‘Lolani Kupita Patsogolo Kwanu Kuwonekera’
“Tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.”—1 AKORINTO 13:11.
1. Kodi ndimotani mmene kukula kuliri umboni wa chozizwitsa cha chilengedwe?
KUYAMBIRA pakadzira kamene kangawonedwe kokha ndi maikolosikopo, nangumi angakule kukhala cholengedwa chautali wa mamitala 30 ndi kulemera matani oposa 80. Mofananamo, kuchokera pakambewu kamodzi kochepetsetsa, mtengo wa sequoia waukulukuluwo ungakule kufikira mamitala 90 kutalika. Ndithudi, kukula ndiko chimodzi cha zozizwitsa za moyo. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, tingawoke ndi kuthirira, koma ali “Mulungu amene akulitsa.”—1 Akorinto 3:7.
2. Kodi ndimtundu wotani wa kukula umene unanenedweratu m’Baibulo?
2 Komabe, pali mtundu wina wa kukula umene mofananamo uli wodabwitsa. Ndiwo umene unanenedweratu ndi mneneri Yesaya kuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:22) Ulosi umenewu ukuphatikizapo kuwonjezereka kwa anthu a Mulungu, ndipo ukukwaniritsidwa mumkhalidwe waukulu m’tsiku lathu.
3. Kodi ndimotani mmene lipoti la chaka chautumiki cha 1991 linasonyezera kuti Yehova akufulumizitsa ntchito ya anthu ake?
3 Lipoti la chaka cha utumiki cha 1991 la ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova limasonyeza kuti chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chinafika pachiŵerengero chapamwamba chatsopano cha 4,278,820, ndipo chiwonkhetso cha anthu 300,945 anabatizidwa mkati mwa chakacho. Pokhala ndi unyinji wotero wa atsopano oloŵa m’gulu, mipingo yatsopano 3,191 inaumbidwa, limodzi ndi chiŵerengero choyenerera kuumbira madera atsopano ndi zigawo. Izi zitanthauza mipingo yatsopano yoposa isanu ndi itatu patsiku, pafupifupi dera latsopano limodzi masiku aŵiri alionse. Ndikuwonjezereka kodabwitsa chotani nanga! Mwachiwonekere, Yehova akufulumizitsa zinthu, ndipo dalitso lake liri pazoyesayesa za anthu ake.—Salmo 127:1.
Nthaŵi ya Kudzipenda
4. Kodi ndimafunso otani amene ayenera kulingaliridwa pamene tikuyang’ana mtsogolo?
4 Ngakhale kuli kwakuti nkosonkhezera mtima kuliwona, dalitso limeneli limabweretsanso mathayo akutiakuti. Kodi padzakhala anthu okula msinkhu ofunitsitsa kusamalira zosoŵa zauzimu za atsopano onseŵa? Pamene tikuyang’ana mtsogolo, kuli kochititsa kakasi kuganiza za chiŵerengero cha apainiya, atumiki otumikira, akulu, ndi oyang’anira oyendayenda amene adzafunika kusamalira kuwonjezereka ndi kufutukuka, ndiponso chiŵerengero cha antchito odzifunira ofunika m’maofesi anthambi ndi Nyumba za Beteli kuzungulira dziko lonse kuchirikiza ntchito imeneyo. Kodi chiŵerengero chachikulu cha anthu chimenechi chidzachokera kuti? Palibe kukayikira kuti kututako nkwakukulu. Koma kodi ndani lerolino amene ali okhoza kusamalira antchito onse ofunika kututa dzinthuzo?—Mateyu 9:37, 38.
5. Kodi ndimikhalidwe yotani imene iri m’madera ena chifukwa cha kuwonjezereka kofulumira?
5 Mwachitsanzo, kwasimbidwa kuti, m’mbali zina za dziko, muli mipingo yokhala ndi ofalitsa Aufumu ochuluka kufikira zana otumikiridwa ndi mkulu mmodzi yekha limodzi ndi mtumiki wotumikira mmodzi kapena aŵiri. Nthaŵi zina mkulu mmodzi amafunikira kutumikira m’mipingo iŵiri. Kumalo ena kusoŵa kwa aminisitala Achikristu oyeneretsedwa kuchititsa maphunziro Abaibulo nkwakukulu kwambiri kotero kuti atsopano afunikira kuikidwa pampambo woyembekezera. Ndiponso, m’madera ena mipingo yatsopano ikuumbidwa pamlingo wofulumira kwambiri kwakuti mipingo itatu, inayi, kapena ngakhale isanu ifunikira kugwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu imodzi. Mwinamwake inu mwawona chiwonjezeko chonga chimenechi m’dera lanu.
6. Kodi nchifukwa ninji kudzipenda kuli kwapanthaŵi yake kwa ife?
6 Kodi zonenedwa pamwambapa zikutiuzanji? Kuti chifukwa cha nthaŵiyi, tonsefe tifunikira kupenda mikhalidwe yathu kuwona ngati tikugwiritsira ntchito nthaŵi yathu bwino kwambiri ndi chuma kotero kuti tichitepo kanthu pakusoŵako. (Aefeso 5:15-17) Mtumwi Paulo analembera Akristu Achihebri a m’zaka za zana loyamba kuti: “Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.” (Ahebri 5:12) Monga momwe mwawuwo akusonyezera, Akristu alionse paokha amafunikiranso kukula. Ndipo pali upandu weniweni waukulu wakuti munthu angamangokhalabe muukhanda wauzimu mmalo mwa kupita patsogolo kuuchikulire Wachikristu. Mogwirizana ndi zimenezi, Paulo amatifulumiza kuti: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.” (2 Akorinto 13:5) Kodi mwadzipenda kuwona ngati mwakhala mukukula mwauzimu chiyambire nthaŵi yaubatizo wanu? Kapena kodi mwakhala mutangoima chiriri? Komabe, kodi ndimotani mmene munthuwe ungadziŵire?
‘Zizoloŵezi Zachibwana’
7. Kuti kupita patsogolo kwathu kwauzimu kuwonekere, kodi tiyenera kuchitanji?
7 “Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingilira ngati mwana, ndinaŵerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana,” anatero mtumwi Paulo. (1 Akorinto 13:11) M’kukula kwauzimu, panthaŵi ina tonsefe tinali monga ana m’kuganiza kwathu ndi machitidwe. Komabe, kuti kupita patsogolo kuwonekere, tiyenera kuchotsa ‘zizoloŵezi zachibwana,’ monga momwe Paulo ananenera. Kodi nchiyani chimene chiri zina za zizoloŵezi zachibwana zimenezi?
8. Malinga ndi mawu a Paulo pa Ahebri 5:13, 14, kodi nchiti chimene chiri chizoloŵezi china cha khanda lauzimu?
8 Choyamba, wonani mawu a Paulowo pa Ahebri 5:13, 14 akuti: “Yense wakudya mkaka alibe chizoloŵezi cha mawu a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chiri cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” Kodi ndinu ‘wozoloŵerana ndi mawu a chilungamo’? Kodi mumadziŵa Mawu a Mulungu, Baibulo, mokwanira kotero kuti mukhoza kuligwiritsira ntchito “kusiyanitsa chabwino ndi choipa”? Paulo anati anthu aakulu msinkhu ali okhoza kutero chifukwa chakuti amadya mokhazikika “chakudya chotafuna.” Motero, chikhumbo cha munthu kapena njala ya chakudya chauzimu chotafuna ndicho chisonyezero chabwino cha kuti kaya munthuyo wakula mwauzimu kapena adakali khanda lauzimu.
9. Kodi ndimotani mmene njala ya munthu yauzimu iriri chisonyezero chake cha kupita patsogolo kwauzimu?
9 Pamenepo, kodi njala yanu yauzimu njotani? Kodi mumalingalira motani kakonzedwe ka chakudya chauzimu chambiri chimene Yehova amapereka mokhazikika kupyolera m’mabukhu Abaibulo ndi misonkhano Yachikristu ndi misonkhano yadera? (Yesaya 65:13) Mosakayikira mumasangalala kwambiri ngati mabukhu atsopano atulutsidwa pamisonkhano yachigawo ya chaka ndi chaka. Koma kodi mumachita nawonji pamene mufika kunyumba? Kodi mumachitanji pamene kope latsopano la magazini a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! lafika? Kodi mumapatula nthaŵi kuti muŵerenge zofalitsidwa zimenezi, kapena mumangosuzumira kokha mkati mwake kuti muwone mfundo zazikulu ndiyeno kuwaika pamodzi ndi ena pashelefu yanu? Mafunso ofananawo akhoza kufunsidwa ponena za misonkhano Yachikristu. Kodi mumafika pamisonkhano yonse mokhazikika? Kodi mumaikonzekerera ndiponso kukhalamo ndi phande? Mwachiwonekere ena agwera m’chizoloŵezi choipa cha kudya kwauzimu, kungoyepula pamwamba ndi kudya mothamanga, kunena kwake titero. Nkosiyana chotani nanga ndi mmene kunaliri ndi wamasalmo, amene anati: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.” Ndiponso, Mfumu Davide anati: “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu: m’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.” (Salmo 35:18; 119:97) Mwachiwonekere, ukulu umene timasonyeza nawo chiyamikiro cha makonzedwe auzimu ndiwo chisonyezero cha kupita kwathu patsogolo kwauzimu.
10. Kodi ndichizoloŵezi chotani cha khanda lauzimu chimene chasonyezedwa pa Aefeso 4:14?
10 Paulo anatchula chizoloŵezi china cha khanda lauzimu pamene anachenjeza kuti: “Tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa.” (Aefeso 4:14) Monga momwe makolo amadziŵira bwino lomwe, ana ali ndi chidwi pazinthu zonse. Mwanjira ina chimenechi ndicho chizolŵezi chabwino chifukwa chakuti chimawakhozetsa kutulukira ndi kuphunzira ndipo pang’ono ndi pang’ono kukula kukhala anthu aakulu msinkhu. Komabe, upandu wake wagona m’kukhala kwawo osavuta kucheukitsidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. Choipirapo kwambiri ndicho chakuti, chifukwa cha kusoŵa chidziŵitso, kaŵirikaŵiri chidwi chimenechi chimawatsogolera kumavuto aakulu, ngakhale kudziika paupandu iwo eni ndi anthu ena. Zimenezi zirinso zowona ponena za makanda auzimu.
11. (a) Kodi Paulo anali kulingaliranji pamene anagwiritsira ntchito mawu akuti “mphepo yonse ya chiphunzitso”? (b) Kodi ndi‘mphepo’ zotani zimene timayang’anizana nazo lerolino?
11 Komabe, kodi nchiyani chimene Paulo anali kulingalira pamene ananena kuti makanda auzimu amatengekatengeka ndi “mphepo yonse ya chiphunzitso”? Panopo, “mphepo” ikutembenuzidwa kuchokera kuliwu Lachigiriki aʹne·mos, limene International Critical Commentary imanena kuti mwachiwonekere “nlosankhidwa kukhala loyenerera m’lingaliro la kukhoza kusintha.” Zimenezi zikuchitiridwa chitsanzo bwino lomwe ndi mawu otsatira a Paulowo, “ndi tsenga la anthu.” Liwulo “tsenga” m’chinenero chake choyambirira kwakukulukulu limatanthauza “mayere” kapena “kuseŵera mayere,” ndiko kuti, seŵero la wa mwaŵi ndani. Mfundo yake njakuti timayang’anizana ndi malingaliro atsopano mosalekeza ndi zolondoledwa zimene zingawonekere kukhala zopanda upandu, zosayesa, ngakhale kukhaladi zoyenerera. Mawu a Paulo kwakukulukulu amagwira ntchito kunkhani zokhudza chikhulupiriro chathu—timagulu topititsa patsogolo umodzi wa matchalitchi wapadziko lonse, zolinga za chitaganya ndi zandale, ndi zina zotero. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 4:1.) Koma lamulo la makhalidwe abwinolo likugwiranso ntchito ponena za kudzikometsera ndi mafashoni zosinthasintha mosalekeza zadzikoli—masitayelo, zosangulutsa, zakudya, njira zosungira thanzi kapena kudzilimbitsa thupi, ndi zina zotero. Chifukwa cha kupanda chidziŵitso ndi chiweruzo chabwino, khanda lauzimu lingacheukitsidwe monkitsa ndi zinthu zotero ndipo motero lingalepheretsedwe kupanga kupita patsogolo kwauzimu ndi kulephera kusenza mathayo ake ofunika kwambiri Achikristu.—Mateyu 6:22-25.
12. Kodi ana ang’ono amasiyana motani ndi anthu achikulire ponena za kusenza thayo?
12 Chizoloŵezi china cha achichepere ndicho cha kufuna kwawo chithandizo ndi chisamaliro kosalekezako. Iwo samazindikira kapena kudera nkhaŵa ndi mathayo; ubwana ndiwo nthaŵi ya moyo pamene pafupifupi chirichonse chiri chosangalatsa ndi maseŵera. Monga momwe Paulo ananenera, ‘amalankhula monga khanda, kuganiza monga khanda, kulingalira monga khanda.’ Iwo amawona zinthu mopepuka kuti ena adzawasamalira. Zofananazo zinganenedwe ponena za khanda lauzimu. Pamene watsopano apereka nkhani yake yoyamba ya Baibulo kapena ayamba kumene kutuluka muutumiki wakumunda, kholo lauzimu limakondwera kuchita zirizonse kuthandiza. Kodi chimachitika nchiyani ngati watsopanoyo apitirizabe kudalira pachithandizo chotero ndi kutsimikizira kukhala wosakhoza kulandira mathayo akudzisamalira? Mwachiwonekere zimenezo zikakhala chisonyezero cha kusadzigwiritsira ntchito kwake.
13. Kodi nchifukwa ninji aliyense ayenera kuphunzira kusenza katundu wa iye mwini?
13 Ponena za zimenezi kumbukirani chilangizo cha mtumwi Paulo chakuti ngakhale kuti tiyenera “kunyamulirana zothodwetsa,” komabe “yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:2, 5) Zowonadi, pamafunikira nthaŵi ndi kuyesayesa kuti munthu aphunzire kusenza mathayo ake Achikristu, ndipo kungatanthauze kudzimana m’mbali zina. Komabe, kukakhala kulakwa kwakukulu kudzilola kukhala wophatikizidwa kwambiri m’zokondweretsa ndi maseŵera a moyo, kaya kukhale kusanguluka, maulendo, ziwiya zazing’ono zogwiritsira ntchito, kapena ngakhale kulondoledwa kosafunikira kwa ntchito yakudziko, kwakuti munthu amangokhala chabe wowonerera, titero kunena kwake, wopanda chikhumbo cha kuwonjezera kukhala ndi phande kwake m’ntchito yopanga ophunzira kapena kukalimirira kupita patsogolo kwauzimu ndi thayo. “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha,” anafulumiza motero wophunzira Yakobo.—Yakobo 1:22; 1 Akorinto 16:13.
14. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhutira ndi kusonyeza zikhotetero za khanda lauzimu?
14 Inde, pali zizoloŵezi zambiri zosavuta kuzizindikira zimene zimasiyanitsa khanda ndi munthu wachikulire. Komabe, chinthu chofunika, monga momwe Paulo ananenera, ndicho chakuti pang’ono ndi pang’ono tichotse zizoloŵezi zaubwana ndi kukula. (1 Akorinto 13:11; 14:20) Apo phuluzi, tingakhale otsalira m’lingaliro lauzimu. Koma kodi munthu amapita patsogolo motani? Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa m’kusunga kukula msinkhu kwauzimu kumka kuuchikulire?
Mmene Kupita Patsogolo Kumawonekera
15. Kodi ndimasitepe oyambirira otani amene amachitika pokula?
15 Eya, kodi kukula kwakuthupi kumachitika motani? Munthu aliyense amayamba kukhala ndi moyo monga selo limodzi,” imafotokoza motero The World Book Encyclopedia. “Selolo limaloŵetsa zinthu ndi kuzisanduliza kukhala njerwa zomangira zimene limafunikira kuti likule. Motero, selo limodzi limakulira mkati. Selo limeneli lingadzichulukitse ndi kugaŵanika kupanga maselo ena. Mchitidwe wa kumanga, kudzichulukitsa, ndi kugaŵanikako ndiwo kukula.” Mfundo yofunika pano ndiyo yakuti kukulako kumachitika mkati. Pamene chakudya choyenera chiloŵetsedwa, kupukusidwa, ndi kugwiritsiridwa ntchito, kukula kumachitika. Zimenezi zimawoneka bwino lomwe m’chochitika cha khanda lobadwa chatsopano. Monga momwe tidziŵira, khandalo limadya chakudya cholinganizidwa mwapadera mosalekeza, mkaka, umene uli ndi mafuta ochuluka ndi maprotini, zithu zimene zimafunika pokukula. Ndi chotulukapo chotani? Mlingo wa kukula kwa khandalo ponena za kunenepa ndi kutalika m’chaka choyamba sungayerekezeredwe konse ndi chaka china chirichonse cha kukula kozoloŵereka pamoyo wonse wakhandalo.
16. Kodi ndimtundu wanji wa kukula umene umawonedwa mwa ophunzira Baibulo ochuluka, ndipo kodi zimenezo zimatheketsedwa motani?
16 Pali zambiri zimene timaphunzira kuchokera m’kukula kwakuthupi kumeneku kumene tingagwiritsire ntchito kukupita kwathu patsogolo kwauzimu kuchokera pazoyambirira kumka kuuchikulire. Choyamba, programu ya kudya mosalekeza njofunika. Taganizirani kalelo pamene munayamba kuphunzira Baibulo kwanthaŵi yoyamba. Ngati muli wofanana ndi anthu ena ochuluka, mwinamwake simunadziŵe chirichonse ponena za Mawu a Mulungu. Koma mlungu ndi mlungu munakonzekera zigawo zanu zophunziridwa ndipo munali ndi phunziro lanu la Baibulo, ndipo munthaŵi yochepa chabe, munafikira pakuzindikira ziphunzitso zonse zazikulu Zamalemba. Zimenezo, muyenera kuvomereza kuti, zinali kukula kwapadera, ndipo konseko kunali chotulukapo cha kudya pa Mawu a Mulungu mokhazikika!
17. Kodi nchifukwa ninji programu ya kulandira chakudya chauzimu yokhazikika iri yofunika kotheratu?
17 Komabe, bwanji tsopano lino? Kodi mumatsatirabe programu yokhazikika ya kulandira chakudya? Munthu sayenera kuganiza kuti kokha chifukwa chakuti iye wabatizidwa, palibe chifukwa chirichonse chofunira phunziro lokhazikika ndi ladongosolo loloŵetsera chakudya chauzimu. Ngakhale kuti Timoteo anali woyang’anira Wachikristu wokula msinkhu, Paulo anamfulumiza kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15) Nkofunika kwambiri chotani nanga kuti aliyense wa ife afunikira kuchita motero! Ngati muli wokondweretsedwa m’kupangitsa kupita patsogolo kwanu kuwonekera, zoyesayesa zotero nzofunika kotheratu.
18. Kodi kupita patsogolo kwa munthu kumawonekera motani?
18 Kulola kupita patsogolo kwa munthu kuwonekera sikumatanthauza kupanga kuyesayesa kwapadera kwa kudziwonetsera ponena za zimene munthuyo amadziŵa kapena kuyesa kuchititsa chidwi ena. Yesu anati: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika” ndipo, “mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 5:14; 12:34) Pamene mitima yathu ndi maganizo zidzazidwa ndi zinthu zabwino za Mawu a Mulungu, sitingachitire mwina kusiyapo kusonyeza zimenezi m’zimene timachita ndi kunena.
19. Kodi tiyenera kukhala otsimikizira kuchitanji ponena za kupita kwathu patsogolo kwauzimu, ndipo ndi chotulukapo chotani m’malingaliro?
19 Chifukwa chake, funso ndilo lakuti: Kodi mumaphunzira Baibulo mokhazikika ndi kufika pamisonkhano Yachikristu kudzalandira chakudya chokhutiritsa chimene chingasonkhezere kukula kwanu kwamkati, kwauzimu? Musakhutiritsidwe ndi kukhala wowonerera wamphwayi pankhani ya kukula kwauzimu. Tengani masitepe otsimikizirika kuti mutsimikizire kuti mukugwiritsira ntchito mokwanira chakudya chauzimu chochuluka chimene Yehova amapereka. Ngati muli munthu amene ‘amakondwera m’chilamulo cha Yehova, ndipo mumaŵerenga molingalira chilamulocho usana ndi usiku,’ pamenepo kunganenedwenso kwa inu kuti: ‘Mudzafanana ndi mtengo wooka pamitsinje ya madzi, umene umabala zipatso zake panyengo yake ndipo tsamba lake silimafota, ndipo zonse zomwe muchita mudzapambana.’ (Salmo 1:2, 3) Komabe, kodi nchiyani chimene chingachitidwe kutsimikizira kuti mudzapitirizabe kupanga kupita patsogolo kwauzimu? Zimenezi tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungayankhe?
◻ Kodi nchifukwa ninji kupenda kupita patsogolo kwathu kwauzimu kuli kwapanthaŵi yake?
◻ Kodi ndimotani mmene kukula kwauzimu kuliri kogwirizana ndi njala yauzimu?
◻ Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwa mawu akuti “mphepo yonse ya chiphunzitso”?
◻ Kodi nchifukwa ninji aliyense ayenera kudzinyamulira katundu wake?
◻ Kodi kupita patsogolo kwauzimu kumapezedwa motani?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi mumapatula nthaŵi ya kuŵerenga mabukhu ofotokoza Baibulo?