-
Pitirizani ‘Kuyembekezera Moleza Mtima’Nsanja ya Olonda—2013 | November 15
-
-
9-11. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:3 lakwaniritsidwa? Fotokozani.
9 Werengani 1 Atesalonika 5:1-3. Posachedwapa anthu adzanena kuti: “Bata ndi mtendere!” Kuti tisapusitsidwe ndi mawu amenewa, tiyenera ‘kukhalabe maso ndiponso oganiza bwino.’ (1 Ates. 5:6) Tiyeni tikambirane zinthu zimene zikusonyeza kuti anthu adzanena mawuwo posachedwapa. Kukambirana zimenezi kungatithandize kukhalabe maso.
10 Nkhondo ziwiri zapadziko lonse zitatha, anthu ankanenanena za mtendere. Mwachitsanzo, nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, bungwe la League of Nations linakhazikitsidwa n’cholinga choti pakhale mtendere. Kenako pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, bungwe la United Nations linakhazikitsidwa ndipo anthu ankaganiza kuti libweretsa mtendere. Maboma ambiri komanso atsogoleri azipembedzo akhala akudalira mabungwe amenewa kuti abweretse mtendere. Umboni wake ndi wakuti mu 1986, bungwe la United Nations linalengeza kuti chaka chimenechi ndi chaka chamtendere padziko lonse. Ndiyeno m’chakachi, atsogoleri a mayiko ambiri komanso azipembedzo anapita ku Assisi m’dziko la Italy kukapempherera mtendere limodzi ndi mtsogoleri wa tchalitchi cha Katolika.
11 Koma zimene zinachitika mu 1986 komanso pa nthawi zina sizinakwaniritse ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3. Tikutero chifukwa chakuti “chiwonongeko chodzidzimutsa” sichinafikebe.
12. Kodi timadziwa chiyani zokhudza kunena kuti: “Bata ndi mtendere”?
12 Kodi ndi ndani amene adzanene kuti: “Bata ndi mtendere”? Kodi atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi achikhristu komanso a zipembedzo zina adzachita chiyani? Nanga atsogoleri a maboma adzachita zotani pa nthawi imeneyo? Malemba safotokoza zimenezi. Koma chimene tikudziwa n’chakuti kaya adzanena bwanji, mawuwo sadzakhala oona. Dziko loipali lidzakhalabe m’manja mwa Satana. Tingati lawoleratu ndipo silidzasintha. Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati Mkhristu angakhulupirire mawu abodza ochokera kwa Satana amenewa n’kuyamba kulowerera m’nkhani za m’dzikoli.
-
-
Pitirizani ‘Kuyembekezera Moleza Mtima’Nsanja ya Olonda—2013 | November 15
-
-
14. N’chiyani chikusonyeza kuti Babulo Wamkulu watsala pang’ono kuwonongedwa?
14 Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, adzawonongedwa. Pa nthawi imene adzawonongedwe, anthu sadzatha kumuthandiza. Ngakhale panopa, umboni woti adzawonongedwa posachedwapa ukuoneka. (Chiv. 16:12; 17:15-18; 18:7, 8, 21) Nkhani za m’nyuzipepala ndiponso pa TV zikusonyeza kuti anthu ayamba kale kudana ndi zipembedzo ndiponso atsogoleri ake. Komabe atsogoleri a Babulo Wamkulu amaganiza kuti zinthu zili bwinobwino. Koma adzadabwa. Mawu akuti “Bata ndi mtendere!” akadzanenedwa, atsogoleri andale a m’dziko la Satanali adzaukira zipembedzo zonyenga mwadzidzidzi n’kuziwononga. Amenewo adzakhala mapeto a Babulo Wamkulu. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zonsezi zidzachitike.—Chiv. 18:8, 10.
-