Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 6/15 tsamba 4-7
  • Dipo la Anthu Ambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dipo la Anthu Ambiri
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulipirira ndi Kumasula
  • Dipo Lolinganira
  • Kupereka Munthu Mmodzi Kaamba ka Ambiri
  • Makonzedwe a Dipo ndi Inuyo
  • Dipo Lolinganira kwa Onse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”
    Yandikirani Yehova
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 6/15 tsamba 4-7

Dipo la Anthu Ambiri

PA MARCH 31, 1970, anthu asanu ndi anayi a kagulu ka ku Japani kotchedwa Red Army Faction analanda ndege yonyamula anthu yomwe iwo anakweramo ikuwuluka pafupi ndi Phiri la Fuji mu Japani. Iwo anagwira chikole okweramo oposa 120 ndi ogwiramo ntchito ake ndi kulamula kuti ndegeyo iwapereke ku North Korea.

Pamene ndegeyo inatera mu Seoul, Republic of Korea, wachiŵiri kwa nduna yowona za mayendedwe m’Japani wotchedwa Shinjiro Yamamura analola kupereka moyo wake mmalo mwa ogwidwa chikolewo. Zigaŵengazo zinalola kumtenga iye monga chikole chosungitsa miyoyo yawo, ndi kumasula okweramo onse kusiyapo ogwiramo ntchito. Ndiyeno inanyamuka ulendo wopita ku Pyongyang, kumene zinakadzipereka kwa akuluakulu a boma la North Korea. Pambuyo pake, Bambo Yamamura ndi woyendetsa ndegeyo anabwerera ku Japani osavulala.

M’chochitikachi, munthu mmodzi anakhala chosinthanitsa ndi miyoyo ya ogwidwa chikole oposa 120. Izi zingathandize kuwona mmene munthu mmodzi angaperekere moyo wake monga dipo mmalo mwa anthu ambiri. Koma kuti timvetsetse chiphunzitso cha Baibulo cha dipo, tiyenera kuipenda nkhaniyi mosamalitsa kwambiri.

Choyamba, tiyenera kupenda chiyambi cha uchimo. Baibulo limanena kuti: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Kodi zinachitika motani zimenezo? Munthu wotchulidwayo ndiye Adamu, munthu woyamba kulengedwa. Mukhoza kuŵerenga nkhani ya kulengedwa kwake ndi chimene chinamchititsa kupambuka pa muyezo wa Mulungu. Zimenezi zimafotokozedwa m’machaputala atatu oyamba a Lemba la Genesis.

Cholembedwacho chimavumbula kuti panali wochititsa wosawoneka pamene Adamu anachita tchimo loyamba. Kuti akhutiritse chikhumbo chake cha ulamuliro, wochititsa wosawonekayo anakhala ndi cholinga cha kulamulira Adamu ndi ana ake onse. Wochititsayo anali Satana Mdyerekezi. Amatchedwanso “njoka yokalambayo” chifukwa chakuti anagwiritsira ntchito njoka kuchimwitsa Adamu. (Chivumbulutso 12:9) Ngakhale kuti Mlengi wachikondi wa anthu adauza Adamu kulemekeza kuyenera kwake monga Mulungu kwakusankha chabwino ndi choipa, njokayo inanyenga mkazi wa Adamu, Hava, kupandukira Mulungu. Ndiyeno mkaziyo ananyengerera mwamuna wake ndipo anapanduka iyenso. Mwa njirayo, Adamu anadzitengera ufulu wosadalira pa Mulungu, nakhala wochimwa modzifunira, ndipo moyo wotero ndiwo umene anaupatsira kwa ana ake.

Ifeyo tikuvutikabe ndi zotulukapo zake. Motani? Eya, Mlengiyo analengeza poyera kuti ngati Adamu ndi Hava anasankha dala kusamvera, chotulukapo chikakhala imfa. Mwakuchimwa, Adamu anagulitsa mtundu wonse wa anthu muukapolo ku uchimo ndi imfa.​—Genesis 2:17; 3:1-7.

Kodi ndimotani mmene mtundu wa anthu ukawomboledwa ku mkhalidwe wauchimo umenewo? Yesu Kristu anadza padziko lapansi “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri,” ndipo zimenezi zinatsegula njira yowombolera mtundu wa anthu.​—Mateyu 20:28.

Kulipirira ndi Kumasula

Baibulo limasonyeza kuti kachitidwe kakumasula mtundu wa anthu kanaphatikizapo mbali ziŵiri: (1) Kulipirira ndi (2) kumasula. Ponena za liwu Lachigiriki lakuti (lyʹtron) lomasuliridwa “dipo,” katswiri wa Baibulo Albert Barnes analemba kuti: “Liwu lakuti dipo m’lingaliro lenileni limatanthauza mtengo wolipirira kumasulidwa kwa akaidi. M’nthaŵi yankhondo, pamene akaidi atengedwa ndi adani, ndalama yofunidwa kuti amasulidwe imatchedwa dipo; ndiyo njira imene iwo amamasulidwa nayo. Chotero, chirichonse chimene chimamasula munthu ku chilango, kuvutika, kapena tchimo, chimatchedwa dipo.”

Inde, “chirichonse chimene chimamasula munthu” chikhoza kutchedwa lyʹtron. Motero liwu Lachigiriki limeneli limasonyeza kachitidwe kapena njira yakumasula.a

Mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito liwu lofanana nalo lakuti an·tiʹly·tron kusonyeza mtengo wa malipiro operekedwa monga dipo. Pa 1 Timoteo 2:6, analemba kuti “[Yesu] anadzipereka yekha [dipo lolinganira, NW] mmalo mwa onse.” Pothirira ndemanga pazimenezi, Greek and English Lexicon to the New Testament lolembedwa ndi Parkhurst limati: “Limatanthauza mtengo umene akaidi amawomboledwa nawo kwa adani; ndi kusinthana kumene moyo wa munthu umawomboledwa ndi moyo wa munthu wina.” Chigogomezero panopa chiri pa kulinganiza kapena mphamvu ya mtengo wa dipo woperekedwa wokhutiritsa chiŵeruzo chachilungamo. Kodi ndimotani mmene nsembe ya Yesu yadipo ikukhalira “dipo lolinganira”?

Dipo Lolinganira

Adamu anagulitsa mtundu wonse wa anthu, kuphatikizapo ifeyo, ku uchimo ndi imfa. Mtengo, kapena malipiro amene anapereka anali moyo wake wangwiro waumunthu, ndi kuthekera kwake kwakukhala ndi moyo kosatha. Kulipirira zimenezi, moyo wangwiro wina waumunthu​—dipo lolinganira​—unayenera kuperekedwa. Komabe, palibe munthu aliyense wobadwa kwa anthu opanda ungwiro amene akakhoza kupereka moyo wangwiro wofunikawo waumunthu. (Yobu 14:4; Salmo 51:5) Komabe, mwa nzeru zake, Mulungu anatsegula njira yotulukira mumkhalidwe umenewu. Iye anasamutsira m’mimba mwa namwali moyo wangwiro wa Mwana wake wobadwa yekha kuchokera kumwamba, kuti abadwe monga munthu wangwiro. (Luka 1:30-38; Yohane 3:16-18) Chiphunzitso chimenechi cha kubadwa kwa Yesu mwa namwali sinkhani yongopeka ndi cholinga chokweza woyambitsa chipembedzo. Mmalomwake, chimalongosola kachitidwe kanzeru ka makonzedwe a Mulungu akupereka dipo.

Kuti akwaniritse kuwombolako, Yesu anafunikira kukhala ndi mbiri yabwino nthaŵi yonse imene anali padziko lapansi. Ndipo anachitadi zimenezo. Ndiyeno anafa imfa yopereka nsembe. Mwanjirayi, Yesu analipira mtengo wa moyo wake wangwiro monga dipo lomasulira mtundu wa anthu. (1 Petro 1:19) Motero tikhoza kunena molondola kuti munthu “mmodzi anafera onse.” (2 Akorinto 5:14) Inde, “monga mwa Adamu onse anamwalira, choteronso mwa Kristu, onse akhalitsidwa ndi moyo.”​—1 Akorinto 15:22.

Kupereka Munthu Mmodzi Kaamba ka Ambiri

M’chochitika chotchulidwa poyambirirapo cha kulanda ndege, anthu ogwidwa chikolewo analibe njira iriyonse yodzimasulira, ngakhale ngati anali achuma. Panafunikira chithandizo chakunja, ndipo munthuyo wokhala chosinthanira anayenera kukwaniritsa zofunikira zakutizakuti. Zirinso motero m’njira yaikulu kwambiri ponena za dipo lofunikira kuwombola mtundu wa anthu. Wamasalmo analemba kuti: ‘Iwo . . . odzitamandira pakuchuluka kwa chuma chawo; Kuwombola mbale sangadzamuwombole, kapena kumpereka dipo kwa Mulungu: (Popeza chiwombolo cha moyo wawo ncha mtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthaŵi yonse).’ (Salmo 49:6-8) Ndithudi, mtundu wa anthu unafunikira chithandizo chakunja. Moyo wa munthu mmodzi ukakhala wokwanira kuwombola mtundu wonse wa anthu malinga ngati anakwaniritsa zofunikira zokhutiritsa chiŵeruzo chachilungamo cha Mulungu. Yesu Kristu ndiye munthu yekhayo wangwiro amene anakwaniritsa ziyeneretsozo.

Yehova Mulungu waika makonzedwe akumasula mtundu wa anthu mwakulipira dipo loperekedwa ndi Yesu Kristu. Koma Mulungu wachita zopambana pamenepo. Wapereka chiweruzo cha imfa pa Satana Mdyerekezi, amene anagwetsera mtundu wa anthu muuchimo. (Chivumbulutso 12:7-9) Posachedwapa Yehova adzabindikiritsa wamaliŵongo ameneyo nadzamuweruza pomalizira pake ‘mwakumponyera m’nyanja ya moto ndi sulfure,’ kuphiphiritsira chiwonongeko chamuyaya. (Chivumbulutso 20:1-3, 7-10, 14) Pamene cholengedwa chauzimu choipa chimenechi chidzachotsedwa, ndipo mwakugwiritsira ntchito dipo, mtundu wa anthu udzamasulidwa osati kokha ku ukapolo wa uchimo ndi imfa komanso ku chisonkhezero cha Satana. Pamenepo, pokhala utamasulidwa, ndikutinso nsembe ya dipo yagwiritsiridwa ntchito pa iwo pamlingo wokwanira, mtundu wa anthu omvera udzafikira ungwiro waumunthu.

Makonzedwe a Dipo ndi Inuyo

Pamene aphunzira ponena za nsembe ya dipo la Yesu Kristu, anthu ambiri a Kum’maŵa ayamikira kwambiri zimene Mulungu wawachitira. Kazuo, mwachitsanzo. Moyo wake unali wosuta ndi kuledzera ndi mankhwala osungunulira penti nthaŵi zonse. Akamayendetsa galimoto ali woledzera, kaŵirikaŵiri anaigunditsa ku zinthu. Atatu a mabwenzi ake anadzipha okha pambuyo pakuwonongeratu thanzi lawo. Kazuo nayenso anayesa kudzipha. Koma pambuyo pake, anayamba kuphunzira Baibulo. Posonkhezeredwa ndi chowonadi chimene anachiphunzira, anasankha kuyeretsa moyo wake. Analimbana ndi chizoloŵezi chake chowononga thupi chakusuta mankhwala osungunulira penti, ndipo panali zomgwiritsa mwala zambiri. Anakumana ndi chothetsa nzeru cha zikhumbo ziŵiri, chofuna zinthu zakuthupi ndi chofuna kuchita zinthu zabwino. Ha, anali wokondwa chotani nanga pamene anakhala wokhoza kupemphera kwa Mulungu ndi kupempha chikhululukiro pamaziko a mtengo wa nsembe ya Yesu Kristu yadipo! Mwapemphero ndi chithandizo cha mabwenzi Achikristu, Kazuo analaka vuto lake ndipo tsopano akutumikira mwachimwemwe monga minisitala wa Yehova wa chikumbumtima choyera.

Kodi mwamkumbukira Chisako, wotchulidwa pachiyambi pankhani yapitayo? Kupyolera m’phunziro la Baibulo, iyenso anafikira pakudziŵa makonzedwe achikondi a dipo. Anasonkhezeredwa kwenikweni pamene anaphunzira kuti Mulungu anapereka Mwana wake kumasula mtundu wa anthu ku uchimo. Chisako anadzipereka kwa Yehova. Ngakhale tsopano, pamsinkhu wa zaka 77, amathera pafupifupi maola 90 mwezi uliwonse akuuza ena ponena za chikondi chachikulu cha Yehova ndi chisomo chake chopambana.

Dipo liyenera kukhala lofunika kwambiri kwa inunso. Mwa dipolo, Mulungu adzatsegula njira yopezera ufulu weniweni wa mtundu wa anthu​—ufulu ku uchimo ndi imfa. Kutsogoloku kuli moyo wamuyaya m’paradaiso wapadziko lapansi kaamba ka awo amene amalandira nsembe ya Yesu Kristu yadipo. Chonde gwirizanani ndi Mboni za Yehova ndi kudzipendera nokha kuwona mmene mungamasukire ku uchimo ndi imfa kupyolera m’makonzedwe achikondi a dipo.

[Mawu a M’munsi]

a M’Malemba Achihebri, liwu lakuti pa·dhahʹ ndi mawu ena ofanana nalo amamasuliridwa “kuwombola” kapena “mtengo wowombola,” kusonyeza kumasula kumene kunaphatikizidwamo.​—Deuteronomo 9:26.

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Mwachilolezo cha Mainichi Shimbun

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena