‘Koma Sindimkonda Yehova!’
BOB anali kokha mnyamata wachichepere pamene amayi wake anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Kwa zaka zingapo, iye anatsagana nawo ku Nyumba ya Ufumu ndipo ngakhale m’ntchito yolalikira, ngakhale kuti iye sanabatizidwe konse. Ngakhale kuli tero, pofika nthaŵi imene anafikira pa msinkhu wa pakati pa 13 ndi 19, iye analeka kuyanjana ndi Mboni. Akumakhumudwabe kuchokera ku mkhalidwe woipa umodzi kupita ku wina, iye anaipitsa moyo wake. Ngakhale kuti akudzinenerabe kukhala akukhulupirira zinthu zambiri zomwe anaphunzira kuchokera m’Baibulo, chimenechi sichinali chokwanira kupanga iye kufuna kubwereranso ku gulu la Yehova. Nchifukwa ninji Bob akudzimva mwa njira imeneyi?
Lingalirani chitsanzo china. David anali mtumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zingapo. Kamodzikamodzi, mafunso anadutsa m’malingaliro ake kulinga ku ziphunzitso zina za Baibulo. Koma iye nthaŵi zonse anathetsa mavutowo mwa kulingalira kuti monga mmene ziriri ndi kusonkhanitsa zidutswa zomwazikana za chithunzi kukhala chithunzi chathunthu, munthu samaleka kokha chifukwa chakuti chidutswa chimodzi kapena ziŵiri sizikuwoneka kukwanira poyambirira. Iye anali wokhutiritsidwa kuyembekeza pa Yehova kaamba ka kumveketsedwa. Koma pena pake m’lingaliro limenelo, David anadzinenera kuti iye sanali wokhozanso kudzikhutiritsa iyemwini m’njira imeneyo. Ataleka mathayo ake autumiki, iye mwamsanga anasiya chowonadi. Kodi nchiyani chinachititsa kusinthako m’kuganiza kwake?
Ndithudi, chiri choswa mtima kuwona awo omwe timakonda akuleka pa liŵiro la moyo. Mosakaikira, timafuna kuchita zonse zomwe tingathe kuwathandiza iwo. (2 Akorinto 12:15; Agalatiya 5:7) Koma nchiyani kwenikweni chimene chimapangitsa munthu kugwa kuchoka ku chowonadi? Kodi nchiyani chomwe chingachitidwe kuthandiza munthu woteroyo kubwerera pa liŵirolo? Ndipo kodi nchiyani chimene munthu ayenera kuchita ngati zikhoterero zoterozo zimayamba kukula mwa iye?
Mtima, Chikumbumtima, ndi Chikhulupiriro
Pali chinthu chimodzi chofunika kudziŵa ponena za awo omwe aleka chowonadi. Ochulukira a iwo samatero chifukwa chakuti sakukhulupiriranso kuti icho ndicho chowonadi. Mosemphana kwenikweni, ambiri a iwo amanena kuti, “Ndidziŵa kuti ichi ndicho chowonadi, koma . . . ” kapena, “Ngati pali chowonadi chirichonse, ndidziŵa kuti ndi chimenechi.” Pansi pa mitima yawo, ambiri a iwo amakhulupirirabe kuti chomwe achiphunzira kuchokera m’Baibulo ndicho chowonadi. Koma m’njira ina yake iwo alefula dzanja lawo ndi kutaya changu chawo. Yakobo ananena kuti: “Chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”—Yakobo 2:26.
Chikhulupiriro chowona chimaloŵetsamo kuposa kungokhala ndi chidziŵitso kapena kukhulupirira kuti chinachake chiri chowona. M’malo mwa kungokhala kugwira ntchito kwa maganizo, chikhulupiriro chimaloŵetsamo mtima wophiphiritsira, popeza Baibulo limatiwuza kuti: “Ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo.” (Aroma 10:10) Molingalirika, kenaka, Baibulo limalozera ku mtima monga magwero a mavuto pamene munthu ayamba kupatuka. Monga mmene Paulo anachenjezera: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.”—Ahebri 3:12.
Kuti titsimikizire kuti mtima umaloŵetsedwamo mozama, tingamvetsere kwa Diane, yemwe anali anagwa. Pamene Akristu anzake anayesera kumthandiza, iye momasuka anayankha kuti, “Sindingabwererenso kwa Yehova. Sindimkonda iye!” Iye anadziŵa kuti chinthu chokha chomwe chikanamthandiza iye kukhala chifupi ndi Yehova Mulungu chiri chikondi kaamba ka iye monga Munthu ndipo monga Amene ayenerera kudzipereka kwake. M’chenicheni, unali mtundu umenewu wa chikondi womwe unamsonkhezera iye kupereka moyo wake kwa Yehova poyambirira. Koma mwanjira inayake iye sanachimvenso chikondi choterocho. Popanda icho, iye anadziŵa kuti akangochita zinthu mwachabe ngati anati abwerenso. Koma kodi ndimotani mmene munthu amatayira chikondi chimene kwa nthaŵi ina chinali chomvedwa mozama chotero?
Chabwino, Paulo anatchula “mtima woipa wopanda chikhulupiro.” Mu nkhani zina, kusoŵeka kwa chikhulupiriro koteroko kumatulukapo kuchokera ku kulola mtima kukhumba zinthu zimene Yehova Mulungu amaletsa kapena kukana chinachake chimene iye amalamula. Mtima chotero umakhala wogawanika ndipo sumakhalanso wokwanira kulinga kwa Yehova. Kenaka, atalingalira kuti njira ya kachitidwe ya wina siri yovomerezedwa ndi Mulungu, njira yosavuta kupeŵa kuyang’anizana kowonjezereka iri ‘kulekana ndi Mulungu wamoyo.’ (Yerekezani ndi Genesis 3:8-10.) M’malo mwa kulapa, “mtima woipa” umasonkhezera wina kuchotsapo Yehova ndi chifuno chake kuchoka m’moyo wake. Munthu wopanda chikhulupiriro chotero amaleka chowonadi.
M’nkhani zina, m’malo mwa kuvutika ndi zowawa za chikumbumtima kaamba ka njira ina yake, munthu amalola mtima wake mwachinyengo kumusonkhezera iye kufunafuna pothaŵira mwa luntha kupyolera m’kukaikira, kupeza zolakwa, kapena ngakhale mpatuko. Ngati angadzikhutiritse iyemwini kuti kapangidwe konse ka chikhulupiriro chake kali kolakwika, iye samadzimvanso wathayo kukhala ndi moyo mkati mwa malire ake. Anthu oterowo amakankhira pambali chikumbumtima chabwino ndi kukumana ndi ‘kutayikiridwa chikhulupiriro chawo.’—1 Timoteo 1:19.
Ndithudi, munthu angaleke chowonadi kaamba ka chifukwa china. Koma mosasamala kanthu za chimene icho chiri, chifupifupi mosakanika chimaloŵetsamo mtima. Kaamba ka chifukwa chimenechi, ulidi wa panthaŵi yake uphungu wakuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”—Miyambo 4:23.
Kubwereranso Kuli Kothekera
Kuvomereza kuti zikhoterero zolakwika za ife eni zinali pa maziko a kutayikiridwa kwathu kwa chikhulupiriro kumatenga kulimba mtima. Koma kuchita tero ndiko sitepi loyambirira kulinga ku kugwirira ntchito pa kubwerera kwathu ku unansi wolimba ndi Yehova. Chokumana nacho cha Steve, mpainiya mu England, chimachitira bwino fanizo nsonga imeneyi.
Ngakhale kuti Steve sanagwe konse m’chowonadi, pa nthaŵi ina anayamba kudzimva wopanda kanthu ndi wosoweka chikhutiritso. Pamene iye analalikira kwa ena, mawu ake anamveka opanda kanthu m’makutu a iyemwini. Pamene Steve anali pakati pa abale ndi alongo ake auzimu, anadzimva wosayenera malowo, monga ngati sanali mmodzi wa iwo.
Mwachimwemwe kaamba ka Steve, iye anazindikira kuti vuto linali mwa iyemwini. “Sindinapange chophophonya cha kudzilekanitsa ine mwini kotero kuti ndiganizire zinthu, ngati kuti kunali magwero ena a kuwuziridwa mkati mwathupi lopanda ungwiro omwe akapereka mayankho olondola,” akukumbukira tero Steve. (Yerekezani ndi Aroma 7:18.) M’malomwake, iye anazindikira kuti anayenera kufufuza mtima wake ndi kuzula zikhumbo za chinyengo zomtsogolera iye kusiya chowonadi. Kuyambira pa maziko enieni, iye anagwirira ntchito pa kulimbitsanso chikondi chake kaamba ka Mulungu ndi chikhulupiriro m’Mawu Ake. Lerolino, Steve mwachimwemwe akutumikira monga m’mishonale.
Mmene Ena Angathandizire
Sialiyense yemwe wataikiridwa kapena akutaya dzanja lake pa chowonadi amene amawona zinthu mowonekera bwino monga mmene Steve anachitira. M’chenicheni, kaŵirikaŵiri kuli kutayikiridwa kumeneku kwa kuwona kwauzimu kwabwino komwe kumatsogolera ku kugwa komalizira. Apa ndipo pomwe Akristu anzathu angapereke thandizo. (Aroma 15:1; Agalatiya 6:1) Kodi ndimotani mmene chimenechi chingachitidwire bwino koposa?
Mwachidziŵikire, sikuli kokwanira kuitanira kapena kulimbikitsa munthu woteroyo kubwerera. Zokhumudwitsa zifunikira kudziŵidwa ndi kuchotsedwa. Zoyesayesa ziyenera kupangidwa kuitanira ku mtima wa munthu wofookayo kapena wosakangalika. Kukambitsirana komasuka, koma kokoma mtima, kofikana pa mtima kungathandize munthuyo. Kugwiritsira ntchito malemba onga 1 Timoteo 1:19, Ahebri 3:12, ndi Yeremiya 17:9, 10 kungamuthandize iye kufufuza mwakuya pansi pa mtima wake ndi kuwona chomwe chikumpangitsa iye ‘kulekana ndi Mulungu wamoyo.’
Pamene zochititsazo zazindikiridwa, zoyesayesa ziyenera kutsogozedwa kulinga ku kuchita ndi izo. Mtima wakuthupi wodwala ufunikira chisamaliro ndipo mwinamwake kutumbula kowawitsa ngati wodwalayo ati apulumuke. Chiri chofanana ndi mtima wophiphiritsira wovutitsidwa. Zikhumbo zolakwika, zikhoterero kulinga ku kudziimira pawokha, kapena zinthu zina zomwe zikupangitsa mtimawo kukhala wosokera ziyenera kuchotsedwa ngati uti ukhale wovomereza kachiŵirinso. Akristu okangalika angapempherenso ndi munthu wosakangalikayo, ngakhale kuphunzira Baibulo ndi iye ngati akulu akulingalira chimenechi kukhala cholangizika. Kokha m’njira zoterozo ndi mmene mtima ungadzutsidwenso ndi munthuyo kuyamba kukonda Yehova kachiŵirinso.—Miyambo 2:1-5.
Chimenechi chinali chowona m’nkhani ya Diane. Kukambitsirana ndi Akristu ofikapo kunamthandiza iye kuzindikira chimene anafunikira kuchita kotero kuti adzutsenso chikondi chake kaamba ka Yehova. Atazindikira kuti anafunikira kudziŵa Yehova mwathithithi kachiŵirinso, Diane analandira thandizo loperekedwalo. Pambuyo pophunzira Baibulo kwa chifupifupi chaka chimodzi, iye ndi mwamuna wake anakhalanso atamandi a Yehova okangalika.
Popeza kuti chikondi chimaloŵetsamo ntchito, kaŵirikaŵiri kuli kuchita chimene Yehova amanena ndi kukumana ndi thandizo lachikondi komwe kumatsimikizira kukhala kokhutiritsa koposa. Inde, ntchito imathandiza munthu kupezanso chikondi chimene nthaŵi ina chinasonkhezera mtima wake. (Salmo 34:8) Chimenechi chingayambike mwa kutenga masitepi okangalika kugonjetsa zikhumbo zolakwika kapena kuwongolera zikhoterero zosayenera za mtima. Chilakiko chirichonse m’nkhondo imeneyi chiri sitepi loyandikira ku kubwezera mtima kwa Yehova. (Miyambo 23:26; 1 Petro 2:1-3) Pamene mtima ugonjetsedwa, chikhumbo chimakula kugawana m’chomwe chirimo ndi ena. Chotero, mwamsanga pamene omwe kale anali ofalitsa a Ufumu osakangalika ayeneretsedwa, iwo ayenera kuthandizidwa kugawanamo m’ntchito yolalikira, popeza kuti “ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso.”—Aroma 10:10.
Kwa aliwonse odzimva kuti sakumkondanso Yehova, msewu wobwerera ku moyo waumulungu ungakhale wautali ndipo wovuta. Komabe, kubwerera kwauzimu kwa Steve ndi Diane kuli umboni wakuti kusintha kwa mtima kungachitike. Inde, kubwezeretsedwanso kuli kothekera kupyolera m’kugwira ntchito kwa mzimu wa Yehova, kugwiritsiridwa ntchito kwa Mawu ake, ndi chigwirizano chokhalitsidwa chatsopano ndi gulu lake. Chiri chiyembekezo chathu chowona mtima ndi pemphero kuti anthu oterowo angathandizidwe kusangalala kachiŵirinso m’kulambira Yehova ndi utumiki wopatulika monga awo okonda Yehova ndi mtima wonse.—Marko 12:30; 1 Akorinto 13:8; 3 Yohane 1-4.