chinabadwa mu 1919. Koma Chigwirizanocho chinali chogwiritsa mwala chachikulu. Mu 1939 dziko linalowetsedwanso mu nkhondo ya dziko—nkhondo yomwe inali yakupha kwambiri kuposa yoyambayo.
Mu Nkhondo ya Dziko ya II, mizinda yambiri inachepetsedwa kukhala bwinja, kusinthira moyo wa anthu wamba kukhala loto. Kenaka mu 1945 mabomba a atomu anaponyedwa pa Hiroshima ndi Nagasaki, kulowetsa munthu mu mbadwo wa nyukliya. Mitambo yowopsya yonga bowa yomwe inakwera pa mizinda iŵiri ya chiJapan imeneyo inali chizindikiro cha chiwopsyezo chomwe chakhalirira pa mtundu wa anthu chiyambire kalelo.
Ngakhale kuli tero, ngakhale mabomba amenewo asanagwe, makonzedwe anali kupangidwa kaamba ka kukhazikitsa gulu longa Chigwirizano cha Mitundu chosagwira ntchitocho. Chotulukapo chinali Gulu la Mitundu Yogwirizana, limene kwenikweni linali ndi zonulirapo zofananazo zonga za chinzakecho—zija za kusungirira mtendere wa dziko. Nchiyani chomwe ilo lafikiritsa? Chabwino, sipanakhale nkhondo ya dziko chiyambire 1945, koma pakhala nkhondo zazing’ono zambiri mu zimene mamiliyoni a anthu afa.
Kodi ichi chikutanthauza kuti mtundu wa anthu sudzawona nkhomwe kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu kupyolera mwa Yesaya kuti anthu ‘sadzaphunziranso nkhondo’? Ayi. Icho chimangotanthauza kuti ichi sichidzabweretsedwa ndi munthu. Baibulo, lomwe limatchedwa kuti ‘kuwunika kwa pa njira pathu,’ liri bukhu lomwe liri ndi lonjezo lowuziridwa limenelo. Ndipo liri Baibulo lomwe limasonyeza kuti palibe wina laiyense kuposa Mulungu iyemwini amene potsirizira pake adzapangitsa nkhondo kulekeka.—Salmo 119:105.
Mapeto ku Nkhondo Zonse
Monga mmene zatchulidwira m’nkhani yapitayo, panali gulu m’zana loyamba lomwe linakhazikitsa ubale wa mitundu yonse mu limene chikanakhala chosalingalirika kwa chiwalo chimodzi kuyambitsa nkhondo pa mbale wake kapena mlongo. Uwu unali mpingo Wachikristu, umene ziwalo zake zinali mlingaliro lenileni ‘zitasula malupanga awo kukhala anangwape.’ Lerolino, pamene kuli kwakuti mtundu wa munthu monga gulu sungapange njira m’kuthetsa nkhondo, kachiŵirinso pali gulu la anthu lomwe lafikiritsa chonulirapo chozizwitsa chofananachi. Kodi iwo ndani?
M’zaka za kumayambiriro kwa 1914, gulu laling’ono limeneli linali ndi chidaliro m’Baibulo. Chotero, iwo anadziŵa kuti zoyesayesa za anthu za kuthetsa nkhondo sizikapambana. Kuchokera ku kuphunzira kwawo Baibulo, iwo anaphunzira kuti chaka cha 1914 chikakhala posinthira pa zinthu m’mbiri ya munthu, ndipo anapereka chenjezo la ichi kwa zaka 40. Zowonadi ku ulosi wa Baibulo, 1914 inali kuyambika kwa nthaŵi yozindikiridwa ndi njala, miliri, ndi zivomezi, limodzinso ndi nkhondo. (Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11) Ponena za Nkhondo ya Dziko ya I, katswiri wa mbiri yakale James Cameron analemba kuti: “Mu 1914 dziko, monga mmene linadziŵikira pa nthaŵiyo ndi kulandiridwa, linafika ku mapeto.”
Nkhondo imeneyo isanathe, mliri wa flu wowopsya unakantha pa mlingo wa dziko lonse ndipo unapha anthu 20 miliyoni—oposa kuwirikiza nthaŵi ziŵiri chiŵerengero cha asilikali omwe anafa mu nkhondo yeniyeniyo. Kuyambira pamenepo, matenda onga ngati kansa ndi, posachedwa kwambiri, AIDS awopsyeza mtundu wa anthu.
Tsopano dziŵani ulosi wina wa Baibulo: “Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.” (Mateyu 24:12) Kodi ichi chikukwaniritsidwa? Motsimikizirika! Tsiku ndi tsiku, ofalitsa nkhani amavumbula kusayeruzika kwa dziko lonse: kupha, kulanda, ndi kuvutitsa kwa chisawawa. Kuwonjezerapo, kulosera kwa ndale zadziko ponena za Nkhondo ya dziko ya II kunali kwakuti ikabweretsa “ufulu ku mantha.” Mosiyanako, Baibulo molondola linaneneratu kuti anthu “akakomoka ndi mantha kuyembekezera zinthu zirinkudza pa dziko lapansi.” (Luka 21:26) Kachiŵirinso zoneneratu za munthu zinali zolakwa, ndipo mawu a ulosi wa Mulungu anali owona.
Woyambitsa Nkhondo Wamkulu
Woyambitsa nkhondo ali iye amene amapangitsa nkhondo. Andale zadziko, atsogoleri achipembedzo, ndipo ngakhale amuna a za malonda achitako mbali imeneyi. Koma woyambitsa nkhondo wamkulu koposa sali wina koposa Satana Mdyerekezi, wotchedwa m’Malemba “mulungu wa dongosolo iri la zinthu.”—2 Akorinto 4:4.
Satana anawukira motsutsana ndi Yehova Mulungu zaka zikwi zingapo zapitazo, ndipo pambuyo pake iye ananyenga gulu la angelo m’kugwirizana naye. Koma mu 1914 nthaŵi yake inatha. Baibulo limatiuza ife kuti: “Ndipo munali nkhondo m’mwamba: Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka, chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi pa dziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”—Chivumbulutso 12:7-9.
Ichi chimalongosola chifukwa chimene dziko lapansi lakhalira malo owopsya chotere chiyambire 1914. Baibulo linaneneratu chotulukapo cha kugwa kwa Satana: “Tsoka mtunda ndi nyanja . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamutsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Kodi nthaŵiyo ndi yaifupi chotani? Yesu ananena kuti: “Mbadwo uwu [umene unawona zochitika zoyambira mu 1914] sudzatha kuchoka kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:34) Zinthu ziti? Matsoka onse ndi ngozi zimene Yesu analosera kaamba ka tsiku lathu.
Ngakhale kuli tero, Baibulo limasonyeza kuti mosasamala kanthu za kulephera kwa Chigwirizano cha Mitundu ndi kupanda mphamvu komwe kulipo kwa Gulu la Mitundu Yogwirizana, mitundu siikasiya zoyesayesa zawo za kupanga mtendere. Ndithudi, nthaŵi ikafika pamene iwo akalingalira kuti apambana. Pakakhala mfuu yaikulu ya “mtendere ndi chisungiko,” koma ichi chikatsatiridwa ndi “chiwonongeko chobukapo” cha dziko loipa iri. Akumakhala mu mdima, anthu akadzidzimutsidwa ndi kusinthika kwa zinthu kumeneku, komwe kukadza “monga mbala usiku.”—1 Atesalonika 5:2, 3.
Nkuchiyani kumene ichi chikatsogolera? Ku nkhondo yomwe ndithudi iri “nkhondo yothetsa nkhondo”: nkhondo ya Armagedo, yotchedwa m’Baibulo “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Ichi chikatanthauza chiwonongeko cha mbali zonse zoipa ndi achirikizi awo. “Oipa adzadulidwda.” (Chivumbulutso 16:14-16; Salmo 37:9) Potsirizira pake, Satana, woyambitsa nkhondo wamkulu, adzatsekeredwa m’malo kumene iye sakakhala ndi chisonkhezero chowonjezereka pa anthu. Kenaka, iye nayenso akayenera kuwonongedwa.—Chivumbulutso 20:1-3, 7-10.
Dziŵani, ngakhale kuli tero, kuti iyi siikakhala nkhondo ya kusakaza kosalingalira ndi kupha kopanda lingaliro kwa opanda liwongo ndi aliwongo mofanana. Pakakhala opulumuka, ndipo awa akakhala amene “akupereka kwa [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku.” Inde, awo amene amasiya kuphunzira nkhondo ngakhale tsopano lino ndipo amatsatira njira za mtendere za Mkristu wowona adzapulumuka nkhondo yomalizira, yaikulu imeneyi. Kodi iwo akakhala ambiri? Baibulo limawatcha iwo “khamu lalikulu, ndipo palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, lochokera ku mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.”—Chivumbulutso 7:9, 14, 15.
Pambuyo pa Mkuntho
Ndi mpumulo wotani nanga umene awa akaumva! M’malo mwa maboma ambiri a utundu, padzakhala kokha boma limodzi: Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) M’malo mwa onyada ndi odzikweza, ofatsa adzalandira dziko lapansi ndi “kukondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) “Mulungu yekha . . . adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro kapena kulira kapena chowawitsa.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Yehova “akaletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi.” Malupanga akasulidwa kukhala zolimira, nthungo kukhala anangwape, ndipo ‘sadzaphunziranso nkhondo.’—Salmo 46:8, 9; Yesaya 2:4.
Kodi inu simungakonde kukhala m’dziko loterolo? Ndithudi muyenera kutero! Chabwino, kuthekera kulipo. Sitepi loyambirira liri kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kudzitsimikizira inu eni kuti chiyembekezo chimenechi ndi chowona ndipo chozikidwa pa maziko abwino. Kenaka, pezani kuchokera m’Baibulo chimene chiri chifuno cha Mulungu kaamba ka inu tsopano ndi kuchita mogwirizana. Zowona, kuphunzira kumatanthauza kuyesayesa, koma kuli koyenerera chimenecho. Yesu ananena kuti chidziŵitso chimene mudzachipeza, ngati muchigwiritsira ntchito moyenerera, chidzatanthauza “moyo wosatha.” (Yohane 17:3) Kodi pali china chirichonse chofunika kwambiri kuposa chimenecho?