Yamikirani Utumiki Wanu Wopatulika
KUTI chonulirapo chilichonse chopindulitsa chifikiridwe, tiyenera kukhala ofunitsitsa kupereka malipiro akutiakuti. Kukhala dokotala kumalira zaka za kuphunzira ndi kutsimikiza mtima, limodzinso ndi ndalama. Katswiri wa maseŵera a jiminasitiki amakhala atawonongera nthaŵi yaikulu ya unyamata wake pa kuyesayesa maluso ovutirapo kwambiri pofuna kukhala wokhoza koposa. Woimba piyano waluso nayenso akhoza kuyang’ana kumbuyo pa zaka za kuyeseza kodzipereka.
Komabe, pali chonulirapo china chimene chimadzetsa mapindu amene amapambana kwambiri malipiro alionse amene angaperekedwe. Kodi nchiyani chimenecho? Ndicho mwaŵi wa kukhala mtumiki wa Wam’mwambamwamba, Yehova Mulungu. Mosasamala kanthu za zinthu zimene tingatayirepo monga, nthaŵi, ndalama, kapena nyonga, mwaŵi wa kupereka utumiki wopatulika kwa Mlengi wathu umadzetsa mphotho zosayerekezereka. Mawu a mtumwi Paulo ali oona akuti: “Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Tiyeni tione mmene zimenezi ziliri zoona.
Pamene Tiphunzira za Mulungu kwa Nthaŵi Yoyamba
Ambiri amene amalabadira mbiri yabwino ndi kuyamba kuphunzira Baibulo mwachionekere samazindikira ukulu wa masinthidwe amene adzachitika m’miyoyo yawo. Choyamba, wophunzira Baibulo watsopano angataye mabwenzi amene satha kumvetsetsa chifukwa chake iye samagwirizananso nawo m’zinthu zimene iye tsopano amazidziŵa kukhala zonyoza Mulungu. (1 Petro 4:4) Ena angayang’anizane ndi chitsutso cha m’banja ndipo angavutike maganizo poona kuti awo amene iwo amawakonda akusonyeza kuipidwa, ngakhale chidani, kwa Yehova. (Mateyu 10:36) Amenewo angakhale malipiro ovuta kuwapereka.
Kuntchito kapena kusukulu, kudzakhalanso malipiro ofunika kuwapereka. Wophunzira Baibulo watsopano m’kupita kwanthaŵi adzaleka kutengamo mbali m’mapwando adziko ndi zikondwerero zina. Sadzamvetseranso malankhulidwe osayenera a anzake apantchito kapena anzake apasukulu, ndipo sadzasekanso nawo nthabwala zotukwana. Mmalomwake, adzayesa kugwiritsira ntchito chilangizo chopezeka pa Aefeso 5:3, 4: “Dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.”
Masinthidwe oterowo angachititse wophunzira Baibulo kukhala wakunja. Zimenezi zingakhale zovuta, makamaka kwa wachichepere kusukulu. Poyang’anizana ndi mapwando a holide nthaŵi ndi nthaŵi, limodzinso ndi ziphunzitso zokana Mulungu, zonga ngati chisinthiko, ndi chisonkhezero cha nthaŵi zonse cha kutsatira aunyinji, Akristu achichepere afunikira kumenya nkhondo yosalekeza ya chikhulupiriro. Kutsatira njira za Mulungu kudzawachititsa kukhala osiyana ndi ena ndipo kungawachititse kusekedwa ndi anzawo a m’kalasi ndi aphunzitsi omwe. Zimenezi nzovuta kwambiri kuzilola m’zaka za kukwiya msanga zoyambira 13 mpaka 19, koma chiyanjo cha Mulungu chili choyenerera malipiro amenewo.
Kodi Izo Zilidi Zotayika?
Zinthu zina zimene poyamba zimaoneka kukhala zotayika zimadzakhala madalitso. Ena amafunikira kutaya chizoloŵezi cha fodya. (2 Akorinto 7:1) Chimenechi chingakhale chovuta, koma limakhala dalitso lotani nanga pamene chizoloŵezi chovulaza chimenechi chigonjetsedwa potsirizira pake! Zilinso motero ponena za kugonjetsa kumwerekera ndi anamgoneka kapena zakumwa zoledzeretsa. Moyo umakhala wabwinopo chotani nanga popanda zizoloŵezi zowononga zotero! Ena amafunikira kulungamitsa maukwati awo. Awo okhala pamodzi popanda ukwati walamulo amakwatirana mwalamulo kapena kuleka kukhala pamodzi. (Ahebri 13:4) Awo okhala ndi akazi ambiri ayenera kutsala kokha ndi mkazi wokula naye. (Miyambo 5:18) Masinthidwe oterowo amaphatikizapo zotayika, koma amadzetsa mtendere panyumba.
Ganizirani za Mfupo Zake
Kunena zoona, aliyense amene amvera malamulo a Yehova amapinduladi. Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wake, wophunzira Baibulo amayamba kutchula Mlengi wake ndi dzina Lake, Yehova. (Salmo 83:18) Wophunzirayo amafikira pa kukonda Yehova pamene aphunzira ponena za zinthu zodabwitsa zimene Iye wachita ndi zimene adzachitirabe mtundu wa anthu. M’maiko amene kuwopa akufa kuli kofala, iye amataya mantha a za malaulo, akumadziŵa kuti akufa ali chigonere, akumayembekezera chiukiriro. (Mlaliki 9:5, 10) Ndipo ndi chitonthozo chotani nanga atazindikira kuti Yehova samazunza anthu kwamuyaya mu helo! Inde, choonadi chimammasuladi.—Yohane 8:32.
Pamene wophunzirayo agwirizanitsa mokulirakulira moyo wake ndi miyezo ya Yehova, amapeza chikumbumtima choyera ndi ulemu waumwini. Kuphunzira kukhala ndi moyo monga Mkristu weniweni kumamthandiza kusamalira bwino lomwe banja lake, kumene kumadzetsa chikhutiro chachikulu ndi chisangalalo. Ndiyeno pali kupezeka pamisonkhano ku Nyumba Yaufumu. Nchochitika chosangalatsa chotani nanga! Kumeneko amapeza anthu amene amasonyezadi chikondi chenicheni chimene Baibulo limanena kuti chiyenera kudziŵikitsa anthu a Mulungu. (Salmo 133:1; Yohane 13:35) Kalankhulidwe kawo kali kaudongo ndi kolimbikitsa pamene alankhula “zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:11) Inde, kuyanjana ndi “gulu lonse la abale” kuli magwero a chimwemwe. (1 Petro 2:17, NW) Mayanjano abwino oterowo amathandiza wophunzira Baibulo kuvala “munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.”—Aefeso 4:24.
Sitepe la Kudzipatulira
Pamene munthu apita patsogolo m’chidziŵitso, potsirizira pake amasonkhezeredwa ndi kukonda kwake Yehova kuti apatulire moyo wake kwa iye ndi kusonyeza chizindikiro cha kudzipatulira kumeneku mwa ubatizo wa m’madzi. (Mateyu 28:19, 20) Uphungu wa Yesu ndi wakuti asanatenge sitepe limeneli, ophunzira ake aŵerengere mtengo. (Luka 14:28) Kumbukirani, Mkristu wodzipatulira amaika chifuniro cha Yehova patsogolo nafulatira zinthu za thupi. Iye amachita zamphamvu kuti ataye “ntchito za thupi” ndi kukulitsa ‘zipatso za mzimu.’ (Agalatiya 5:19-24) Uphungu wopezeka pa Aroma 12:2 tsopano umachita mbali yaikulu m’moyo wake: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” Motero, Mkristu wodzipatulira amakhala ndi moyo wake ndi ganizo latsopano la chifuno.
Komabe, talingalirani zimene iye amalandira. Choyamba, iye tsopano ali pa unansi ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. Iye amalengezedwa wolungama mwa lingaliro la kukhala bwenzi la Mulungu! (Yakobo 2:23) Ndi tanthauzo lozamirapo, iye amatcha Mulungu kuti “Atate wathu wa Kumwamba.” (Mateyu 6:9) Dalitso lina kwa wodzipatulira watsopano ndilo kudziŵa kuti moyo ulidi ndi chifuno ndi kuti iye akukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuno chimenecho. (Mlaliki 12:13) Polondola chitsogozo cha Yesu, akhoza kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wonama mwa kukhalabe wokhulupirika. Zimenezo zimasangalatsa mtima wa Yehova chotani nanga!—Miyambo 27:11.
Ndithudi, pamene Mkristu apirira m’njira ya chikhulupiriro, pamakhalanso zinthu zina zotayirapo. Kuphunzira Mawu a Mulungu kwaumwini ndi kwa mpingo kumafuna nthaŵi. (Salmo 1:1-3; Ahebri 10:25) Nthaŵi ya utumiki wakumunda iyenera kuwomboledwa ku zochita zina. (Aefeso 5:16) Nthaŵi ndi nyonga zimafunikiranso kuti mupezeke pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndi kuti mupite kumisonkhano yawo yadera ndi yachigawo. Mungafunikire kudzimana kuti mugaŵanemo m’kusamalira ndi ndalama Nyumba Yaufumu ndi ntchito yolalikira ya padziko lonse. Komabe, monga momwe Akristu okwanira mamiliyoni angaperekere umboni wa zimenezo, kutengamo mbali m’zinthu zimenezo ndi mtima wonse kumadzetsa chimwemwe. Yesu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Mfupo za kuchirikiza ntchito ya Yehova zimachuluka kwambiri kuposa malipiro ake. Pamene tikukhwima, utumiki wathu umakhala wobala zipatso zochuluka ndi wosangalatsa kwambiri. Ndithudi, palibe chinthu china chilichonse chimene chingatipatse chikhutiro chonga chimene timachipeza mwa kuphunzitsa munthu wina choonadi cha Baibulo ndi kumuona akuyamba kulambira Yehova. Ndipo ngati wolambira watsopanoyo ali chiŵalo cha banja, mwinamwake mwana yemwe waphunzitsidwa “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye,” zimenezo zimadzetsa chisangalalo chapadera. (Aefeso 6:4) Tikuona madalitso olemeretsa a Mulungu pa zoyesayesa zathu za kukhala “antchito anzake.”—1 Akorinto 3:9.
Mfupo Zina za Utumiki Wokhulupirika
Zoona, tidzakhala ndi mavuto malinga ngati dongosolo la zinthu ili lilipobe. Mwachionekere, mavutowo adzakulirakulira pamene nthaŵi ya Mdyerekezi ifupikirafupikira. Tingakumane ndi chizunzo kapena kupirira chiyeso. Koma chidziŵitso chakuti Mulungu ali nafe chimatitonthoza ndipo chimatipatsa nyonga ya kupirira nayo. (1 Akorinto 10:13; 2 Timoteo 3:12) Akristu anzathu ena apirira kuchitiridwa mwankhanza kwa zaka zambiri, koma amachirimika chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu. Awo amene amakhoza kupirira mayesero a mitundu yosiyanasiyana amamva mmene anamvera atumwi pamene anakwapulidwa namasulidwa. Machitidwe 5:41 amasimba kuti: “Pamenepo ndipo anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.”
Mfupo ya kupirira imaposa malipiro ake ngakhale tsopano lino. Koma kumbukirani, chipembedzo “chikhala nalo lonjezano” osati chabe la “ku moyo uno” komanso “la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Nzaulemerero chotani nanga ziyembekezo za munthu amene apirira! Ngati mukhala wokhulupirika, mudzapulumuka chisautso chachikulu chimene chidzakhala mapeto a dongosolo ili la zinthu. Kapena ngati mumwalira chisanafike chochitika chachikulu chimenecho, mudzaukitsidwa m’dziko latsopano limene lidzatsatirapo. (Danieli 12:1; Yohane 11:23-25) Talingalirani za chisangalalo chimene mudzakhala nacho panthaŵi imeneyo pamene mudzakhala wokhoza kunena kuti: “Ndi thandizo la Yehova, ndakhoza!” Nkosangalatsa chotani nanga kukhalamo m’dziko latsopano limenelo, limene “lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Inde, kumatayitsa kanthu kena kutumikira Mulungu. Koma poyerekezera ndi mfupo zake, kanthu kotayikako kamakhala kosanunkha kanthu. (Afilipi 3:7, 8) Poona zonse zimene Mulungu amachitira atumiki ake tsopano ndi zimene adzawachitirabe mtsogolo, timabwereza mawu a wamasalmo akuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?”—Salmo 116:12.