Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 38 tsamba 188-192
  • Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Womapitabe Patsogolo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Achinyamata, Yesetsani Kuti Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Chititsani Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kupita Kwanu Patsogolo Kuzionekera
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 38 tsamba 188-192

Phunziro 38

Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere

1, 2. N’chifukwa ninji tonsefe timafunikira kuganiza zopita patsogolo?

1 Pokhala mutaphunzira mosamalitsa ndi kugwiritsa ntchito maphunziro onse a m’buku lino, kodi tsopano mwakonzekera kumaliza Sukulu ya Utumiki Wateokalase? Ayi, pakuti imeneyi ndi sukulu yopitirizabe yophunzitsa ulaliki. Sipakhala kumaliza ponena za kusonkhanitsa chidziŵitso chaumulungu ndi kuchita zimene timaphunzira. M’malo mwake, monga wophunzira wakhama mutha kupitabe patsogolo ndi kuonekera kwa aja okudziŵani.

2 Mtumwi Paulo analimbikitsa wolambira mnzake wachinyamata Timoteo kuti ‘asamale kuŵerenga, kuchenjeza, kuzisamalitsa, ndi kukhala m’zimenezo, kuti kukula mtima kwake [“kupita kwake patsogolo,” NW ] kuonekere kwa onse.’ (1 Tim. 4:13, 15) Inunso, pokhala wolambira Mulungu mmodzimodziyo mukhoza kupita patsogolo moonekera kwa ena. Mungapitebe patsogolo popanda kufika polekezera. Yehova ndiye gwero la chidziŵitso chonse choona, ndipo gwero limenelo lili ngati chitsime chakuya kwenikweni cha madzi otsitsimutsa. Ngakhale sitingafike polekezera kuya kwake, tingathe kumatungabe madzi ake a moyo ndi chitsitsimutso mpaka kalekale. (Aroma 11:33, 34; Yes. 55:8, 9) Nangano m’motani mmene kupita patsogolo kwanu kungaonekere kwa okuonani?

3, 4. Kodi kupita patsogolo kumasonyezedwa motani m’sukulu yateokalase ndi pamisonkhano ina ya mpingo?

3 Njira zoonetsera kupita patsogolo. Njira imodzi yoonetsa kupita kwanu patsogolo ndiyo nkhani zanu za m’sukulu yateokalase. Inuyo mungaone ngati simunapite patsogolo kwenikweni, koma ena angaone kuti mwapita patsogolo kwambiri. M’nkhani imeneyi tonse timakhala ngati mwana amene amaona kuti kukula kwake kukutenga nthaŵi yaitali kwambiri, koma pamene achibale afika kudzacheza, amadabwa kuti: “Ha, ndi mmene wakulira choncho!” Taganizirani nkhani yoyambirira imene munapereka m’sukulu. Kodi mukuikumbukira? Eya, taiyerekezani imeneyo ndi nkhani zimene mwakamba posachedwapa. Mukuona kuti mwaphunzira zambiri ndipo mwadziŵa zochuluka kuchokera nthaŵi imeneyo, si choncho nanga? Chotero pitanibe patsogolo osabwerera m’mbuyo.

4 Kupita patsogolo kumeneko sikuonekera pankhani za m’sukulu yateokalase zokha. Kumaonekeranso pamisonkhano ya mpingo. Kodi mumafika pamisonkhano nthaŵi zonse? Ngati mumatero, umenewo ndi umboni wakuti mukupita patsogolo, ndi kuti mumayamikira zogaŵira za Yehova zotipatsa thanzi lauzimu. Ndiponso, mayankho amene timapereka pamisonkhano angaperekenso umboni wa kupita patsogolo. Aja amene amayankha m’mawu awoawo, m’malo mongoŵerenga mayankho, amaonetsa kupita patsogolo kwawo. Mofananamo, aja amene amapereka ndemanga ponena za tanthauzo ndi phindu la chidziŵitso chimene timaphunzira pa miyoyo yathu amasonyeza kuti akukulitsa luntha lawo. Motero, kufika pamisonkhano nthaŵi zonse ndi kutengapo mbali mogwira mtima, n’kofunika kuti kuonekere makamaka pofuna kuona kuti tapita patsogolo motani.

5. Kodi chimapereka umboni n’chiyani kuti wina akupita patsogolo mu utumiki wake wakumunda?

5 Nanga bwanji za kupita kwanu patsogolo mu utumiki wakumunda? Kumbukirani mmene munamvera pamene munafika pakhomo loyamba lija panthaŵi yoyamba mu utumiki? Yerekezani zimenezo ndi luso lanu la kumakomo tsopano. Pakhala kupita patsogolo, si choncho nanga? Chikhalirechobe, mosakayika konse mukuonabe kuti m’pofunika kuti mupitebe patsogolo kukhala wogwira mtima polalikira ndi pophunzitsa. Ndiponso, kodi n’kotheka kuti mutenge mbali yokulirapo m’magawo onse a ulaliki amene ali otheka kwa inu? Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.” (1 Ates. 4:1) Pamene mukupitabe patsogolo, mukumatenga mbali mokwanira mu utumiki wa Yehova, ulaliki wanu ndi kuphunzitsa kwanu kudzakhala kogwira mtima mowirikiza, komanso chiyamikiro chanu cha mwayi umene muli nawo wotumikira Yehova chidzakhala chozamirapo. Chinkana eninyumba asalabadire, mudzakuonabe kukhala mwayi pogwiritsidwa ntchito ndi Yehova kulalikira uthenga wake kwa anthu.

6. Kodi nkhani zimene munthu amakamba zingaonetse motani kuti wina akukula mwauzimu?

6 Kupita patsogolo kwa munthu kumaonekeranso m’nkhani zake zokambirana. Yesu anati ‘m’kamwa mwa munthu mumalankhula zochuluka zochokera mu mtima.’ (Luka 6:45) Pamene nkhani za munthu ziyedzamira kwambiri kwa Yehova ndi zolinga zake, m’poonekeratu kuti munthuyo akupita patsogolo. Zimasonyeza kuti iyeyo akukula m’kuyamikira Yehova, ndi kuti akuyandikira pafupi kwambiri ndi Mulungu. Ndipo pamene tim’yandikira kwambiri Mulungu, m’pamenenso timakhala otetezeka kwambiri.

7. Kodi kupita patsogolo m’kugwiritsa ntchito mapulinsipulo a Baibulo kungaonekere kuti?

7 Kupita patsogolo kumaonekeranso pogwiritsa ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Kodi si zoona kuti panopo mukuchita zinthu mosiyana ndi mmene munkachitira musanadziŵe Mawu a Yehova? Mwachidziŵikire kupita kwanu patsogolo kumeneko kochita zinthu m’njira ya Yehova kumaonekera m’zochita zanu kwina kulikonse kumene mungakhale. Kumaonekera panyumba panu, mmene mumachitira kwa apabanja panu. Kumaonekera mmene mumatumikirira pamaudindo anu. Kuntchito yakuthupi mumakhala wosamala kwambiri kuti musunge mapulinsipulo a Baibulo. Zonsezo ndi umboni wakuti mwapita patsogolo kwambiri. Koma pamfundo imeneyinso tonsefe tikhoza kulimbikirabe kuti tipite patsogolo, tikumayesetsa kugwiritsa ntchito mapulinsipulo a Baibulo mokwanira.

8, 9. Ngati tidzipereka pothandiza ofalitsa ena, kodi zimenezo zimasonyeza chiyani, ndipo pali mipata yotani imene tingachitire zimenezo?

8 Dziperekeni. Njira ina imene tingaonetsere kupita kwathu patsogolo ndiyo kudzipereka pa utumiki wa Yehova pamlingo wokulirapo. Salmo 110:3 limafotokoza kuti: “Anthu anu adzadzipereka eniake tsiku la chamuna chanu.” Kodi zili choncho kwa inu? Kodi mungadzatero pamlingo wokulirapo m’tsogolo muno?

9 Mungaonetse chidwi chanu mwa kudzipereka pothandiza ena, mukumasonyeza nkhaŵa yeniyeni pa iwo. Akulu mu mpingo angakupempheni kuti muthandize abale kapena alongo m’njira ina. Amenewo angafunikire kuti muwathandize kupita ku misonkhano. Kodi ndinu wodzipereka kuwathandiza? Simuyenera kuyembekeza kuti wina achite kukupemphani kuti muthandize. Bwanji osadzipereka, kuti muthandize aja ooneka kuti akufunikira chithandizo? Kodi pali aliyense amene akudwala kapena amene anam’goneka m’chipatala? M’posafunikira kuti tiyembekeze akulu kuti achite kutiuza. Mukhoza kuchita changu ndi kukawaona kapena kuwathandiza m’njira ina iliyonse ngati mwadziŵa chosoŵa chawo. Kodi muli ndi phunziro la Baibulo la banja lokhazikika m’nyumba mwanu? Kodi sikungakhale kothandiza ku banja lina loyamba chatsopano kusonkhana limene lilibe phunziro loterolo, mutamaliyitana nthaŵi ndi nthaŵi kudzakhala nanu limodzi paphunziro la banja lanu? Kapena ngati mumaloŵa nokha mu utumiki wakumunda, kodi alipo ena amene angakonde kupita nanu mutawapempha kuti apite nanu? Bwanji osakonzekera pasadakhale kuti mukapemphe wofalitsa wina kuti akatsagane nanu? Inde, atumiki a Yehova ndi anthu otanganidwa kwambiri masiku ano, koma chidwi chathu chofuna kuthandiza abale ndi alongo athu chili umboni wa kupita kwathu patsogolo. “Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo apabanja la chikhulupiriro.”—Agal. 6:10.

10, 11. Malinga n’kunena kwa 1 Timoteo 3:1, kodi abale angadzipereke motani?

10 Ngati ndinu mbale, mutha kudzipereka mwa kuyesetsa kufikira ziyeneretso zofotokozedwa m’Mawu a Mulungu kwa aja amene amatsogolera mu mpingo. Timoteo Woyamba 3:1 amayamikira aja amene amakalimira kukhala oyang’anira. Zimenezo sizitanthauza kulimbikira ndi cholinga choti mudzionetsere ayi, kapena kuti mupikisane ndi ena. M’malo mwake, ndiko kulimbikira kuti muoneke kukhala Mkristu wofika pamsinkhu mwauzimu, “mwamuna mkulu,” woyenerera ndi wofunitsitsa kutumikira paudindo uliwonse umene angaikidwepo. Ndipo “amuna akulu” ndi atumiki otumikira n’ngofunikira ambiri mu mpingo uliwonse kuti atsogoze pakuphunzitsa, kulalikira ndi kusamalira maudindo ena a mpingo.

11 Odziperekawo angasangalale ndi mwayi wochuluka mu mpingo. Iwo angapemphedwe kukhala m’zitsanzo pamsonkhano wa utumiki kapena kuthandiza akulu ndi atumiki otumikira chifukwa asonyeza kufunitsitsa kwawo ndi kukhala odalirika pochita ntchito iliyonse imene apatsidwa. Nthaŵi yake ikafika, kudzipereka kwawoko ndi kupita kwawo patsogolo kumawasonyeza kukhala abale amene angavomerezedwe kukhala atumiki otumikira. N’chifukwa chiyani iwo amasankhidwa? Chifukwa chakuti iwo asonyeza kudzipereka kwawo ndipo apita patsogolo, moti tsopano afikira ziyeneretso zimene Yehova wazipereka m’Mawu ake. Osankhidwawo kukhala atumiki nthaŵi ndi nthaŵi amakhala ndi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kuti aphunzitsidwe zoŵirikiza pakayendetsedwe ka zinthu mu mpingo.

12, 13. Kodi ndi mwayi wosiyanasiyana wotani umene ulipo kwa ambiri ofunitsitsa amenenso ali okhoza kudzipereka?

12 Ulipo mwayi wochuluka wosiyanasiyana umene onse angasangalale nawo ngati ali ofunitsitsa komanso ngati mkhalidwe wawo uwalola. Kodi mungadzipereke nthaŵi ndi nthaŵi kukhala mpainiya wothandiza monga momwe ena masauzande ambiri achitira? Mwinamwake mukhoza kukhala mpainiya wokhazikika ndi kuwonjezera chiŵerengero chawo chomawirikiza nthaŵi zonse. Kodi mikhalidwe yanu ndi maganizo anu kulinga ku utumiki wa Yehova zingakuloleni kudzipereka ndi kusamukira ku malo ena kukatumikira komweko, ngati kuli kusoŵa? Ambiri achita zimenezo monga apainiya apadera, kapena mwa kupita ku sukulu ya Gileadi ndi kuloŵa ntchito yaumishonale, kapena monga ofalitsa amene asamuka kukatumikira kumene kusoŵa kuli kokulirapo. Ena akutumikira m’nyumba za Beteli zosiyanasiyana kuzungulira dziko lonse lapansi. Iwo adalitsidwa kwambiri chifukwa adzipereka mofunitsitsa kwa Yehova.

13 Zino ndi nthaŵi zosangalatsa kukhalapo ndi moyo. Yehova akutsogolera ntchito yodabwitsa yolalikira ndi yophunzitsa kuti ichitike m’dziko lonse lapansi ‘m’masiku ano otsiriza.’ Pamene Yehova akugaŵirani gawo lina la utumiki, kudzera m’gulu lake, dzifunseni kuti: “Kodi si Yehova akundigaŵira chimenechi?” Pendani mikhalidwe yanu ndi mtima wanu. Mwachionekere panthaŵi imeneyo inuyo mudzakhala mutapita patsogolo ndithu, ndi kusonyeza kufunitsitsa, ndipo zimenezo n’zabwino. Koma kodi zilipo njira zina zimene mungasonyezere kupita kwanu patsogolo, kuti mudzipereke pamlingo wokulirapo? Pamene mukukula m’kulabadira malangizo a Yehova ndi kutsatira utsogoleri wake, mudzalandira madalitso ochuluka. Atumiki a Yehova odzipereka kuzungulira dziko lonse lapansi akhoza kuikira umboni wakuti zimenezo n’zoonadi. Ndithudi, pakupita kwathu patsogolo m’pamene pagonanso mdalitso waukulu kopambana, moyo wamuyaya m’dziko latsopano la Mulungu. Ndicho chifukwa chake Mawu a Mulungu amafulumiza kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako [“kupita kwako patsogolo”] kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”—1 Tim. 4:15, 16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena