Musalole Kuti Nyonga Yanu Ikhale Chofooka Chanu
Sitima yapamadzi yotchedwa Titanic ya zipinda 16 zosatha kulowa madzi, ankaganizira kuti n’njosakhoza kumira. Pa ulendo wake woyamba m’chaka cha 1912, inatenga theka lokha la mabwato ofunikira populumutsa miyoyo. Sitima yapamadzi imeneyo inagunda chimwala chachikulu cha madzi oundana ndi kumira, ndipo miyoyo ya anthu oposa 1,500 inatayika.
MFUMU yoopa Mulungu ya Yerusalemu wakale Uziya anali mtsogoleri wagulu la nkhondo wanzeru kwambiri. Ndi thandizo la Yehova, anagonjetsa adani ake mmodzi ndi mmodzi. “Ndi dzina [la Uziya] linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwitsa, mpaka analimbikatu.” Koma kenako “mtima wake unakwezeka . . . nalakwira Yehova Mulungu wake.” Chifukwa chakuti Uziya anadzikuza, anakanthidwa ndi khate.—2 Mbiri 26:15-21; Miyambo 16:18.
Nkhani ziŵirizi zikutiphunzitsa kuti ngati nyonga isoŵa nzeru, kudekha, ndi kudzichepetsa, mosavuta ingathe kukhala zofooka kapena zokhumudwitsa. Zimenezitu n’zofunika kuzilingalira mozama, chifukwa chakuti mwa njira zosiyanasiyana, aliyense wa ife ali ndi nyonga inayake kapena mphatso, ndipo timafuna kuti zimenezi zikhale zopindulitsa komanso magwero a chimwemwe kwa enife ndi kwa ena, makamaka kwa Mlengi wathu. Ndithudi, tiyenera kugwiritsa ntchito mokwanira mphatso iliyonse ya Mulungu yomwe tingakhale nayo koma panthaŵi imodzimodziyo tiyenera kuisamala kuti ikhale yopindulitsa.
Mwachitsanzo, munthu amene amakondetsa ntchito yake mosavuta angapange mphatso imeneyi kukhala chofooka mwa kuloŵerera m’ntchitoyo mopambanitsa. Munthu wosamala pochita zinthu sangapusitsidwe kapena kunyengedwa mosavuta, koma angakhale wosamala posasankhira ena chochita. Kugwira bwino ntchito nako kulinso mbali ina yabwino zedi, koma kukachitidwa mopambanitsa, mwakuti n’kunyalanyaza zoti ukugwira ntchitoyo ndi anthu, chotsatira chake chingakhale kugwiritsa ntchito anthuwo mopanda chikondi, kuwaikira malamulo okhwima zomwe zimabala chisoni. Choncho lingalirani za nyonga yanu kwa kanthaŵi. Kodi mumaigwiritsa ntchito bwino? Kodi ili dalitso kwa ena? Choposa zonse, kodi mumaigwiritsa ntchito polemekeza Yehova, Gwero la “mphatso iliyonse yabwino”? (Yakobo 1:17) Kuti tichitedi zimenezi, tiyeni tipende mosamala kwambiri zitsanzo zina zingapo za nyonga yomwe ingathe kukhala zofooka, kapenanso zokhumudwitsa ngati sitingasamale.
Gwiritsani Ntchito Luso Lakuganiza Mwanzeru
Kuganiza mwaluso kulidi choloŵa chabwino zedi. Komabe, kungakhale chofooka ngati kutipangitsa kukhala wodzidalira mopambanitsa kapenanso kutipanga kukhala ndi malingaliro odzikuza, makamaka ngati ena akutiyamikira kwambiri kapena ngati akutitamanda mopitirira muyezo. Kapena tingayambe kuona Mawu a Mulungu ndi zofalitsa zophunzirira zozikidwa pa Baibulo ngati maphunziro wamba.
Kudzidalira mopambanitsa kungaonekere m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ngati wina wake woganiza mwaluso apatsidwa nkhani mumpingo wachikristu, mwinamwake nkhani yapoyera kapena nkhani iliyonse mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase, iye angayambe mochedwa kwambiri kukonzekera nkhaniyo, mwinanso osapempha n’komwe madalitso kwa Yehova. M’malo mwake, amadalira chidziŵitso chomwe ali nacho ndiponso luso lake la kungoganiza zonena nthaŵi yomweyo. Kwa kanthaŵi, luso lachibadwidwelo lingaphimbe kulephera kwake kukhala wosamala koma popanda madalitso a Yehova, kupita patsogolo kwake mwauzimu kudzazilala, ngakhalenso kuimiratu. N’kuwonongatu mphatso yabwino kumeneku!—Miyambo 3:5, 6; Yakobo 3:1.
Winanso wanzeru kwambiri atha kumangofuna kupeza chidziŵitso poŵerenga Baibulo ndi zothandizira pophunzira Baibulo. Komabe, chidziŵitso choterocho ‘chimangotukumula,’ kapena chimapangitsa munthu kudzikuza; ‘sichimangirira’ ubale wachikondi wachikristu. (1 Akorinto 8:1; Agalatiya 5:26) Kumbali ina, munthu wauzimu, mosasamala kanthu za maluso ake, nthaŵi zonse amapempha ndi kukhulupirira mzimu wa Mulungu. Nyonga yake imapitirizabe kukhala yopindulitsa zedi pamene iye akukula m’chikondi, kudzichepetsa, chidziŵitso, ndi nzeru, ndipo zonsezi zimachitika molinganizika bwino.—Akolose 1:9, 10.
Luso lingakhalenso chofooka ngati m’luso lathu lomwelo tikhala wodzikuza, zomwe zingasonyeze kuti sindife odekha. Munthu yemwe ali ndi mphatso yapadera, komanso amene akum’khumbira monkitsawo, angaiŵale kuti Yehova “sasamalira aliyense wanzeru mumtima,” ngakhale atakhala waluso chotani. (Yobu 37:24) Mawu a Mulungu amati; “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Ngakhale kuti mtumwi Paulo anali wanzeru zabasi ndi wophunzira kwambiri, iye anati kwa Akorinto: “Ine, abale, mmene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru . . . Ine ndinakhala nanu mofooka ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri. Ndipo mawu anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mawu okopa a nzeru, koma m’chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.”—1 Akorinto 2:1-5.
Munthu wanzeru zenizeni sanyengedwa ndi kaonedwe kadziko ka nzeru, kapena ndi zomwe anthu amati n’chipambano. Choncho m’malo mogwiritsa ntchito nzeru zake kuti atamandidwe ndi anthu kapena kuti asonkhanitse chuma, iye amapereka zabwino zake zonse kwa Yemwe anam’patsa moyo ndi maluso akewo. (1 Yohane 2:15-17) Pochita zimenezo amasunga zinthu za Ufumu choyamba m’moyo wake, kukhala wobala zipatso monga “mtengo wooka pa mitsinje ya madzi.” Chifukwa cha madalitso a Yehova, osati maluso ake achibadwa, “zonse azichita apindula nazo.”—Salmo 1:1-3; Mateyu 6:33.
Lolani Chikristu Chiwonjezere Nyonga Yanu
Chikristu mwa icho chokha, n’chodzala ndi nyonga yapamwamba zedi pochiyerekezera ndi mafilosofi akudziko. Mwachitsanzo, njira ya moyo yachikristu, imapanga amuna okwatira ndi akazi okwatiwa abwino kwambiri, anansi abwino koposa, komanso antchito abwino zedi, anthu omwe n’ngokoma mtima, aulemu, amtendere, ndi akhama. (Akolose 3:18-23) Komanso, maphunziro achikristu a kulankhula ndi kuphunzitsa amamanga maluso abwino a kulankhulana. (1 Timoteo 4:13-15) Choncho, n’zosadabwitsa kuti kaŵirikaŵiri olemba anthu ntchito amafuna Akristu kuti awapatse maudindo owonjezeka kapenanso kuwakweza pantchito. Koma n’zotheka kuti nyonga yoteroyo igwiritsidwe ntchito molakwika ngati singayang’aniridwe bwino. Kukwezedwa pantchito kapena kupatsidwa ntchito yapamwamba kungatanthauze kudzipereka kotheratu ku kampaniyo, kuphonya misonkhano yachikristu mobwerezabwereza, kapena kuthera nthaŵi yofunika ku ntchitoyo m’malo moti acheze ndi banja lake.
Ku Australia mkulu wina mumpingo wachikristu, wabanja lake, yemwenso bizinesi yake inkamuyendera bwino zedi, zinali zotheka kwa iye kupeza chuma chambiri ndi kutchuka. Komabe iye anakana chiyeso chokhala wopambana m’njira imeneyo m’dongosolo lino. Iye anati: “Ndinali kufuna kuti nthaŵi yambiri idzitha ndikucheza ndi banja langa komanso ndikuchita utumiki wachikristu.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Choncho ine ndi mkazi wanga tinagwirizana kuti mosamalitsa ine ndiyenera kuchepetsa nthaŵi imene ndimathera pa ntchito yanga yakuthupi. N’kugwiriranji ntchito kwa masiku asanu mlungu uliwonse ngati sindifunikira kutero?” Mwa kusintha zina ndi zina molingalira bwino m’moyo wake, mkulu ameneyu anaona kuti anali wokhozabe kusamalira banja lake mwa kugwira ntchito masiku atatu kapena anayi pamlungu. M’kupita kwanthaŵi, anamuitana kuti akathandize kusamalira maudindo ena monga kutumikira mu Komiti ya Nyumba Yamsonkhano yakwawoko komanso kuyang’anira misonkhano yachigawo. Nyonga yake yotsogozedwa mwanzeruyo inadzetsa chimwemwe ndi kukhutira kwa iye ndi banja lake.
Kusamalira Maudindo Molinganizika
Amuna achikristu akulimbikitsidwa kukalamira maudindo a utumiki mumpingo. “Ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira [kapena mtumiki wotumikira], aifuna ntchito yabwino.” (1 Timoteo. 3:1) Mofanana ndi nyonga yomwe yatchulidwa kale ija, kufunitsitsa kulandira maudindowo kuyeneranso kulingaliridwa bwino. Aliyense sayenera kutenga mautumiki ambirimbiri omwe angamutayire chimwemwe chake muutumiki wa Yehova. Inde, mzimu wofunitsitsa n’ngwoyamikirika, ndithudi n’ngwofunika, potitu Yehova savomereza mzimu wosadzipereka, koma kufunitsitsako kuyenera kusonyezedwa modekha ndi ‘modziletsa.’—Tito 2:12; Chivumbulutso 3:15, 16.
Kudekha, kuzindikira, ndi kukhala tcheru kwa Yesu kunachititsa ngakhale anthu onyozeka kukhala omasuka pamaso pake. Mofananamo lerolino, anthu amakhala omasuka ndi awo omwe nyonga yawo ndiyo umunthu wachifundo komanso kusamala za ena. Mumpingo wachikristu, akulu okoma mtima ndi ofikirika amenewo alidi “mphatso za amuna” zamtengo wapatali zedi. Ali ngati “pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.”—Aefeso 4:8; Yesaya 32:2.
Koma akulu ayenera kugaŵa moyenerera nthaŵi yomwe amathera pothandiza ena ndi imene iwo amafuna popanga phunziro laumwini, posinkhasinkha, popemphera, ndiponso, popanga utumiki wapoyera. Kaŵirikaŵiri, akulu omwe n’ngokwatira amafunanso kukhala ndi nthaŵi yosamalira mabanja awo, ndi kukhala ofikirika kwa aliyense m’banjamo.
Akazi Aluso Ndiwo Madalitso Aakulu Koposa
Monganso akulu aluso, akazi auzimu alinso choloŵa chabwino zedi ku gulu la Yehova. Nthaŵi zambiri, akazi ali ndi mphatso yokhala odera nkhaŵa za anthu ena, khalidwe limene Yehova amaliyamikira ndi kulilimbikitsa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Komano, ‘kupenyerera’ za ena kumeneku kuli ndi malire ake, chifukwa palibe Mkristu yemwe angafune kukhala “wodudukira”; kapena kukhala wamiseche.—1 Petro 4:15; 1 Timoteo 5:13.
Akazi ali ndi mphatso zinanso zambiri. Mwachitsanzo, mkazi wachikristu, angakhale ndi mphatso yoganiza bwino kuposa mwamuna wake. Komabe, monga “mkazi waluso” yemwe amaopa Yehova, adzalemekeza mwamuna wake ndi kugwiritsa ntchito mphatso yakeyo pothangata mwamunayo, osati kupikisana naye. Ndipo m’malo mochita nsanje kapena kumam’nyogodola, mwamuna wanzeru, ndi wodzichepetsa adzalemekeza nyonga ya mkazi wakeyo ndi kuzinyadira. Adzalimbikitsa mkazi wakeyo kuti agwiritse ntchito maluso akewo mmene angathere kuti amange banja lake ndi kuthandiza ana ake ‘kuopa Yehova,’ monga momwe iye amachitira. (Miyambo 31:10, 28-30, NW; Genesis 2:18) Amuna ndi akazi odekha ndi odzichepetsa choterowo, amakhala ndi mabanja omwe amalemekezadi Yehova.
Kulamulira Umunthu Wamphamvu
Umunthu wamphamvu womwe umasonyezedwa pa chilungamo ndi kuchita chifuno cha Yehova ndi mtima wonse ungakhalenso chinthu chabwino pamene usonyezedwa modziletsa komanso modzichepetsa. Komabe, ungathe kukhala chofooka ngati uchititsa munthu kulamulira kapena kuopseza ena. Zimenezi n’zoona makamaka mumpingo wachikristu. Akristu ayenera kukhala omasuka kwa wina ndi mnzake, ngakhale pamene akulu a mpingo alinawo limodzi.—Mateyu 20:25-27.
Ndiyeno akuluwo ayeneranso kukhala omasukirana wina ndi mnzake mwa iwo okha. Ndipo pamene akumana pamodzi, zosankha zawo ziyenera kusonkhezeredwa ndi mzimu woyera, osati mphamvu ya umunthu. Ndithudi, mzimu woyera ungasonkhezere mkulu aliyense m’bungwelo, kuphatikizapo mkulu yemwe ali wamng’ono kwambiri kapena yemwe sakonda kuyankhulapo nthaŵi zambiri. Choncho omwe ali ndi umunthu wamphamvu, ngakhale atadzimva kuti akunena zoona, ayenera kulamulira nyonga yawo mwa kuphunzira luso la kugonjera, motero ‘kuchitira ulemu’ akulu anzake. (Aroma 12:10) Mlaliki 7:16 akuchenjeza mwachikondi kuti: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?”
Yehova, Gwero la “mphatso iliyonse yabwino,” amagwiritsa ntchito nyonga yake yodabwitsa mwaungwiro wonse. (Yakobo 1:17; Deuteronomo 32:4) Ndipotu iye ali Mphunzitsi wathu! Choncho tiyeni tiphunzire kuchokera kwa iye ndi kulimbikira, ponse paŵiri pokulitsa mphatso kapena nyonga yathu yachibadwa, ndi poigwiritsa ntchito mwanzeru, modekha, ndi mwachikondi. Tidzakhalatu dalitso lalikulu zedi kwa ena!
[Zithunzi patsamba 27]
Kupita patsogolo mwauzimu kumadalira pa kuphunzira mwapemphero ndi kudalira Yehova
[Chithunzi patsamba 29]
Kupenyerera za ena limodzi ndi kudekha kuli dalitso
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Courtesy of The Mariners’ Museum, Newport News, VA