Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 9/15 tsamba 14-19
  • Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka Kwaumulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka Kwaumulungu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Chili Kudzipereka Kwaumulungu
  • Kodi Ndimotani Mmene Timapezera Kudzipereka Kwaumulungu?
  • Kusonyeza Kudzipereka Kwaumulungu Panyumba
  • Kudzipereka Kwaumulungu ndi Utumiki
  • Onjezerani Kudzipereka kwa Mulungu pa Chipiriro Chanu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Londolani Kudzipereka Kwaumulungu Monga Akristu Obatizidwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Tsatirani Chitsanzo cha Yesu cha Kudzipereka Kwaumulungu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu”
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 9/15 tsamba 14-19

Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka Kwaumulungu

“Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro, pachipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu.”​—2 PETRO 1:5, 6, NW.

1, 2. (a) Kuyambira m’ma 1930, kodi nchiyani chimene chinachitikira Mboni za Yehova zokhala m’maiko olamuliridwa ndi Nazi, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova anachitira pansi pa nkhanza zimenezi?

INALI nthaŵi yamdima m’mbiri ya zaka za zana la 20. Kuyambira m’ma 1930, Mboni za Yehova zikwi zambiri m’maiko olamuliridwa ndi Nazi zinamangidwa mosayenera ndi kuponyedwa m’misasa yachibalo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zinasunga uchete wawo ndi kukana kutamanda Hitler. Kodi zinachitiridwa motani? “Palibe kagulu kena ka andende . . . kamene kanachitiridwa nkhanza yomkitsa ndi asilikali a SS mofanana ndi Ophunzira Baibulo [Mboni za Yehova]. Inali nkhanza ya kuzunza mwakuthupi ndi maganizo kosatha, kuzunza kosafotokozeka.”​—Karl Wittig, yemwe kale anali mkulu wa m’boma la Germany.

2 Kodi Mbonizo zinachita motani? M’buku lake lakuti The Nazi State and the New Religions: Five Case Studies in Non-Conformity, Dr. Christine E. King anati: “Ndi kwa Mboni zokha [mosiyana ndi magulu ena azipembedzo] kumene boma silinapezeko chipambano.” Inde, Mboni za Yehova monga gulu zinachilimika zolimba, ngakhale kuti kwa mazana ambiri a izo, zimenezi zinatanthauza kupirira kufikira imfa.

3. Kodi nchiyani chimene chakhozetsa Mboni za Yehova kupirira mayesero aakulu?

3 Kodi nchiyani chimene chakhozetsa Mboni za Yehova kupirira mayesero otero osati mu Nazi wa Germany yekha koma kuzungulira dziko lonse? Atate wawo wakumwamba wawathandiza kupirira chifukwa cha kudzipereka kwawo kwaumulungu. “Yehova adziŵa kupulumutsa odzipereka mwaumulungu poyesedwa iwo,” amafotokoza motero mtumwi Petro. (2 Petro 2:9, NW) Pachiyambiyambi m’kalata yomweyo, Petro anali atalangiza Akristu kuti: “Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro, pachipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu.” (2 Petro 1:5, 6, NW) Chotero chipiriro nchogwirizanitsidwa kwambiri ndi kudzipereka kwaumulungu. Kwenikweni, kuti tipirire kufikira mapeto, tiyenera ‘kulondola kudzipereka kwaumulungu’ ndi kukusonyeza. (1 Timoteo 6:11) Koma kodi kwenikweni kudzipereka kwaumulungu nchiyani?

Chimene Chili Kudzipereka Kwaumulungu

4, 5. Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani?

4 Nauni Lachigiriki lotembenuzidwa “kudzipereka kwaumulungu” (eu·seʹbei·a) kwenikweni lingatembenuzidwe kukhala “kuchitira ulemu koyenera.”a (2 Petro 1:6, Kingdom Interlinear) Limapereka lingaliro la kukonda Mulungu ndi mtima wonse. Malinga nkunena kwa W. E. Vine ajekitiviyo eu·se·besʹ, kwenikweni kutanthauza “kuchita mantha moyenera,” amasonyeza “nyonga, yolamulidwa ndi mantha oyera kwa Mulungu, osonyezedwa ndi ntchito zodzipereka.”​—2 Petro 2:9, Int.

5 Chifukwa chake mawu akuti “kudzipereka kwaumulungu” amanena za ulemu kapena kudzipereka kwa Yehova kumene kumatisonkhezera kuchita chimene chili chomkondweretsa. Zimenezi zimachitidwa ngakhale povutika ndi mayesero aakulu chifukwa chakuti timakonda Mulungu kochokera mumtima. Kumamatirana kokhulupirika ndi Yehova kumeneku, nkumene kumasonyezedwa ndi njira imene timakhalira ndi moyo wathu. Akristu owona akufulumizidwa kupemphera kotero kuti akhale “a moyo wodekha ndi auchete odzazidwa ndi kudzipereka kwaumulungu.” (1 Timoteo 2:1, 2, NW) Malinga nkunena kwa olemba dikishonale J. P. Louw ndi E. A. Nida, “m’zinenero zingapo [eu·seʹbei·a] wa pa 1 Tm 2.2 angatembenuzidwe moyenerera kukhala ‘kukhala ndi moyo monga momwe Mulungu akufunira’ kapena ‘kukhala ndi moyo monga momwe Mulungu watiuzira.’”

6. Kodi kugwirizana kwa chipiriro ndi kudzipereka kwaumulungu nkotani?

6 Tsopano tikhoza kuzindikira bwino kwambiri mgwirizano umene uli pakati pa chipiriro ndi kudzipereka kwaumulungu. Chifukwa chakuti timakhala ndi moyo monga momwe Mulungu afunira​—ndi kudzipereka kwaumulungu​—timakwiyitsa dziko, limene limadzetsa ziyeso za chikhulupiriro mosalekeza. (2 Timoteo 3:12) Koma palibe njira imene tikanasonkhezeredwa nayo kupirira ziyeso zotero ngati sitikanamamatirana ndi Atate wathu wakumwamba. Ndiponso, Yehova amachitapo kanthu pakusonyezedwa kwa kudzipereka kwamtima wonse kumeneko. Tayerekezerani mmene kumamkhudzira mtima kuyang’ana pansi pano ali kumwamba ndi kuona awo amene, chifukwa cha kudzipereka kwawo kwa iye, akuyesayesa kumkondweretsa mosasamala kanthu za mitundu yosiyanasiyana ya chitsutso. Mposadabwitsa kuti iye ali wofunitsitsa ‘kupulumutsa odzipereka mwaumulungu poyesedwa iwo’!

7. Kodi nchifukwa ninji kudzipereka kwaumulungu kuyenera kukulitsidwa?

7 Komabe, ife sitimabadwa ndi kudzipereka kwaumulungu, ndiponso sitimakupeza chabe chifukwa cha kukhala ndi makolo opembedza Mulungu. (Genesis 8:21) Mmalomwake, kuyenera kukulitsidwa. (1 Timoteo 4:7, 10) Tiyenera kuchitapo kanthu kuti tiwonjezere kudzipereka kwaumulungu pachipiriro ndi pachikhulupiriro chathu. Petro akuti zimenezi zimafunikira “changu chonse.” (2 Petro 1:5) Nangano, kodi ndimotani mmene tingapezere kudzipereka kwaumulungu?

Kodi Ndimotani Mmene Timapezera Kudzipereka Kwaumulungu?

8. Malinga nkunena kwa mtumwi Petro, kodi nchiyani chimene chili mfungulo yopezera kudzipereka kwaumulungu?

8 Mtumwi Petro anafotokoza za mfungulo yopezera kudzipereka kwaumulungu. Iye anati: “Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m’chidziŵitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu. Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi [kudzipereka kwaumulungu, NW], mwa chidziŵitso cha iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa iye yekha.” (2 Petro 1:2, 3) Chotero kuti tiwonjezere kudzipereka kwaumulungu pachikhulupiriro chathu ndi chipiriro, tiyenera kukula m’chidziŵitso cholongosoka, ndiko kuti, kukhala ndi chidziŵitso chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu chodzaza, kapena chokwanira.

9. Kodi ndimotani mmene tingafanizirire za mmene kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Kristu kumaloŵetseramo zoposa kungowadziŵa?

9 Kodi kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi Kristu kumatanthauzanji? Mwachionekere, kumaloŵetsamo zoposa kuwadziŵa chabe. Mwachitsanzo: Inu mungakhale mukudziŵa munthu amene mumakhala naye moyandikana ndipo mungampatsedi moni mwakumtchula dzina. Koma kodi mungamkongoze ndalama zambirimbiri? Kutalitali, pokhapokha ngati munadziŵadi kuti munthuyo ngwotani. (Yerekezerani ndi Miyambo 11:15.) Mofananamo, kudziŵa Yehova ndi Yesu molongosoka, kapena mokwanira, kumatanthauza zoposa kungokhulupirira kuti iwowo aliko ndi kudziŵa maina awo. Kuti tikhale ofunitsitsa kupirira m’mayesero kaamba ka iwo kufikiradi paimfa, tiyenera kuwadziŵa bwino kwenikweni. (Yohane 17:3) Kodi zimenezi zimaphatikizapo chiyani?

10. Kodi kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova ndi Yesu kumaphatikizapo zinthu ziŵiri ziti, ndipo chifukwa ninji?

10 Kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka, kapena chokwanira chonena za Yehova ndi Yesu kumaphatikizapo zinthu ziŵiri: (1) kuwadziŵa monga anthu​—mikhalidwe yawo, malingaliro, ndi njira​—ndipo (2) kutsanzira chitsanzo chawo. Kudzipereka kwaumulungu kumaphatikizapo kumamatirana ndi Yehova ndi mtima wonse ndipo kumeneku kumasonyezedwa ndi moyo wathu. Chifukwa chake, kuti tichipeze tiyenera kudziŵana ndi Yehova ndi kukhala ozoloŵerana ndi chifuniro chake ndi njira zimene zili zotheka kuchitidwa ndi munthu. Kuti tidziŵedi Yehova, mwa amene tinalengedwa m’chifanizo chake, tiyenera kugwiritsira ntchito chidziŵitso chotero ndi kuyesayesa kufanana naye. (Genesis 1:26-28; Akolose 3:10) Ndipo popeza kuti Yesu anatsanzira Yehova mwangwiro m’zimene ananena ndi kuchita, kudziŵa Yesu molongosoka ndiko chithandizo chamtengo wapatali m’kukulitsa kudzipereka kwaumulungu.​—Ahebri 1:3.

11. (a) Kodi tingapeze motani chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Kristu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kusinkhasinkha pazimene timaŵerenga?

11 Komabe, kodi ndimotani mmene tingapezere chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi Kristu? Mwakuphunzira mosamalitsa Baibulo ndi zofalitsidwa zina zofotokoza Baibulo.b Komabe, ngati phunziro lathu laumwini la Baibulo liti litichititse kupeza kudzipereka kwaumulungu, kuli kofunika kuti tipatule nthaŵi ya kusinkhasinkha, ndiko kuti, kupenda, kapena kuganizitsa, pazimene timaŵerenga. (Yerekezerani ndi Yoswa 1:8.) Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika? Kumbukirani kuti kudzipereka kwaumulungu ndiko kukonda Mulungu kochokera pansi pa mtima. M’Malemba, liwu lakuti kusinkhasinkha, mobwerezabwereza limagwirizanitsidwa ndi mtima wophiphiritsira​—munthu wamkati. (Salmo 19:14; 49:3; Miyambo 15:28) Pamene tisinkhasinkha moyamikira zimene timaŵerenga, zinthuzo zimaloŵa m’munthu wathu wamkati, motero zikumasonkhezera mtima wathu, ndi kusonkhezera maganizo athu. Mpokhapo pamene phunzirolo lingalimbitse kumamatirana kwathu ndi Yehova ndi kutisonkhezera kukhala ndi moyo umene umakondweretsa Mulungu ngakhale poyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta kapena mayesero ovuta.

Kusonyeza Kudzipereka Kwaumulungu Panyumba

12. (a) Malinga nkunena kwa Paulo, kodi ndimotani mmene Mkristu angachitire kudzipereka kwaumulungu panyumba? (b) Kodi nchifukwa ninji Akristu owona amasamalira makolo okalamba?

12 Choyamba kudzipereka kwaumulungu kuyenera kusonyezedwa panyumba. Mtumwi Paulo akuti: “Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” (1 Timoteo 5:4) Kusamalira makolo okalamba kuli, monga momwe Paulo akunenera, chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu. Akristu owona amapereka chisamaliro chotero osati kokha chifukwa cha kuzindikira thayolo koma chifukwa cha kukonda makolo awo. Komabe, kuposa zimenezo, iwo amazindikira za kufunika kwa thayo limene Yehova amaika pakusamalira banja la munthu. Amadziŵa bwino lomwe kuti kukana kuthandiza makolo awo m’nthaŵi ya kusoŵa kukakhala kofanana ndi ‘kukana chikhulupiriro Chachikristu.’​—1 Timoteo 5:8.

13. Kodi nchifukwa ninji kusonyeza kudzipereka kwaumulungu panyumba kungakhale kopereka vuto, koma kodi ndichikhutiro chotani chimene chimakhalapo chifukwa cha kusamalira makolo a munthuwe?

13 Zowonadi, nthaŵi zina nkovuta kuchita kudzipereka kwaumulungu panyumba. Ziŵalo za banja zingakhale zili zokhalirana patali. Ana achikulire angakhale ali ndi thayo la kusamalira mabanja awo ndipo angakhale akuvutikira kupeza ndalama. Mkhalidwe kapena ukulu wa chisamaliro chofunidwa ndi kholo ungathe kukhala cholemetsa mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwamalingaliro kwa anthu amene akupereka chisamalirocho. Komabe, pangakhale chikhutiro chenicheni m’kudziŵa kuti kusamalira makolo a munthuwe sikumachititsa kokha ‘kubwezeredwa’ komanso kumakondweretsa Uyo “amene kuchokera kwa iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina.”​—Aefeso 3:14, 15.

14, 15. Simbani za chitsanzo cha chisamaliro choperekedwa mwaumulungu chochitidwa ndi ana kwa kholo.

14 Talingalirani za chitsanzo chogwira mtima kwambiridi. Ellis ndi abale ndi alongo ake asanu ali ndi thayo lovuta la kusamalira atate wawo panyumba. “Mu 1986 atate anadwala sitiroko, imene inawapangitsa kukhala opuŵala kotheratu,” akufotokoza motero Ellis. Ana asanu ndi mmodziwo amathandizana kusamalira atate wawo, kuyambira pakuwasambitsa kufikira pakutsimikizira kuti akutembenuzidwa nthaŵi ndi nthaŵi pakama kotero kuti asachite zilonda. “Timawaŵerengera mabuku, kulankhula nawo, kuwalizira nyimbo. Sitili otsimikiza ngati amadziŵa zimene zikuchitika kwa iwo, koma timawachitira zinthu monga ngati kuti akuzindikira zonse.”

15 Kodi nchifukwa ninji anawo amasamalira atate wawo monga momwe amachitiramo? Ellis akupitiriza kuti: “Amayi atamwalira mu 1964, Atate anatilera ali okha. Panthaŵiyo, tinali azaka zoyambira pa 5 kufika pa 14. Ndiwo amene anatithandiza panthaŵiyo; tsopano nafenso tiyenera kuwathandiza.” Mwachionekere, kupereka chisamaliro chotero nkovuta, ndipo nthaŵi zina anawo amatopa nazo. “Koma timazindikira kuti mkhalidwe wa atatewo ngwakanthaŵi,” akutero Ellis. “Tikuyembekezera nthaŵiyo pamene thanzi la atate lidzabwezeretsedwa pamkhalidwe wabwino ndipo tidzagwirizanitsidwanso ndi amayi.” (Yesaya 33:24; Yohane 5:28, 29) Ndithudi, chisamaliro choperekedwa ndi mtima wonse chimenecho kwa kholo chiyenera kukondweretsa mtima wa Uyo amene amalamulira ana kulemekeza makolo awo!c​—Aefeso 6:1, 2.

Kudzipereka Kwaumulungu ndi Utumiki

16. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chifukwa chachikulu cha zimene timachita muutumiki?

16 Pamene tivomereza chiitano cha Yesu cha ‘kumtsatira mosalekeza,’ timaloŵa ntchito yaumulungu ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 16:24; 24:14; 28:19, 20) Mwachionekere, kukhala ndi phande muutumiki kuli thayo Lachikristu mu “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1) Komabe, cholinga chathu polalikira ndi kuphunzitsa chiyenera kukhala choposa kukhala ntchito kapena thayo chabe. Kukonda kwathu Yehova mwakuya kuyenera kukhala chifukwa chachikulu cha zimene timachita ndi kuchuluka kwake muutumiki. “Mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 12:34) Inde, pamene mitima yathu isefukira ndi kukonda Yehova, timasonkhezereka kuchitira umboni za iye kwa ena. Pamene kukonda kwathu Yehova kuli chisonkhezero chathu, utumiki wathu umakhala chisonyezero chenicheni cha kudzipereka kwathu kwaumulungu.

17. Kodi tingakulitse motani chisonkhezero choyenera cha utumiki?

17 Kodi ndimotani mmene tingakulitsire chisonkhezero chabwino cha utumiki? Sinkhasinkhani moyamikira pazifukwa zitatu zimene Yehova watipatsa za kumkondera. (1) Timakonda Yehova chifukwa cha zimene watichitira. Palibe chikondi choposa chimene anasonyeza popereka dipo. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) (2) Timakonda Yehova chifukwa cha zimene akutichitira tsopano lino. Tili ndi ufulu wa kulankhula ndi Yehova momasuka, amene amayankha mapemphero athu. (Salmo 65:2; Ahebri 4:14-16) Pamene tiika zinthu Zaufumu pamalo oyamba, timalandira zosoŵa zathu zochilikizira moyo. (Mateyu 6:25-33) Timalandira chakudya chauzimu choperekedwa mokhazikika chimene chimatithandiza kulimbana ndi mavuto amene timakumana nawo. (Mateyu 24:45) Ndipo tili ndi dalitso la kukhala mbali ya gulu lonse la abale la padziko lonse limene limatilekanitsa ndi dziko. (1 Petro 2:17) (3) Timakondanso Yehova chifukwa cha zimene adzatichitira. Chifukwa cha chikondi chake, ‘tagwira moyo weniweniwo’​—moyo wosatha wamtsogolo. (1 Timoteo 6:12, 19) Pamene tilingalira za mmene Yehova anatikondera, ndithudi mitima yathu idzatisonkhezera kukhala ndi phande lokwanira m’kuuza ena za iye ndi zifuno zake zamtengo wapatali! Sipafunikira ena kutiuza zonse zimene tiyenera kuchita kapena kuchuluka kwa ntchito imene tiyenera kuchita muutumiki. Mitima yathu idzatisonkhezera kuchita zimene tingathe.

18, 19. Kodi ndichopinga chotani chimene mlongo wina anagonjetsa kuti akhale ndi phande muutumiki?

18 Ngakhale poyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta, mtima wosonkhezeredwa ndi kudzipereka kwaumulungu udzasonkhezereka kunena. (Yerekezerani ndi Yeremiya 20:9.) Zimenezi zasonyezedwa m’nkhani ya Stella, mkazi Wachikristu wamanyazi kwambiri. Pamene anayamba kuphunzira Baibulo, analingalira kuti, ‘Sindidzatha kumka kunyumba ndi nyumba!’ Iye akufotokoza kuti: “Ndinkakhala chete nthaŵi zonse. Sindinkatha kufikira anthu ndi kuyamba kukambitsirana nawo.” Pamene anapitiriza kuphunzira, kukonda kwake Yehova kunakula, ndipo anakulitsa chikhumbo chachikulu chofuna kuuza ena ponena za iye. “Ndikukumbukira kuti ndinauza mphunzitsi wanga wa Baibulo kuti, ‘Ndimafuna kwambiri kulankhula, koma sindimatha kutero, ndipo zimenezo zimandivutitsa maganizo.’ Sindidzaiŵala zimene anandiuza: ‘Stella, khala woyamikira chifukwa chakuti umafuna kunena ndi ena.’”

19 Posapita nthaŵi, Stella anayamba kuchitira umboni kwa mnansi wake woyandikana naye. Ndiyeno anapanga sitepe limene linali lalikulu kwa iye​—anakhala ndi phande muutumiki wa kunyumba ndi nyumba kwanthaŵi yoyamba. (Machitidwe 20:20, 21) Iye akukumbukira kuti: “Ndinalemba ulaliki wanga. Koma ndinkachita mantha kwambiri kwakuti ngakhale kuti ndinali nawo, sindinathe kuyang’ana pazolembedwa zanga!” Tsopano, zaka 35 pambuyo pake, Stella adakali wamanyazi kwambiri mwachibadwa. Komabe, iye amakonda utumiki wakumunda ndipo akupitiriza kukhalamo ndi phande lenileni.

20. Kodi ndichitsanzo chotani chimene chikusonyeza kuti chizunzo ngakhale kuikidwa m’ndende sizingaletse Mboni zodzipatulira za Yehova kunena ndi anthu?

20 Chizunzo kapena ngakhale kuikidwa m’ndende sizingaletse Mboni zodzipereka za Yehova kunena. Talingalirani za chitsanzo cha Ernst ndi Hildegard Seliger a ku Germany. Chifukwa cha chikhulupiriro chawo, iwo anathera zaka zoposa 40 kuphatikiza pamodzi za onse aŵiri, m’misasa ya chibalo ya Nazi ndi ndende za Akomyunizimu. Ngakhale pamene anali m’ndendemo, iwo anapitirizabe kuchitira umboni kwa andende ena. Hildegard akukumbukira kuti: “Akuluakulu andende anandiyesa munthu waupandu koposa, chifukwa chakuti, monga momwe mlonda wina wachikazi ananenera, ndinkanena za Baibulo tsiku lonse. Chotero ndinaikidwa m’ndende yapansi.” Potsirizira pake atamasulidwa, Mbale ndi Mlongo Seliger anadzipereka muntchito yanthaŵi yonse ya utumiki Wachikristu. Onsewo anatumikira mokhulupirika kufikira paimfa zawo, Mbale Seliger mu 1985 ndipo mkazi wake mu 1992.

21. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tiwonjezere kudzipereka kwaumulungu pachipiriro chathu?

21 Mwakuphunzira mosamalitsa Mawu a Mulungu ndi kupatula nthaŵi ya kusinkhasinkha pazimene timaphunzira, tidzawonjezera chidziŵitso chathu cholongosoka chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Zimenezi, nazonso, zidzachititsa kupeza kwathu mlingo wokwanira wa mkhalidwe wamtengo wapatali umenewo​—kudzipereka kwaumulungu. Popanda kudzipereka kwaumulungu sitingathe kupirira mayesero osiyanasiyana amene amadza pa ife monga Akristu. Chotero tiyeni titsatire uphungu wa mtumwi Petro, tikumapitiriza ‘kuwonjezera pachikhulupiriro chathu chipiriro ndi pachipiriro chathu kudzipereka kwaumulungu.’​—2 Petro 1:5, 6, NW.

[Mawu a M’munsi]

a Ponena za eu·seʹbei·a, William Barclay amati: “Mbali ya liwuli yakutiyo seb- [phata] ndiyo imatanthauza ulemu kapena kulambira. Eu ndiliwu Lachigiriki lotanthauza bwino; motero, eusebeia ndiko kulambira, kulemekeza koperekedwa bwino ndiponso moyenera.”​—New Testament Words.

b Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, masamba 12-17, kaamba ka makambitsirano onena za mmene tingaphunzirire kuti tiwonjezere chidziŵitso chathu cha Mawu a Mulungu.

c Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1987, masamba 13-18, kaamba ka makambitsirano atsatanetsatane a mmene tingachitire kudzipereka kwaumulungu kwa makolo okalamba.

Kodi Yankho Lanu Nlotani?

◻ Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani?

◻ Kodi kugwirizana kwa chipiriro ndi kudzipereka kwaumulungu nkotani?

◻ Kodi mfungulo ya kupeza kudzipereka kwaumulungu nchiyani?

◻ Kodi ndimotani mmene Mkristu angachitire kudzipereka kwaumulungu panyumba?

◻ Kodi nchiti chimene chiyenera kukhala chifukwa chachikulu cha zimene timachita muutumiki?

[Chithunzi patsamba 18]

Chipiriro ndi kudzipereka kwaumulungu zinasonyezedwa ndi Mboni za Yehova zoikidwa m’ndende mumsasa wachibalo wa Nazi ku Ravensbrück

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena