Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ws mutu 1 tsamba 4-12
  • Chikhumbo cha Mtendere ndi Chisungiko Padziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhumbo cha Mtendere ndi Chisungiko Padziko Lonse
  • Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambi cha Ulamuliro Wotsutsa
  • Njira ya Kukhalira ndi Mtendere ndi Mulungu
  • Saali Mbusa wa “Kagulu ka Nkhosa” Kokha
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Mtendere wa Umulungu Kaamba ka Awo Ophunzitsidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
ws mutu 1 tsamba 4-12

Chaputala 1

Chikhumbo cha Mtendere ndi Chisungiko Padziko Lonse

1, 2. Kodi nchofunika chofulumira chotani chimene anthu onse ali nacho, ndipo chifukwa ninji?

MTENDERE ndi chisungiko ndizo zimene tifuna pano padziko lapansi. Kufunika kwa mkhalidwe wokhumbika wotero sikunakhale kofulumira kwambiri lerolino koposa ndi kalelonse. Zimenezi ziri zowona osati kokha kwa ife monga anthu alionse paokha komanso ndi mabanja athunthu a anthu kuzungulira dziko.

2 Ndicho chifukwa chake nzika za dziko lapansi tsopano zikukhala ndi moyo m’nthaŵi zochititsa chidwi! ‘Kodi zimenezi zingakhale zotero motani,’ inu mungafunse, ‘popeza ife tsopano tikukhala ndi moyo m’nthaŵi zochititsa mantha koposa m’mbiri ya anthu onse, nyengo ya zida zankhondo za nyukliya?’

3. (a) Kodi nchiyani chimene chanenedwa kukhala chifukwa chimene mitundu yakhalira ndi bomba lanyukliya? (b) Kodi nchiyani chimene lingaliro lachibadwa lingasonyeze?

3 Mitundu yokwanira isanu ndi itatu ikusimbidwa kukhala yokhoza kupanga bomba lanyukliya. Ndipo kukuyerekezeredwa kuti maiko 31 akhoza kukhala ndi zida zanyukliya podzafika chaka cha 2000. Chifukwa chawo cha kukhalira ndi mabomba a mkhalidwe wowopsa chikunenedwa kukhala kudzitchinjiriza, kuwopseza mitundu ina yonyamula zida mofananamo, kuwopa kuti mitundu inayo ingayilipsire ndi nyukliya. Mwa kuwona mkhalidwe wotero wa dziko, lingaliro lachibadwa lingasonyeze kuti mitundu iyenera kuvomereza kukhalira pamodzi mwa kuwopana.

4. Ngakhale kuli kwakuti Mlengi sanadodometse zoyesayesa za anthu za kufunafuna chisungiko, kodi iye ali ndi chifuno chotani m’zimenezi?

4 Komabe, kodi uli, mtendere wopangidwa ndi anthu wokha umene timafuna, limodzi ndi chitetezo chimene munthu angagaŵire? Ngakhale kuli kwakuti Mlengi sanadodometse zoyesayesa za anthu za kukhazikitsa ndi kusunga mtendere ndi chisungiko padziko lonse lapansi, iye ali ndi njira yake yotsimikizirika yakukhutiritsira chikhumbo chathu chachibadwa cha mtendere ndi chisungiko. Iye anali ndi nthaŵi yake yoikidwiratu ya kuchotsa onse ododometsa chisungiko cha okhumba kumlambira. Ha, tingakhale achimwemwe chotani nanga kudziŵa kuti nthaŵi yake ya zimenezi yayandikira!

5. Kodi nchiyani chimene wamasalmo wouziridwa ananena ponena za dziko lapansi, ndipo kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha Mlengi kaamba ka anthu?

5 Pambuyo pa zaka zikwi zochuluka za mbiri ya mavuto a anthu, kuyenera kuyembekezeredwa kuti payenera kukhala chikhumbo chachikulu cha padziko lonse lapansi cha mtendere ndi chisungiko. Dziko lapansi lakhala malo achibadwa a munthu kuyambira pachiyambi penipeni pa kukhalako kwa anthu. Wamasalmo wouziridwa ananena kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Kuyambira pachiyambi penipeni, chinali chifuno cha Mlengi wachikondi kuti munthu ayenera kusangalala ndi moyo wokwanira kwawo kudziko lapansi loperekedwa ndi Mulungu.

6. Kodi ndim’nkhani yotani mmene munthu woyamba ndi mbadwa zake akakhoza kuchita mofanana ndi Mulungu?

6 Mogwirizana ndi kunena kwa cholembedwa cha chilengedwe pa Genesis 2:7, “Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” Palibe cholengedwa china chamoyo padziko lapansi chimene chinali ndi munthu wamoyo kapena mlingo wa luso la munthu—chokhoza kuchita mofanana ndi Mulungu m’kugwiritsira ntchito ulamuliro. Ndiponso, ulamuliro umenewu sunali kudzalekezera pa cholengedwa choyamba chaumunthu koma unali kudzagwiritsiridwanso ntchito ndi ana ake.

7. Kodi ndimotani mmene Adamu anadzakhalira ndi mkazi, ndipo kodi ananenanji pamene cholengedwa changwiro chimenechi chinaperekedwa kwa iye?

7 Chifukwa cha chimenecho, Mlengi anapatsa Adamu mkazi. Mkaziyo anali kudzakhala amayi ŵa nzika zonse zamtsogolo zaumunthu padziko lapansi. Ndicho chifukwa chake, atapatsidwa cholengedwa changwiro chimenechi, mwamuna anati: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” Chifukwa chake anamutcha iye mkazi waumunthu, ’ish·shahʹ, umene uli mpangidwe wachikazi wa liwu Lachihebri lotembenuzidwa mwamuna, ndiko kuti, ’ish.—Genesis 2:21-23.

8. Kodi ndimalangizo otani amene Mlengi anapereka kwa aŵiri oyamba okwatirana aumunthu?

8 Mlengi ndi Atate wakumwamba anati kwa okwatirana oyamba: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Umenewu unali mchitidwe watsopano kotheratu m’mbiri ya zolengedwa zaluntha. Nzika zauzimu zokhala kumiyamba yosawoneka sizinachititsidwe kukhalako mwa kubalana.

9. Kodi Salmo 8:4, 5 limalongosola motani kakonzedwe ka Mulungu ka zinthu?

9 Mposadabwitsa kuti, panthaŵi ya kulengedwa kwa dziko lapansi, “nyenyezi zammaŵa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Panthaŵiyo, zonse zinali mu mtendere ndi chigwirizano m’chilengedwe chonse chathunthu. M’salmo lachisanu ndi chitatu, atachita chidwi ndi kakonzedwe ka Mulungu ka zinthu, wamasalmoyo anadzuma ponena za munthu kuti: “Munamtchepsa pang’ono ndi mulungu, munamveka iye korona waulemerero ndi ulemu.” (Vesi 4, 5) Mogwirizana ndi kunena kwa salmo limeneli, Mulungu anaika zinthu zonse pano padziko lapansi pansi pa mapazi a munthu.

Chiyambi cha Ulamuliro Wotsutsa

10. (a) Mkazi asanakhale ndi pakati pa munthu woyamba, kodi chinabuka nchiyani? (b) Motero kodi nchiyani chimene chikakhazikitsidwa pa anthu?

10 Modabwitsa, mkaziyo asanatenge pakati pa mwana woyamba waumunthu, chipanduko chinabuka m’gulu la chilengedwe chonse la Yehova Mulungu. Mkhalidwewo ukatsogolera ku kukhazikitsidwa kwa ulamuliro watsopano, ulamuliro watsopano woposa waumunthu, pa anthu—ngati anthuwo akalekanitsidwa ndi kutalikirana ndi gulu la chilengedwe chonse la Yehova. Ulamuliro wotsutsana ndi wake ukakhazikitsidwa. Zimenezi zinafunikiritsa kuti bodza loyamba linenedwe limene linaika Yehova mu mkhalidwe wosayenera.

11. Mwa kuika Yehova mu mkhalidwe wosayenera, kodi wopanduka woyamba anakhala chiyani?

11 Kunenedwa kwa bodza loyamba kunapangitsa wopandukira Mulungu ameneyo kukhala wabodza woyamba, mdyerekezi woyamba, kapena woneneza. Mosiyana kotheratu, Yesu Kristu anati: “Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo.” (Yohane 14:6) Kwa otsutsa ake achipembedzo, Yesu anati: “Muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi, pakuti mwa iye mulibe chowonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwiniwake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wabodza.”—Yohane 8:44.

12. (a) Kodi ndimotani mmene Mdyerekezi anachititsira bodza loyamba kunenedwa, ndipo kodi chiyambukiro chake chinali chotani pa Hava? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo pamene Adamu anadya chipatso choletsedwa?

12 Mwa kulankhula kudzera mwa njoka m’munda wa Edene, kapena paradaiso wachisangalalo, Mdyerekezi anachititsa bodza loyamba kunenedwa kwa mkazi woyamba. Iye ananena kuti Mlengi wa mkaziyo anali wabodza, ndipo motero anadodometsa mtendere wa maganizo a Hava. Iye anampangitsa kukhala ndi lingaliro la kusatetezereka mu mkhalidwe wake woyerekezeredwa wa kupulukira, chotero iye anadya chipatso choletsedwa. Anapeza chipambano pa mwamuna wake, Adamu, kuti adye chipatso choletsedwa limodzi naye ndipo kugwirizana naye m’kupandukira kwake Yehova Mulungu. (Genesis 3:1-6) Aŵiri okwatirana osamverawo anataya mtendere wawo ndi Mulungu ndipo anatulutsidwira kunja kwa paradaiso wachisangalalo kukakhala kunja mu mkhalidwe wosatetezereka. Aroma 5:12 amalongosola mkhalidwe womvetsa chisoni umenewu, kumati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”

13. Kodi nchosankha chotani chimene aliyense wa ife ayenera kupanga lerolino?

13 Mkhalidwe wa m’tsiku lathu ukutifunikiritsa kupanga chosankha chotsimikizirika. Chiri chosankha pakati pa ulamuliro wa wotsutsayo Satana Mdyerekezi, “Mulungu wanthaŵi ino ya pansi pano,” ndi ulamuliro wa Yehova, Mulungu Wam’mwambamwamba ndi Wamphamvuyonse wachilengedwe chonse.—2 Akorinto 4:4; Salmo 83:18.

Njira ya Kukhalira ndi Mtendere ndi Mulungu

14. Kodi ndi mtendere ndi chisungiko zotani zimene tingayambe kusangalala nazo ngakhale tsopano?

14 Modzivulaza iwo eni, anthu ambiri alibe chikhumbo cha kuvomereza kapena kukhulupirira makonzedwe a Mulungu Wamphamvuyonse kaamba ka olambira ake a kusangalala ndi mtendere ndi chisungiko ngakhale mu mkhalidwe womvetsa chisoni koposa wa zochitika za anthu umenewu. Komabe, Yehova ali “Mulungu wa mtendere,” ndipo uli mwaŵi wathu wodalitsidwa tsopano kuloŵa mu mtendere ndi chisungiko zimene sizidzalephera konse. (Aroma 16:20; Afilipi 4:6, 7, 9) Uli mtendere ndi chisungiko zimene iye amapereka ngakhale tsopano kugulu la atumiki ake a padziko lapansi, gulu lake lowoneka, m’kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake odalirika nthaŵi zonse. Ndiwo mtendere ndi chisungiko zimene tingakhale nazo kokha mwa kugwirizana ndi gulu lake lowoneka padziko lapansi.

15. Kodi kuli kupanda nzeru kuganiza kuti Mulungu ali ndi gulu, ndipo kodi Yesu Kristu anavomereza chiyani?

15 Sikungakhale kogwirizana ndi ziphunzitso zomvekera bwino za Malemba kukhulupirira kuti Mulungu alibe gulu, anthu olinganizidwa, gulu lokha limene iye amavomereza. Yesu Kristu anazindikira kuti Atate wake wakumwamba anali ndi gulu lowoneka. Kufikira pa Pentekoste 33 C.E., linali gulu Lachiyuda lokhala mu unansi wa pangano ndi Yehova Mulungu pansi pa Chilamulo cha Mose.—Luka 16:16.

16. (a) Kodi Mose anali mtetezi pakati pa ayani? (b) Kodi Mose Wamkuluyo, Yesu Kristu, ali Mtetezi pakati pa ayani?

16 Monga momwedi mtundu wakale wa Israyeli unaliri mu unansi wa pangano ndi Yehova Mulungu kupyolera mwa mtetezi Mose, chotero mtundu wa Israyeli wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” uli ndi unansi wa pangano kupyolera mwa mtetezi. (Agalatiya 6:16) Kuli monga momwedi mtumwi Paulo analembera kwa wantchito mnzake Wachikristu: “Pali Mulungu mmodzi, ndi mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu.” (1 Timoteo 2:5) Kodi Mose anali mtetezi pakati pa Yehova ndi anthu alionse? Ayi, iye anali mtetezi pakati pa Mulungu wa Abrahamu, Isake, ndi Yakobo ndi mtundu wa mbadwa zawo zakuthupi. Mofananamo, Mose Wamkulu, Yesu Kristu, saali Mtetezi pakati pa Yehova Mulungu ndi anthu onse. Iye ali Mtetezi pakati pa Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu, ndi mtundu wa Israyeli wauzimu, umene uli wolekezera kokha ku mamembala 144 000. Mtundu wauzimu umenewu uli wofanana ndi kagulu ka nkhosa ka anthu onga nkhosa a Yehova.—Aroma 9:6; Chivumbulutso 7:4.

Saali Mbusa wa “Kagulu ka Nkhosa” Kokha

17. (a) Kodi nchiyani chimene Yehova Mulungu wagaŵira Yesu Kristu kukhala? (b) Kodi Yesu ananenanji kwa awo amene adzalandira Ufumu wakumwamba?

17 M’Salmo 23:1, Mfumu Davide wa Israyeli wakale anauziridwa kunena kuti: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasoŵa.” Yehova, Mbusa Wamkulu, wagaŵira Yesu Kristu kukhala “mbusa wabwino.” (Yohane 10:11) Pa Luka 12:32, Yesu anadzitcha iyemwini kwa awo amene iye ali Mbusa wawo Wabwino kuti: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.”

18. (a) Kodi ndani lerolino amene amafanana ndi Anetini ndi ana a atumiki a Solomo amene sanali Aisrayeli? (b) Kodi iwo ali ogwirizana kwambiri ndi ayani?

18 M’nthaŵi zakale, panali osakhala Ayuda, monga Anetini ndi ana a akapolo a Solomo osakhala a Israyeli, amene anagwirizana ndi mtundu wa Israyeli. (Ezara 2:43-58; 8:17-20) Mofananamo lerolino, pali amuna ndi akazi amene ali odzipereka kotheratu kwa Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu, amene saali Aisrayeli auzimu. Komabe, iwo ali, ogwirizana ndi otsalira a Israyeli wauzimu chifukwa cha kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu “amene anadzipereka yekha chiombolo mmalo mwa onse.” (1 Timoteo 2:6) Lerolino, ameneŵa ali ndi chiŵerengero chachikulu kwambiri kuposa 144-000 cha Aisrayeli auzimu, amene adzalandira choloŵa cha Ufumu wakumwamba.

19. Kodi Yesu Kristu ananenanji kusonyeza kuti akakhala Mbusa wa oposa “kagulu ka nkhosa”?

19 Motero m’nthaŵi yokwanira ya Mulungu, Yesu Kristu anali kudzagaŵiridwa, kukhala Mbusa pagulu lalikulu kwambiri la anthu onga nkhosa amene akalandira choloŵa cha padziko lapansi kupyolera mwa iye. Ameneŵa ndiwo amene anali kuwalingalira pamene anati: “Nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” Akumalingalira “nkhosa zina” zimenezi mtumwi Yohane analembanso za Yesu kuti: “Ndiye chiombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.”—Yohane 10:16; 1 Yohane 2:2.

20. (a) Kodi ndimotani mmene chiŵerengero cha “kagulu kankhosa” chimayerekezedwera ndi otsalira a “nkhosa zina”? (b) Kodi chisamaliro chaubusa cha Mbusa Wabwino chimatanthauzanji kwa iwo onse?

20 Lerolino, pali pafupifupi 9 000 odzinenera kukhala mamembala a otsalira a “kagulu ka nkhosa” ka nkhosa zauzimu. Kumbali ina, pali anthu mamiliyoni ambiri amene agwirizana ndi otsalira odzozedwa m’kutsatira mapazi a Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. Iwo akupezedwa m’maiko oposa 200 kuzungulira dziko lonse lapansi. Kodi chisamaliro chaubusa cha Mbusa Wabwino ameneyu chimatanthauzanji kwa iwo onse? Chimatanthauza kusangalala ndi mtendere ndi chisungiko! Ngati iwo analibe mtendere pakati pawo, sipakanakhala chigwirizano chochokera pansi pa mtima ndi kugwirizana kosasweka pakati pawo. Ngati iwo analibe kuderana nkhaŵa kwachikondi pakati pawo kwa wina ndi mnzake pankhani zauzimu, iwo sakanakhala ndi chisungiko chimene amasangalala nacho. Motero, chikhumbo chawo cha mtendere ndi chisungiko padziko lonse lapansi chayamba kukwaniritsidwa ngakhale tsopano.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Mlengi ali ndi njira yake yangwiro yokwaniritsa chikhumbo cha anthu cha mtendere ndi chisungiko

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena