NKHANI YOPHUNZIRA 35
Pitirizani “Kulimbikitsana”
“Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 ATES. 5:11.
NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 5:11, kodi tonsefe timagwira nawo ntchito iti?
KODI mpingo wanu unagwirapo ntchito yomanga kapena kukonza Nyumba ya Ufumu? Ngati ndi choncho, muyenera kuti mukukumbukira nthawi yoyamba imene munasonkhana m’Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo. Muyeneranso kuti munathokoza kwambiri Yehova. Mwinanso munakhudzidwa kwambiri moti munalephera kuimba bwino nyimbo yoyamba. Nyumba zathu za Ufumu zomangidwa bwino zimachititsa kuti Yehova atamandike. Komatu pali ntchito inanso yomanga imene tikamagwira nawo timachititsa kuti iye atamandike kwambiri. Ndipo ndi yamtengo wapatali kuposa nyumba zonse zimene tingamange. Ntchito imeneyi ndi yolimbikitsa anthu omwe amabwera kunyumba zolambirirazi. Mtumwi Paulo ankaganizira za ntchito imeneyi pomwe analemba mawu a pa 1 Atesalonika 5:11, lemba lomwe likutsogolera nkhaniyi.—Werengani.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Mtumwi Paulo ndi chitsanzo chabwino cha munthu yemwe ankadziwa kulimbikitsa Akhristu anzake. Iye ankawachitira chifundo. Munkhaniyi tikambirana mmene anathandizira abale ndi alongo ake kuti (1) azipirira mayesero, (2) azikhala mwamtendere komanso (3) azikhulupirira kwambiri Yehova. Tiyeni tione zimene tingachite kuti tizimutsanzira n’kumalimbikitsa abale ndi alongo athu masiku ano.—1 Akor. 11:1.
PAULO ANKATHANDIZA ABALE NDI ALONGO AKE KUPIRIRA MAYESERO
3. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankaona zinthu moyenera?
3 Paulo ankakonda kwambiri abale ndi alongo ake. Popeza kuti nayenso ankakumana ndi mavuto, ankatha kuchitira chifundo Akhristu anzake akamakumana ndi mayesero. Pa nthawi ina ndalama zinamuthera moti ankafunika kuti azigwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wa iyeyo ndi anzake omwe anali nawo. (Mac. 20:34) Paulo ankadziwa ntchito yokonza matenti. Choncho atafika ku Korinto, poyamba ankagwira ntchito imeneyi limodzi ndi Akula ndi Purisikila. Koma “sabata lililonse,” ankalalikira kwa Ayuda ndi Agiriki. Kenako kutabwera Sila ndi Timoteyo, “Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu.” (Mac. 18:2-5) Nthawi zonse iye ankakumbukira cholinga chake chachikulu pa moyo, chomwe chinali kutumikira Yehova. Popeza kuti ankachita khama pa nkhani yolalikira komanso kugwira ntchito, iye ankatha kulimbikitsa abale ndi alongo ake. Anawakumbutsa kuti asamalole mavuto komanso udindo wopezera banja zinthu zofunika kuwachititsa kuti azinyalanyaza “zinthu zofunika kwambiri,” zomwe ndi chilichonse chokhudza kulambira Yehova.—Afil. 1:10.
4. Kodi Paulo ndi Timoteyo anathandiza bwanji Akhristu anzawo kuti apirire pamene ankazunzidwa?
4 Pasanapite nthawi yaitali mpingo wa ku Tesalonika utangokhazikitsidwa, Akhristu kumeneko anayamba kutsutsidwa kwambiri. Anthu achiwawa atalephera kupeza Paulo ndi Sila, anakokera “abale ena kwa olamulira a mzindawo,” akufuula kuti: “Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara.” (Mac. 17:6, 7) Tangoganizani mmene Akhristu atsopanowo anachitira mantha, ataona kuti anthu amumzindawo awaukira. Iwo akanatha kusiya kuchita khama potumikira Yehova, koma Paulo sankafuna kuti zimenezi ziwachitikire. Ngakhale kuti iye ndi Sila ankafunika kuchoka, iwo anaonetsetsa kuti mpingo watsopanowo ukusamalidwa moyenera. Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Tesalonikawo kuti: “Tinatumiza Timoteyo . . . kuti adzakulimbitseni ndi kukutonthozani pa chikhulupiriro chanu, kuti pasapezeke wina wopatutsidwa ndi masautso amenewa.” (1 Ates. 3:2, 3) Timoteyo ayenera kuti anazunzidwapo m’tauni yakwawo ku Lusitara. Analinso ataona mmene Paulo analimbikitsira abale kumeneko. Pokumbukira mmene Yehova anawadalitsira, Timoteyo akanatha kutsimikizira abale ndi alongo atsopanowo kuti nawonso zinthu ziwayendera bwino.—Mac. 14:8, 19-22; Aheb. 12:2.
5. Kodi m’bale wina dzina lake Bryant anapindula bwanji atathandizidwa ndi mkulu?
5 Kodi Paulo analimbikitsanso Akhristu anzake m’njira ina iti? Pa ulendo wawo wobwerera ku Lusitara, Ikoniyo ndi Antiokeya, Paulo ndi Baranaba ‘anaika akulu mumpingo uliwonse.’ (Mac. 14:21-23) Mosakayikira amuna amene anasankhidwawo ankalimbikitsa mipingoyo monga mmenenso akulu masiku ano amachitira. Taganizirani zimene m’bale wina dzina lake Bryant ananena. Iye anati: “Ndili ndi zaka 15, bambo anga anachoka panyumba ndipo mayi anga anachotsedwa. Ndinkangodzimva kuti ndili ndekhandekha ndipo ndinafooka.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza Bryant kupirira? Iye anati: “Mkulu wina dzina lake Tony ankalankhula nane kumisonkhano komanso pa nthawi zina. Anandifotokozera za anthu ena omwe ankakumana ndi mayesero koma n’kumakhalabe osangalala. Anandiwerengera lemba la Salimo 27:10 ndipo nthawi zambiri ankandifotokozera zokhudza Hezekiya, yemwe anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti bambo ake sanali chitsanzo chabwino.” Kodi zimene mkuluyu anachita zinathandiza bwanji Bryant? Iye anati: “Popeza kuti Tony anandilimbikitsa, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse womwe ndimasangalala nawo.” Akulu, muzikhala tcheru kuti muthandize anthu omwe ali ngati Bryant, amene angafunike “mawu abwino” olimbikitsa.—Miy. 12:25.
6. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito bwanji nkhani za anthu akale polimbikitsa abale ndi alongo ake?
6 Paulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti pali “mtambo wa mboni waukulu” wa amuna ndi akazi omwe anapirira mavuto chifukwa chothandizidwa ndi Yehova. (Aheb. 12:1) Paulo ankadziwa kuti nkhani za anthu akale omwe anakwanitsa kupirira mavuto osiyanasiyana, zikanathandiza abale ndi alongowo kukhala olimba mtima komanso kupitirizabe kuganizira za “mzinda wa Mulungu wamoyo.” (Aheb. 12:22) N’chimodzimodzinso masiku ano. Ndani salimbikitsidwa akamawerenga nkhani zokhudza mmene Yehova anathandizira Gidiyoni, Baraki, Davide, Samueli ndi enanso ambiri? (Aheb. 11:32-35) Nanga bwanji zitsanzo za atumiki a Mulungu a masiku ano? Kulikulu lathu la padziko lonse, nthawi zambiri timalandira makalata ochokera kwa abale ndi alongo omwe amafotokoza kuti chikhulupiriro chawo chinalimba pambuyo powerenga mbiri ya moyo wa mmodzi wa atumiki a Yehova okhulupirika a masiku ano.
PAULO ANASONYEZA ABALE AKE MMENE ANGAKHALIRE MWAMTENDERE
7. Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo a Paulo a pa Aroma 14:19-21?
7 Timalimbikitsa abale ndi alongo athu tikamayesetsa kulimbikitsa mtendere mumpingo. Sitimalola kuti kusiyana maganizo pa nkhani zosiyanasiyana kutigawanitse. Komanso sitimaumirira ufulu wathu pa nkhani zimene siziphwanya mfundo za m’Baibulo. Taganizirani chitsanzo pa nkhaniyi. Mumpingo wa Chikhristu ku Roma munali Ayuda ndi anthu a mitundu ina. Kungochokera pamene Chilamulo cha Mose chinasiya kugwira ntchito, panalibenso malamulo oletsa kudya zakudya zina. (Maliko 7:19) Kuchokera nthawi imeneyo, Akhristu ena a Chiyuda ankaona kuti akhoza kudya zakudya za mtundu wina uliwonse. Komabe ena ankaona kuti si bwino kudya zakudya zina. Izi zinachititsa kuti mumpingo mukhale kugawikana. Paulo anatsindika kufunika kokhala mwamtendere ndipo anati: “Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.” (Werengani Aroma 14:19-21.) Pamenepatu Paulo anathandiza Akhristu anzakewo kuona kuti kukangana pa nkhani zimenezi kukanabweretsa chisokonezo pakati pawo komanso mumpingo. Iye anali wokonzekanso kusintha mmene ankachitira zinthu kuti asakhumudwitse ena. (1 Akor. 9:19-22) Ifenso masiku ano tingalimbikitse ena komanso kukhala nawo pa mtendere, ngati timapewa kukangana pa nkhani zimene aliyense amafunika kusankha yekha.
8. Kodi Paulo anatani ataona kuti nkhani ina ikhoza kusokoneza mtendere mumpingo?
8 Paulo anapereka chitsanzo chabwino pokhalabe mwamtendere ndi anthu amene ankasemphana naye maganizo pa nkhani zina zofunika. Mwachitsanzo, ena mumpingo ankafuna kuti Akhristu omwe sanali Ayuda azidulidwa, mwina poopa kutsutsidwa ndi Ayuda ena. (Agal. 6:12) Paulo sanagwirizane ndi maganizo amenewa koma m’malo moumirira kuti anthuwo atsatire maganizo ake, modzichepetsa, iye anapempha malangizo kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu. (Mac. 15:1, 2) Zimene anachitazi zinathandiza Akhristuwo kuti azisangalala ndipo mumpingo munali mtendere.—Mac. 15:30, 31.
9. Kodi tingatsanzire bwanji Paulo?
9 Ngati pabuka kusamvana pa nkhani inayake, timalimbikitsa mtendere popempha malangizo kwa abale amene Yehova wawasankha kuti azitsogolera mumpingo. Nthawi zambiri malangizo ochokera m’Baibulo tingawapeze m’mabuku athu kapena m’malangizo ena operekedwa ndi gulu. Tikamayesetsa kutsatira malangizowa, m’malo moumirira maganizo athu, timathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere.
10. Kodi n’chiyaninso china chimene Paulo anachita polimbikitsa mtendere mumpingo?
10 Paulo ankalimbikitsa mtendere poganizira makhalidwe abwino a abale ndi alongo ake osati zimene ankalakwitsa. Mwachitsanzo, kumapeto kwa kalata imene analembera Akhristu a ku Roma, iye anatchula mayina ambiri. Ndipo nthawi zambiri ankatchula zinthu zabwino zimene anthuwo ankachita. Tingatsanzire Paulo poyamikira kuchokera pansi pa mtima makhalidwe abwino amene abale ndi alongo athu ali nawo. Tikamachita zimenezi tingathandize kuti abale ndi alongo mumpingo azigwirizana komanso azikondana kwambiri.
11. Kodi tingatani kuti tibwezeretse mtendere tikasemphana maganizo ndi ena?
11 Nthawi zina ngakhalenso Akhristu olimba mwauzimu angasemphane maganizo kapena kukangana kumene. Zimenezi zinachitikirapo Paulo ndi mnzake wapamtima Baranaba. Amuna awiriwa anasemphana maganizo pa nkhani yoti atenge Maliko pa ulendo wawo wotsatira waumishonale. Pakati pawo panabuka “mkangano woopsa” moti mpaka anapatukana. (Mac. 15:37-39) Koma pambuyo pake amuna atatuwa anagwirizana zomwe zinasonyeza kuti ankaona mtendere komanso mgwirizano mumpingo kukhala wofunika kwambiri. Patapita nthawi, Paulo anafotokoza zinthu zabwino zokhudza Baranaba ndi Maliko. (1 Akor. 9:6; Akol. 4:10) Ifenso tiyenera kuthetsa kusamvana kulikonse komwe tingakhale nako ndi ena mumpingo n’kupitiriza kumaona makhalidwe abwino amene ali nawo. Tikatero tidzalimbikitsa mtendere ndi mgwirizano.—Aef. 4:3.
PAULO ANALIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHA ABALE NDI ALONGO AKE
12. Kodi ndi mavuto ena ati omwe abale ndi alongo athu amakumana nawo?
12 Timalimbikitsa abale ndi alongo athu tikamawathandiza kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Ena amanyozedwa ndi achibale awo omwe si a Mboni, anzawo a kuntchito kapena a kusukulu. Enanso akudwala matenda aakulu kapena akuvutika maganizo chifukwa chokhumudwa ndi zinazake. Palinso ena omwe akhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo kwa nthawi yaitali akhala akuyembekezera mapeto a dzikoli. Zinthu ngati zimenezi zingayese chikhulupiriro cha Akhristu masiku ano. Akhristu a mu nthawi ya atumwi ankakumananso ndi mavuto ngati amenewa. Ndiye kodi Paulo anatani kuti alimbikitse abale ndi alongo akewa?
Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi tingalimbikitse bwanji ena? (Onani ndime 13)b
13. Kodi Paulo anathandiza bwanji amene ankanyozedwa chifukwa cha zimene ankakhulupirira?
13 Paulo anagwiritsa ntchito Malemba pothandiza abale ndi alongo ake kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti Akhristu omwe anali Ayuda ankavutika kuyankha achibale awo akamawanyoza ponena kuti Chiyuda ndiye chipembedzo choona osati Chikhristu. N’zodziwikiratu kuti kalata ya Paulo yopita kwa Aheberi inalimbikitsa kwambiri Akhristu amenewa. (Aheb. 1:5, 6; 2:2, 3; 9:24, 25) Mfundo zokhutiritsa zomwe iye anawalembera zikanawathandiza kuti aziyankha anthu omwe ankawatsutsa. Masiku anonso tingathandize Akhristu anzathu omwe amanyozedwa kuti azigwiritsa ntchito mabuku othandiza pophunzira Baibulo pofotokoza zimene amakhulupirira. Komanso ngati achinyamata athu amanyozedwa chifuwa chokhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa, tingawathandize kupeza mfundo zimene zingawathandize kufotokoza chifukwa chake amakhulupirira zimenezo m’kabuku kakuti, Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? komanso kakuti, Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.
Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi tingalimbikitse bwanji ena? (Onani ndime 14)c
14. Kodi Paulo ankachitanso chiyani ngakhale kuti ankatanganidwa ndi ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa?
14 Paulo analimbikitsa abale ndi alongo ake kuti azisonyeza chikondi pochita “ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Iye anathandiza abale ndi alongo akewa osati ndi mawu okha komanso ndi zochita. Mwachitsanzo, Akhristu a ku Yudeya atavutika ndi njala, Paulo anathandiza nawo powapatsa zinthu zofunika. (Mac. 11:27-30) Ndipotu ngakhale kuti Paulo ankatanganidwa ndi ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, nthawi zonse ankafunafuna njira zothandizira ena pa zimene ankafunikira. (Agal. 2:10) Pochita zimenezi, iye analimbikitsa Akhristu anzakewo kuti azidalira kuti Yehova adzawathandiza. Ifenso masiku ano tikamadzipereka kugwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso luso lathu pothandiza ena pa nthawi ya ngozi zam’chilengedwe, timathandiza abale ndi alongo kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Zimenezi n’zimene zimachitikanso ngati nthawi zonse timathandiza pa ntchito ya padziko lonse ndi ndalama zathu. Tikamathandiza m’njira zimenezi komanso zina, timachititsa abale ndi alongo athu kuti azikhulupirira kuti Yehova sadzawataya ngakhale pang’ono.
Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi tingalimbikitse bwanji ena? (Onani ndime 15-16)d
15-16. Kodi tizichita bwanji zinthu ndi anthu omwe chikhulupiriro chawo chafooka?
15 Paulo anapitirizabe kulimbikitsa anthu amene chikhulupiriro chawo chinafooka. Ankawachitira chifundo komanso kulankhula nawo mokoma mtima. (Aheb. 6:9; 10:39) Mwachitsanzo, m’kalata yopita kwa Aheberi nthawi zambiri anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti nayenso ankafunika kutsatira malangizo omwe ankaperekawo. (Aheb. 2:1, 3) Mofanana ndi Paulo, ifenso timapitiriza kulimbikitsa anthu amene chikhulupiriro chawo chafooka powasonyeza kuti timawaganizira. Komanso tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timawakonda. Kulankhula nawo mwachikondi komanso mokoma mtima kungawalimbikitse kwambiri.
16 Paulo anatsimikizira abale ndi alongo akewo kuti Yehova ankadziwa ntchito zabwino zimene ankachita. (Aheb. 10:32-34) Ifenso tingachite zimenezi tikamathandiza Mkhristu mnzathu yemwe chikhulupiriro chake chafooka. Tingamufunse kuti atifotokozere mmene anayambira choonadi kapenanso kumulimbikitsa kuti aganizire mmene Yehova anamuthandizirapo m’mbuyomu. Tingagwiritse ntchito mpata umenewu kumutsimikizira kuti Yehova sanaiwale ntchito zosonyeza chikondi zomwe iye anachita komanso kuti sadzamusiya. (Aheb. 6:10; 13:5, 6) Kucheza nawo mwa njira imeneyi, kungalimbikitse abale ndi alongo athu okondedwawo kuti azifunitsitsa kupitirizabe kutumikira Yehova.
‘PITIRIZANI KULIMBIKITSANA’
17. Kodi ndi luso liti limene tiyenera kupitiriza kulikulitsa?
17 Mofanana ndi wogwira ntchito zomangamanga, yemwe luso lake limawonjezeka m’kupita kwa nthawi, ifenso tingawonjezere zomwe timachita polimbikitsana. Tingathandize ena kupirira mayesero amene akukumana nawo, powafotokozera zitsanzo za anthu akale omwe anapirira. Tingalimbikitse mtendere potchula zabwino zimene ena amachita, kupewa zinthu zimene zingasokoneze mtendere, komanso kubwezeretsa mtendere pakakhala kusemphana maganizo. Ndiponso tingapitirize kulimbikitsa chikhulupiriro cha abale ndi alongo athu powafotokozera mfundo zofunika za choonadi, powathandiza kupeza zimene akufunikira komanso kulimbikitsa amene chikhulupiriro chawo chafooka.
18. Kodi ndinu wotsimikiza mtima kuchita chiyani?
18 Abale ndi alongo amene amathandiza pa ntchito yomanga nyumba za gulu amakhala osangalala komanso okhutira. Ifenso tikhoza kumasangalala komanso kukhala okhutira tikamathandiza abale ndi alongo athu mumpingo kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mosiyana ndi nyumba zimene m’kupita kwa nthawi zimawonongeka, zotsatirapo za zimene timachita polimbikitsa ena, zidzakhalapo mpaka kalekale. Choncho tiyeni titsimikize mtima kupitirizabe “kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 Ates. 5:11.
NYIMBO NA. 100 Alandireni Bwino
a Moyo si wophweka m’dzikoli. Abale ndi alongo athu akukumana ndi mavuto ambiri. Tikhoza kuwathandiza kwambiri ngati titamafufuza njira zowalimbikitsira. Pa nkhaniyi tingachite bwino kuganizira chitsanzo cha mtumwi Paulo.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Bambo akusonyeza mwana wake wamkazi mmene angagwiritsire ntchito mfundo zopezeka m’mabuku athu pokana kuchita nawo Khirisimasi.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja lapita m’dera lina m’dziko lawo kukathandiza pa nthawi ya ngozi zam’chilengedwe.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu akuyendera m’bale wina yemwe chikhulupiriro chake chafooka. Iye akumusonyeza zithunzi za Sukulu ya Utumiki Waupainiya yomwe analowera limodzi zaka zambiri m’mbuyomo. Zithunzizo zikumukumbutsa mmene ankasangalalira pa nthawiyo. M’baleyo akufuna kuyambiranso kusangalala ngati mmene ankachitira pamene ankatumikira Yehova. Patapita nthawi, iye anayambiranso kusonkhana.