Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 5/1 tsamba 18-22
  • Lambirani Mlengi, Osati Chilengedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lambirani Mlengi, Osati Chilengedwe
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufulumiza Kwapadera
  • Kupewa Kulambira Cholengedwa
  • Nthanthi ya Mulungu Mayi Wachikazi
  • Kulambira Kosayenera
  • Kodi Mariya Ndi Amayi a Mulungu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mariya (Amayi ŵa Yesu)
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Mariya ndi “Amayi wa Mulungu”?
    Galamukani!—1996
  • Bodza Lachisanu: Mariya Ndi Amayi a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 5/1 tsamba 18-22

Lambirani Mlengi, Osati Chilengedwe

“Ali Yehova Mulungu wako amene uyenera kulambira, ndipo kuli kwa iye yekha kumene uyenera kupereka utumiki wopatulika.”​—LUKA 4:8, “NW.”

1. Ndimotani mmene kalongosoledwe kakuti “kulambira” kalongosoledwera, ndipo kodi kulambira kowona kuyenera kuperekedwa motani?

KALONGOSOLEDWE kakuti “kulambira” kalongosoledwa mu dikishonale mwa njira iyi: “Kulingalira ndi ulemu, kulemekeza, kapena kudzipereka kwakukulu, ngakhale kopambanitsa.”a Ndani amene ayenera kupatsidwa kulambira koteroko? Yesu Kristu ananena kuti: “Uzikonda [Yehova, “NW”] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Ndiponso, pamene anapatsidwa maufumu onse a dziko ngati iye akachita kokha “kachitidwe ka kulambira” kwa Satana, Yesu anakana, akumalengeza kuti: “Ali Yehova Mulungu wako amene uyenera kulambira, ndipo kuli kwa iye yekha kumene uyenera kupereka utumiki wopatulika.” (Luka 4:7, 8, NW) Kuchokera ku mawu ndi machitidwe a Yesu, chiri chachiwonekere kuti kokha Yehova Mulungu ayenera kulambiridwa. Kulambira kumeneku kumaphatikizapo “utumiki wopatulika,” popeza kuti “chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”​—Yakobo 2:26.

2. Nchifukwa ninji chiri choyenera kulambira Mlengi yekha?

2 Kulambira Yehova kotero kuli koyenerera chifukwa iye ali Mfumu Yaikulu ya chilengedwe cha ponseponse chonse, Mlengi wa miyamba yochititsa mantha ndi dziko lapansi ndi mitundu yake yonse ya moyo. Monga wotero, iye yekha ali woyenera kulingaliridwa ndi “ulemu, kulemekeza, kapena kudzipereka kwakukulu, ngakhale kopambanitsa” ku mbali ya anthu. Baibulo limalongosola kuti: “Muyenera inu, [Yehova, NW], ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chibvumbulutso 4:11) Mowonadi, palibe munthu wamba, palibe chinthu chamoyo kapena chopanda moyo, chingakhale choyenera “ulemu, chilemekezo, kapena kudzipereka” koteroko. Yehova yekha ali woyenerera “kudzipereka kotheratu.”​—Eksodo 20:3-6, NW.

Kufulumiza Kwapadera

3. Nchifukwa ninji pali kufulumiza kwapadera kaamba ka ife kulambira Mulungu?

3 Chifukwa chakuti tikukhala m’nyengo ya chiweruzo, tsopano pali kufulumiza kwapadera kwa kulambira Mulungu moyenerera. Zotulukapo zotheratu zikugamulidwa. Mawu a ulosi a Mulungu amatiwuza ife kuti mu “masiku otsiriza” amenewa a dongosolo la kachitidwe ka zinthu lomwe liripoli, Kristu Yesu wafika mu ulemerero wa kumwamba “ndi angelo onse pamodzi naye.” Kaamba ka chifuno chotani? Yesu iyemwini ananeneratu chifuno chimenecho, akumanena kuti: “Ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” Nkhosa zidzachoka kumka ku “moyo wosatha.” Mbuzi zidzachoka kumka ku “chilango chosatha.”​—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 25:31, 32, 46, NW.

4. (a) Ndimotani mmene Paulo akuzindikiritsira awo amene adzawonongedwa kotheratu pamapeto a dziko lino? (b) Ndi mkhalidwe wotani umene ukusonyezedwa ndi awo omwe akupeza moyo wosatha?

4 Mtumwi Paulo analemba ponena za “vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera [mbiri yabwino yonena za, NW] Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.” (2 Atesalonika 1:7-9) Chotero, chiwonongeko chosatha chiri chotulukapo cha anthu osamva, onga mbuzi omwe sakufuna kudziŵa ponena za zifuno za Mulungu kapena omwe akukana kuchitapo kanthu pamene iwo ali ndi mwaŵi. Koma “moyo wosatha” uli chotulukapo cha anthu odzichepetsa, onga nkhosa omwe akufuna kudziŵa ponena za Yehova, omwe amamvetsera ku malangizo ake, ndi omwe kenaka amadzigonjetsera ku chifuniro chake. Baibulo limanena kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amane achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”​—1 Yohane 2:17; onaninso 2 Petro 2:12.

5, 6. (a) Nchiyani chimene munthu ayenera kuchita kuti apeze chowonadi ponena za Yehova ndi zifuno zake? (b) Nchifukwa ninji tingakhale achidaliro kuti ofunafuna chowonadi adzapezana ndi chowonadi mosasamala kanthu za mkhalidwe wawo wa moyo?

5 Anthu onga nkhosa ali ofunitsitsa kupereka nsembe nthaŵi, nyonga, ndi magwero a zakuthupi kufunafuna chowonadi. Iwo amachita chimene Miyambo 2:1-5 imanena kuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, Ndi kusunga malamulo anga; Kutcherera makutu ako ku nzeru, Kulozetsa mtima wako kukuzindikira; Ukaitananso luntha, Ndi kufuulira kuti Ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, Ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; Pompo udzazindikira kuwopa Yehova Ndi kumdziŵadi Mulungu.”

6 Kufunitsitsa kwa kufunafuna kaamba ka Yehova kuli kumene kumalekanitsa anthu onga nkhosa kuchokera kwa onga mbuzi. “Ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.” (1 Mbiri 28:9) Chotero, mosasamala kanthu za fuko kapena mtundu wa munthuyo, mosasamala kanthu za maphunziro ake, kaya wolemera kapena wosauka, ngati iye mowona mtima afunafuna kaamba ka chowonadi chonena za Mulungu, iye adzachipeza icho. Kuchokera ku malo owonera a kumwamba, Kristu ndi angelo ake adzawona ku icho kuti wofunafunayo wapezana ndi chowonadi, mosasamala kanthu za kumene munthuyo amakhala. Kodi kufunafuna kumeneku kudzakhala kopatsa mphoto motani? Yesu ananena kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”​—Yohane 17:3; onaninso Ezekiele 9:4.

Kupewa Kulambira Cholengedwa

7, 8. (a) Ndi ngozi yotani imene iripo m’kulambira anthu? (b) Longosolani “ulemu wopambanitsa, kulemekeza, kapena kudzipereka” kumene Mariya amalingaliridwa nako.

7 Anthu ambiri kuzungulira pa dziko lapansi amalingalira anthu​—amoyo kapena akufa​—ndi “ulemu, kulemekeza, kapena kudzipereka kopambanitsa.” Pamene kuli kwakuti iwo angadzimve kuti iyi iri mbali ya kulambira kwawo kwa Mulungu, iko m’chenicheni kumawapatutsa iwo kuchoka ku kulambira kowona. Ichi chimatsegula njira kaamba ka iwo kukhulupirira ziphunzitso ndi kudziloŵetsa m’machitachita omwe ali osemphana ndi chifuno cha Mulungu. Chitsanzo chimodzi chowonekera chiri njira mu imene Mariya, amayi a Yesu, akuwonedwera ndi mamiliyoni a anthu a ponse paŵiri maiko a Roma Katolika ndi Chikatolika cha Eastern Orthodox.

8 Mafano ndi zithunzithunzi zopakidwa utoto za Mariya zimagwadiridwa mu mkhalidwe wa kulambira, ndipo m’chiphunzitso chalamulo cha tchalitchi, iye akulozeredwako kukhala “Namwali Mariya Theotokos.” Liwu lakuti the·o·to’kos limatanthauza “wobala Mulungu” kapena “amayi a Mulungu.” New Catholic Encyclopedia ikunena kuti: “Mariya ali amayi a Mulungu. . . . Ngati Mariya sali ndithudi amayi a Mulungu, chotero Kristu sali Mulungu wowona limodzinso ndi munthu wowona.” Chotero, monga mbali ya chiphunzitso chawo cha Utatu, zipembedzo zimenezi zimaphunzitsa kuti Yesu anali Mulungu Wamphamvuyonse mu mkhalidwe waumunthu, kupanga Mariya kukhala “amayi a Mulungu.” Magwero amodzimodziwo akuwonjezera kuti kudzipereka kwa Mariya kumaphatikiza: “(1) kupatulikitsidwa, kapena kuzindikira kwa ulemu kwa kulemekezeka kwa Namwali woyera Amayi a Mulungu; (2) kupembedzera, kapena kuitanira pa Mkazi wathu kaamba ka kuloŵereramo kwake kwa umayi ndi kwa umfumukazi; . . . ndi mapemphero a mwamseri [kwa Mariya].”

9. Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Mariya anali “amayi a Mulungu”?

9 Ngakhale kuli tero, liwu lakuti the·o·toʹkos silimawoneka m’Malemba owuziridwa. Ndipo palibe kwina kulikonse kumene Baibulo limanena kuti Mariya anali “amayi a Mulungu.” Yesu sanaphunzitse icho, osatinso Akristu a m’zana loyamba. M’kuwonjezerapo, Baibulo mwachimvekere limasonyeza kuti Yesu sanali Mulungu Wamphamvuyonse mu mkhalidwe waumunthu koma anali Mwana wa Mulungu.b Ndithudi, pamene Mariya anadziŵitsidwa ndi mngelo kuti iye akabala mwana wamwamuna, iye anawuzidwa kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe. Chifukwa chachenso yemwe adzabadwa adzatchedwa woyera, mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35, NW) Chotero Yesu anali Mwana wa Mulungu, osati Mulungu iyemwini mu mkhalidwe waumunthu. Ndiponso, Mariya anali amayi a mwana wa Mulungu Yesu, osati amayi a Mulungu mu mkhalidwe waumunthu. Chimenecho ndicho chifukwa chake osati Yesu ngakhalenso ophunzira ake anatcha nkomwe Mariya “amayi a Mulungu.”

10, 11. (a) Ndi zitsanzo zotani zimene zimasonyeza mmene Yesu anawonera amayi ake? (b) Ndimotani mmene atumwi ndi ophunzira a Yesu anawonera amayi ake?

10 Njira imene Yesu anawonera amayi ake imasonyeza malo ake okhala ndi polekezera. Pa phwando la ukwati mu Kana, cholembera cha Baibulo chimatiwuza ife kuti: “Ndipo pakutha vinyo, amake a Yesu ananena naye, Alibe vinyo. Yesu ananena naye, Mkazi, ndiri ndi chiyani ndi inu?” Pano Roman Catholic Douay Version ya Baibulo imaŵerenga kuti: “Mkazi, chimenecho nchiyani kwa ine ndi inu?” (Yohane 2:3, 4) Pa chochitika china, winawake anati kwa iye: “Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.” Umenewo unali mwaŵi wabwino kwa Yesu wa kupereka ulemu wapadera kwa amayi ake ndi kusonyeza kuti ena ayenera kuchita chofananacho. M’malomwake, Yesu anati: “Ayi, Inde, koma odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”​—Luka 11:27, 28.

11 Zilozero zoterozo zimasonyeza kuti Yesu anatenga chisamaliro kusapereka kudzipereka kapena ulemu wosayenera kwa Mariya kapena kuitana iye ndi dzina laulemu lirilonse lapadera. Iye sanalole unansi wawo kumusonkhezera iye. Ndipo atumwi ndi ophunzira anatsatira chitsanzo chake, popeza kulibe kulikonse m’zolembedwa zawo zowuziridwa kumene Mariya wapatsidwa ulemu wosayenerera, dzina laulemu, kapena chisonkhezero. Pamene kuli kwakuti iwo anamlemekeza iye monga amayi a Yesu, iwo sanapite kupyola pa chimenecho. Ndithudi iwo sanalozere nkomwe kwa iye monga “amayi a Mulungu.” Iwo anadziŵa kuti Yesu sanali Mulungu Wamphamvuyonse mu mkhalidwe waumunthu ndipo, chotero, kuti Mariya mothekera sangakhale amayi a Mulungu, malo opitirira kwambiri pa chimene Mawu a Mulungu amalola kaamba ka Mariya.

Nthanthi ya Mulungu Mayi Wachikazi

12. Nkuti ndipo ndi liti pamene lingaliro lakuti Mariya anali “amayi a Mulungu” linayambira?

12 Nkuti, kenaka, kumene lingaliro limeneli linayambira? Ilo mwapang’onopang’ono linaloŵerera mu Chikristu cha Dziko cha mpatuko m’mazana achitatu ndi achinayi a Nyengo yathu Yachisawawa. Ichi chinali tero makamaka pamapeto pa chaka cha 325 C.E. pamene Bungwe la Nicaea linatenga chiphunzitso chosakhala cha m’malemba chakuti Kristu anali Mulungu. Pamene lingaliro lolakwika limenelo linalandiridwa, chinakhala chopepuka kuphunzitsa kuti Mariya anali “amayi a Mulungu.” Ponena za ichi, The New Encyclopædia Britannica ikulongosola kuti: “Dzina laulemu [‘amayi a Mulungu’] likuwoneka kukhala linabuka m’kugwiritsira ntchito kodzipereka, mwinamwake mu Alexandria, nthaŵi ina m’zana la 3 kapena la 4 . . . Podzafika kumapeto kwa zana la 4, Theotokos inali itazikhazikitsa iyo yeni mwachipambano m’zigawo zosiyanasiyana za tchalitchi.” New Catholic Encyclopedia ikudziŵitsa kuti chiphunzitsocho chinalandiridwa mwalamulo “Chiyambire Bungwe la pa Efeso mu 431.”

13. Nchiyani motsimikizirika chimene chinasonkhezera Bungwe la pa Efeso mu 431 C.E. kulengeza mwalamulo Mariya kukhala “amayi a Mulungu”?

13 Chosangalatsa chiri kumene bungwe limeneli linakumanira ndi chifukwa chake. Bukhu lakuti The Cult of the Mother-Goddess, lolembedwa ndi E. O. James, likulongosola kuti: “Bungwe la pa Efeso linasonkhana mu nyumba yotchuka yopempherera ya Theotokos mu 431. Kumeneko, ngati kwina kulikonse, m’mzinda wokhala ndi mbiri yoipa kaamba ka kudzipereka kwake ku Artemis, kapena Diana monga mmene Aroma anatchulira iye, kumene fano lake linanenedwa kukhala linagwa kuchokera kumwamba, pansi pa mthunzi wa kachisi yaikulu yoperekedwa kwa Magna Mater [Mayi Wamkulu] chiyambire 330 B.C. ndipo yokhala ndi, mogwirizana ndi mwambo, malo okhalapo a kanthaŵi a Mariya, dzina laulemu lakuti ‘wobala Mulungu’ silikanalephera konse kusungiliridwa.”

14. Ndimotani mmene mbiri yakale inatsimikizira kuti chiphunzitso chimenechi chiri chachiyambi chachikunja?

14 Chotero mofanana ndi mmene uliri Utatu, chiphunzitso cha “amayi a Mulungu” chiri chiphunzitso cha chikunja chodziwonetsera monga chikhulupiriro Chachikristu. Icho chinali chotchuka mu zipembedzo zakunja mazana angapo Kristu asanafike. The New Encyclopædia Britannica ikulongosola pansi pa mutu wakuti “mulungu mayi wachikazi”: “Iriyonse ya mitundu ya milungu yachikazi ndi zisonyezero zaukazi za kulenga, kubadwa, kubala, kugwirizana kwa kugonana, kulera, ndi zungulirezungulire wa kukula. Liwulo lagwiritsiridwanso ntchito ku zinthu zowumbidwa zochulukira zotchedwa Stone Age Venuses ndi Namwali Mariya. . . . Palibe mwambo womwe sunagwiritsire ntchito zisonyezero zina zaukazi m’kusonyeza milungu yake. . . . Mkaziyo ali mtetezi ndi mlezi wa mwana waumulungu ndipo, mwa kufutukula, wa mtundu wonse wa anthu.” Chotero, wansembe wa Chikatolika Andrew Greely akunena m’bukhu lake lakuti The Making of the Popes 1978 kuti: “Chisonyezero cha Mariya chimagwirizanitsa Chikristu mwachindunji ku zipembedzo zakale [zachikunja] za mulungu mayi wachikazi.”

Kulambira Kosayenera

15. (a) Nchiyani chomwe chinakula mu Chikristu cha Dziko ponena za Mariya? (b) Mogwirizana ndi Baibulo, ndani yekha amene angalankhule ndi Mulungu kaamba ka ife?

15 Kudzinenera kuti Mariya anali “amayi a Mulungu” kumakweza iye ku malo amene anthu angakhoterere ku kumulambira, ndipo chimenecho ndi chimene chachitika kwa zaka mazana angapo. Mazana a mamiliyoni a anthu m’maiko ambiri apemphera kwa iye kapena kupyolera mwa iye ndipo apereka kudzipereka kolambira ku mafano ndi zithunzithunzi zopakidwa utoto zake. Pamene kuli kwakuti anthanthi zaumulungu angayesere kuika chodzikhululukira pa ichi mwakunena kuti kulambira kwa Mariya koteroko kuli kokha njira yosakhala yachindunji ya kulambirira Mulungu, mmenemo simmene Mulungu amawonera icho. “Pali Mulungu mmodzi, ndi mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu.” (1 Timoteo 2:5; 1 Yohane 2:1, 2) Yesu iyemwini ananena kuti: “Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.”​—Yohane 14:6.

16. Ndimotani mmene Petro ndi Yohane akumveketsera kuti kokha Yehova ayenera kulambiridwa?

16 Kupatsa Mariya kudzipereka mwachindunji kapena mosakhala mwachindunji, kupemphera kwa iye, kugwadira mafano ndi zithunzithunzi zopakidwa utoto zake, kuli kulambira chilengedwe m’malo mwa Mlengi. Iko kuli kulambira mafano, ndipo Akristu akulangizidwa “kuthaŵa kupembedza mafano.” (1 Akorinto 10:14) Pamene Korneliyo Wachikunja anagwada mopereka ulemu kwa mtumwi Petro, dziŵani chomwe chinachitika: “Ndipo panali pakuloŵa Petro, Korneliyo anakomana naye, nagwa pa mapazi ake, namlambira. Koma Petro anamuwutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.” (Machitidwe 10:25, 26) Kugwada molambira kwa munthu kunali kosayenera, ndipo Petro sakanalandira iko. Ndiponso, pambuyo pa kulandira masomphenya kuchokera kwa mngelo, mtumwi Yohane akusimba kuti: “Ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo, wakundiwonetsa izo. Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mawu a bukhu iri; lambira Mulungu.” (Chibvumbulutso 22:8, 9) Ngati osati ngakhale mngelo wa Mulungu akayenera kulambiridwa, ndi ochepera chotani nanga anthu kapena mafano awo.

17. Nchiyani chimene bukhu lanazonse la Chikatolika limavomereza kuti chingakhale chotulukapo cha kupatulikitsidwa kwa Mariya?

17 Kunena kuti kudzipereka koteroko kwa Mariya kungatulukepo m’kulambira kosayenera kwavomerezedwa ndi The Catholic Encyclopedia. Kulembedwa koyambirira kwa ntchito imeneyi kunalongosola kuti: “Kunena kuti kudzipereka kotchuka kumeneku kwa Namwali Wodalitsidwa kunali kaŵirikaŵiri kupezedwapo ndi kudzipereka konkitsa ndi kunyazitsa, chiri chosatheka kuchikana.”

18. Kodi chiphunzitso chosakhala cha m’malemba choterocho chingachokere ku magwero otani?

18 Kodi chiphunzitso chosakhala cha m’malemba choterocho chikanachokera ku magwero ati? Magwero enieni ayenera kukhala Mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi. (Yohane 8:44) Nchifukwa ninji iye angapititse patsogolo chiphunzitso choterocho? Kuti achepsye ndi kunyazitsa Mfumu Ambuye Yehova, kukwezeka anthu, ndi kupangitsa chisokonezo. Icho chimapatutsa anthu kuchoka ku kulambira kowona ndi kuwapangitsa iwo m’malomwake kuyang’ana kwa zolengedwa kaamba ka chipulumtuso. Kwa mazana angapo icho chawonjezera mphamvu ya atsogoleri achipembedzo kwa anthu wamba, omwe anaphunzitsidwa kuti iwo ayenera kukhala ogonjera kotheratu kwa atsogoleri awo achipembedzo chifukwa atsogoleri achipembedzo okha anali ndi chidziŵitso cha nthanthi ya zaumulungu yocholowana imeneyo.

19, 20. (a) Nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti ziweruzo za Mulungu zisanaperekedwe, anthu onga nkhosa adzapeza chowonadi? (b) Ndi mafunso otani omwe adzakulitsidwa m’nkhani yotsatira?

19 Ngakhale kuli tero, yesu ananeneratu kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Ndipo Yehova akulonjeza kuti kupyolera mwa kulalikira Ufumu, iye adzasonkhanitsa anthu onse onga nkhosa ‘kuwaphunzitsa za njira zake kotero kuti angayende m’mayendedwe ake.’ (Yesaya 2:2-4) Chifukwa chakuti iwo asonkhanitsidwa ku kulambira koyera kwa Yehova, Yesu anati ponena za iwo: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Chotero awo omwe akufunafuna kaamba ka chowonadi adzachipeza icho ndipo adzamasulidwa kuchoka ku ziphunzitso za chipembedzo chonyenga zomwe zimaletsa anthu kuchita chifuniro cha Mlengi.

20 Pali ziphunzitso zina za chipembedzo zolandiridwa mwachisawawa ndi machitachita omwe apatutsa anthu kuchoka ku kulambira kowona kwa Mlengi, kupereka kudzipereka kwa chilengedwe. Kodi nziti zomwe ziri zina za izi, ndipo nchiyani chomwe chatulukapo kuchokera ku izo? Nchiyani chimene kulambira kowona kumaphatikiza? Nkhani yotsatira idzasanthula mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

a Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary, 1986.

b Onani Nsanja ya Olonda, June 1, 1988, masamba 10-20.

Ndimotani Mmene Mukayankhira?

◻ Ndimotani mmene Yesu mwachimvekere anasonyezera kuti Yehova yekha ayenera kulambiridwa?

◻ Nchifukwa ninji tsopano pali kufulumiza kwapadera m’kulambira moyenerera?

◻ Nchifukwa ninji Mariya sayenera kupatsidwa ulemu wosayenera?

◻ Kodi lingaliro lakuti Mariya ali “amayi a Mulungu” linachokera kuti?

◻ Ndimotani mmene atumwi Petro ndi Yohane anagogomezera kuti Yehova yekha ayenera kulambiridwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena